Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

 NKHANI YA PACHIKUTO | KODI PALI AMENE ANGADZIWIRETU ZA M’TSOGOLO?

Zina Zimachitika, Koma Zambiri Sizichitika

Zina Zimachitika, Koma Zambiri Sizichitika

Kodi inuyo mumafuna mutadziwa za tsogolo lanu? Anthu ambiri amafuna atadziwa za m’tsogolo. Palinso ena amene amalosera zimene zichitike m’tsogolo koma si zonse zimene zimachitikadi. Taonani zitsanzo zotsatirazi:

  • ASAYANSI amagwiritsa ntchito zipangizo zapamwamba komanso ndalama zambiri kuti adziwiretu zinthu zosiyanasiyana. Zinthu zimenezi ndi monga zokhudza mmene kuwonongedwa kwa chilengedwe kudzakhudzire dziko lapansili komanso ngati kudera linalake kugwe mvula tsiku lotsatira.

  • AKATSWIRI A MALONDA NDIPONSO AKATSWIRI PA NDALE amaneneratu zimene zidzachitike pa nkhani zokhudza bizinezi komanso ndale. Anthu ambiri amaona kuti munthu wina wolemera kwambiri, dzina lake Warren Buffett, ndi wolosera. Amamuona chonchi chifukwa zambiri zomwe amanena zokhudza bizinezi, zimachitikadi. Palinso katswiri wina pa ndale, dzina lake Nate Silver yemwe amagwiritsa ntchito zimene akatswiri ena apeza ndipo amadziwiratu zomwe zidzachitike pa nkhani zosiyanasiyana, monga nkhani zandale za ku America komanso zokhudza mafilimu a Hollywood omwe angalandire mphotho.

  • ZOLEMBA ZINA ZAKALE zimaonedwa ngati maulosi. Anthu ena amaona kuti zomwe analemba munthu wina, dzina lake Michel de Notredame m’zaka za m’ma 1500, zikukwaniritsidwa panopa. Komanso anthu ena ankati kalendala ya Amaya yomwe inatha pa December 21, 2012, inkasonyeza zoti padzikoli pachitika zinthu zoopsa.

  • ATSOGOLERI ACHIPEMBEDZO nthawi zambiri amalosera kuti padzikoli padzachitika zinthu zoopsa. Iwo amachita zimenezi pofuna kuchenjeza anthu kapena pongofuna kuti anthu ambiri alowe tchalitchi chawo. Munthu wina, dzina lake, Harold Camping limodzi ndi otsatira ake, analengeza kuti dzikoli liwonongedwa mu 2011. Koma dziko ndi ili lilipoli mpaka pano.

  • OWOMBEZA amanena kuti ali ndi mphamvu zapadera zodziwira za m’tsogolo. Mwachitsanzo, Edgar Cayce ndi Jeane Dixon analosera molondola zokhudza zinthu zomwe zinachitika m’zaka m’ma 1900. Koma anthu amenewa analoseranso zinthu zina zambiri zomwe sizinachitike. Mwachitsanzo, Dixon analosera kuti nkhondo yachitatu ya padziko lonse iyamba mu 1958, ndipo Cayce analosera kuti dera lonse la New York limizidwa ndi nyanja m’ma 1970.

Ndiye kodi pali njira iliyonse yomwe ingatithandize kudziwa za m’tsogolo molondola? Funso limeneli ndi lofunika kwambiri, chifukwa kudziwiratu za zinthu zomwe zidzachitike m’tsogolo kungakuthandizeni kudziwa zoyenera kuchita pa moyo wanu.