Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kodi Yesu adzachita chiyani m’tsogolomu?

M’chaka cha 33 C.E., Yesu anaphedwa, kuukitsidwa kenako n’kukwera kumwamba. Patapita nthawi Yesu anapatsidwa mphamvu zolamulira monga Mfumu. (Danieli 7:13, 14) M’tsogolomu, Yesu monga Mfumu adzabweretsa mtendere padzikoli komanso adzathetsa umphawi.—Werengani Salimo 72:7, 8, 13.

Monga Mfumu, Yesu adzayeretsa dziko lopanda chilungamoli

Yesu monga wolamulira, adzachitira anthu zinthu zodabwitsa padzikoli. Adzagwiritsa ntchito mphamvu zimene Atate wake anamupatsa ndipo adzathandiza anthu kukhala angwiro. Anthu adzasangalala kwambiri padziko lapansili chifukwa sadzakalamba komanso kufa.—Werengani Yohane 5:26-29; 1 Akorinto 15:25, 26.

Kodi Yesu akuchita chiyani panopa?

Panopa Yesu akutsogolera ntchito yolalikira imene otsatira ake oona akugwira padziko lonse. Otsatira akewa amafikira anthu n’cholinga chowauza zimene Baibulo limanena zokhudza Ufumu wa Mulungu. Yesu ananena kuti adzapitirizabe kutsogolera ntchito imeneyi mpaka pamene Ufumu wa Mulungu udzawononge maboma a anthu.—Werengani Mateyu 24:14; 28:19, 20.

Yesu akuthandizanso anthu kuti akhale ndi moyo wabwino pogwiritsa ntchito mpingo woona wachikhristu. Iye adzapitirizabe kutsogolera Akhristu amenewa mpaka pa nthawi imene azidzawononga dziko loipali, n’kuwalowetsa m’dziko latsopano.—Werengani 2 Petulo 3:7, 13; Chivumbulutso 7:17.