Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI BAIBULO LILI NDI UTHENGA WOTANI?

Mulungu Akonza Zopulumutsa Anthu

Mulungu Akonza Zopulumutsa Anthu

Mulungu analonjeza Abulahamu kuti “mbewu” ija idzakhala m’modzi mwa zidzukulu zake. Kudzera mwa mbewuyi, anthu a “mitundu yonse” adzadalitsidwa. (Genesis 22:18) Patapita nthawi, Yakobo, yemwe anali mdzukulu wa Abulahamu, anasamukira ku Iguputo komwe banja lake linakula n’kukhala mtundu wa Isiraeli.

Kenako, dziko la Iguputo linayamba kulamuliridwa ndi mfumu yankhanza, yomwe inkagwiritsa ntchito Aisiraeli ngati akapolo. Mulungu anasankha Mose kuti akhale mneneri ndipo anatsogolera mtundu wa Isiraeli kuchoka ku Iguputo kukadutsa pa Nyanja Yofiira, yomwe inagawika pakati mozizwitsa. Pambuyo pake, Mulungu anapatsa Aisiraeli malamulo, kuphatikizapo Malamulo Khumi, omwe ankawatsogolera komanso kuwatetezera. Malamulowo ankatchula nsembe zimene angapereke kuti akhulululukidwe machimo. Mulungu anauzanso Mose kuti auze Aisiraeli zoti adzawatumizira mneneri wina. Mneneriyo ndi amene anali “mbewu” yolonjezedwa ija.

Patapita zaka pafupifupi 500, Mulungu analonjeza mfumu Davide kuti “mbewu” imene inalonjezedwa m’munda wa Edeni idzalamulira ufumu womwe sudzatha. Mbewuyo idzakhala Mesiya, kapena kuti Mpulumutsi wosankhidwa ndi Mulungu, ndipo idzapulumutsa anthu onse ndi kubwezeretsa Paradaiso padziko lapansi.

Kudzera mwa Davide komanso aneneri ena, Mulungu anafotokoza zambiri zimene zikanathandiza anthu kuzindikira Mesiya. Analosera zoti Mesiya adzakhala wodzichepetsa ndi wachifundo ndiponso kuti muulamuliro wake simudzakhala njala, kupanda chilungamo komanso nkhondo. Anthu onse azidzakhala mwamtendere ndi anthu anzawo komanso ndi zinyama. Zinthu zonse zomwe sizinali mbali ya cholinga cha Mulungu zidzatha, monga matenda, mavuto komanso imfa ndipo anthu amene anamwalira adzauka.

Mulungu analosera kudzera mwa mneneri Mika kuti Mesiya adzabadwira ku Betelehemu. Analoseranso kudzera mwa mneneri Danieli kuti adzachita kuphedwa ndiponso kuti Mulungu adzamuukitsa kwa akufa kenako n’kumuika monga Mfumu kumwamba. Danieli anadziwiratunso zoti Ufumu wa Mesiya udzalowa m’malo mwa maufumu onse a padziko lapansi ndipo udzalamulira mpaka kalekale. Koma kodi zimene analosera zokhudza Mesiya zinachitikadi?

Nkhaniyi yachokera m’mabuku a Genesis chaputala 22 mpaka 50; Ekisodo; Deuteronomo; 2 Samueli; Masalimo; Yesaya; Danieli; Mika; Zekariya 9:9.