Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 KALE LATHU

“Ntchito Yokolola Idakalipo Yambiri”

“Ntchito Yokolola Idakalipo Yambiri”

George Young anafika ku Rio de Janeiro mu March 1923

M’CHAKA cha 1923, M’bale George Young anakamba nkhani muholo ina yaikulu ku São Paulo. Kunabwera anthu ambirimbiri moti holoyo inadzaziratu. Iye ankakamba nkhaniyo pang’onopang’ono kuti munthu wina azimasulira m’Chipwitikizi. Panasonkhana anthu 585 ndipo ankamvetsera mwatcheru. Malemba a m’Chipwitikizi ankaonetsedwa pogwiritsa ntchito pulojekita. Kumapeto kwa nkhaniyo, panagawidwa timabuku 100 takuti Anthu Mamiliyoni Ambiri Amene Ali ndi Moyo Sadzafa. Timabukuto tinali m’Chipwitikizi, Chingelezi, Chijeremani ndi Chitaliyana. Anthu anasangalala kwambiri ndi nkhaniyi ndipo anayamba kuuza anzawo. Patangopita masiku awiri, anthu anadzazanso muholoyi kuti amvetsere nkhani ina. Koma kodi zonsezi zinayamba bwanji?

Mu 1867, mtsikana wina dzina lake Sarah Bellona Ferguson anasamuka ku United States kupita ku Brazil. Mu 1899, Sarah anawerenga mabuku ofotokoza Baibulo amene mchimwene wake anabweretsa kuchokera ku United States. Iye atangowerenga, anadziwa kuti wapeza choonadi. Sarah ankakonda kwambiri kuwerenga ndipo anapempha kuti azimutumizira nthawi zonse Nsanja ya Olonda yachingelezi. Iye ankasangalala kwambiri ndi zimene ankawerenga ndipo analembera kalata M’bale C. T. Russell. M’kalatayo ananena kuti iye ndi “umboni wakuti palibe munthu amene angakhale kutali kwambiri moti sangamve uthenga wa m’Baibulo.”

Kabuku kachipwitikizi kakuti Kodi Anthu Angalankhule ndi Akufa?

Sarah Ferguson ankayesetsa kuphunzitsa anthu Baibulo koma ankalakalaka kutabwera anthu ena oti adzamuthandize iyeyo, banja lake ndiponso anthu ena abwino a ku Brazil. Ndiyeno mu 1912, abale a ku Beteli ya ku Brooklyn anamuuza kuti kukubwera munthu amene watenga timapepala tambirimbiri tachipwitikizi ta mutu wakuti Kodi Akufa Ali Kuti? Mu 1915, Sarah ananena kuti ankadabwa kumva kuti Ophunzira Baibulo ambiri ankaganiza kuti apita kumwamba posachedwa. Iye analemba kuti: “Ndiye zitha bwanji ku Brazil kuno komanso ku South America? . . . Mukaganizira  kukula kwa South America mutha kuona kuti ntchito yokolola idakalipo yambiri.” Ntchito imene mlongoyu ananena inadzagwiridwadi.

Cha m’ma 1920, anyamata 8 ochokera ku Brazil anapita ku misonkhano mumzinda wa New York pamene ankadikira kuti sitima yawo yankhondo ikonzedwe. Atabwerera ku Rio de Janeiro, ankauza anthu zinthu zabwino zimene anaphunzira m’Baibulo. Pasanapite nthawi mu March 1923, M’bale George Young, yemwe anali woyang’anira woyendayenda, anafika mumzinda wa Rio de Janeiro. Iye anapeza anthu ambiri ofuna kuphunzira Baibulo. Choncho anakonza zoti mabuku ambiri amasuliridwe m’Chipwitikizi. Kenako M’bale Young anapita kumzinda wa São Paulo, womwe unali ndi anthu pafupifupi 600,000. Monga tafotokozera kumayambiriro, atafika anakamba nkhani n’kugawira timabuku tija. Iye anati: “Popeza ndinali ndekha, ndinayenera kudalira manyuzipepala kuti ndiitane anthu kudzamvetsera nkhani.” Iye ananenanso kuti: “Nkhanizi zinali zoyamba kukambidwa pambuyo poti Ophunzira Baibulo alembetsa kuboma la Brazil.”

Pamene M’bale Young ankakamba nkhani, malemba ankasonyezedwa pogwiritsa ntchito pulojekita

Mu Nsanja ya Olonda ya December 15, 1923 munali lipoti la dziko la Brazil. Mu lipotili munali mawu akuti: “Tikaganizira zoti ntchito yolalikira inayamba pa June 1 ndipo pa nthawiyo kunalibe mabuku alionse, titha kuona kuti Ambuye akudalitsa kwambiri ntchitoyi.” Lipotilo linanenanso kuti kuwonjezera pa nkhani ziwiri zimene M’bale Young anakamba ku São Paulo kunakambidwanso nkhani zina 19. Nkhanizi zinakambidwa kuyambira pa June 1 mpaka September 30 ndipo anthu onse amene anapezeka anakwana 3,600. Uthenga wa Ufumu unkafalikira mumzinda wa Rio de Janeiro. Patangopita miyezi yochepa, mabuku achipwitikizi oposa 7000 anagawidwa. Nsanja ya Olonda yachipwitikizi yoyamba inatuluka mu 1923 ndipo inali ndi nkhani za m’magazini a November ndi December.

Sarah Bellona Ferguson, yemwe anali woyamba kuitanitsa Nsanja ya Olonda yachingelezi ku Brazil

George Young anakaona Sarah Ferguson ndipo Nsanja ya Olonda inafotokoza zimene zinachitika M’bale Young atafika kunyumba kwawo. Magaziniyo inati: “Atakumana pabalaza mlongoyu anasowa chonena. Kenako anagwira dzanja la M’bale Young n’kumuyang’anitsitsa. Ndiyeno anamufunsa kuti: ‘Koma ndinudi woyang’anira woyendayenda weniweni?’” Pasanapite nthawi iye limodzi ndi ana ake ena anabatizidwa. Mlongoyu anadikira zaka 25 kuti abatizidwe. Nsanja ya Olonda ya August 1, 1924 inanena kuti anthu 50 anabatizidwa ku Brazil ndipo ambiri mwa iwo anali ochokera ku Rio de Janeiro.

Panopa patha zaka 90 kuchokera nthawi imeneyo ndipo munthu sangafunsenso kuti: “Ndiye zitha bwanji ku Brazil kuno komanso ku South America?” Tikutero chifukwa chakuti ku Brazil kuli abale ndi alongo oposa 760,000 amene akulalikira uthenga wabwino. Uthengawu ukulalikidwanso ku South America konse mu Chipwitikizi, Chisipanishi komanso zilankhulo zina zambiri. Mu 1915, Sarah Ferguson ananena zoona pamene anati: “Ntchito yokolola idakalipo yambiri.”—Nkhaniyi yachokera ku Brazil.

I.B.S.A. stands for International Bible Students Association.