Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI TIMAFUNIKIRADI MULUNGU?

N’chifukwa Chiyani Ena Amaganiza Kuti Anthufe Sitifunikira Mulungu?

N’chifukwa Chiyani Ena Amaganiza Kuti Anthufe Sitifunikira Mulungu?

“Kodi inunso mumakhulupirira kuti kulibe Mulungu? Palinso anthu ena ambirimbiri omwe amakhulupirira kuti kulibe Mulungu.” Mawu amenewa analembedwa pa chikwangwani china posachedwapa. Chikwangwanichi chinalipiridwa ndi gulu lina la anthu omwe amati kulibe Mulungu. Anthu amenewa amaona kuti safunikira Mulungu pa moyo wawo.

Komanso anthu ambiri amene amakhulupirira kuti kuli Mulungu amachita zinthu ngati Mulungu kulibe. Ponena za anthu a m’tchalitchi chake, bishopu wina wakatolika dzina lake Salvatore Fisichella, ananena kuti: “Kuona zimene ifeyo timachita, munthu sangakhulupirire kuti ndife Akhristu chifukwa zochita zathu sizisiyana ndi anthu amene amati kulibe Mulungu.”

Anthu ena amaona kuti alibe nthawi yoti aziganizira za Mulungu. Amaganiza kuti Mulungu ali kutali kwambiri moti sangawathandize pa moyo wawo. Iwo amafuna Mulungu zinthu zikawavuta n’cholinga choti angowathandiza pa mavuto awowo.

Anthu ena satsatira zimene chipembedzo chawo chimaphunzitsa mwina chifukwa amaona kuti n’zosathandiza. Mwachitsanzo, ku Germany, Akatolika 76 pa 100 alionse amaona kuti sizolakwika kuti mwamuna ndi mkazi azikhalira limodzi asanakwatirane, ngakhale kuti zimenezi n’zotsutsana ndi zimene Baibulo komanso tchalitchi chawo chimaphunzitsa. (1 Akorinto 6:18; Aheberi 13:4) Koma sikuti ndi Akatolika okha amene amachita zimenezi. Akuluakulu azipembedzo zambiri akudandaula kuti anthu awo amachita zinthu ngati “anthu amene amati kulibe Mulungu.”

Zitsanzo zimenezi ndi zimene zikubweretsa funso lakuti: Kodi anthufe timafunikiradi Mulungu? Nkhani imeneyi si yachilendo. Inayamba kalekale ndipo inalembedwa koyambirira kwa Baibulo. Kuti tipeze yankho la funso limeneli, tiyeni tikambirane nkhani zingapo zimene zinatchulidwa m’buku la Baibulo la Genesis.