Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Kuuka kwa Yesu Kumatithandiza Bwanji?

Kodi Kuuka kwa Yesu Kumatithandiza Bwanji?

“Wauka kwa akufa.”—MAT. 28:6.

1, 2. (a) Kodi atsogoleri achipembedzo anafunsa Petulo kuti chiyani? (b) Kodi Petulo anayankha bwanji? (Onani chithunzi pamwambapa.) (c) N’chiyani chinathandiza Petulo kuti alimbe mtima?

PASANAPITE nthawi yaitali kuchokera pamene Yesu anaukitsidwa, Petulo anachiritsa munthu wolumala chibadwire. Ndiyeno atsogoleri achipembedzo, amene anachititsa kuti Yesu aphedwe, anakwiya kwambiri n’kumufunsa kuti: “Kodi mwachita zimenezi ndi ulamuliro uti kapena m’dzina la ndani?” Mtumwi Petulo anawayankha molimba mtima kuti: “M’dzina la Yesu Khristu Mnazareti uja, amene inu munamupachika pamtengo, koma amene Mulungu anamuukitsa kwa akufa, kudzera mwa iyeyo, munthu uyu waimirira pamaso panu atachira bwinobwino.”—Mac. 4:5-10.

2 M’mbuyomo, Petulo anakana Yesu katatu chifukwa cha mantha. (Maliko 14:66-72) Koma kodi n’chiyani chinamulimbitsa mtima pa nthawiyi kuti awayankhe chonchi atsogoleri achipembedzowo? N’zoona kuti mzimu woyera unamuthandiza koma iye anatsimikiziranso zoti Yesu waukitsidwa. Kodi iye anatsimikizira bwanji zimenezi? Nanga ndi zinthu ziti zimene zimatichititsanso kutsimikizira kuti Yesu anaukitsidwa?

3, 4. (a) Kodi ndi anthu ati amene anaukitsidwa atumwi asanabadwe? (b) Nanga ndi anthu ati amene anaukitsidwa ndi Yesu?

3 Nkhani ya kuuka kwa akufa sinali yachilendo kwa ophunzira  a Yesu. Tikutero chifukwa chakuti anthu ena anali ataukitsidwapo atumwiwo asanabadwe. Ophunzirawo ankadziwa kuti Mulungu anapatsa Eliya ndi Elisa mphamvu youkitsa akufa. (1 Maf. 17:17-24; 2 Maf. 4:32-37) Munthu wina anaukanso mtembo wake utangoponyedwa m’manda n’kukhudza mafupa a Elisa. (2 Maf. 13:20, 21) Akhristu oyambirira ankakhulupirira nkhani za m’Malemba zimenezi. Ifenso masiku ano timakhulupirira kuti Mawu a Mulungu ndi oona.

4 Mosakayikira, tonsefe talimbikitsidwa powerenga nkhani za anthu amene anaukitsidwa ndi Yesu. Mwachitsanzo, Yesu anaukitsa mwana wa mkazi wina wamasiye ndipo mkaziyo ayenera kuti anadabwa kwambiri. (Luka 7:11-15) Pa nthawi ina, Yesu anaukitsa kamtsikana ka zaka 12. Makolo ake ayenera kuti anasangalala koopsa kuona kuti mwana wawo wauka. (Luka 8:49-56) Anthu ayenera kuti anasangalalanso kwambiri kuona Lazaro akutuluka m’manda ali bwinobwino.—Yoh. 11:38-44.

KUUKA KWA YESU KUNALI KOSIYANA NDI KWA ANTHU ENA

5. Kodi kuuka kwa Yesu kunali kosiyana bwanji ndi kuuka kwa anthu ena m’mbuyomo?

5 Atumwi ankadziwa kuti kuuka kwa Yesu kunali kosiyana ndi kwa anthu ena amene anaukitsidwa m’mbuyomo. Anthu enawo atauka, anadzafanso. Koma Yesu anaukitsidwa ndi thupi lauzimu loti silingawonongeke. (Werengani Machitidwe 13:34.) Petulo analemba kuti Yesu “anaphedwa m’thupi, koma anaukitsidwa monga mzimu.” Panopa “iye ali kudzanja lamanja la Mulungu, pakuti anapita kumwamba, ndipo angelo, maulamuliro, ndi mphamvu zinakhala pansi pake.” (1 Pet. 3:18-22) N’zoona kuti kuuka kwa anthu ena aja kunali kodabwitsa koma sikungafanane ndi kuuka kwa Yesu.

6. Kodi kuuka kwa Yesu kunathandiza bwanji ophunzira ake?

6 Kuuka kwa Yesu kunathandiza kwambiri ophunzira ake. Adani ake ankaganiza kuti wafa basi koma iye anali moyo ndipo thupi lake lauzimulo linali loti palibe angaliwononge. Kuuka kwake kunatsimikizira kuti iye anali Mwana wa Mulungu ndipo izi zinathandiza ophunzira ake kuti asiye kumva chisoni n’kuyamba kusangalala kwambiri. Anasiyanso kuchita mantha n’kukhala olimba mtima kwambiri. Kuuka kwa Yesu kunali kofunika kwambiri kuti cholinga cha Yehova chikwaniritsidwe komanso kuti anthu akhulupirire uthenga wabwino umene unkalalikidwa kulikonse.

7. (a) Kodi Yesu akuchita chiyani panopa? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

7 Ena amaganiza kuti Yesu anangokhala munthu wabwino kwambiri amene anali moyo pa nthawi inayake. Koma atumiki a Yehovafe timadziwa kuti iye adakali moyo ndipo akutsogolera ntchito imene ikukhudza aliyense padzikoli. Iye ndi Mfumu ya Ufumu wa Mulungu ndipo posachedwapa adzathetsa mavuto onse. Adzasinthanso dzikoli kuti likhale paradaiso n’cholinga choti anthu akhalemo kosatha. (Luka 23:43) Yesu akanapanda kuuka, zonsezi sizikanatheka. Koma kodi pali zifukwa ziti zotichititsa kukhulupirira kuti iye anaukadi? Nanga kuuka kwake kumatithandiza bwanji?

YEHOVA ANASONYEZA KUTI ANGAGONJETSE IMFA

8, 9. (a) N’chifukwa chiyani atsogoleri achipembedzo chachiyuda anapempha kuti akhwimitse chitetezo pamanda a Yesu? (b) N’chiyani chinachitika azimayi ena atafika pamandapo?

8 Yesu ataphedwa, ansembe aakulu ndi Afarisi anapita kwa Pilato n’kunena kuti: “Bwana, ife takumbukira kuti wonyenga uja adakali moyo ananena kuti, ‘Patapitua masiku  atatu ndidzauka.’ Choncho lamulani kuti akhwimitse chitetezo pamandapo kufikira tsiku lachitatu, kuti ophunzira ake asabwere kudzamuba ndi kuuza anthu kuti, ‘Anauka kwa akufa!’ pakuti chinyengo chotsirizachi chidzakhala choipa kwambiri kuposa choyamba chija.” Ndiyeno Pilato anawayankha kuti: “Inu muli nawo asilikali olondera. Pitani kakhwimitseni chitetezo monga mmene mukudziwira.” Choncho anakakhwimitsadi chitetezo pamandapo.—Mat. 27:62-66.

9 Thupi la Yesu linaikidwa m’manda osemedwa m’thanthwe ndipo pakhomo pake anatsekapo ndi chimwala chachikulu. Atsogoleri achipembedzo chachiyuda ankafuna kuti Yesu akhalebe m’mandamo mpaka kalekale. Koma izi si zimene Yehova ankafuna. Mariya Mmagadala ndi Mariya wina atapita pamandapo tsiku lachitatu, anapeza chimwalacho chitagubuduzidwa ndipo mngelo anachikhalira. Mngeloyo anauza azimayiwo kuti akasuzumire m’mandawo kuti aone kuti mulibe aliyense. Mngeloyo anati: “Iye sali pano chifukwa wauka kwa akufa.” (Mat. 28:1-6) Yesu anali ataukadi.

10. Kodi Paulo anafotokoza zotani popereka umboni wakuti Yesu anaukitsidwa?

10 Zimene zinachitika pa masiku 40 otsatira zinapereka umboni wamphamvu wakuti Yesu anaukitsidwa. Mtumwi Paulo anafotokoza umboniwu m’kalata yake yopita kwa Akorinto. Iye anati: “Mwa zinthu zofunika kwambiri zimene ndinakupatsirani zija, zimenenso ineyo ndinalandira, panali zonena kuti, Khristu anafera machimo athu, malinga ndi Malemba. Ndiponso kuti anaikidwa m’manda, kenako anaukitsidwa tsiku lachitatu, mogwirizana ndi Malemba. Panalinso zoti anaonekera kwa Kefa, kenako kwa atumwi 12 aja. Ndiyeno anaonekeranso kwa abale oposa 500 pa nthawi imodzi, ndipo ambiri a iwo akali ndi moyo mpaka lero, koma ena anagona mu imfa. Kenako anaonekera kwa Yakobo, kenakonso kwa atumwi onse. Koma pomalizira pake anaonekera kwa ine, ngati khanda lobadwa masiku asanakwane.”—1 Akor. 15:3-8.

KODI TIKUDZIWA BWANJI KUTI YESU ANAUKITSIDWA?

11. N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yesu anauka “mogwirizana ndi Malemba”?

11 Iye anauka “mogwirizana ndi Malemba.” Mawu a Mulungu ananeneratu kuti Yesu adzaukitsidwa. Mwachitsanzo, Davide analemba kuti “wokhulupirika” wa Mulungu sadzamusiya m’Manda. (Werengani Salimo 16:10.) Pa Pentekosite mu 33 C.E., mtumwi Petulo anasonyeza kuti lembali linaneneratu za Yesu. Iye anati: “[Davide] anaoneratu zapatsogolo ndi kuneneratu za kuuka kwa Khristu. Ananeneratu kuti iye sanasiyidwe m’Manda, komanso kuti thupi lake silinavunde.”—Mac. 2:23-27, 31.

12. Kodi Yesu atauka anaoneka kwa anthu ati?

12 Tili ndi umboni wa anthu ambiri amene anamuona ataukitsidwa. Yesu ataukitsidwa anaonekera kwa anthu osiyanasiyana kwa masiku 40. Mwachitsanzo, anaonekera kwa ophunzira ake pafupi ndi manda ndiponso pamsewu wopita ku Emau. (Luka 24:13-15) Iye analankhula ndi anthu osiyanasiyana monga Petulo. Pa nthawi ina, anaonekeranso kwa anthu oposa 500. Umboni umene anthu ambirimbiriwa anapereka ndi wosatsutsika.

13. Kodi khama limene ophunzira anali nalo limasonyeza bwanji kuti sankakayikira zoti Yesu wauka?

13 Ophunzira a Yesu ankalalikira mwakhama za kuuka kwake. Iwo ankazunzidwa komanso kuphedwa chifukwa cholalikira mwakhama za kuuka kwa Yesu. Nkhani yoti Yesu anauka ikanakhala yongopeka, kodi Petulo akanaika moyo wake pangozi n’kunena  zimenezi kwa atsogoleri achipembedzo amene anaphetsa Yesuyo? Petulo ndi ophunzira ena sankakayikira zoti Yesu ali moyo ndipo akutsogolera ntchito imene Mulungu anawapatsa. Kuuka kwa Yesu kunathandiza ophunzirawo kudziwa kuti nawonso akamwalira adzaukitsidwa. Mwachitsanzo, pamene Sitefano ankaphedwa sanakayikire zoti akufa adzauka.—Mac. 7:55-60.

14. N’chiyani chimakutsimikizirani kuti Yesu ali moyo?

14 Pali umboni wakuti iye ndi Mfumu komanso Mutu wa mpingo wachikhristu. Zinthu zikuyenda bwino kwambiri mumpingo wachikhristu, ndipo zili choncho chifukwa chakuti Yesu anauka. Akanakhala kuti sanauke, mwina si bwenzi titamva chilichonse chokhudza iye. Panopa tili ndi umboni wotsimikizira kuti iye ali moyo ndipo akutitsogolera pa ntchito yolalikira uthenga wabwino padziko lonse.

KODI KUUKA KWA YESU KUMATITHANDIZA BWANJI?

15. Kodi kuuka kwa Yesu kumatithandiza bwanji kuti tizilalikira molimba mtima?

15 Kuuka kwa Yesu kumatithandiza kuti tizilalikira molimba mtima. Kwa zaka 2,000, adani a Mulungu akhala akuyesetsa kuletsa ntchito yolalikira uthenga wabwino. Iwo agwiritsa ntchito zinthu monga mpatuko, mawu achipongwe, chiwawa, malamulo oletsa ntchitoyi, kuzunza Akhristu komanso kuwapha. Koma palibe zimene adaniwo achita zomwe zalepheretsa ntchito imeneyi. (Yes. 54:17) Sitiopa anthu amene Satana akuwagwiritsa ntchito chifukwa Yesu ali nafe ndipo akutithandiza mogwirizana ndi zimene analonjeza. (Mat. 28:20) Ngakhale adani athu atayesetsa bwanji, sangatilepheretse kugwirabe ntchito yolalikira.

Kuuka kwa Yesu kumatithandiza kuti tizilalikira molimba mtima (Onani ndime 15)

16, 17. (a) Kodi kuuka kwa Yesu kumatsimikizira bwanji kuti zonse zimene ankaphunzitsa n’zoona? (b) Malinga ndi Yohane 11:25, kodi Mulungu wapatsa Yesu mphamvu yotani?

16 Kuuka kwa Yesu kumatitsimikizira kuti zonse zimene ankaphunzitsa n’zoona. Paulo analemba kuti ngati Khristu sanauke, ndiye kuti zimene Akhristu amakhulupirira komanso kuphunzitsa n’zachabechabe. Katswiri wina wa Baibulo analemba kuti: “Ngati Khristu sanaukitsidwe, . . . ndiye kuti Akhristu ndi anthu omvetsa chisoni chifukwa apusitsidwa kwambiri.” Ngati Yesu sanauke, ndiye kuti mabuku a Uthenga Wabwino amangofotokoza nkhani yomvetsa chisoni yonena za munthu wabwino komanso wanzeru amene anaphedwa ndi adani ake. Koma Khristu anauka ndipo izi zikutsimikizira kuti zonse zimene anaphunzitsa n’zoona. Zikutsimikiziranso kuti zinthu zimene ananena za m’tsogolo zidzakwaniritsidwadi.—Werengani 1 Akorinto 15:14, 15, 20.

17 Yesu anati: “Ine ndine kuuka ndi moyo. Aliyense wokhulupirira mwa ine, ngakhale amwalire, adzakhalanso ndi moyo.” (Yoh. 11:25) Sitiyenera kukayikira kuti mawuwa adzakwaniritsidwa. Yehova wapatsa Yesu mphamvu youkitsa anthu. Ena mwa anthuwo adzakhala kumwamba koma mabiliyoni ambiri adzakhala ndi mwayi wolandira moyo wosatha padziko lapansi. Chifukwa cha nsembe ya Yesu ndiponso kuuka kwake, imfa sidzakhalaponso. Mfundo imeneyi imatilimbikitsa ndiponso kutithandiza kupirira mayesero alionse moti ngakhale imfa sitiiopa.

18. Kodi kuuka kwa Yesu kumatitsimikiziranso za chiyani?

18 Kuuka kwa Yesu kumatitsimikiziranso kuti anthu adzaweruzidwa mwachikondi komanso mogwirizana ndi mfundo za Yehova. Polankhula ndi anthu ena mumzinda wa Atene, Paulo anati: “[Mulungu] akufuna  kudzaweruza m’chilungamo dziko lapansi kumene kuli anthu, kudzera mwa munthu amene iye wamuika. Ndipo wapereka chitsimikizo kwa anthu onse mwa kumuukitsa kwa akufa.” (Mac. 17:31) Mulungu wasankha Yesu kuti aweruze anthu ndipo n’zosakayikitsa kuti adzaweruza mwachilungamo komanso mwachikondi.—Werengani Yesaya 11:2-4.

19. Kodi kukhulupirira kuti Yesu anaukitsidwa kumatithandiza bwanji?

19 Kukhulupirira zoti Yesu anaukitsidwa kumatilimbikitsa kuti tizichita zimene Mulungu amafuna. Ngati Yesu sakanapereka moyo wake nsembe komanso kuuka, sitikanamasulidwa ku uchimo ndi imfa. (Aroma 5:12; 6:23) Yesu akanapanda kuukitsidwa, bwenzi tikungoyendera zoti: “Tiyeni tidye ndi kumwa, pakuti mawa tifa.” (1 Akor. 15:32) Koma sitiyendera maganizo amenewa. M’malomwake, timayembekezera kuti anthu adzaukitsidwa ndipo timayesetsa kutsatira malangizo a Mulungu nthawi zonse.

20. Kodi kuuka kwa Yesu kumasonyeza bwanji kuti Yehova ndi wamphamvu yonse?

20 Kuukitsidwa kwa Yesu kumapereka umboni wosatsutsika wakuti Yehova ndi wamphamvu yonse ndipo “amapereka mphoto kwa anthu omufunafuna ndi mtima wonse.” (Aheb. 11:6) Pamene Yehova anaukitsa Yesu n’kumupatsa moyo wosawonongeka kumwamba, anasonyeza kuti ndi wamphamvu komanso wanzeru kwambiri. Mulungu anasonyezanso kuti adzakwaniritsa malonjezo ake onse. Mwachitsanzo, adzakwaniritsa lonjezo lake lakuti “mbewu” yapadera idzakhala ndi udindo waukulu potsimikizira kuti Mulungu ndi woyenera kulamulira. Yesu anayenera kufa ndiponso kuukitsidwa kuti lonjezoli likwaniritsidwe.—Gen. 3:15.

21. Kodi inuyo mumamva bwanji mukaganizira zoti akufa adzauka?

21 Tiyenera kuyamikira kwambiri Yehova chifukwa chokonza zoti akufa adzauke. Baibulo limatiuza kuti: “Taonani! Chihema cha Mulungu chili pakati pa anthu. Iye adzakhala pamodzi nawo, ndipo iwo adzakhala anthu ake. Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nawo. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.” Tisamakayikire zimenezi chifukwa Yesu Khristu, yemwe anaukitsidwa, ndi amene anauza mtumwi Yohane kuti alembe mawu amenewa ndipo anamuuza kuti: “Lemba, pakuti mawu awa ndi odalirika ndi oona.”—Chiv. 1:1; 21:3-5.