Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Ulamulilo wa Yesu wa Zaka 100 Wakupindulitsani Bwanji?

Kodi Ulamulilo wa Yesu wa Zaka 100 Wakupindulitsani Bwanji?

“Nchito zanu n’zazikulu ndi zodabwitsa, inu Yehova Mulungu, . . . Mfumu yamuyaya.”—CHIV. 15:3.

1, 2. Kodi Ufumu wa Mulungu udzakwanilitsa ciani? Nanga tingatsimikizile bwanji kuti Ufumu umenewo udzabwela?

 KUCIYAMBI kwa caka ca 31 C.E., Yesu Kristu ali paphili lina limene lili pafupi ndi mzinda wa Kaperenao, anaphunzitsa otsatila ake kupemphela kuti: “Ufumu wanu ubwele.” (Mat. 6:10) Masiku ano, anthu ambili amakaikila ngati Ufumu umenewu udzabweladi. Komabe, ife tili ndi cikhulupililo cakuti Yehova adzayankha mapemphelo athu opempha Ufumu wake kuti ubwele.

2 Yehova adzagwilitsila nchito Ufumu kugwilizanitsa banja lake la kumwamba ndi la padziko lapansi. Colinga ca Mulungu cimeneci cidzakwanilitsidwa. (Yes. 55:10, 11) Ndipo zinthu zocititsa cidwi zimene zakhala zikucitika kwa zaka 100 zapitazi, zimaonetsa kuti Yehova ndi Mfumu. Iye akucitila atumiki ake okhulupilika mamiliyoni ambili nchito zazikulu ndi zodabwitsa. (Zek. 14:9; Chiv. 15:3) Komabe, mfundo yakuti Yehova ndi Mfumu ndi yosiyana ndi kubwela kwa Ufumu wa Mulungu umene Yesu anatiphunzitsa kupempha. Kodi zocitika ziŵilizi zikusiyana motani? Nanga zimatikhudza bwanji?

MFUMU YOIKIDWA NDI YEHOVA ICITAPO KANTHU

3. (a) Kodi Yesu anaikidwa liti kukhala Mfumu? Nanga ndi kuti kumene anayambila kulamulila? (b) Kodi mungapeleke umboni wotani wosonyeza kuti Ufumu unakhazikitsidwa mu 1914? (Onani mau a munsi.)

3 Cakumapeto kwa zaka za m’ma 1800, atumiki a Yehova anayamba kumvetsetsa tanthauzo la ulosi wa Danieli umene analemba zaka zoposa 2,500 zapitazo. Ulosi umenewo umati: “M’masiku a mafumu amenewo, Mulungu wakumwamba adzakhazikitsa ufumu umene sudzawonongedwa ku nthawi zonse.” (Dan. 2:44) Kwa zaka zambili ophunzila Baibo anali kunena kuti caka ca 1914 cidzakhala capadela. Anthu ambili panthawiyo anali ndi ciyembekezo cakuti zinthu zidzakhala bwino m’tsogolo. Wolemba nkhani wina anati: “M’caka ca 1914, dziko linali kuoneka kuti zinthu mtsogolo zidzakhala bwino kwambili.” Kenako m’caka cimeneco, nkhondo yoyamba ya padziko lonse inayamba ndipo ulosi wa m’Baibo unakwanilitsidwa. Njala, zivomezi, milili ndi kukwanilitsidwa kwa maulosi ena a m’Baibo ndi umboni wamphamvu wosonyeza kuti Yesu Kristu anayamba kulamulila kumwamba monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu mu 1914. a Mwa kuika Mwana wake monga Mfumu Mesiya, Yehova anakhaladi Mfumu mwa njila ina.

4. Kodi cinthu coyamba cimene Mfumu yatsopano inacita cinali ciani? Nanga kodi inacita ciani pambuyo pake?

4 Cinthu coyamba cimene Mfumu ya Mulungu yatsopano inacita, cinali kucita nkhondo ndi Satana, Mdani wamkulu wa Atate wake. Yesu ndi angelo ake anacotsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba. Zimenezi zinacititsa kuti kumwamba kukhale cisangalalo cacikulu koma padziko lapansi panakhala mavuto ambili kuposa kale lonse. (Ŵelengani Chivumbulutso 12:7-9, 12.) Kenako, Mfumu yatsopanoyo inayamba kuyenga, kuphunzitsa, ndi kulinganiza atumiki ake padziko lapansi kuti acite cifunilo ca Mulungu. Atumiki amenewo anatsatila malangizo a Yesu. Koma kodi ife tikuphunzilapo ciani?

MFUMU MESIYA AYENGA NZIKA ZAKE ZOKHULUPILIKA

5. Kodi ndi kuyeletsa kotani kumene kunacitika kuyambila 1914 mpaka kuciyambi kwa 1919?

5 Pambuyo pakuti Mfumu yatsopanoyo yacotsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba, Yehova analamula Yesu kuti ayendele ndi kuyenga otsatila ake mwakuuzimu padziko lapansi. Mneneli Malaki ananena kuti kumeneku kunali kuyeletsa kwa kuuzimu. (Mal. 3:1-3) Ndipo mbili imaonetsa kuti zimenezi zinacitika kuyambila mu 1914 mpaka kuciyambi kwa 1919. b Kuti tikhale mbali ya banja la Yehova, tiyenela kukhala aukhondo kapena kuti oyela. (1 Pet. 1:15, 16) Tiyenela kupewa kudetsedwa ndi cipembedzo conama kapena ndi ndale za m’dzikoli.

6. Kodi cakudya cakuuzimu cimapelekedwa bwanji? N’cifukwa ciani cakudya cimeneci n’cofunika?

6 Ndiyeno, Yesu anagwilitsila nchito mphamvu zake monga Mfumu kuika “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” Kapolo ameneyu amapeleka cakudya cabwino cakuuzimu nthawi zonse kwa anthu onse amene ali mu “gulu limodzi” limene Yesu akuyang’anila. (Mat. 24:45-47; Yoh. 10:16) Kuyambila mu 1919, kagulu kocepa ka abale odzodzedwa, mokhulupilika kakhala kakugwila nchito yofunika kwambili yopatsa “anchito apakhomo” cakudya cakuuzimu. Cakudya cakuuzimu cimene timalandila kudzela mwa kapolo ameneyu, cimatithandiza kulimbitsa cikhulupililo cathu. Cimatithandizanso kukhalabe oyela mwakuuzimu, mwamakhalidwe, mwamaganizo ndi mwakuthupi. Cifukwa ca cakudya cimeneci, timakhalanso ophunzitsidwa bwino ndiponso okonzekela kucita nchito yofunika kwambili padziko lapansi imene ndi yolalikila. Kodi mukugwilitsila nchito mokwanila zinthu zimenezi?

MFUMU IPHUNZITSA ANTHU AKE KULALIKILA PADZIKO LONSE

7. Kodi Yesu anayamba kugwila nchito yofunika iti pamene anali padziko lapansi? Nanga nchito imeneyi inafunika kugwilidwa mpaka liti?

7 Pamene Yesu anayamba utumiki wake padziko lapansi, iye anakamba kuti: “Ndiyenela kukalengeza uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumizinda inanso, cifukwa ndi zimene anandituma kudzacita.” (Luka 4:43) Kwa zaka zitatu ndi theka, Yesu anali kuona nchito yolalikila uthenga wabwino imeneyi kukhala yofunika kwambili. Iye analangiza ophunzila ake kuti: “Pitani ndi kulalikila kuti, ‘Ufumu wakumwamba wayandikila.’” (Mat. 10:7) Ataukitsidwa, Yesu ananenelatu kuti otsatila ake adzalengeza uthenga umenewu “mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Ndipo anawalonjezanso kuti iye adzawacilikiza panchito yofunika imeneyo mpaka masiku athu ano.—Mat. 28:19, 20

8. Kodi Mfumu inalimbikitsa motani atumiki ake a padziko lapansi kuyamba kulalikila?

8 Podzafika mu 1919, nchito yolalikila ‘uthenga wabwino wa Ufumu’ inapita patsogolo kwambili. (Mat. 24:14) Yesu anali kulamulila kumwamba ndipo anali atasonkhanitsa kagulu kocepa ka atumiki ake oyeletsedwa padziko lapansi. Iwo analabadila ndi mtima wonse malangizo a Yesu akuti alalikile padziko lonse lapansi uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu umene unakhazikitsidwa. (Mac. 10:42) Mwacitsanzo, anthu ocilikiza Ufumu okwana pafupi-fupi 20,000 anasonkhana pa msonkhano waukulu wa mayiko ku Cedar Point, Ohio, U.S.A., mu September 1922. Tangoganizilani mmene io anasangalalila pamene M’bale Rutherford anakamba nkhani ya mutu wakuti “Ufumu Wakumwamba Wayandikila,” ndipo anati: “Onani, Mfumu yayamba kale kulamulila ndipo inu ndinu atumiki ake olengeza ufumuwo. Conco lengezani, lengezani, lengezani Mfumu ndi ufumu wake.” Tsiku lotsatila, anthu okwana 2000 anatengako mbali pa nchito yolalikila ndipo ena anayenda mtunda wamakilomita 72 kucokela pamalo a msonkhano. Pambuyo pa nchitoyi, m’bale wina anati: “Sindidzaiŵala cilengezo cakuti tifunika kulengeza Ufumu ndiponso cangu cimene anthu amene anapezeka pa msonkhanowo anaonetsa.” Ndipo anthu ena ambili ananenanso mau ofananawo.

9, 10. (a) Kodi pali masukulu otani amene amatithandiza pa nchito yolalikila? (b) Kodi inuyo mwapindula bwanji ndi maphunzilo amene mwalandila?

9 Podzafika mu 1922, panali ofalitsa Ufumu acangu oposa 17,000 amene anali kulalikila m’maiko 58 padziko lonse lapansi. Komabe, anthu amenewo anafunika kuphunzitsidwa. M’nthawi za atumwi, Mfumu yoikidwilatu imeneyi inauza ophunzila ake uthenga umene anayenela kulalikila, njila zolalikilila ndi kumene anayenela kulalikila. (Mat. 10:5-7; Luka 9:1-6; 10:1-11) Motsatila citsanzo cimeneci, Yesu amaonetsetsa kuti anthu onse amene amatengako mbali pa nchito yolalikila Ufumu, alandila malangizo ndi kutinso ali ndi zida zogwilitsila nchito n’colinga cakuti alalikile mofika pamtima. (2 Tim. 3:17) Kudzela mumpingo wacikristu, Yesu akuphunzitsa atumiki ake mmene angagwilile nchito yolalikila. Njila imodzi imene iye akucitila zimenezi ndi kudzela m’Sukulu ya Ulaliki. Sukuluyi imacitika m’mipingo yoposa 111,000 padziko lonse lapansi. Cifukwa cogwilitsila nchito zimene amaphunzila, ofalitsa oposa 7 miliyoni ndi okonzeka kulalikila ndi kuphunzitsa m’njila imene imafika pamtima “anthu osiyana-siyana.”—Ŵelengani 1 Akorinto 9:20-23.

10 Kuonjezela pa Sukulu ya Ulaliki, palinso masukulu ena ophunzitsa Baibo amene akonzedwa kuti aphunzitse akulu mumpingo, apainiya, abale osakwatila, Akristu apabanja, a m’Komiti ya Nthambi ndi akazi ao, oyang’anila oyendela ndi akazi ao ndiponso amishonale. c Ophunzila a m’kalasi ina ya Sukulu Yophunzitsa Baibo ya Akristu Ali Pabanja anayamikila kwambili maphunzilo amene analandila. Iwo anati: “Maphunzilo apadela amene talandila akulitsa cikondi cathu pa Yehova ndipo ndife okonzeka kukathandizanso ena.”

11. Kodi olengeza Ufumu akwanitsa bwanji kupitiliza kulalikila mosasamala kanthu za kuukila kwa Satana?

11 Mdani wathu Satana amaona nchito yaikulu yolalikila ndi kuphunzitsa za Ufumu imene ikucitika. Iye amafuna kulepheletsa nchito yathu yolalikila uthenga wa Ufumu, ndipo amacita zimenezi mwa kugwilitsila nchito njila zooneka ndi zobisika. Koma zoyesa-yesa za Satana sizingaphule kanthu. Yehova anaika Mwana wake “pamwamba-mwamba kuposa boma lililonse, ulamulilo uliwonse, amphamvu onse, ambuye onse.” (Aef. 1:20-22) Monga Mfumu, Yesu amagwilitsila nchito mphamvu zake kuti ateteze ndi kutsogolela ophunzila ake ndi colinga cakuti cifunilo ca Atate wake cicitike. d Uthenga wabwino ukulalikidwa, ndipo anthu oona mtima mamiliyoni akuphunzitsidwa njila za Yehova. Ndi mwai wamtengo wapatali kutengako mbali m’nchito yaikulu kwambili imeneyi.

MFUMU ILINGANIZA NZIKA ZAKE KUTI ZIGWILE NCHITO YOCULUKA

12. Kodi ndi kusintha kotani kumene kwacitika m’gulu la Mulungu kocokela pamene Ufumu unakhazikitsidwa?

12 Kucokela pamene Ufumu unakhazikitsidwa mu 1914, Yesu wakhala akukonza zinthu kuti atumiki a Mulungu akhale oyenelela kucita cifunilo ca Atate wake. (Ŵelengani Yesaya 60:17.) M’caka ca 1919, wotsogolela utumiki anaikidwa mumpingo uliwonse kuti azitsogolela pa nchito yolalikila. M’caka ca 1927, nchito yolalikila kunyumba ndi nyumba pa Sondo inalinganizidwa. Mu 1931, atumiki a Yehova anayamba kudziŵika ndi dzina la m’Malemba lakuti Mboni za Yehova, ndipo zimenezi zinawapangitsa kucita zambili pa nchito ya Ufumu. (Yes. 43:10-12) Kuyambila mu 1938, kuika paudindo anthu mumpingo mwa kucita voti kunatha, ndipo anayamba kuikidwa paudindo motsatila mfundo za m’Malemba. M’caka ca 1972, udindo woyang’anila mpingo unapatsidwa ku bungwe la akulu m’malo mwa m’bale mmodzi woyang’anila mpingo. Akulu ndi atumiki othandiza analimbikitsidwa ‘kuweta nkhosa za Mulungu zimene anazisiya m’manja mwao.’ (1 Pet. 5:2) M’caka ca 1976, Bungwe Lolamulila linalinganizidwa kukhala makomiti 6 n’colinga cakuti aziyang’anila nchito ya Ufumu padziko lonse lapansi. Mfumu yoikidwa ya Yehova, yakhaladi ikulinganiza nzika za Ufumu kuti zizicita zinthu mogwilizana ndi njila za Mulungu.

13. Kodi mwalimbikitsidwa bwanji ndi zimene Mfumu Mesiya wakwanitsa kucita mkati mwa ulamulilo wake wa zaka 100?

13 Tangoganizilani zimene Mfumu Mesiya wacita mkati mwa zaka 100 zoyambilila za ulamulilo wake. Iye wayeletsa gulu la anthu odziŵika ndi dzina la Yehova. Iye wakhala akutsogolelanso nchito yolalikila uthenga wa Ufumu m’maiko okwana 239 ndipo waphunzitsanso anthu mamiliyoni ambili ponena za njila za Yehova. Yesu wagwilizanitsanso anthu okhulupilika oposa 7 miliyoni, ndipo onse adzipeleka kucita cifunilo ca Atate wake. (Sal. 110:3) Kunena zoona, nchito za Yehova kudzela mu Ufumu wa Mesiya n’zazikulu ndiponso zodabwitsa. Komabe, tikuyembekezelanso zocitika zina zosangalatsa mtsogolo.

MADALITSO AMENE TIKUYEMBEKEZELA MU UFUMU WA MESIYA

14. (a) Kodi n’ciani cimene timapempha Mulungu kucita tikamapemphela kuti “Ufumu wanu ubwele”? (b) Kodi lemba lathu la caka ca 2014 ndi liti, ndipo n’cifukwa ciani ndi loyenela?

14 Yehova anaveka Mwana wake, Yesu Kristu, cisoti cacifumu monga Mfumu Mesiya mu 1914. Koma cocitika cimeneci sicinali yankho lokwanila la pemphelo lathu lakuti “Ufumu wanu ubwele.” (Mat. 6:10) Baibo inanenelatu kuti Yesu ‘adzapita kukagonjetsa anthu pakati pa adani ake.’ (Sal 110:2) Maboma a anthu amene Satana akulamulila, akutsutsabe Ufumu. Tikamapemphela kuti Ufumu wa Mulungu ubwele, timakhala tikupempha Mulungu kuti Mfumu Mesiya pamodzi ndi olamulila anzake abwele kudzathetsa ulamulilo wa anthu ndi kuononga anthu onse amene amatsutsa Ufumuwo. Cocitika cimeneci cidzakwanilitsa mau a pa Danieli 2:44 amene amasonyeza kuti Ufumu wa Mulungu “udzaphwanya ndi kuthetsa maufumu ena onsewo.” Ufumu umenewu udzaononga adani a Ufumuwo amene ndi maboma andale. (Chiv. 6:1, 2; 13:1-18; 19:11-21) Kwangotsala kanthawi kocepa kuti zimenezi zicitike. Ndipo caka cino ca 2014, Ufumu wa Mulungu wakwanitsa zaka 100 kucokela pamene unakhazikitsidwa kumwamba. M’pake kuti lemba la caka ca 2014 ndi Mateyo 6:10, limene limati: “Ufumu wanu ubwele.”

Lemba lathu la caka ca 2014: Ufumu wanu ubwele.”Mateyu 6:10

15, 16. (a) Kodi ndi zinthu zocititsa cidwi ziti zimene zidzacitika mkati mwa Ulamulilo wa Zaka 1,000? (b) Kodi ndi cinthu comaliza citi cimene Yesu adzacita monga Mfumu Mesiya? Nanga zimenezo zidzakhudza bwanji colinga ca Yehova?

15 Akadzaononga adani a Mulungu, Mfumu Mesiya adzaponya Satana ndi ziŵanda zake kuphompho kwa zaka 1,000. (Chiv. 20:1-3) Popeza kuti Satana ndi ziŵanda zake sadzakhalako, Ufumuwo mwamsanga udzathandiza anthu kupindula ndi dipo lansembe la Yesu ndipo udzacotsa mavuto onse amene timakumana nao cifukwa ca ucimo wa Adamu. Mfumuyo idzaukitsa anthu mamiliyoni ambili amene ali kumanda ndi kupanga makonzedwe akuti anthu oukitsidwawo aphunzitsidwe za Yehova. (Chiv. 20:12, 13) Dziko lonse lapansi lidzakhala paladaiso monga mmene munda wa Edeni unalili. Anthu onse okhulupilika adzakhala angwilo.

16 Pambuyo pa Ulamulilo wa Kristu wa Zaka 1,000, cifunilo ca Yehova cokhudza dziko lapansi cidzakwanilitsidwa. Ndiyeno Yesu adzabwezela Ufumu kwa Atate wake. (Ŵelengani 1 Akorinto 15:24-28.) Sipadzafunikilanso munthu wina kukhala mkhalapakati wathu pakati pa ife ndi Yehova. Ana a Mulungu onse a kumwamba ndi a padziko lapansi adzagwilizana ndi Atate wao wa kumwamba monga banja limodzi.

17. Kodi ndinu wotsimikiza mtima kucita ciani kaamba ka Ufumu?

17 Zinthu zosangalatsa zimene zakhala zikucitika mkati mwa zaka 100 za ulamulilo wa Ufumu zikutitsimikizila kuti Yehova akulamulila ndipo colinga cake cokhudza dziko lapansi cidzakwanilitsidwa. Tiyeni tipitilizebe kukhala atumiki ake okhulupilika ndi kulengeza za Mfumu ndi Ufumu wake. Tili ndi cikhulupililo cakuti Yehova posacedwapa adzayankha pemphelo lathu locokela pansi pamtima lakuti: “Ufumu wanu ubwele.”

a Onani buku lakuti Zimene Baibo Imaphunzitsa M’ceni-ceni patsamba 88 mpaka 92.

b Onani Nsanja ya Mlonda ya July 1, 2013, tsamba 28 mpaka 29, ndime 12.

c Onani Nsanja ya Olonda ya September 15, 2012, tsamba 13-17 pamutu wakuti “Sukulu Zophunzitsa Atumiki a Mulungu Zimasonyeza Kuti Yehova Amatikonda.”

d Kuti muone zitsanzo za milandu imene yatiyendela bwino m’maiko osiyana-siyana, onani Nsanja ya Olonda ya December 1, 1998 tsamba 19 mpaka 22.