Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

 MBIRI YA MOYO WANGA

Zinthu Zosaiwalika pa Utumiki Wanga

Zinthu Zosaiwalika pa Utumiki Wanga

Mu 1947, ansembe achikatolika ku Santa Ana m’dziko la El Salvador ankafuna kusokoneza a Mboni za Yehova. Abale akuchita Phunziro la Nsanja ya Olonda m’nyumba ya amishonale, anyamata ena anaponya zimiyala pakhomo lomwe linali losatseka. Ndiye kunabwera ansembe ndi gulu la anthu. Ena anatenga miyuni ndipo ena ananyamula zifaniziro. Anaponya miyala panyumbayo kwa maola awiri uku akufuula kuti: “Mariya akhale kwamuyaya! Yehova afe!” Iwo ankafuna kuti amishonale athawe m’tauniyo. Izi zinachitika zaka 67 zapitazo ndipo ine ndinali m’nyumbayo. *

NKHANI imene ndafotokozayi inachitika patangotha zaka ziwiri kuchokera pamene ine ndi Evelyn Trabert tinamaliza maphunziro a kalasi ya nambala 4 ya Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibulo. Pa nthawiyo sukuluyi inkachitikira pafupi ndi mzinda wa Ithaca ku New York. Anatitumiza kukatumikira ku Santa Ana m’dziko la El Salvador. Koma ndisanapitirize kufotokoza za umishonale umene ndinachita kwa zaka pafupifupi 29, ndikufuna kuti ndinene zimene zinandithandiza kuyamba umishonale.

ZIMENE ZINANDITHANDIZA KUTI NDITUMIKIRE YEHOVA

Bambo ndi mayi anga anali John ndi Eva Olson ndipo ankakhala mumzinda wa Spokane ku Washington m’dziko la United States. Ine ndinabadwa mu 1923. Makolowa anali achipembedzo cha Lutheran koma sankagwirizana ndi mfundo yoti Mulungu wachikondi angawotche anthu. (1 Yoh. 4:8) Bambo anga ankagwira ntchito kubekale ndipo tsiku lina mnzawo kuntchitoko anawauza kuti Baibulo silinena zoti Mulungu amawotcha anthu. Nthawi yomweyo makolo anga anayamba kuphunzira ndi Mboni za Yehova ndipo anadziwa zimene zimachitika munthu akamwalira.

 Pa nthawiyo ndinali ndi zaka 9 zokha koma ndinkamva makolo anga akuyamikira kwambiri zimene ankaphunzira m’Baibulo. Iwo anasangalala kwambiri atadziwa kuti dzina la Mulungu ndi Yehova komanso atazindikira kuti Mulunguyo si Utatu. Ndinayamba kuphunzira kwambiri mfundo za m’Malemba ndipo ‘choonadi chinayamba kundimasula.’ (Yoh. 8:32) Nthawi zonse ndimasangalala ndikamaphunzira Baibulo ndipo kuliphunzira sikunditopetsa ngakhale pang’ono. Ndinali wamanyazi koma ndinkapita ndi makolo anga kokalalikira. Makolowo anabatizidwa mu 1934 pomwe ine ndinabatizidwa mu 1939 ndili ndi zaka 16.

Ndili ndi makolo anga ku msonkhano wa mumzinda wa St. Louis ku Missouri mu 1941

Ndiyeno mu 1940 makolo anga anagulitsa nyumba ndipo tonse tinayamba upainiya ku Idaho. Tinkachita lendi chipinda china chimene chinali pamwamba pa malo okonzera magalimoto. Abale ndi alongo ankasonkhananso m’nyumba yathuyo. Pa nthawiyo, mipingo yambiri inalibe Nyumba za Ufumu ndipo abale ankangochita lendi nyumba n’kumasonkhanamo.

Mu 1941, ine ndi makolo anga tinapita kumsonkhano waukulu mumzinda wa St. Louis ku Missouri. Ndiyeno Lamlungu lake analitchula kuti ndi “Tsiku la Ana” ndipo ana tonse, a zaka za pakati pa 5 ndi 18, tinauzidwa kuti tikhale kutsogolo. M’bale Joseph F. Rutherford atafika pachimake pa nkhani yake anatiuza kuti: “Ana nonsenu . . . amene mwavomereza kumvera Mulungu ndi Mfumu yake imirirani!” Ndiyeno tonse titaimirira, m’baleyo anati: “Taonani mboni zatsopano za Ufumu zopitirira 15,000!” Izi zinachititsa kuti nditsimikize mumtima mwanga zochita upainiya.

KUMENE TINATUMIKIRA

Patangodutsa miyezi yochepa kuchokera pamene tinachita msonkhanowu, ine ndi makolo anga tinasamukira mumzinda wa Oxnard, kum’mwera kwa California. Tinauzidwa kuti tikayambitse mpingo mumzindawu. Koma tinkakhala mukalavani yokhala ndi bedi limodzi basi. Madzulo alionse ndinkakonza malo anga ogona pamwamba pa tebulo limene tinkadyera. Apatu zinthu zinasintha kwambiri chifukwa kwathu ndinali ndi chipinda changachanga.

Titangotsala pang’ono kufika ku California, dziko la Japan linaphulitsa mabomba ku Pearl Harbor ku Hawaii. Izi zinachitika pa December 7, 1941 ndipo tsiku lotsatira dziko la United States linalowerera nkhondo yachiwiri ya padziko lonse. Asilikali a ku Japan ankazungulira pa sitima zankhondo m’mphepete mwa nyanja ku California n’cholinga choti aphulitse mabomba. Choncho akuluakulu a boma ananena kuti aliyense asayatse magetsi usiku kuti asilikaliwo asaone malo oti aphulitse mabombawo.

Ndiyeno mu September 1942, tinapita ku msonkhano wakuti “Dziko Latsopano Lolamulidwa ndi Mulungu” mumzinda wa Cleveland ku Ohio. Ku msonkhanowu, M’bale Nathan H. Knorr anakamba nkhani ya mutu wakuti: “Kodi Padzikoli Padzakhala Mtendere?” M’nkhaniyi anagwiritsa ntchito Chivumbulutso chaputala 17, pamene Baibulo limafotokoza za “chilombo” chimene “chinalipo, tsopano palibe, komabe chili pafupi kutuluka kuphompho.” (Chiv. 17:8, 11) M’bale Knorr anafotokoza kuti “chilombo” chikuimira bungwe la League of Nations limene linasiya kugwira ntchito mu 1939. Ndiyeno Baibulo linaneneratu kuti bungwe lina lidzalowa m’malo mwa League of Nations ndipo lidzachititsa kuti pakhale mtendere pang’ono. Mu 1945, nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inatha ndipo kunapangidwa bungwe la United Nations. Apa zinali ngati “chilombo” chija chatuluka kuphompho. Pa nthawiyi, a Mboni za Yehova anayamba kugwira ntchito yolalikira mwakhama ndipo gulu linakula kwambiri.

Chikalata chosonyeza kuti ndinamaliza Sukulu ya Giliyadi

 Ulosi umenewu unandithandiza kudziwa za m’tsogolo. Nditamva chilengezo choti Sukulu ya Giliyadi iyamba chaka chotsatira, ndinayamba kulakalaka zokhala mmishonale. Mu 1943, ndinapemphedwa kuti ndizikachita upainiya mumzinda wa Portland ku Oregon. Tinkagwiritsa ntchito galamafoni kuti anthu amve nkhani zochokera m’Baibulo kenako tinkawapatsa mabuku ofotokoza za Ufumu wa Mulungu. Chaka chonsecho ndinkangokhalira kulakalaka kuti ndikhale mmishonale.

Mu 1944, ndinasangalala kwambiri nditaitanidwa ku Giliyadi limodzi ndi Evelyn Trabert, yemwe anali mnzanga wapamtima. Kwa miyezi 5, alangizi athu anatisonyeza zimene tingachite kuti tizisangalala kwambiri pophunzira Baibulo. Tinadabwa kuona kuti alangiziwo anali odzichepetsa kwambiri. Nthawi zina, tikamadya, iwo ankaperekera chakudya. Ndiyeno tinamaliza maphunzirowo pa January 22, 1945.

NDINAYAMBA UMISHONALE

Ine, Evelyn ndiponso Leo ndi Esther Mahan tinafika ku El Salvador mu June 1946. Anthu ambiri ankafuna kumva uthenga wabwino moti zinali ngati m’munda “mwayera kale ndipo m’mofunika kukolola.” (Yoh. 4:35) Tinali ndi msonkhano woyamba ku Santa Ana ndipo tinagwira mwakhama ntchito yoitanira anthu kuti adzamve nkhani ya onse. Tinasangalala kuona anthu pafupifupi 500 atafika. Patangodutsa mlungu umodzi, zimene ndafotokoza kumayambiriro kwa nkhaniyi zinachitika ndipo zinasonyeza kuti ansembe anakwiya kwambiri. Koma sitinathawe m’tauniyo, m’malomwake tinkafunitsitsa kukhalabe kuti tithandize anthu amene ankafuna kuphunzira. Ansembe ankaletsa anthu kuwerenga Baibulo ndipo ambiri sakanatha kuligula. Koma anthuwo ankafunitsitsa kuphunzira. Iwo anasangalala kwambiri kuona kuti tikuphunzira Chisipanishi n’cholinga choti tiziwaphunzitsa za Mulungu woona komanso za Paradaiso amene walonjeza.

Anthu 5 ochokera m’kalasi yathu ya Giliyadi anatumizidwa ku El Salvador. Kuchokera kumanzere: Evelyn Trabert, Millie Brashier, Esther Mahan, ine ndi Leo Mahan

Munthu wina amene ndinayamba kuphunzira naye anali Rosa Ascencio. Atayamba kuphunzira Baibulo, anasiyana ndi mwamuna amene ankakhala naye. Ndiyeno mwamunayo anayambanso kuphunzira. Iwo anakwatirana mwalamulo, kenako n’kubatizidwa ndipo anayamba kutumikira Yehova mwakhama. Pa anthu am’dzikoli, Rosa anali woyamba kuchita upainiya mumzinda wa Santa Ana. *

Rosa anali ndi golosale ndipo akafuna kulowa mu utumiki, ankaitseka podziwa kuti Yehova amuthandiza kupeza zofunika pa moyo. Akatsegulanso patapita maola ochepa, ankadabwa kuona makasitomala ambirimbiri akubwera kudzagula zinthu. Iye anaona lemba la Mateyu 6:33 likukwaniritsidwa ndipo ankatumikira Mulungu mokhulupirika mpaka pamene anamwalira.

Tinkachita lendi nyumba ya munthu wina wogwira ntchito yapamwamba. M’nyumbayo tinkakhalamo amishonale 6. Ndiyeno tsiku lina, wansembe anamuuza kuti amuchotsa mumpingo akapitiriza kutilola kuti tizikhala m’nyumba yake. Koma munthuyo  ankanyansidwa ndi zochita za ansembewo moti anakana zimene anamuuzazo. Anauzanso wansembeyo kuti sangadandaule ngati atamuchotsa. Ndipo anatiuza kuti tikhoza kumakhalabe m’nyumbayo.

MUNTHU WOLEMEKEZEKA ANAKHALA WA MBONI

Ofesi ya nthambi imene inamangidwa mu 1955

Kulikulu la dziko la El Salvador, mmishonale wina ankaphunzira ndi mkazi wina dzina lake Paulina. Mwamuna wake anali Baltasar Perla ndipo anali katswiri wa zomangamanga. Mwamunayu anali wabwino kwambiri koma anasiya kukhulupirira Mulungu chifukwa choona chinyengo cha atsogoleri achipembedzo. Ndiyeno itafika nthawi yomanga ofesi ya nthambi, Baltasar anadzipereka kuti alembe mapulani ake komanso kumanga ofesiyo kwaulere. Anachita zimenezi ngakhale kuti pa nthawiyo sanali Mboni.

Iye atagwira ntchito ndi Mboni pomanga ofesiyo, anazindikira kuti wapeza chipembedzo choona. Anabatizidwa pa July 22, 1955 ndipo pasanapite nthawi yaitali mkazi wakeyo anabatizidwanso. Ali ndi ana awiri ndipo onse akutumikiranso Yehova mokhulupirika. Mwana wawo wamwamuna, dzina lakenso Baltasar, watumikira ku Beteli ya ku Brooklyn kwa zaka 49 ndipo panopa ali mu Komiti ya Nthambi ya ku United States. *

Titayamba kuchita misonkhano yachigawo kulikulu la dzikoli, M’bale Perla anatithandiza kupeza mwayi wogwiritsa ntchito bwalo lamasewero. Poyamba tinkangogwiritsa ntchito mipando yochepa ya m’bwaloli. Koma chaka chilichonse anthu ankawonjezeka moti tinkadzazamo mpaka ena kusowa pokhala. Pa misonkhanoyi ndinkakumana ndi anthu amene ndinkaphunzira nawo Baibulo. Ndinkasangalala kwambiri anthu amene ndinawaphunzitsawo akamandisonyeza anthu amene iwonso anawaphunzitsa. Zinali ngati ndikuona zidzukulu zanga.

M’bale F. W. Franz akulankhula ndi amishonale pa msonkhano

Pa msonkhano wina, mbale wina anabwera n’kunena kuti akufuna alape. Ndinadabwa kwambiri chifukwa sindinkamudziwa. Ndiyeno anati: “Ndine mmodzi mwa anyamata amene ankaponya miyala ku Santa Ana kuja.” Pa nthawiyi anali atayamba kutumikira Yehova. Ndinasangalala koopsa. Zinanditsimikizira kuti kuchita utumiki wa nthawi zonse n’kwabwino kwambiri kuposa ntchito iliyonse.

Msonkhano wathu woyamba ku El Salvador

 NDIKUSANGALALA NDI ZIMENE NDINASANKHA

Ndinachita umishonale ku El Salvador kwa zaka pafupifupi 29. Poyamba ndinali ku Santa Ana, kenako ku Sonsonate, kenako ku Santa Tecla ndipo pomaliza ndinapita kulikulu la dzikoli. Makolo anga anali okhulupirika koma anayamba kuvutika chifukwa cha ukalamba. Ndiyeno mu 1975 ndinaganiza zosiya umishonale n’kubwerera ku Spokane kuti ndikawathandize. Ndinasankha zimenezi pambuyo popemphera kwambiri.

Bambo anga anamwalira mu 1979. Ndiyeno ndinkasamalira mayi anga koma thupi lawo linkangofookabe. Ndinapitiriza kuwasamalira kwa zaka 8 ndipo anamwalira ali ndi zaka 94. Pa nthawi imeneyi ndinkatopa kwambiri ndipo zinkandisokoneza maganizo. Chifukwa choda nkhawa, ndinayamba kudwala mashingozi. Koma ndinkapemphera kwambiri ndipo Yehova ankandilimbitsa mtima moti ndinapirira bwinobwino. Zinali ngati Yehova akundiuza kuti ‘adzanditenga, kundinyamula ndiponso kundipulumutsa mpaka kukalamba.’—Yes. 46:4.

Mu 1990, ndinasamukira mumzinda wa Omak ku Washington. Kumeneko ndinasangalala kulalikiranso anthu olankhula Chisipanishi ndipo ambiri amene ndinaphunzira nawo anabatizidwa. Chifukwa choona kuti ndikuvutika kusamalira nyumba yanga ndinasamuka ku Omak mu November 2007. Ndinakakhala m’nyumba yaing’ono m’tauni yapafupi yotchedwa Chelan. Ndimayamikira zimene abale ndi alongo mumpingo wachisipanishi amachita pondisamalira. Palibe anthu okalamba ena mumpingowu choncho onse amandiona ngati agogo awo.

Ndinasankha kuti ndisakwatiwe kapena kukhala ndi ana n’cholinga choti ndizitumikira Yehova “popanda chododometsa.” (1 Akor. 7:34, 35) Ngakhale zili choncho, ndili ndi abale ndi alongo ambiri amene ali ngati ana anga. Ndinazindikira kuti m’dziko lakaleli sitingakhale ndi zonse zimene tikufuna. Choncho ndinaona kuti kutumikira Yehova ndi mtima wonse ndi chinthu chofunika kuika pa malo oyamba. M’dziko latsopano tidzakhala ndi nthawi yambiri yochita zinthu zambiri zosangalatsa. Lemba limene ndimakonda kwambiri ndi Salimo 145:16 limene limalonjeza kuti Yehova ‘adzakhutiritsa zokhumba za chamoyo chilichonse.’

Upainiya umandithandiza kuchita zinthu ngati wachinyamata

Panopa ndili ndi zaka 91 koma ndidakali ndi thanzi labwino ndipo ndikuchitabe upainiya. Ndimaona kuti upainiya umandithandiza kuchita zinthu ngati wachinyamata komanso kukhala ndi cholinga. Pamene ndinkafika ku El Salvador ntchito yolalikira inali itangoyamba kumene. Ngakhale kuti Satana wakhala akuyesetsa kusokoneza ntchitoyi, m’dzikoli muli ofalitsa oposa 39,000. Zimenezi zalimbitsa kwambiri chikhulupiriro changa. Zikuonekeratu kuti mzimu wa Yehova ukuthandiza anthu ake.

^ ndime 4 Onani Buku Lapachaka la Mboni za Yehova lachingelezi la 1981, tsamba 45 ndi 46.

^ ndime 19 Onani nkhani yake mu Buku Lapachaka lachingelezi la 1981, tsamba 41 ndi 42.

^ ndime 24 Onani Buku Lapachaka lachingelezi la 1981, tsamba 66 mpaka 67 ndiponso tsamba 74 mpaka 75.