Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kulambira kwa Pabanja Kuzikhala Kosangalatsa

Kulambira kwa Pabanja Kuzikhala Kosangalatsa

Bambo wina wa ku Brazil anati: “Tikayamba Kulambira kwa Pabanja, sitisiya mpaka usiku. Pena ndimachita kunena kuti, ‘Basi tisiye.’” M’bale wina ku Japan ananena kuti akayamba Kulambira kwa Pabanja, mwana wake wa zaka 10 safuna kuti asiye. Pofotokoza chifukwa chake, m’baleyo anati: “Pa nthawi imeneyi amalimbikitsidwa ndipo amanjoya.”

Koma izi si zimene zimachitika m’mabanja ena ndipo ana ena sasangalala ikafika nthawi ya Kulambira kwa Pabanja. Kodi vuto limakhala chiyani? Bambo wina wa ku Togo anati: “Kulambira Yehova kuyenera kukhala kosangalatsa.” Ngati sikusangalatsa mwina vuto ndi mmene mukuchitira kulambirako. Koma mabanja ambiri aona kuti tsiku la Kulambira kwa Pabanja likhoza kukhala “losangalatsa kwambiri” ngati mmene buku la Yesaya limanenera za tsiku la Sabata.—Yes. 58:13, 14.

Abale ambiri azindikira kuti Kulambira kwa Pabanja kumakhala kosangalatsa kwambiri ngati aliyense m’banjamo ali womasuka. Ralf, yemwe ali ndi ana aakazi atatu wamwamuna m’modzi, ananena kuti akamachita kulambira kwa pabanja zimangokhala ngati akucheza osati kuphunzira ndipo aliyense amalankhula momasuka. N’zoona kuti nthawi zina zimavuta kuthandiza aliyense kuti asangalale komanso azilankhulapo momasuka. Mlongo wina anati: “Nthawi zina ndimatopa kwambiri moti ndimalephera kuchititsa Kulambira kwa Pabanja m’njira yosangalatsa.” Kodi ndi zinthu ziti zimene zingathandize kuti Kulambira kwa Pabanja kuzikhala kosangalatsa?

MUZISINTHASINTHA

M’bale wina wa ku Germany, amene ali ndi ana awiri ananena kuti: “Tikufunika kumasinthasintha.” Natalia amene ali ndi ana awiri anati: “Chofunika kwambiri ndi kusinthasintha osati kumangochita zimodzimodzi.” Mabanja ambiri amachita zinthu zosiyanasiyana pa  Kulambira kwa Pabanja. Mwachitsanzo, m’bale wina wa ku Brazil dzina lake Cleiton, amene ali ndi ana awiri achinyamata, anati: “Zimathandiza kuti muphunzire zambiri osatopa ndipo aliyense m’banjamo amakhala ndi zochita.” Makolo angaganizire mwana aliyense payekha n’kumachita zinthu zosiyanasiyana mogwirizana ndi misinkhu ya anawo. Makolo angasankhe nkhani imene ikukhudza aliyense m’banjamo ndipo angathe kumasinthasintha nkhani zoti akambirane komanso kachitidwe kake.

Kodi mabanja ena amatani kuti azichita zinthu zosiyanasiyana? Mabanja ena amayamba ndi kuimba nyimbo zingapo zotamanda Yehova. Juan wa ku Mexico ananena kuti: “Nyimbo zimathandiza kuti maganizo athu akhazikike tisanayambe kuphunzira.” Ana ake awiri ndi amene amasankha nyimbo zogwirizana ndi nkhani zimene aphunzire pa kulambirako.

Sri Lanka

Mabanja ena amawerengera limodzi Baibulo. Iwo amagawana mawu a anthu osiyanasiyana kuti azisinthanasinthana powerenga. M’bale wina wa ku Japan ananena kuti, “Poyamba ndinkaona ngati zachibwana.” Koma ana awo awiri ankasangalala kuona makolo awo akuchitira nawo limodzi zimenezi. Mabanja ena amachita masewero a nkhani za m’Baibulo. M’bale wina wa ku South Africa, dzina lake Roger, amene ali ndi ana awiri ananena kuti, “Kawirikawiri ana amaona mfundo zina m’nkhani ya m’Baibulo zimene makolofe sitinazione.”

South Africa

Njira ina yothandiza kuti muzichita zinthu zosiyanasiyana ndi kugwirira limodzi ntchito yopanga chifaniziro cha chingalawa cha Nowa kapena kachisi wa Solomo. Ntchito imeneyi ingafune kuti mufufuze mfundo zosiyanasiyana m’mabuku athu, ndipo zimenezi zingakhale zosangalatsa kwambiri. Mwachitsanzo, banja lina ku Asia linkachita masewera ofanana ndi bawo koma oyenda motsatira maulendo a umishonale a Paulo. Mabanja ena amachita masewera omwewo koma otsatira ulendo wa Aisiraeli pochoka ku Iguputo. Mnyamata wina wa zaka 19 wa ku Togo dzina lake Donald anati: “Kusinthasintha zochita pa Kulambira kwa Pabanja kunathandiza kuti kulambirako kuzikhala kosangalatsa komanso kuti tonse m’banja tizisangalala.” Kodi ndi zinthu ziti zimene mungachite kuti kulambira kwanu kwa pabanja kuzikhala kosangalatsa?

United States of America

KUKONZEKERA N’KOFUNIKA

N’zoona kuti kusinthasintha kumathandiza kuti Kulambira kwa Pabanja kukhale kosangalatsa. Koma kuti zimene tikuphunzirazo zikhale zothandiza aliyense ayenera kumakonzekera. Nthawi zina ana amatopa msanga, choncho bambo ayenera kuganizira mofatsa nkhani imene akufuna kukaphunzira n’kuikonzekera bwino. M’bale wina ananena kuti, “Ndikakonzekera, aliyense amasangalala ndi phunzirolo.” M’bale wina wa ku Germany amauza onse m’banja lake zimene adzaphunzire milungu yotsatira. M’bale wina wa ku Benin, amene ali ndi ana 6, amaperekeratu mafunso oti adzakambirane akadzamaliza kuonerera DVD pa Kulambira kwa Pabanja. Izi zikusonyeza kuti kukonzekera kumathandiza kuti Kulambira kwa Pabanja kukhale kosangalatsa.

Anthu onse m’banja akadziwiratu zimene adzaphunzire mlungu wotsatira, amakambirana zimenezo tsikulo lisanafike, ndipo zimenezi zimathandiza kuti aziyembekezera tsikulo mwachidwi. Ngati aliyense m’banjamo wauzidwa zoti adzachite, amaona kuti ali ndi udindo pa tsikulo.

MUSAMACHITE MODUMPHADUMPHA

Mabanja ambiri zimawavuta kuti azichita Kulambira kwa Pabanja mlungu uliwonse.

Abale ena amagwira ntchito nthawi yaitali kuti apeze zofunika pabanja lawo. Mwachitsanzo, m’bale wina ku Mexico amapita kuntchito 6 koloko m’mawa ndipo amaweruka 8 koloko madzulo. Nthawi zinanso pamafunika kusintha tsiku la Kulambira kwa Pabanja chifukwa chakuti mukufunika kuchita zinthu zina zokhudzanso kulambira Yehova.

Koma tiyenera kuyesetsabe kuti tisamachite modumphadumpha. Kamtsikana kena ka zaka 11 ku Togo kananena kuti banja lawo limayesetsa pa nkhaniyi. Iye anati: “Timaonetsetsa kuti Kulambira kwa Pabanja kusalephereke ndipo nthawi zina timalolera kuchita usiku ngati panali zochita zina.” Mabanja ena amasankha masiku oyambirira a mlungu kuti azichita Kulambira kwa Pabanja. Amachita dala zimenezi kuti akalephera pa tsikulo achite tsiku lina koma m’kati mwa mlungu womwewo.

Kumbukirani kuti zimene timachita pa tsikuli ndi kulambira Yehova. Choncho mlungu uliwonse, mawu apakamwa pa munthu aliyense m’banja mwanu ayenera kukhala ngati ‘ana amphongo a ng’ombe amene mukuwapereka nsembe’ kwa Yehova. (Hos. 14:2) Yesetsani kuti aliyense m’banja mwanu azisangalala pa nthawi imeneyi chifukwa “chimwemwe chimene Yehova amapereka ndicho malo anu achitetezo.”—Neh. 8:9, 10.