Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mukukalamila Udindo?

Kodi Mukukalamila Udindo?

AKULU aŵili anaitana Fernando * kuti akambe naye pambali. Iye anacita mantha. Pambuyo pakuti woyang’anila dela wacezela mpingo wao maulendo angapo aposacedwapa, akulu anafotokozela Fernando zimene ayenela kucita kuti ayenelele maudindo oonjezeleka mumpingo. Koma m’kupita kwa nthawi Fernando anayamba kukaikila ngati adzayenelela kukhala mkulu. Woyang’anila dela anacezelanso mpingo wao ca posacedwapa. Nanga tsopano akulu adzamuuza ciani?

Pamene mkulu anali kukamba Fernando anamvetsela. M’kuluyo anagwila mau a pa 1 Timoteyo 3:1 ndi kumuuza kuti, akulu alandila kalata yoonetsa kuti iye wayamikilidwa kukhala mkulu. Zimenezi zinam’dabwitsa Fernando, ndipo anafunsa kuti, “Mwati bwanji?” Mkuluyo anabwelezanso zimene anakamba, ndipo Fernando anaonetsa kukondwela pankhope yake. Ndiyeno, cilengezo citapelekedwa ku mpingo, onse anakondwela kwambili.

Kodi kufuna udindo mumpingo n’kulakwa? Osati kwenikweni. Lemba la 1 Timoteyo 3:1 limati, “ngati munthu aliyense akuyesetsa [kapena kuti kukalamila] kuti akhale woyang’anila, akufuna nchito yabwino.” Abale ambili amene atsatila malangizo amenewa apita patsogolo, ndipo ayenelela maudindo mumpingo. Zotsatilapo n’zakuti anthu a Mulungu adalitsidwa mwa kukhala ndi akulu ndi atumiki othandiza ambilimbili. Komabe, cifukwa ca kuonjezeka kwa mipingo, pafunikila abale ambili kuti akalamile maudindo. Nanga njila yabwino yocitila zimenezi ndi iti? Kodi aja amene akukalamila kukhala oyang’anila ayenela kudela nkhawa monga mmene Fernando anacitila?

KODI ‘KUYESETSA KUKHALA WOYANG’ANILA’ KUMATANTHAUZANJI?

Mau a m’Baibulo akuti “akuyesetsa” anamasulilidwa kucokela ku mau a Cigiliki amene amatanthauza kufunitsitsa, kapena kukalamila. Mwina tingaganizile munthu amene akuyesetsa kuti athyole cipatso cokongola colendewela mu mtengo. Koma kukalamila sikutanthauza kukhumbila mwadyela ‘kukhala woyang’anila.’ N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti colinga ca aja amene afuna kutumikila  monga akulu ndico kucita “nchito yabwino” osati kupeza mpando.

Ziyeneletso zina za nchito yabwino zipezeka pa lemba la 1 Timoteyo 3:2-7 ndi Tito 1:5-9. Ponena za miyezo yapamwamba imeneyi, m’bale wina dzina lake Raymond, amene watumikila monga mkulu kwa zaka zambili anati: “Cinthu cacikulu kwa ine ndi kukhala mmene tilili. N’zoona kuti kulalikila ndi kuphunzitsa n’kofunika, koma zimenezi sizingapose pa kukhala wopanda cifukwa cotinenezela, wosacita zinthu mopitilila malile, woganiza bwino, wadongosolo, woceleza alendo, ndi wololela.”

‘Yesetsani’ kutumikila mpingo m’njila zosiyanasiyana

M’bale amene akukalamila udindo amakhala wopanda cifukwa comunenezela mwa kupewa kusaona mtima ndi cidetso. Sacita zinthu mopitilila malile, amaganiza bwino, ndi wadongosolo, ndipo ndi wololela. Motelo, abale sam’kaikila kuti ndi woyenelela kukhala woyang’anila, ndi kuti angawathandize akakhala ndi mavuto. Cifukwa cokhala woceleza, iye amalimbikitsa acicepele ndi atsopano m’coonadi. Ndipo amathandiza ndi kutonthoza odwala ndi okalamba cifukwa cokonda zabwino. Iye amakulitsa makhalidwe amenewa kuti apindulitse ena, osati ndi colinga cakuti ayenelele udindo. *

Bungwe la akulu ndi lofunitsitsa kupeleka uphungu ndi cilimbikitso kwa m’baleyo, koma zili kwa iye kukwanilitsa ziyeneletso za m’Malemba. Henry, amene watumikila monga woyang’anila kwa zaka zambili anati: “Ngati mukukalamila, yesetsani kugwila nchito mwakhama kuti muonetse kuti mukuyenelela.” Pofotokoza lemba la Mlaliki 9:10 iye anati: “‘Ciliconse cimene dzanja lako lapeza kuti licite, ucicite ndi mphamvu zako zonse.’ Nchito iliyonse imene akulu akupatsani muyenela kuigwila ndi mtima wonse. Muzikonda nchito iliyonse imene mwapatsidwa mumpingo, kuphatikizapo kupsela. M’kupita kwa nthawi, nchito zanu ndi khama lanu zidzadziŵika.” Ngati mufuna kudzatumikila monga mkulu mtsogolo, muzigwila nchito mwakhama ndi kukhala wokhulupilika pa utumiki uliwonse wopatulika. Ndipo khalani wodzicepetsa m’malo mongofuna cabe udindo.—Mat. 23:8-12.

 PEWANI MAGANIZO NDI ZOCITA ZOSAYENELA

Abale ena amene akukalamila maudindo mumpingo, mwamacenjela angapusitse akulu n’colinga cakuti awayamikile kukhala akulu. Ndipo ena amakhumudwa akulu akawapatsa uphungu. Anthu aconco ayenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimangofuna kupititsa patsogolo zofuna zanga kapena ndimafuna kusamalila nkhosa za Yehova modzicepetsa?’

Abale amene akukalamila ayenela kukumbukila ciyeneletso cina ca akulu, cakuti ayenela ‘kukhala zitsanzo kwa gulu la nkhosa.’ (1 Pet. 5:1-3) Aja amene ndi zitsanzo zabwino mumpingo amapewa maganizo ndi zocita zosayenela. Iwo ayenela kukhala odekha kaya ali kale paudindo kapena ai. Munthu akakhala mkulu si ndiye kuti wakhala wangwilo. (Num. 12:3; Sal. 106:32, 33) Ndiponso, m’bale ‘sangadziŵe kanthu kalikonse kum’tsutsa mumtima mwake,’ koma ena angadziŵe zofooka zake. (1 Akor. 4:4) Conco, akulu akakupatsani uphungu woyenelela wocokela m’Baibulo, yesetsani kuulandila ndi mtima wonse, ndipo gwililamponi nchito.

BWANJI NGATI MWAYEMBEKEZELA KWA NTHAWI YAITALI?

Abale ambili angaone kuti ayembekezela kwa nthawi yaitali asanaikidwe pa udindo. Ngati ‘mwayesetsa kuti mukhale woyang’anila’ kwa zaka zambili, kodi nthawi zina mumadela nkhawa? Ngati n’conco, onani mau awa: “Cinthu cimene unali kuyembekezela cikalepheleka cimadwalitsa mtima. Koma comwe unali kufuna cikacitika cimakhala ngati mtengo wa moyo.”—Miy. 13:12.

Ngati zimene munthu alakalaka sizicitika, zingam’dwalitsa mtima. Ndi mmene Abulahamu nayenso anamvelela. Yehova anam’lonjeza kuti adzakhala ndi mwana, koma panapita zaka zambili kuti iye ndi mkazi wake Sara akhale ndi ana. (Gen. 12:1-3, 7) Abulahamu mu ukalamba wake anapempha kuti: “Yehova Ambuye Wamkulu Koposa, mudzandipatsa ciani ine? Taonani ndilibe mwana . . . Simunandipatse mbeu.” Yehova anam’tsimikizila kuti lonjezo lake lonena za mwana lidzakwanilitsidwa. Koma panapita zaka 14 kuti mau a Mulungu akwanilitsike.—Gen. 15:2-4; 16:16; 21:5.

Pamene Abulahamu anali kuyembekezela, kodi anataya mtima potumikila Yehova? Iyai, sanatelo. Sanakaikile ngakhale pang’ono malonjezo a Mulungu. Iye anayembekezelabe zotsatilapo zake zabwino. Mtumwi Paulo alemba kuti: “Abulahamu ataonetsa kuleza mtima, analandila lonjezo limeneli.” (Aheb. 6:15) Potsilizila pake, Mulungu Wamphamvuyonse anadalitsa kwambili munthu wokhulupilika ameneyu. Tingaphunzile ciani kwa Abulahamu?

Ngati mumalakalaka kutumikila monga mkulu, koma zimenezo sizicitika ngakhale kuti papita zaka zambili, pitilizani kudalila Yehova. Pitilizanibe kutumikila Mulungu mwacimwemwe. Warren, amene wathandiza abale ambili kupita patsogolo kuuzimu anafotokoza cifukwa cake. Iye anati: “Kuti wina ayenelele kukhala mkulu payenela kupita nthawi. M’kupita kwa nthawi, luso la m’bale, mmene amacitila zinthu, ndi mmene amasamalilila maudindo  ake zimadziŵika pang’onopang’ono. Ena amaona kuti akakhalako ndi udindo winawake ndiye kuti akupita patsogolo. Koma maganizo aconco ndi oipa ndipo angasokoneze munthu. Ngati mukutumikila Yehova mokhulupilika, mosasamala kanthu za udindo wanu mumpingo, ndiye kuti mukupita patsogolo.”

M’bale wina anayembekezela kwa zaka zoposa 10 asanakhale mkulu. Pofotokoza zocitika za m’buku la Ezekieli caputala 1, iye anakamba zimene anaphunzilapo mwa kunena kuti: “Yehova amatsogolela galeta lake, gulu lake pa liŵilo limene iye afuna. Cofunika kwambili si nthawi yathu, koma ya Yehova. Pankhani yofuna kukhala mkulu, cofunika kwambili si ine, zimene ndifuna kapena malo amene ndifuna kutumikila. Zimene ndifuna si zimene Yehova angaone kuti n’zimene ndifunikila.”

Ngati mufuna kudzagwila yabwino ya oyang’anila acikristu mtsogolo, yesetsani kukalamila mwa kuthandiza mpingo kukhala wacimwemwe. Ngati mwaona kuti zimenezo sizicitika mwamsanga, pewani kuda nkhawa ndipo musataye mtima. Raymond, amene tam’chula poyamba, anati: “Ngati munthu amafunitsitsa kukhala wochuka zimavuta kuti akhale wokhutila. Aja amene amadela nkhawa nthawi zonse, sapeza cimwemwe cimene cimabwela cifukwa cotumikila Yehova.” Motelo, pitilizani kukulitsa cipatso ca mzimu wa Mulungu, makamaka kuleza mtima. Ndipo yesetsani kupita patsogolo kuuzimu mwa kuphunzila Baibulo. Onjezelani nchito yanu yolalikila uthenga wabwino ndi kuphunzitsa ena Baibulo. Ndipo muzitsogolela banja lanu pa zinthu zauzimu ndi pa kulambila kwa pabanja. Muziyanjana ndi abale ndi alongo anu. Pamene mupita patsogolo kuti mukwanilitse colinga canu, mudzakondwela kutumikila Yehova.

Kukalamila maudindo mumpingo ndi dalitso locokela kwa Yehova. Iye ndi gulu lake afuna kuti aja amene akukalamila azimutumikila mokondwela. Mulungu amathandiza ndi kudalitsa onse amene amam’tumikila ndi zolinga zabwino. Ndithudi, madalitso ake onse ndi oona ndipo “saonjezelapo ululu.”—Miy. 10:22.

Ngakhale kuti mwakalamila kwa nthawi yaitali, pali zambili zimene mungacite kuti mulimbitse ubale wanu ndi Mulungu. Mukayesetsa kukulitsa makhalidwe ofunika ndi kugwila nchito mwakhama mumpingo, koma osanyalanyaza banja lanu, Yehova sadzaiŵala zonse zimene mwacita pom’tumikila. Conco, lekani kuti kutumikila Yehova kukhale kokondweletsa kwa inu, mosasamala kanthu za udindo umene muli nao.

^ par. 2 Maina m’nkhani ino asinthidwa.

^ par. 8 Mfundo za m’nkhani ino zimagwilanso nchito kwa aja amene afunitsitsa kukhala atumiki othandiza. Ziyeneletso zimene io afunikila kukwanilitsa zipezeka pa 1 Timoteyo 3:8-10, 12, 13.