Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

“Yehova Amadziŵa Anthu Ake”

“Yehova Amadziŵa Anthu Ake”

“Koma ngati munthu akukonda Mulungu, ameneyo amadziŵika kwa Mulungu.”—1 AKOR. 8:3.

1. Fotokozani nkhani ya m’Baibulo imene ionetsa maganizo odzinama amene anthu ena a Yehova anakhala nao. (Onani cithunzi cili kuciyambi kwa nkhani ino.)

TSIKU lina m’maŵa, Mkulu wa Ansembe Aroni anaimilila pakhomo la cihema ca Yehova, atanyamula nsembe yofukiza m’cofukizila nsembe. Pafupi ndi iye panali Kora ndi anthu ake okwanila 250, naonso atanyamula zofukizila nsembe. (Num. 16:16-18) Onse anali kuoneka ngati kuti ndi alambili okhulupilika a Yehova. Komabe mosiyana ndi Aroni, anthu onsewo anali odzikhudza, ndipo anali kufuna kulanda udindo wa Mose. (Num. 16:1-11) Iwo anadzinamiza mwa kuganiza kuti Mulungu adzavomeleza kulambila kwao. Koma maganizo amenewo anali ngati kunyoza Yehova. Iye amaona mitima ndipo anaona kuti m‘mitima mwao munali cinyengo.—Yer. 17:10.

2. Kodi Mose analosela ciani? Nanga mau ake anakwanilitsidwa motani?

2 Kutatsala tsiku limodzi kuti zimenezi zicitike, Mose analosela molunjika kuti: “Maŵa m’maŵa, Yehova aonetsa amene ali wake.” (Num. 16:5) Ndipo zimenezo zinacitikadi. Ndithudi, Yehova anasiyanitsa alambili oona ndi onama pamene ‘moto wocokela kwa Yehova, unapseleza [Kora ndi] amuna 250 amene anali kupeleka nsembe zofukiza aja.’ (Num. 16:35; 26:10)  Ndipo panthawi imodzimodziyo, Yehova anapulumutsa Aroni, kuonetsa kuti iye anali wansembe weniweni ndipo anali kulambiladi Mulungu.—Ŵelengani 1 Akorinto 8:3.

3. (a) Ndi cocitika citi cimene cinacitika m’nthawi ya mtumwi Paulo? (b) Yehova anacita ciani ndi apandu amenewo patapita zaka mahandiledi?

3 Zofanana ndi zimenezi zinacitikanso m’nthawi ya mtumwi Paulo patapita zaka 1500. Anthu ena odzicha kuti ndi Akristu anatengela ziphunzitso zonyenga. Koma anapitilizabe kukhala mbali ya mpingo. Mwa kuona kwa umunthu, ampatuko amenewa anali ofanana ndi ena onse mu mpingo. Koma mpatuko wao ukanaononga Akristu okhulupilika. Mimbulu imeneyi m’zovala za nkhosa inayamba ‘kuononga cikhulupililo ca ena.” (2 Tim. 2:16-18) Komabe, Yehova sanangoyang’ana cabe. Ndipo Paulo ayenela kuti anadziŵa bwino zimenezi cifukwa ca mmene Mulungu anacitila ndi Kora ndi anthu ake patapita zaka mahandiledi. Conco, tiyeni tikambitsilane nkhani yocititsa cidwi ndi kuona zimene tiphunzilapo.

“INE NDINE YEHOVA, SINDINASINTHE”

4. Kodi Paulo anali wotsimikiza mtima za ciani? Nanga mau ake kwa Timoteyo anaonetsa bwanji zimenezi?

4 Paulo anali wotsimikiza kuti Yehova amakudziŵa kulambila kwa cinyengo. Ndiponso, anali wotsimikiza mtima kuti Yehova amazindikilanso anthu amene amam’mvela. Mau amene Paulo analembela Timoteyo mouzilidwa amaonetsa kuti iye anali wotsimikiza mtima kuti Mulungu amadziŵa anthu ake. Ponena za mmene ampatuko anakhudzila mpingo, Paulo analemba kuti: “Komabe, maziko olimba a Mulungu adakali cikhalile, ndipo ali ndi cidindo ca mau akuti: ‘Yehova amadziŵa anthu ake,’ ndiponso akuti: ‘Aliyense wochula dzina la Yehova aleke kucita zosalungama.’”—2 Tim. 2:18, 19.

5, 6. Kodi mau amene Paulo anagwilitsila nchito akuti “maziko olimba a Mulungu” ndi ofunika motani? Nanga zimenezi zinam’khudza bwanji Timoteyo?

5 Kodi mau amene Paulo anagwilitsila nchito m’lembali ndi ofunika motani? Mu Baibulo lonse, ndi lemba limeneli cabe limene lili ndi mau akuti, “maziko olimba a Mulungu.” Baibulo limagwilitsila nchito mau akuti “maziko,” kunena zinthu zosiyanasiyana. Mwacitsanzo, Yerusalemu mzinda waukulu wa Isiraeli umanenedwa kuti maziko. (Sal. 87:1,  2) Udindo wa Yesu m’makonzedwe a Yehova umanenedwanso kuti maziko. (1 Akor. 3:11; 1 Pet. 2:6) Nanga Paulo anali kukamba ciani pamene analemba za “maziko olimba a Mulungu”?

6 Paulo anakamba za “maziko olimba a Mulungu” pamene anagwila mau a Mose onena za nkhani ya Kora ndi anthu ake ya pa Numeri 16:5. Mwacionekele, Paulo anali kukamba zocitika za m’nthawi ya Mose kuti alimbikitse Timoteyo. Ndiponso, iye anali kukumbutsa Timoteyo kuti Yehova amadziŵa munthu akayamba kukhala ndi maganizo opanduka. Conco, ampatuko mu mpingowo sakanalepheletsa colinga ca Yehova monga zinalili m’nthawi ya Kora. Paulo sanafotokoze zonse zimene “maziko olimba a Mulungu” anali kuimila. Koma mwacionekele zimene anauza Timoteyo zinam’thandiza kudalila Yehova kwambili.

7. N’cifukwa ciani tingakhale ndi cidalilo cakuti Yehova adzacita zinthu mwa cilungamo ndi mokhulupilika?

7 Miyezo yapamwamba ya Yehova ndi yodalilika. Salimo 33:11 limati, “Zolinga za Yehova zidzakhalapo mpaka kalekale. Maganizo a mumtima mwake adzakhalapo ku mibadwomibadwo.” Malemba ena amanena kuti ulamulilo wa Yehova, kukoma mtima kwake kosatha, cilungamo cake ndi coonadi cake zidzakhala kosatha. (Eks. 15:18;  Sal. 106:1; 112:9; 117:2) Lemba la Malaki 3:6 limati: “Ine ndine Yehova, sindinasinthe.” Ndiponso, Yakobo 1:17 limakamba kuti Yehova “sasintha ngati kusuntha kwa mthunzi.”

“CIDINDO” CIMENE CIMALIMBITSA CIKHULUPILILO

8, 9. Ndi phunzilo lotani limene titengapo pa fanizo la Paulo la “cidindo”?

8 Mau a Paulo olembedwa pa 2 Timoteyo 2:19 amachula za maziko. Ndipo maziko amenewo ali ndi cidindo ca uthenga. Nthawi zakale, sizinali zodabwitsa kuona mau ozokotedwa pa maziko a nyumba oonetsa amene anaimanga kapena mwiniwake. Paulo anali mlembi wa Baibulo woyamba kugwilitsila nchito fanizo limeneli. * Cidindo pa “maziko olimba a Mulungu” cinali ndi mauthenga aŵili. Woyamba ndi wakuti “Yehova amadziŵa anthu ake,” ndipo waciŵili ndi wakuti “Aliyense wochula dzina la Yehova aleke kucita zosalungama.” Zimenezi zimatikumbutsa mau apa lemba la Numeri 16:5.(Ŵelengani.)

9 Kodi tiphunzilapo ciani pa “cidindo” ca m’fanizo la Paulo? Kwa anthu amene amadziŵika ndi Mulungu, mfundo za Yehova zinganenedwe mwacidule m’mbali ziŵili izi: (1) Yehova amakonda anthu okhulupilika kwa iye, ndipo (2) Yehova amadana ndi cisalungamo. Kodi mfundo zimenezi tingazigwilitsile nchito motani pankhani ya ampatuko mu mpingo?

10. Kodi zocita za ampatuko zinakhudza motani Akristu a m’nthawi ya Paulo?

10 Mwacionekele, Timoteyo ndi Akristu ena anada nkhawa kwambili ndi zocita za ampatuko anali pakati pao. Mwina Akristu ena anadabwa cifukwa cake anthu amenewo analoledwa kukhalabe mu mpingo. Ndipo mwina anadzifunsa kaya ngati Yehova anali kusiyanitsa Akristu okhulupilika ndi Akristu acinyengo.—Mac. 20:29, 30.

Timoteyo sanatengeke ndi zocita za ampatuko (Onani ndime 10-12)

11, 12. N’cifukwa ciani kalata ya Paulo inalimbitsa cikhulupililo ca Timoteyo?

11 Kalata ya Paulo mwacionekele inalimbitsa cikhulupililo ca Timoteyo. Inam’kumbutsa zimene zinacitika pamene Aroni wokhulupilikayo anayanjidwa ndi Mulungu. Inam’kumbutsanso zimene zinacitika pamene cinyengo ca Kora ndi anzake cinadziŵika. Iwo anakanidwa ndi kuphedwa. Paulo anaonetsa kuti ngakhale kuti panali Akristu onyenga pakati pao, Yehova anali kuwadziŵa anthu ake monga mmene anawadziŵila m’nthawi ya Mose.

 12 Yehova sasintha, ndipo ndi wodalilika. Iye amadana ndi cisalungamo, ndipo panthawi yake adzacotsapo anthu amene apitiliza kucita zosalungama. Popeza Timoteyo anali ‘kuitanila pa dzina la Yehova,’ iye anafunika kucitapo kanthu kuti akanize zocita zosalungama za Akristu onyenga. *

KULAMBILA KOONA SIKUDZAPITA PACABE

13. Kodi tingatsimikize mtima za ciani?

13 Ifenso tingalimbikitsidwe mwa kuuzimu ndi mau ouzilidwa a Paulo. Coyamba, n’zolimbikitsa kudziŵa kuti Yehova amadziŵa bwino anthu okhulupilika kwa iye. Kumeneku sikudziŵa mwacisawawa. M’malo mwake, Yehova amasamalila anthu amene iye adziŵa. Baibulo limati: “Maso a Yehova akuyendayenda padziko lonse lapansi kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wao uli wathunthu kwa iye.” (2 Mbiri 16:9) Conco, tingakhale ndi cidalilo cakuti zimene timacitila Yehova ‘mocokela mumtima’ sizidzapita pacabe.—1 Tim. 1:5; 1 Akor. 15:58.

14. Ndi kulambila kotani kumene Yehova sakondwela nako?

14 N’zolimbikitsanso kudziŵa kuti Yehova sakondwela ndi kulambila kwa cinyengo. Pamene maso ake “akuyendayenda padziko lonse lapansi,” iye amadziŵanso anthu amene mitima yao si ‘yanthunthu kwa iye.’ Lemba la Miyambo 3:32 limati: “Munthu wocita zaciphamaso Yehova amanyansidwa naye.” Iye amanyansidwa ndi munthu amene amazionetsela kuti ndi wokhulupilika, koma amene mwamseli amacita zosalungama. Ngakhale kuti munthu wa conco anganamize anthu kwa kanthawi, Yehova Mulungu wamkulu ndi wacilungamo amatiuza kuti, “wobisa macimo ake zinthu sizidzamuyendela bwino.”—Miy. 28:13; ŵelengani 1 Timoteyo 5:24; Aheberi 4:13.

15. Kodi tiyenela kupewa ciani? Nanga n’cifukwa n’ciani?

15 Anthu ambili a Yehova amadzipeleka moona mtima pom’lambila. N’zosatheka kuti wina mu mpingo mwadala ayambe kulambila mwacinyengo. Komabe, ngakhale masiku ano, zimene zinacitika m’nthawi ya Mose ndi m’nthawi ya Akristu oyambilila zingacitikenso. (2 Tim. 3:1, 5) Conco, kodi tiyenela kuyamba kukaikila kukhulupilika kwa Akristu anzathu? Iyai! N’kulakwa kuyamba kukaikila abale ndi alongo athu popanda maziko enieni. (Ŵelengani Aroma 14:10-12; 1 Akor. 13:7.) Ndiponso, kukhala ndi cizoloŵezi cokaikila kukhulupilika kwa ena mu mpingo kungaononge ubwenzi wathu ndi Yehova.

16. (a) Kodi aliyense wa ife angacite ciani kuti cinyengo cisazike mizu m’mitima yathu? (b) Kodi nkhani imene ili m’kabokosi yakuti, “ Pitilizani Kudziyesa . . . ” itiphunzitsa ciani?

16 Mkristu aliyense payekha “ayese nchito yake, kuti aone kuti ndi yotani.” (Agal. 6:4) Cifukwa copanda ungwilo, nthawi zina tingakhale ndi maganizo acinyengo m’mitima yathu. (Aheb. 3:12, 13) Conco, nthawi ndi nthawi tiyenela kupenda colinga cathu potumikila Yehova. Tingadzifunse kuti: ‘Kodi ndimatumikila Yehova cifukwa com’konda ndi kulemekeza ulamulilo wake? Kodi ndimangoyang’ana cabe madalitso amene ndidzalandila m’Paladaiso?’ (Chiv. 4:11) Ife tonse tidzapindula kwambili ngati timapenda zocita zathu ndi kucotsa cinyengo ciliconse m’mitima yathu.

KUKHULUPILIKA KUMABWELETSA CIMWEMWE

17, 18. N’cifukwa ciani tiyenela kukhala okhulupilika ndi oona mtima polambila Yehova?

17 Ngati tiyesetsa kukhala okhulupilika ndi oona mtima polambila, tidzalandila madalitso ambili. Wamasalimo anati: “Wodala  ndi munthu amene Yehova sanamusungile colakwa cake, amene alibe mtima wacinyengo.” (Sal. 32:2) Inde, anthu amene amacotsa cinyengo ciliconse m’mitima yao amakhala acimwemwe, ndipo adzakhalanso ndi cimwemwe ceniceni mtsogolo.

18 Panthawi yake, Yehova adzavumbula onse amene amacita zoipa kapena a moyo wapaŵili, ndipo adzasiyanitsa “pakati pa munthu wolungama ndi woipa ndiponso pakati pa munthu amene akutumikila Mulungu ndi amene sanatumikilepo Mulungu.” (Mal. 3:18) Pakali pano, n’zolimbikitsa kudziŵa kuti “maso a Yehova ali pa olungama, ndipo makutu ake amamva pembedzelo lao.”—1 Pet. 3:12.

^ par. 8 Lemba la Chivumbulutso 21:14, limanena za maziko okwanila 12, amene anali ndi maina a atumwi 12. Lembali linalembedwa zaka zambili Paulo atalembela kale Timoteyo makalata.

^ par. 12 M’nkhani yotsatila tidzaphunzila mmene tingatsatilile citsanzo ca Yehova pankhani yoleka kucita zosalungama.