Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tifunika Kukhala Oyela m’Makhalidwe Athu Onse

Tifunika Kukhala Oyela m’Makhalidwe Athu Onse

“Inunso khalani oyela m’makhalidwe anu onse.”—1 PET. 1:15.

1, 2. (a) Kodi Yehova amafuna kuti anthu ake akhale ndi khalidwe lotani? (b) Ndi mafunso ati amene adzayankhidwa m’nkhani ino?

MOUZILIDWA, mtumwi Petulo anagwila mau a m’buku la Levitiko. Iye anafotokoza kuti Akristu ayenela kukhala oyela monga mmene Aisiraeli anafunikila kukhalila oyela. (Ŵelengani 1 Petulo 1:14-16.) Yehova amene ndi “Woyela” amafuna kuti odzozedwa ndi a “nkhosa zina” azicita zonse zimene angathe kuti akhale oyela m’makhalidwe ao onse.Yoh. 10:16.

2 M’nkhani ino, tidzakambilana mfundo zina za m’buku la Levitiko, zimene zidzatithandiza kuphunzila miyezo ya Mulungu ya ciyelo, ndi mmene tingaigwilitsile nchito paumoyo wathu. Tidzakambilananso mafunso awa: Kodi kupeputsa malamulo a Mulungu tiyenela kukuona motani? Tingaphunzile ciani m’buku la Levitiko cimene cingatithandize kucilikiza ulamulilo wa Yehova? Nanga tiphunzilapo ciani pa nsembe zimene Aisiraeli anali kupeleka?

MUSAPEPUTSE MALAMULO A MULUNGU

3, 4. (a) N’cifukwa ciani Akristu sayenela kupeputsa malamulo ndi mfundo za m’Baibulo? (b) Nanga n’cifukwa ciani sitiyenela kubwezela coipa ndi kusunga cakukhosi?

3 Ngati tifuna kokondweletsa Yehova, tifunika kutsatila kwambili malamulo ndi mfundo zake, ndipo sitiyenela kutengela  khalidwe lopeputsa malamulo ndi mfundo zimenezo. Ngakhale kuti sitili pansi pa Cilamulo ca Mose, malamulo ake amatithandiza kudziŵa zimene Mulungu amavomeleza ndi zimene savomeleza. Mwacitsanzo, Aisiraeli anauzidwa kuti: “Usabwezele coipa kapena kusungila cakukhosi anthu amtundu wako. Uzikonda mnzako mmene umadzikondela wekha. Ine ndine Yehova.”—Lev. 19:18.

4 Yehova safuna kuti tizibwezela coipa, ndi kusunga cakukhosi. (Aroma 12:19) Ngati tinganyalanyaze malamulo ndi mfundo za Mulungu, zimenezo zingakondweletse Mdyelekezi, ndi kunyozetsa dzina la Yehova. Ngati munthu wina watikhumudwitsa mwadala, tisalole kukhala ziwiya za Satana zosungilamo mkwiyo. Mulungu watipatsa mwai wokhala ziwiya ‘zoumbidwa ndi dothi,’ zosungilamo zinthu zamtengo wapatali, umene ndi utumiki. (2 Akor. 4:1, 7) Conco, sitiyenela kusunga mkwiyo, umene uli ngati poizoni, m’ziwiya zosungilamo zinthu zamtengo wapatali.

5. Tingaphunzile ciani pa nkhani ya Aroni ndi imfa ya ana ake? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

5 Pa Levitiko 10:1-11, timaŵelengapo cocitika cimene cinabweletsa cisoni ku banja la Aroni. Yehova anatuma moto kucoka kumwamba kuti unyeketse Nadabu ndi Abihu, ana a Aroni. Ndiyeno, Mulungu anauza Aroni kuti sayenela kumva cisoni mwanjila iliyonse. Zimenezi zinayesa cikhulupililo ca Aroni ndi banja lake. Kodi mumaonetsa kuti ndinu woyela mwa kupewa kuyanjana ndi aliyense wa m’banja amene ndi wocotsedwa?—Ŵelengani 1 Akorinto 5:11.

6, 7. (a) Tisanasankhe zopita ku cikwati cimene cidzacitikila m’chalichi, ndi mfundo zofunika ziti zimene tiyenela kuganizilapo mwakuya? (Onani mau a munsi.) (b) Tingafotokoze motani zifukwa zimene takanila kupita ku cikwati cimene cidzacitikila m’chalichi?

6 Mwina sitingayesedwe mofanana ndi Aroni ndi banja lake. Nanga bwanji ngati tapemphedwa kukapezeka ndi kutengako mbali pa cikwati ca wacibale wathu amene si Mboni, cimene cidzacitikila m’chalichi? Palibe lamulo lacindunji la m’Malemba lotiletsa kukapezekapo. Koma m’Baibulo muli mfundo zina zimene zingatithandize kupanga cosankha. *

7 Kufunitsitsa kwathu kukhala oyela kungakhumudwitse acibale athu amene si Mboni. (1 Pet. 4:3, 4) N’zoona kuti timayesetsa kuti tisawakhumudwitse. Conco, ndi bwino kukamba nao mokoma mtima, koma mosapita m’mbali. Tingacite zimenezi pasadakhale, ndi kuwayamikila pa ciitano cao. Ndiyeno, tingawafotokozele kuti tifuna akasangalale pa cikwati cao. Ndipo sitifuna kuti io ndi anthu oitanidwa akacite manyazi ife tikadzakana kutenga nao mbali m’miyambo yacipembedzo. Imeneyi ndi njila imodzi imene tingaonetsele kuti sitikupeputsa zimene timakhulupilila.

KHALANI KUMBALI YA ULAMULILO WA YEHOVA

8. Kodi buku la Levitiko limagogomezela bwanji za ulamulilo wa Yehova?

8 Buku la Levitiko limagogomezela za ulamulilo wa Yehova. Nthawi zoposa 30, timaŵelenga kuti malamulo a m’buku la Levitiko anacokela kwa Yehova. Mose anadziŵa zimenezi, ndipo anacita zonse zimene Yehova anam’lamulila. (Lev. 8:4, 5) Mofananamo, nthawi zonse tizicita zimene Wolamulila wathu, Yehova, amafuna kuti ticite. Gulu la Mulungu limatithandiza kuti tikwanitse kucita zimenezi. Koma cikhulupililo cathu cingayesedwe pamene tili tokha, monga mmene zinalili kwa Yesu m’cipululu. (Luka 4:1-13) Ngati timacilikiza ulamulilo wa Mulungu ndi kum’khulupilila, palibe aliyense angaticititse kuti tipeputse  malamulo ake. Ndipo sitidzaopa anthu.—Miy. 29:25.

9. N’cifukwa ciani anthu a Mulungu amadedwa ndi mitundu yonse?

9 Pokhala otsatila a Kristu ndiponso Mboni za Yehova, timazunzidwa padziko lonse. Zimenezi n’zosadabwitsa cifukwa Yesu anati: “Anthu adzakupelekani ku cisautso ndipo adzakuphani. Mitundu yonse idzadana nanu cifukwa ca dzina langa.” (Mat. 24:9) Komabe, ngakhale kuti timadedwa, timapitilizabe kulalikila za Ufumu ndi kukhalabe oyela pamaso pa Yehova. Nanga n’cifukwa ciani timadedwa ngakhale kuti ndife anthu oona mtima, a makhalidwe abwino, ndi otsatila malamulo? (Aroma 13:1-7) Cifukwa cakuti tapanga Yehova kukhala Ambuye wathu Wamkulu Koposa. Timalambila “iye yekha basi,” ndipo sitipeputsa malamulo ake ndi mfundo zake zolungama.—Mat. 4:10.

10. N’ciani cinacitika kwa m’bale wina atatengako mbali m’ndale?

10 Cifukwa cina n’cakuti ‘sitili mbali ya dzikoli.’ Conco, sititengako mbali pa nkhondo ndi ndale za m’dzikoli. (Ŵelengani Yohane 15:18-21; Yesaya 2:4.) Akristu ena odzipeleka kwa Mulungu analoŵelela m’ndale. Pambuyo pake, ambili a io analapa ndipo anakhalanso paubale ndi Atate wathu wacifundo wakumwamba. (Sal. 51:17) Komabe, ena ocepa sanalape. Mwacitsanzo, pa nkhondo yaciŵili ya padziko lonse, asilikali anasonkhanitsa abale athu okwanila 160 a zaka zosafika 45, amene anali m’ndende zonse za ku Hungary ndi kuwaika pamalo amodzi. Ndipo anawakakamiza kuloŵa nchito ya usilikali. Abale okhulupilika anakana kuloŵa usilikali, koma abale 9 pa gulu limenelo anavomela ndipo analandila zovala za usilikali. Pambuyo pa zaka ziŵili, mmodzi wa aja amene anavomela kuloŵa usilikali, anali pa gulu la asilikali amene anasankhidwa kukapha Mboni zokhulupilika. Ndipo pakati pa Mbonizo, panali wacibale wake. Koma zinthu zitasintha, Mboni zimenezo sizinaphedwe.

PATSANI YEHOVA ZABWINO KOPOSA

11, 12. Tiphunzilapo ciani pa nsembe zimene Aisiraeli akale anali kupeleka?

11 Mogwilizana ndi Cilamulo ca Mose, Aisiraeli anafunikila kupeleka nsembe zoyenela. (Lev. 9:1-4, 15-21) Nsembe zimenezo zinayenela kukhala zopanda cilema cifukwa zinali kuimila nsembe yangwilo ya Yesu. Ndipo popeleka nsembe iliyonse, Aisiraeli anafunikila kutsatila malangizo oikidwa. Mwacitsanzo, ganizilani zimene mai amene wabeleka mwana anafunika kupeleka. Lemba la Levitiko 12:6 limati: “Ndiyeno masiku a kuyeletsedwa kwake cifukwa cobeleka mwana wamwamuna kapena wamkazi akakwana, azibweletsa kwa wansembe, pakhomo la cihema cokumanako, nkhosa yaing’ono yamphongo yosapitilila caka cimodzi kuti ikhale nsembe yopseleza. Azibweletsanso mwana wa nkhunda kapena njiŵa kuti ikhale nsembe yamacimo.” Ngakhale kuti malamulo a Mulungu anali acindunji, malamulowo aonetsa kuti iye ndi wacikondi ndi wololela. Ngati mai sanakwanitse kupeleka nkhosa, iye anali kuloledwa kupeleka ana a nkhunda aŵili kapena njiŵa ziŵili. (Lev. 12:8) Ngakhale kuti wopelekayo anali wosauka, iye anali wokondedwa ndipo anayamikilidwa mofanana ndi ena amene anapeleka nsembe zodula kwambili. Kodi tiphunzilapo ciani pankhaniyi?

12 Mtumwi Paulo analimbikitsa okhulupilila anzake kupeleka “nsembe” zacitamando kwa Mulungu. (Aheb. 13:15) Milomo yathu iyenela kulengeza poyela dzina loyela la Yehova. Abale ndi alongo ogontha amagwilitsila nchito cinenelo camanja kutamanda Mulungu. Akristu odwala amam’tamanda mwa kulalikila pafoni, kulemba  makalata, ndi kulalikila kwa owayang’anila ndi obwela kuwaona. Zimene tingacite potamanda Yehova zimadalila mmene thanzi lathu lilili, koma tiyenela kupeleka nsembe zabwino koposa.—Aroma 12:1; 2 Tim. 2:15.

13. N’cifukwa ciani tiyenela kupeleka lipoti lathu la mu ulaliki?

13 Nsembe zathu zacitamando kwa Mulungu zimacokela pansi pamtima cifukwa timam’konda. (Mat. 22:37, 38) Nanga tiyenela kucita bwanji tikapemphedwa kupeleka lipoti lathu la utumiki wakumunda? Tiyenela kupeleka ndi mtima wonse cifukwa mwa kucita zimenezo, timaonetsa kuti ndife odzipeleka kwa Mulungu. (2 Pet. 1:7) N’zoona kuti sitiyenela kukakamizika kuthela nthawi yambili mu ulaliki kuti tizipeleka maola ambili. Ndiye cifukwa cake, ngati wofalitsa sangakwanitse kucita zambili mu ulaliki cifukwa ca ukalamba kapena thanzi, angapeleke mphindi 15, m’malo mwa maola athunthu. Popeza zimenezi n’zimene angakwanitse kucita, Yehova amakondwela nazo. Iye amadziŵa kuti abale ndi alongo athu amam’konda, ndi kuti amafunitsitsa kukhala Mboni zake. Mofanana ndi Aisiraeli amene sanali kukwanitsa kupeleka nsembe zodula kwambili, atumiki a Yehova okondedwa amene sangakwanitse kucita zambili, naonso angapeleke lipoti. Ndipo lipoti la wofalitsa aliyense limaikidwa pamodzi ndi lipoti la padziko lonse. Zimenezi zimathandiza gulu kukonzekela pasadakhale za nchito yolalikila yamtsogolo. Ndiye cifukwa cake, tifunikila kupeleka lipoti lathu la mu ulaliki.

KUPHUNZILA BAIBULO NDIPONSO NSEMBE ZACITAMANDO

14. Fotokozani cifukwa cake tiyenela kucita khama kuphunzila Baibulo.

14 Pambuyo pophunzila mfundo zina za m’buku la Levitiko, kodi mukuyamikila kwambili kuti buku limeneli linalembedwa m’Baibulo? (2 Tim. 3:16) Mwina tsopano ndinu wotsimikiza mtima kwambili kukhalabe woyela, osati cabe cifukwa cakuti n’zimene Yehova amafuna, koma cifukwa cakuti timafunikila kucita zinthu zom’kondweletsa. Mwina zimene mwaphunzila m’nkhani ziŵilizi ponena za buku la Levitiko, zakulimbikitsani kufuna kuphunzila zambili m’Malemba. (Ŵelengani Miyambo 2:1-5.) Pendani mwapemphelo ndi kuona ngati mumacita khama kuphunzila Baibulo. Mosakaikila, mumafuna kuti Yehova alandile nsembe zanu zacitamando. Koma kodi mumalola mapulogalamu a pa TV, maseŵela a pa vidiyo, maseŵela olimbitsa thupi, ndi zimene mumakonda kusokoneza kupita kwanu patsogolo kuuzimu? Ngati n’conco, mudzapindula kwambili kuganizila mfundo zina zimene mtumwi Paulo analemba m’buku la Aheberi.

Kodi mumaika phunzilo la Baibulo ndi Kulambila kwa Pabanja patsogolo m’moyo wanu? (Onani ndime 14)

15, 16. N’cifukwa ciani Paulo anakamba mosapita m’mbali polembela Akristu aciheberi?

15 Paulo anakamba mosapita m’mbali pamene analembela Akristu anzake aciheberi. (Ŵelengani Aheberi 5:7, 11-14.) Iye anawauza kuti: “Inu mumacedwa kumvetsa zinthu.” N’cifukwa ciani Paulo anawauza mosapita m’mbali? Mofanana ndi Yehova,  iye anali kuwakonda ndipo anali kuwadela nkhawa cifukwa anali kumwa cabe mkaka, m’malo mwa cakudya cotafuna ca kuuzimu. Ngakhale kuti kudziŵa ziphunzitso zoyambilila n’kofunika, tifunikila kudya “cakudya cotafuna,” cimene ndi ziphunzitso zozama za m’Baibulo. Zimenezi zidzatithandiza kukula kuuzimu.

16 M’malo mopita patsogolo ndi kukhala aphunzitsi, Aheberi anafunikila wowaphunzitsa. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti io sanali kudya “cakudya cotafuna.” Motelo, dzifunseni kuti: ‘Kodi ndimadya cakudya cotafuna ca kuuzimu? Kodi ndimanyalanyaza kupemphela ndi kuphunzila Baibulo? Ngati n’conco, kodi vuto lingakhale cizoloŵezi canga cophunzila?’ Sitiyenela kulalikila cabe, koma tiyenela kuphunzitsa ndi kupanga ophunzila.—Mat. 28:19, 20.

17, 18. (a) N’cifukwa ciani nthawi zonse tiyenela kudya cakudya ca kuuzimu? (b) Tiyenela kuiona bwanji nkhani ya kumwa zoledzeletsa tisanacite zinthu za kuuzimu?

17 Yehova safuna kuti anthu ake aziphunzila Baibulo cifukwa codziimba mlandu. N’zoona kuti kuphunzila Baibulo kungakhale kovuta kwa ambili a ife. Komabe, ngakhale kuti tatumikila Mulungu kwa zaka zambili kapena kwa nthawi yocepa, tiyenela kupitiliza kudya cakudya cotafuna ca kuuzimu. Kucita zimenezo n’kofunika kuti tipitilizebe kukhala oyela.

18 Kuti tikhale oyela, tifunikila kuphunzila Malemba mosamalitsa ndi kucita zimene Mulungu amafuna. Ganizilani za ana a Aroni, Nadabu ndi Abihu, amene anaphedwa cifukwa cofukiza “pamoto wosaloledwa,” mwina cifukwa cakuti anali okolewa. (Lev. 10:1, 2) Ndiyeno ganizilaninso zimene Mulungu anauza Aroni. (Ŵelengani Levitiko 10:8-11.) Kodi nkhani imeneyi itiphunzitsa kuti sitiyenela kumwa zakumwa zina zoledzeletsa tisanapite ku misonkhano yacikristu? Ganizilani mfundo izi: Ife sitili pansi pa Cilamulo ca Mose. (Aroma 10:4) M’maiko ena, okhulupilila anzathu amamwa zakumwa zoledzeletsa mosapitilila malile pa cakudya asanapite ku misonkhano. Ndipo pamwambo wa Pasika, panali kukhala makapu anai a vinyo. Poyambitsa mwambo wa Cikumbutso, Yesu anauza atumwi ake kuti amwe vinyo amene anali kuimila magazi ake. (Mat. 26:27) Baibulo limaletsa kumwa moŵa mopitilila malile ndi kuledzela. (1 Akor. 6:10; 1 Tim. 3:8) Ndipo Akristu ambili cikumbumtima cao cimawaletselatu kumwa vinyo asanacite zinthu zilizonse za kuuzimu. Komabe, malinga ndi maiko, mikhalidwe imasiyanasiyana. Koma cofunika kwa Akristu ndi ‘kusiyanitsa pakati pa cinthu copatulika ndi coipitsidwa,’ kuti akhale ndi khalidwe loyela limene limakondweletsa Mulungu.

19. (a) Tingacite bwanji kuti tizipindula ndi kulambila kwa pabanja ndi phunzilo laumwini? (b) Kodi mwatsimikiza mtima kucita ciani pankhani ya kukhalabe woyela?

19 Ngati tifufuza mosamalitsa, tingapeze mfundo zabwino za m’Mau a Mulungu. Gwilitsilani nchito zida zofufuzila kuti mupindule kwambili ndi kulambila kwa pabanja ndi phunzilo laumwini. Mudziŵeni bwino Yehova ndi cifunilo cake, ndipo muyandikileni kwambili. (Yak. 4:8) Tizipemphela kwa Mulungu monga mmene wamasalimo anaimbila kuti: “Tsegulani maso anga kuti ndione zinthu zodabwitsa za m’cilamulo canu.” (Sal. 119:18) Tisapeputse malamulo ndi mfundo za m’Baibulo. Koma tizimvela mocokela pansi pamtima malamulo apamwamba a Yehova, amene ndi “Woyela,” ndi kutengako mbali mwakhama pa “nchito yolengeza uthenga wabwino wa Mulungu.” (1 Pet. 1:15; Aroma 15:16). Conco, m’masiku otsiliza ano, tiyeni tonse tikhale oyela m’makhalidwe athu, ndi kukhala kumbali ya ulamulilo wa Mulungu wathu woyela, Yehova.

^ par. 6 Onani “Mafunso Ocokera kwa Owerenga” mu Nsanja ya Olonda ya May 15, 2002.