Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Abusa, Tsanzirani Abusa Aakulu

Abusa, Tsanzirani Abusa Aakulu

“Khristu anavutika chifukwa cha inu, ndipo anakusiyirani chitsanzo kuti mutsatire mapazi ake mosamala kwambiri.”—1 PET. 2:21.

1, 2. (a) Kodi chimachitika n’chiyani ngati m’busa akusamalira bwino nkhosa? (b) N’chifukwa chiyani anthu ambiri m’nthawi ya Yesu anali ngati nkhosa zopanda m’busa?

NKHOSA zimasangalala ngati m’busa wake akuzisamalira bwino. Buku lina lofotokoza za kuweta nkhosa linati: “M’busa amene amangosiya nkhosa zake kuti zizidya osazisamalira bwinobwino, patangopita zaka zochepa, amaona kuti nkhosazo zayamba kufooka ndiponso kudwala.” Choncho nkhosa zimakhala zathanzi ngati m’busa wake akuzisamalira bwino.

2 N’chimodzimodzi ndi gulu la nkhosa za Mulungu. Ngati abusa amasamalira bwino nkhosa iliyonse, zinthu zimayenda bwino mumpingo. Kumbukirani kuti Yesu ataona gulu la anthu, anamva chisoni chifukwa “anali onyukanyuka ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) Kodi vuto linali chiyani? Anthu amene anapatsidwa udindo wophunzitsa anthu Chilamulo cha Mulungu anali ankhanza, opondereza ndiponso achinyengo. Atsogoleri a mu Isiraeli sankasamalira bwino anthu awo, m’malomwake ankawasenzetsa ‘katundu wolemera’ pamapewa awo.—Mat. 23:4.

3. Kodi akulu ayenera kukumbukira chiyani akamagwira ntchito yawo monga abusa?

3 Zimenezitu zikusonyeza kuti akulu, omwe ndi abusa, ali ndi udindo waukulu kwambiri. Nkhosa zimene akuweta ndi za Yehova ndiponso Yesu, yemwe ndi “mbusa wabwino.” (Yoh. 10:11) Yesu anagula nkhosazi ndi “magazi ake amtengo wapatali,” choncho anazigula “pamtengo wokwera” kwambiri. (1 Akor. 6:20; 1 Pet. 1:18, 19) Apa anasonyeza kuti amazikonda kwambiri chifukwa analolera kupereka moyo wake pogula nkhosazo. Akulu ayenera kukumbukira nthawi zonse kuti iwo  ndi abusa aang’ono amene akuyang’aniridwa ndi Mwana wa Mulungu Yesu Khristu, yemwe ndi “m’busa wamkulu wa nkhosa.”—Aheb. 13:20.

4. Kodi tikambirana chiyani m’nkhani ino?

4 Ndiyeno kodi abusawa ayenera kuweta bwanji nkhosa za Mulungu? Akhristu onse amauzidwa kuti ‘azimvera amene akutsogolera pakati pawo.’ Pomwe akulu amalangizidwa kuti ‘asamachite ufumu pa anthu amene ali cholowa chochokera kwa Mulungu.’ (Aheb. 13:17; werengani 1 Petulo 5:2, 3.) Ndiyeno funso n’kumati, Kodi akulu angatsogolere bwanji nkhosa popanda kuchita ufumu? Kapena tifunse kuti, Kodi akulu angatani kuti azikwaniritsa udindo umene Mulungu wawapatsa woyang’anira nkhosa zake popanda kupitirira malire?

“ADZAWANYAMULIRA PACHIFUWA PAKE”

5. Kodi tikuphunzira chiyani za Yehova kuchokera pa lemba la Yesaya 40:11?

5 Ponena za Yehova, mneneri Yesaya anati: “Iye adzaweta gulu lake lankhosa ngati m’busa. Adzasonkhanitsa pamodzi ana a nkhosa ndi dzanja lake, ndipo adzawanyamulira pachifuwa pake. Nkhosa zoyamwitsa adzayenda nazo mosamala.” (Yes. 40:11) Lembali likusonyeza kuti Yehova amaganizira ndiponso kusamalira nkhosa zofooka kapena zimene zikufunika kutetezedwa kwambiri mumpingo. M’busa amadziwa mavuto a nkhosa iliyonse ndipo amakhala wokonzeka kuzisamalira. N’chimodzimodzinso ndi Yehova. Iye amadziwa mavuto a munthu aliyense mumpingo ndipo ndi wokonzeka kumusamalira. Mofanana ndi m’busa amene amanyamula kamwana ka nkhosa pachifuwa pake, Yehova yemwe ndi “Tate wachifundo chachikulu,” adzatithandiza kwambiri pa nthawi ya mavuto. Adzatilimbikitsa tikakhala pamayesero aakulu kapena pamene tikufunikira thandizo lapadera.—2 Akor. 1:3, 4.

6. Kodi akulu angatsanzire bwanji Yehova?

6 Apatu akulu angaphunzire mfundo yofunika kwambiri kuchokera kwa Atate wathu wakumwamba. Mofanana ndi Yehova, iwo ayenera kudziwa mavuto a nkhosa. Akadziwa zimenezi, akhoza kuwathandiza ndiponso kuwalimbikitsa moyenera. (Miy. 27:23) Choncho akulu ayenera kulankhulana momasuka ndi Akhristu anzawo. N’zoona kuti sayenera kulowerera nkhani zina. Komabe, amakhala tcheru kuti adziwe zimene zikuchitikira abale ndi alongo mumpingo ndipo amakhala okonzeka ‘kuthandiza ofooka.’—Mac. 20:35; 1 Ates. 4:11.

7. (a) Kodi abusa ankachita chiyani ndi nkhosa za Mulungu m’nthawi ya Ezekieli ndi Yeremiya? (b) Kodi tingaphunzire chiyani pa zimene Yehova anachita podzudzula abusa osakhulupirikawo?

7 Taganizirani mmene abusa a nkhosa za Mulungu ankachitira zinthu m’nthawi ya Ezekieli ndi Yeremiya. Yehova anawadzudzula chifukwa sankasamalira bwino nkhosa zake. Popeza kuti nkhosazo zinalibe m’busa, zinkagwidwa ndi “zilombo zonse zakutchire” ndiponso zinkabalalika. Abusawo sankadyetsa nkhosazo koma ankazidyera masuku pamutu ndipo “anali kumangodzidyetsa okha.” (Ezek. 34:7-10; Yer. 23:1) Atsogoleri a matchalitchi amene amati ndi achikhristu amachitanso zomwezi ndipo Mulungu amadana nawo. Izi zikusonyeza kuti akulu ayenera kusamalira nkhosa za Yehova moyenera komanso mwachikondi.

“NDAKUPATSANI CHITSANZO”

8. Kodi akulu angatsanzire bwanji Yesu polangiza abale awo?

8 Chifukwa cha uchimo, Akhristu ena amachedwa kumvetsa zimene Mulungu  amafuna. Iwo amavutika kutsatira malangizo a m’Malemba ndipo nthawi zina amachita zinthu ngati sadziwa bwinobwino Mawu a Mulungu. Kodi akulu ayenera kutani zoterezi zikachitika? Iwo ayenera kukhala oleza mtima ngati Yesu. Paja ophunzira a Yesu ankavutana kwambiri pa nkhani yoti wamkulu ndani mu Ufumu. Yesu sanatope nawo koma anapitiriza kuwaphunzitsa ndiponso kuwalangiza kuti ayenera kukhala odzichepetsa. (Luka 9:46-48; 22:24-27) Yesu anawasambitsanso mapazi. Limeneli ndi phunziro lofunika kwambiri kwa akulu achikhristu pa nkhani ya kudzichepetsa.—Werengani Yohane 13:12-15; 1 Pet. 2:21.

9. Kodi Yesu analimbikitsa ophunzira ake kupewa mtima wotani?

9 Pa nthawi ina, Yakobo ndi Yohane anasonyeza kuti sankaona udindo wa abusa mmene Yesu ankauonera. Atumwi awiriwa ankafuna kukhala ndi malo apamwamba mu Ufumu. Koma Yesu anawathandiza powauza kuti: “Inu mukudziwa kuti olamulira a anthu a mitundu ina amapondereza anthu awo ndipo akuluakulu amasonyeza mphamvu zawo pa iwo. Sizili choncho pakati panu, koma aliyense wofuna kukhala wamkulu pakati panu ayenera kukhala mtumiki wanu.” (Mat. 20:25, 26) Atumwiwo anafunika kupewa mtima wofuna ‘kuchita ufumu’ kapena wofuna ‘kusonyeza mphamvu zawo kwa ena.’

10. (a) Kodi Yesu amafuna kuti akulu aziweta bwanji nkhosa? (b) Kodi Paulo anapereka chitsanzo chotani pa nkhaniyi?

10 Yesu amafuna kuti akulu azimutsanzira poweta nkhosa. Iwo ayenera kuchita zinthu ndi Akhristu monga atumiki anzawo osati mabwana awo. Umenewu ndi mtima umene mtumwi Paulo anali nawo. Tikutero chifukwa chakuti analangiza akulu a ku Efeso kuti: “Inu mukudziwa bwino mmene ndinali kukhalira nanu nthawi zonse kuchokera tsiku loyamba limene ndinaponda m’chigawo cha Asia. Ndinali kutumikira Ambuye monga kapolo, modzichepetsa kwambiri.” Paulo ankafuna kuti akuluwo azithandiza Akhristu anzawo modzipereka ndiponso modzichepetsa. Iye anati: “M’zinthu zonse ndakuonetsani kuti mwa kugwira ntchito molimbika chomwechi, muthandize ofookawo.” (Mac. 20:18, 19, 35) Paulo anauza Akhristu a ku Korinto kuti iye sanali wolamulira chikhulupiriro chawo koma anali wantchito mnzawo kuti akhale ndi chimwemwe. (2 Akor. 1:24) Apatu Paulo anapereka chitsanzo chabwino kwa akulu pa nkhani ya kudzichepetsa ndiponso kudzipereka.

‘GWIRANI MWAMPHAMVU MAWU OKHULUPIRIKA’

11, 12. Kodi mkulu angathandize bwanji Mkhristu mnzake kusankha zochita?

11 Akulu ayenera ‘kugwira mwamphamvu mawu okhulupirika pamene akuphunzitsa mwaluso.’ (Tito 1:9) Koma azichita zimenezi “ndi mzimu wofatsa.” (Agal. 6:1) Iwo sayenera kukakamiza abale ndi alongo kuchita zinazake koma ayenera kuyesetsa kuwalimbikitsa mowafika pamtima. Mkulu akhoza kuuza Mkhristu mnzake mfundo za m’Malemba zimene zingamuthandize kusankha zochita komanso angakambirane naye zimene mabuku athu amanena pa nkhaniyo. Akhoza kulimbikitsanso munthuyo kuganizira mmene zosankha zake zingakhudzire ubwenzi wake ndi Yehova. Mkuluyo angamuthandize kuona kufunika kopempha Mulungu kuti amutsogolere posankha zochita. (Miy. 3:5, 6) Atakambirana naye zinthuzi, angachite bwino kumulola kuti asankhe yekha zochita.—Aroma 14:1-4.

12 Udindo wa akulu ndi kuthandiza anthu  kutsatira mfundo za m’Malemba. Choncho ayenera kugwiritsa ntchito Baibulo mwaluso ndipo malangizo awo ayenera kuchokera m’Malemba. Kuchita zimenezi kumawathandiza kuti asagwiritse ntchito udindo wawo molakwika. Akuluwo ayenera kukumbukira kuti iwo ndi abusa aang’ono basi ndipo aliyense mumpingo adzayankha mlandu kwa Yehova ndi Yesu chifukwa cha zochita zake.—Agal. 6:5, 7, 8.

“MUKHALE ZITSANZO KWA GULU LA NKHOSA”

Akulu amathandiza mabanja awo kukonzekera utumiki (Onani ndime 13)

13, 14. Kodi mkulu angakhale chitsanzo chabwino m’njira ziti?

13 Mtumwi Petulo atalangiza akulu mumpingo kuti ‘asamachite ufumu pa anthu amene ali cholowa chochokera kwa Mulungu,’ anawalimbikitsa kuti ‘akhale zitsanzo kwa gulu la nkhosa.’ (1 Pet. 5:3) Kodi akulu angakhale bwanji zitsanzo kwa nkhosa? Tiyeni tione zinthu ziwiri zofunika kwa m’bale amene “akuyesetsa kuti akhale woyang’anira.” Choyamba, ayenera kukhala “woganiza bwino.” Izi zikutanthauza kuti ayenera kumvetsa mfundo za m’Mawu a Mulungu komanso ayenera kudziwa mmene angazigwiritsire ntchito pa moyo wake. Azichita zinthu moleza mtima ndipo asamapupulume posankha zochita. Chachiwiri, ayenera kukhala “woyang’anira bwino banja lake.” Izi zikutanthauza kuti ngati mkulu ali ndi banja, ayenera kupereka chitsanzo pa nkhani yoyang’anira banja lake chifukwa “ngati munthu sadziwa kuyang’anira banja lake, ndiye mpingo wa Mulungu angausamalire bwanji?” (1 Tim. 3:1, 2, 4, 5) Abale ndi alongo mumpingo akaona kuti akulu akuchita zimenezi amawadalira ndi kuwalemekeza kwambiri.

14 Akulu angakhalenso chitsanzo chabwino kwa Akhristu anzawo ngati amatsogolera pa ntchito yolalikira. Pa nkhani imeneyi, Yesu anapereka chitsanzo kwa oyang’anira. Kulalikira uthenga wabwino inali ntchito yofunika kwambiri kwa Yesu. Iye anaphunzitsanso ophunzira ake kuti azigwira ntchito imeneyi. (Maliko 1:38; Luka 8:1) Masiku ano, abale ndi alongo amasangalala akayenda limodzi ndi akulu mu utumiki. Iwo amaona khama la akuluwo pa ntchito yofunikayi ndipo amaphunzira zambiri akamaona mmene akuphunzitsira. Anthu mumpingo akaona akulu akulalikira uthenga wabwino mwakhama, ngakhale kuti amakhala otanganidwa kwambiri, amalimbikitsidwa ndipo amatengera chitsanzo chawo. Akulu akhoza kuperekanso chitsanzo chabwino akamakonzekera bwino misonkhano yampingo komanso kugwira nawo ntchito zina monga kuyeretsa ndi kukonza Nyumba ya Ufumu.—Aef. 5:15, 16; werengani Aheberi 13:7.

Oyang’anira amapereka chitsanzo chabwino mu utumiki (Onani ndime 14)

“THANDIZANI OFOOKA”

15. N’chifukwa chiyani akulu ayenera kuyendera nkhosa nthawi ndi nthawi?

15 M’busa wabwino amathandiza mwamsanga nkhosa imene yadwala kapena  yavulala. Akulunso ayenera kuthandiza mwamsanga munthu aliyense amene akuvutika kapena amene wafooka. Anthu okalamba komanso odwala angafunike kuwathandiza m’njira zina. Koma chofunika kwambiri ndi thandizo lauzimu. (1 Ates. 5:14) Achinyamata angamavutikenso polimbana ndi “zilakolako zaunyamata.” (2 Tim. 2:22) Choncho m’busa amafunika kuyendera abale ndi alongo nthawi ndi nthawi kuti azidziwa zimene zikuwachitikira ndiponso kuwalimbikitsa ndi malangizo ochokera m’Malemba. Akamachita zimenezi mwamsanga zimathandiza kuti mavuto ambiri asafike poipa kwambiri.

16. Kodi akulu angathandize bwanji nkhosa zimene zili ndi mavuto aakulu?

16 Koma bwanji ngati vutolo lafika poti likhoza kusokoneza ubwenzi wa munthuyo ndi Yehova? Pa nkhani imeneyi, Yakobo anati: “Kodi pali wina amene akudwala pakati panu? Aitane akulu a mpingo, ndipo iwo amupempherere ndi kumupaka mafuta m’dzina la Yehova. Pemphero lachikhulupiriro lidzachiritsa wodwalayo, ndipo Yehova adzamulimbitsa. Ndiponso ngati anachita machimo, adzakhululukidwa.” (Yak. 5:14, 15) Akulu akadziwa kuti Mkhristu wina akudwala mwauzimu, ayenera kumuthandiza mwamsanga ngakhale pamene ‘sanawaitane.’ Akulu akamapemphera ndi abale awo, kuwapempherera ndiponso kuthandiza amene akuvutika, amasonyeza kuti iwo ndi abusa abwino osamalira nkhosa za Mulungu.—Werengani Yesaya 32:1, 2.

17. Kodi chimachitika n’chiyani ngati akulu akutsanzira “m’busa wamkulu”?

17 Abusa akamachita chilichonse m’gulu la Yehova amayesetsa kutsanzira Yesu Khristu, yemwe ndi “m’busa wamkulu.” Akulu amenewa akamasamalira nkhosa, zinthu zimayenda bwino mumpingo ndipo nkhosazo zimakhala zathanzi. Chifukwa cha zonsezi, timayamikira ndiponso kutamanda Yehova yemwe ndi Mbusa wathu wamkulu koposa.