Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mumayamikira Mwayi Wogwira Ntchito ndi Yehova?

Kodi Mumayamikira Mwayi Wogwira Ntchito ndi Yehova?

“Ndife antchito anzake a Mulungu.”—1 AKOR. 3:9.

1. (a) Kodi Yehova amamva bwanji akamagwira ntchito? (b) Kodi Yehova wakhala akuchita chiyani?

YEHOVA amasangalala ndi ntchito imene akugwira. (Sal. 135:6; Yoh. 5:17) Iye wakhala akupereka ntchito zabwino kwa angelo ndi anthu n’cholinga choti nawonso azisangalala. Mwachitsanzo, analola kuti Mwana wake woyamba agwire nawo ntchito yolenga zinthu. (Werengani Akolose 1:15, 16.) Baibulo limanena kuti Yesu asanabwere padzikoli anali limodzi ndi Mulungu kumwamba monga “mmisiri waluso.”—Miy. 8:30.

2. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti Yehova amapereka ntchito kwa angelo.

2 M’Baibulo muli zitsanzo zambiri zosonyeza kuti Yehova amapereka ntchito kwa angelo. Adamu ndi Hava atachimwa n’kuthamangitsidwa m’Paradaiso, Mulungu “anaika akerubi kum’mawa kwa munda wa Edeniwo. Anaikanso lupanga loyaka moto, limene linali kuzungulira mosalekeza, kutchinga njira yopita ku mtengo wa moyo.” (Gen. 3:24) Lemba la Chivumbulutso 22:6 limasonyezanso kuti Yehova “anatumiza mngelo wake kudzaonetsa akapolo ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwa.”

 KODI YEHOVA AMAPATSANSO ANTHU ZOCHITA?

3. Kodi Yesu ankatsanzira bwanji Atate wake pamene anali padziko lapansi?

3 Yesu ali padziko lapansi ankagwira mosangalala ntchito imene Yehova anamupatsa. Iye ankatsanziranso Atate wake chifukwa ankapatsa ophunzira ake zochita. Powathandiza kudziwa kuti adzachita zinthu zambiri zosangalatsa, Yesu anati: “Ndithudi ndikukuuzani, Wokhulupirira ine, nayenso adzachita ntchito zimene ine ndimachita, ndipo adzachita ntchito zazikulu kuposa zimenezi, chifukwa ine ndikupita kwa Atate.” (Yoh. 14:12) Yesu anasonyeza kuti ntchitoyi ndi yofunika kugwiridwa mwachangu. Iye anati: “Tiyenera kugwira ntchito za iye amene anandituma ine kudakali masana. Usiku ukubwera pamene munthu sangathe kugwira ntchito.”—Yoh. 9:4.

4-6. (a) N’chifukwa chiyani timayamikira zimene Nowa ndi Mose anachita? (b) Kodi ntchito zonse zimene Yehova amapatsa anthu n’zofanana bwanji?

4 Yesu asanabwere padzikoli, Yehova ankapatsanso anthu ntchito zofunika kwambiri. Ngakhale kuti Adamu ndi Hava analephera kugwira ntchito imene Yehova anawapatsa, panali anthu ena amene ankamumvera. (Gen. 1:28) Mwachitsanzo, Yehova anapatsa Nowa malangizo omangira chingalawa kuti anthu apulumuke Chigumula. Iye anamvera ndi mtima wonse zimene Yehova anamuuza. Timayamikira zimene anachitazi chifukwa zathandiza kuti tonsefe tikhale moyo.—Gen. 6:14-16, 22; 2 Pet. 2:5.

5 Mose anapatsidwanso malangizo omangira chihema komanso okhudza ansembe ndipo anamvera zonse. (Eks. 39:32; 40:12-16) Timayamikira zimene iye anachita atapatsidwa malangizowa. N’chifukwa chiyani tikutero? Paja mtumwi Paulo ananena kuti zinthu za m’Chilamulo zinkaimira zinthu zina zabwino kwambiri zimene zikuchitika panopa.—Aheb. 9:1-5, 9; 10:1.

6 Ntchito zimene Yehova amapatsa atumiki ake zimasintha mogwirizana ndi cholinga chake. Koma ntchito zonse n’zofanana chifukwa zakhala zikulemekeza Yehova komanso kuthandiza anthu. N’chimodzimodzi ndi ntchito zimene Yesu anagwira asanabwere padzikoli komanso atabwera. (Yoh. 4:34; 17:4) Masiku anonso, ntchito zimene timapatsidwa zimalemekeza Yehova. (Mat. 5:16; werengani 1 Akorinto 15:58.) Tiyeni tione ntchito zina zimene zikuchitika masiku ano.

TIZISANGALALA NDI NTCHITO IMENE TAPATSIDWA

7, 8. (a) Fotokozani ntchito zimene Akhristu apatsidwa. (b) Kodi tiyenera kuchita chiyani tikalandira malangizo ochokera kwa Yehova?

7 N’zosangalatsa kwambiri kuti Yehova wapatsa anthu ochimwafe mwayi wogwira naye ntchito. (1 Akor. 3:9) Ntchito zimene anthu amagwira pomanga malo a misonkhano, Nyumba za Ufumu ndiponso maofesi a nthambi zikufanana ndi zimene Nowa ndi Mose anagwira. Kaya mukukonza Nyumba ya Ufumu ya kwanu kapena mukumanga nawo likulu lathu kutauni ya Warwick ku New York, muyenera kuyamikira kwambiri mwayi wanu. (Onani chithunzi patsamba 23 chosonyeza mmene likululo lidzaonekera.) Tikutero chifukwa chakuti ntchito zonsezo ndi utumiki wopatulika. Koma ntchito yaikulu ya Akhristu ndi yothandiza anthu kudziwa Yehova. Ntchitoyi imalemekezanso Yehova ndiponso kuthandiza anthu. (Mac. 13:47-49) Gulu la Mulungu limatipatsa malangizo amene amatithandiza kugwira bwino ntchitoyi. Malangizo ena amakhala oti tisiye zimene tikuchita n’kuyamba kuchita zina.

8 Atumiki a Yehova okhulupirika amakhala ndi mtima wofunitsitsa kutsatira malangizo onse ochokera kwa Yehova. (Werengani Aheberi 13:7, 17.) Poyamba, mwina sitingamvetse zifukwa zosinthira. Komabe tiyenera kumvera  chifukwa chodziwa kuti kusintha kulikonse kumene Yehova amafuna kumakhala kothandiza.

9. Kodi akulu amapereka chitsanzo chotani?

9 Zimene akulu amachita potsogolera mumpingo zimasonyeza kuti ali ndi mtima wofunitsitsa kuchita zimene Yehova amafuna. (2 Akor. 1:24; 1 Ates. 5:12, 13) Iwo amagwira ntchito mwakhama ndipo amayesetsa kutsatira malangizo ngati gulu lasintha zinthu. Amachita zimenezi akapatsidwa malangizo atsopano okhudza ntchito yolalikira Ufumu. Mwina poyamba akulu ena ankaopa kuyesa njira zina zatsopano zolalikirira, koma kenako anaona ubwino wake. Mwachitsanzo, apainiya anayi ku Germany anaganiza zotsatira malangizo a mu Utumiki Wathu wa Ufumu. Iwo anapita kukalalikira kudera limene kunali mashopu ndi maofesi kumene abale ndi alongo sankafikako. Mmodzi mwa iwo anali Michael ndipo anati: “Tinali tisanalalikirepo m’dera ngati limenelo kwa zaka zambiri ndiye tinkachita mantha. Yehova ayenera kuti anadziwa zimenezi chifukwa anatithandiza kuti zinthu zitiyendere bwino. Tikusangalala kwambiri kuti tinatsatira malangizo a mu Utumiki Wathu wa Ufumu ndiponso kudalira Yehova.” Kodi inuyo mumafunitsitsa kuyesa njira zatsopano zolalikirira m’gawo lanu?

10. Kodi ndi zinthu ziti zimene zasintha m’gulu la Yehova posachedwapa?

10 Nthawi zina, zinthu zimasintha m’gulu la Yehova. Mwachitsanzo, posachedwapa maofesi a nthambi ena anaphatikizidwa. Abale ndi alongo a m’nthambizo anafunikanso kusintha. Koma pasanapite nthawi, anaona ubwino wake. (Mlal. 7:8) Abale ndi alongowo ali ndi mwayi wothandiza kuti ntchito ya Yehova iyende bwino kwambiri masiku ano.

11-13. Kodi anthu ena achita zotani chifukwa cha kusintha kwa zinthu m’gulu la Yehova?

11 Tingaphunzire zambiri kwa anthu amene anali m’nthambi zimene zinaphatikizidwazo. Ena anali atatumikira m’nthambizo kwa zaka zambiri. Mwachitsanzo, m’bale wina dzina lake Rogelio ndi mkazi wake ankatumikira kunthambi ina ya ku Central America imene inali ndi anthu ochepa. Koma iwo anapemphedwa kukatumikira kunthambi ya ku Mexico imene ili ndi anthu ambirimbiri. Rogelio anati: “Kusiyana ndi achibale ndiponso anzathu kunali kovuta kwambiri.” M’bale wina dzina lake Juan yemwe anapemphedwanso kukatumikira ku Mexico anati: “Zili ngati ndabadwanso chifukwa anthu onse ndi achilendo. Ndiyenera kuzolowera miyambo ndiponso kaganizidwe katsopano.”

12 Abale ndi alongo ena amene ankatumikira m’nthambi zina ku Ulaya anapemphedwanso kuti apite kunthambi ya ku Germany. Kunena zoona sizinali zapafupi. Mwachitsanzo, amene anali kunthambi ya ku Switzerland anazolowera kuona mapiri okongola. Pomwe anthu amene anali ku Beteli ya ku Austria ankamasuka kwambiri chifukwa chakuti inali yaing’ono. Koma abale a m’mayiko awiriwa anafunika kuchoka n’kupita ku Germany.

13 Anthu amene anasamukira m’dziko lina, anafunika kuzolowera malo ogona atsopano, anthu atsopano komanso mwina ntchito zatsopano. Anasinthanso mpingo ndi gawo lolalikira ndipo mwina anayamba kulalikira m’chilankhulo chatsopano. Zonsezi zimakhala zovuta. Koma n’chifukwa chiyani abale ndi alongo ambiri amalolera kusintha zinthu zimenezi?

14, 15. (a) Kodi anthu ena asonyeza bwanji kuti amayamikira kugwiritsidwa ntchito ndi Yehova kwina kulikonse? (b) Kodi tikuphunzira chiyani kwa anthu amenewa?

14 Mlongo wina dzina lake Grethel anati: “Ndinavomera kusamuka pofuna kusonyeza kuti ndimakonda kwambiri Yehova  kuposa dziko linalake, malo enaake kapena ntchito inayake.” Mlongo wina dzina lake Dayska anati: “Ndinakumbukira kuti amene wandipempha kuti ndisamuke ndi Yehova, choncho ndinavomera mosangalala.” André ndi Gabriela ankaonanso choncho ndipo anati: “Tinaona kuti umenewu ndi mwayi wosonyeza kuti kutumikira Yehova n’kofunika kwambiri kuposa zofuna zathu. Tinkadziuza kuti, ‘Si bwino kuchita makani ngati Yehova watipempha kuti tisinthe zinazake.’”

Kugwira ntchito ndi Yehova ndi mwayi waukulu kwambiri

15 Pophatikiza nthambi zina, abale ndi alongo ena anapemphedwa kuti akachite upainiya. Zoterezi zinachitika pamene anaphatikiza nthambi ya ku Denmark, ku Norway ndi ku Sweden n’kupanga nthambi imodzi imene imatchedwa nthambi ya ku Scandinavia. Ena amene anapemphedwa kuchita zimenezi anali Florian ndi mkazi wake Anja. Iwo anati: “Ngakhale kuti zinali zovuta, tinasangalala ndi utumiki watsopanowu. Timayamikira kugwiritsidwa ntchito ndi Yehova kwina kulikonse. Tikuona kuti iye watidalitsa kwambiri.” N’zoona kuti mwina zinthu sizingasinthe chonchi pa moyo wathu koma ndi bwino kutsanzira mtima wa abale ndi alongowa n’kumaika patsogolo zinthu zokhudza Ufumu. (Yes. 6:8) Yehova amadalitsa anthu amene amamutumikira mokhulupirika kulikonse kumene angapemphedwe kupita.

PITIRIZANI KUGWIRA NTCHITO NDI YEHOVA MOSANGALALA

16. (a) Kodi lemba la Agalatiya 6:4 limatilimbikitsa kuchita chiyani? (b) Kodi mwayi waukulu umene tingakhale nawo ndi uti?

16 Anthu ochimwafe timakonda kudziyerekezera ndi anthu ena. Koma Mawu a Mulungu amatiuza kuti tiyenera kungochita zimene ifeyo tingakwanitse. (Werengani Agalatiya 6:4.) Ambirife tilibe udindo uliwonse m’gulu la Yehova. Komanso sikuti tonsefe tingakhale apainiya, amishonale kapena kutumikira ku Beteli. N’zoona kuti kuchita zinthu zimenezi ndi mwayi waukulu. Koma mwayi  waukulu kwambiri umene tonsefe tili nawo ndi wogwira ntchito yolalikira limodzi ndi Yehova. Tiyenera kuyamikira kwambiri mwayi umenewu.

17. (a) Kodi m’dzikoli tiyenera kuvomereza mfundo iti? (b) N’chifukwa chiyani sitiyenera kutaya mtima?

17 M’dzikoli zinthu zina zingatilepheretse kuchita zambiri potumikira Yehova. Tikhoza kulephera kuchita zinthu zina chifukwa cha udindo wathu m’banja, thanzi lathu kapena mavuto ena. Koma sitiyenera kutaya mtima. Tonsefe tili ndi mwayi wogwira ntchito ndi Mulungu pouza anthu za dzina lake ndiponso Ufumu wake. Chofunika kwambiri ndi kuchita zonse zimene tingathe pomutumikira komanso kupempherera anthu ena amene akuchita zambiri. Tizikumbukira kuti Yehova amaona kuti munthu aliyense amene amamutamanda ndi wofunika kwambiri.

18. Kodi panopa tiyenera kuchita chiyani, osati chiyani? Perekani chifukwa.

18 Ngakhale kuti ndife anthu ochimwa, Yehova amafunitsitsa kugwira nafe ntchito. Tiziyamikira kwambiri mwayi wogwira ntchito ndi Mulungu wathu m’masiku otsiriza ano. Choncho tiyenera kukhala ofunitsitsa kutumikira Yehova osati kutsatira zofuna zathu. Tizikumbukira kuti m’dziko latsopano ndi mmene tidzakhala ndi “moyo weniweniwo.” Moyowu udzakhala wosatha, wosangalatsa ndiponso wamtendere.—1 Tim. 6:18, 19.

Kodi mumayamikira mwayi wanu wotumikira Yehova? (Onani ndime 16 mpaka 18)

19. Kodi tikuyembekezera chiyani m’tsogolomu?

19 Posachedwapa tilowa m’dziko latsopano. Choncho tingachite bwino kukumbukira zimene Mose anauza Aisiraeli atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Iye anati: “Yehova Mulungu wako adzakuchititsa kukhala ndi zinthu zosefukira pa ntchito iliyonse ya manja ako.” (Deut. 30:9) Nkhondo ya Aramagedo ikadzatha, anthu onse amene akhala akugwira ntchito ndi Mulungu adzalowa m’dziko latsopano limene iye wawalonjeza. Pa nthawiyo, tidzagwira ntchito yatsopano yokonza dzikoli kuti likhale paradaiso.