Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Anthu Amene Mulungu Wawo Ndi Yehova”

“Anthu Amene Mulungu Wawo Ndi Yehova”

“Odala ndi anthu amene Mulungu wawo ndi Yehova.”—SAL. 144:15.

1. Kodi anthu ena amati bwanji pa nkhani ya anthu a Mulungu?

ANTHU ambiri amaona kuti zipembedzo sizikuthandiza anthu. Amaona kuti Mulungu sakusangalala ndi zipembedzozi chifukwa chakuti zimene zimaphunzitsa komanso kuchita n’zosemphana ndi zimene iye amafuna. Koma amaganiza kuti m’zipembedzo zonse muli anthu ena okhulupirika amene Mulungu amawaona kuti ndi anthu ake. Choncho amaona kuti palibe vuto kukhalabe m’zipembedzozo. Koma kodi umu ndi mmene Mulungu amaonera zinthu? Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambirane mbiri ya anthu a Yehova.

PANGANO LIMENE MULUNGU ANACHITA NDI ANTHU AKE

2. Kodi ndi ndani amene anakhala anthu a Yehova, ndipo n’chiyani chinkawasiyanitsa ndi anthu ena? (Onani chithunzi pamwambapa.)

2 Pafupifupi zaka 4,000 zapitazo, Yehova anasankha ana a Abulahamu kuti akhale mtundu wake. Abulahamu ankatsogolera anthu mahandiredi angapo ndipo amatchedwa ‘tate wa onse okhala ndi chikhulupiriro.’ (Aroma 4:11; Gen. 14:14) Olamulira  a ku Kanani ankalemekeza kwambiri Abulahamu ndipo ankamuona kuti anali “mtsogoleri woikidwa ndi Mulungu.” (Gen. 21:22; 23:6) Yehova anachita pangano ndi Abulahamu komanso ana ake. (Gen. 17:1, 2, 19) Mulungu anauza Abulahamu kuti: “Ili ndi pangano limene anthu inu muyenera kulisunga, la pakati pa ine ndi inu, ngakhalenso mbewu yobwera pambuyo pa inu. Mwamuna aliyense pakati pa inu azidulidwa. Muzichita mdulidwe kuti ukhale chizindikiro cha pangano la pakati pa ine ndi inu.” (Gen. 17:10, 11) Pomvera zimenezi, Abulahamu ndi amuna onse a m’nyumba yake anadulidwa. (Gen. 17:24-27) Mdulidwe unali chizindikiro chosiyanitsa ana a Abulahamu ndi anthu ena ndiponso chosonyeza kuti Yehova anachita nawo pangano.

3. Kodi ana a Abulahamu anakhala bwanji mtundu waukulu wa anthu?

3 Yakobo, yemwe ankadziwikanso kuti Isiraeli, anali mdzukulu wa Abulahamu ndipo anali ndi ana aamuna okwana 12. (Gen. 35:10, 22b-26) Anawo anadzakhala mitu ya mafuko 12 a Isiraeli. (Mac. 7:8) Yosefe, yemwe anali mwana wa Yakobo, anadzakhala woyang’anira nyumba ya Farao komanso zakudya zonse za mu Iguputo. Kenako Yakobo ndi banja lake anasamukira ku Iguputo chifukwa cha njala. (Gen. 41:39-41; 42:6) Ali kumeneko, ana a Yakobo anachuluka kwambiri ndipo anakhala mtundu waukulu wa anthu.—Gen. 48:4; werengani Machitidwe 7:17.

YEHOVA ANAPULUMUTSA ANTHU AKE

4. Kodi poyamba ana a Yakobo ankakhala bwanji ndi Aiguputo?

4 Farao amene ankadziwana ndi Yosefe analandira bwino ana a Yakobo. (Gen. 47:1-6) Iwo anakhala ku Iguputo kwa zaka zoposa 200 m’dera lotchedwa Goseni, lomwe linali pafupi ndi mtsinje wa Nailo. (Gen. 45:9, 10) Pa zaka 100 zoyambirira, ankakhala mwamtendere ndi Aiguputo. Iwo ankakhala m’midzi yawo ndipo ankaweta ziweto. Aiguputo ankadana ndi anthu oweta nkhosa koma anayenera kumvera lamulo la Farao lolola Aisiraeli kuti azikhala kumeneko.—Gen. 46:31-34.

5, 6. (a) Kodi moyo wa anthu a Mulungu unasintha bwanji ku Iguputo? (b) Kodi Mose anapulumuka bwanji ali mwana? (c) Kodi Yehova anathandiza bwanji anthu ake?

5 Koma “patapita nthawi, mfumu ina yomwe sinam’dziwe Yosefe inayamba kulamulira mu Iguputo ndipo zinthu zinasinthiratu. Mfumuyo inauza anthu ake kuti: ‘Taonani! Ana a Isiraeli achuluka kwambiri ndipo ndi amphamvu kuposa ife.’ Chotero, Aiguputo anagwiritsa ana a Isiraeli ntchito yaukapolo mwankhanza. Iwo anasautsa moyo wa Aisiraeliwo powagwiritsa ntchito yowawa yaukapolo, yomwe inali yoponda matope ndi kuumba njerwa. Anawagwiritsa ntchito yaukapolo wa mtundu uliwonse m’munda, ndi ukapolo wa mtundu uliwonse umene anatha kuwagwiritsa ntchito mwankhanza.”—Eks. 1:8, 9, 13, 14.

6 Faraoyo analamula kuti ana aamuna onse achiheberi aziphedwa akangobadwa. (Eks. 1:15, 16) Ndiyeno Mose anabadwa pa nthawi imeneyi. Atafika miyezi itatu, mayi ake anakamubisa kumtsinje. Mwana wamkazi wa Farao anamupeza n’kumutenga kuti akhale mwana wake. Koma anamupereka kwa mayi ake a Moseyo, dzina lawo a Yokebedi, kuti amulere pa zaka zake zoyambirira. Mose anakula bwino n’kukhala mtumiki wa Yehova wokhulupirika. (Eks. 2:1-10; Aheb. 11:23-25) Yehova ataona mavuto a Aisiraeli, anagwiritsa ntchito Mose kuti awapulumutse.—Eks. 2:24, 25; 3:9, 10; 15:13; werengani Deuteronomo 15:15.

 ANTHUWO ANAKHALA MTUNDU WOSANKHIDWA NDI MULUNGU

7, 8. Kodi Yehova anachita chiyani kuti anthu ake akhale mtundu woyera?

7 Yehova anali asanapatse Aisiraeli malamulo komanso kusankha ansembe koma ankawaonabe kuti ndi anthu ake. Mose ndi Aroni anapemphedwa kukauza Farao kuti: “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Lolani anthu anga apite m’chipululu kuti akachite chikondwerero.’”—Eks. 5:1.

8 Koma Farao sankafuna kuti amasule Aisiraeli. Choncho Yehova anabweretsera Aiguputo miliri 10. Kenako anawononga Farao ndi asilikali ake pa Nyanja Yofiira kuti apulumutse anthu ake. (Eks. 15:1-4) Patapita miyezi pafupifupi itatu, Yehova anachita pangano ndi Aisiraeli ku phiri la Sinai ndipo anawalonjeza kuti: “Ngati mudzalabadiradi mawu anga ndi kusunga pangano langa, pamenepo mudzakhaladi chuma changa chapadera pakati pa anthu ena onse . . . ndi mtundu wanga woyera.”—Eks. 19:5, 6.

9, 10. (a) Malinga ndi Deuteronomo 4:5-8, kodi Chilamulo chinasiyanitsa bwanji Aisiraeli ndi anthu a mitundu ina? (b) Kodi Aisiraeli anayenera kuchita chiyani kuti akhale “anthu oyera kwa Yehova”?

9 Kwa zaka zambiri, anthu a Yehova ankatsogoleredwa ndi mitu ya mabanja imene inkakhalanso ngati oweruza ndiponso ansembe. (Gen. 8:20; 18:19; Yobu 1:4, 5) Izi ndi zimene zinkachitikanso ku Iguputo, Aisiraeli asanakhale akapolo. Koma Yehova anagwiritsa ntchito Mose kuti apereke malamulo kwa Aisiraeli omwe ankawasiyanitsa ndi mitundu ina. (Werengani Deuteronomo 4:5-8; Salimo 147:19, 20.) Chilamulo chinkanena kuti pazikhala ansembe ndiponso “akulu” anzeru ndi olemekezeka oti aziweruza anthu. (Deut. 25:7, 8) Mu Chilamulocho munali malangizo othandiza mtundu watsopanowu pa nkhani yolambira komanso zinthu zina.

10 Aisiraeli atatsala pang’ono kulowa m’Dziko Lolonjezedwa, Yehova anawakumbutsa malamulo ake. Mose anawauza kuti: “Lero Yehova wakuchititsani kunena kuti mudzakhala anthu ake, chuma chapadera, monga mmene anakulonjezerani, ndiponso kuti mudzasunga malamulo ake onse, ndi kuti adzakukwezani pamwamba pa mitundu ina yonse imene anapanga. Zimenezi zidzakudzetserani chitamando, mbiri yabwino ndi kukongola, mukapitiriza kukhala anthu oyera kwa Yehova Mulungu wanu.”—Deut. 26:18, 19.

ANTHU A MITUNDU INA ANKALANDIRIDWANSO

11-13. (a) Kodi ndani ankalandiridwanso m’gulu la anthu a Mulungu? (b) Kodi anthu a mitundu ina ankafunika kuchita chiyani kuti ayambe kulambira Yehova?

11 Ngakhale kuti Aisiraeli anali mtundu wosankhidwa ndi Yehova padzikoli, iye sankaletsa kuti anthu a mitundu ina akhale nawo limodzi. Mwachitsanzo, analola “khamu la anthu a mitundu yosiyanasiyana,” kuphatikizapo Aiguputo ena, kuti apite ndi Aisiraeli pamene ankawapulumutsa ku Iguputo. (Eks. 12:38) Mwina ena a Aiguputowo anali “atumiki a Farao” omwe anamvera chenjezo la Mose pa nthawi ya mliri wa nambala 7.—Eks. 9:20.

12 Aisiraeli atatsala pang’ono kuwoloka mtsinje wa Yorodano kuti alowe m’dziko la Kanani, Mose anawauza kuti: “Muzikonda mlendo wokhala pakati panu.” (Deut. 10:17-19) Ngati munthu wa mtundu wina anavomera kutsatira malamulo amene Mose anapereka, Aisiraeli ankayenera kumulola kuti azikhala nawo pamodzi. (Lev. 24:22) Anthu ena a mitundu ina anayamba kutumikira Yehova ndipo anali ndi maganizo amene Rute anali nawo. Paja iye anauza Naomi kuti: “Anthu a mtundu wanu adzakhala anthu a  mtundu wanga, ndipo Mulungu wanu adzakhala Mulungu wanga.” (Rute 1:16) Anthuwa anayamba kutsatira Chiyuda ndipo amuna anadulidwa. (Eks. 12:48, 49) Yehova anawalandiranso kuti akhale m’gulu la anthu ake.—Num. 15:14, 15.

Aisiraeli ankakonda anthu a mitundu ina (Onani ndime 11 mpaka 13)

13 Pamene Solomo ankapereka kachisi, anapempha Yehova kuti azimva mapemphero a anthu a mitundu ina. Iye anati: “Mlendo amene sali mmodzi wa anthu anu Aisiraeli, amene wabwera kuchokera kudziko lakutali chifukwa cha dzina lanu lalikulu, ndi dzanja lanu lamphamvu ndi mkono wanu wotambasuka, ndipo iwo abwera n’kupemphera atayang’ana nyumba ino, inuyo mumve muli kumwamba, malo anu okhala okhazikika, ndipo muchite mogwirizana ndi zonse zimene mlendoyo wakupemphani. Mutero n’cholinga choti anthu a mitundu yonse ya padziko lapansi adziwe dzina lanu, kuti akuopeni mofanana ndi mmene anthu anu Aisiraeli amachitira, ndiponso kuti adziwe kuti dzina lanu lili panyumba imene ndamangayi.” (2 Mbiri 6:32, 33) M’nthawi ya Yesu, anthu a mitundu ina ankafunikanso kugwirizana ndi anthu a Mulungu kuti ayambe kulambira Yehova.—Yoh. 12:20; Mac. 8:27.

MTUNDUWU UNALI MBONI

14-16. (a) N’chifukwa chiyani Yehova ankafuna kuti Aisiraeli akhale mboni zake? (b) Kodi masiku ano anthu a Yehova ayenera kuchita chiyani?

14 Aisiraeli ankalambira Yehova pomwe anthu a mitundu ina ankalambira milungu ina. Ndiyeno anthu anafunika kudziwa kuti Mulungu woona ndi uti? M’nthawi ya Yesaya, Yehova ananena kuti funsoli liyenera kuyankhidwa ngati mmene zimakhalira pozenga mlandu m’khoti. Iye anauza milungu inayo kuti ipereke mboni zawo. Anati: “Mitundu yonse isonkhanitsidwe pamalo amodzi, ndipo mitundu ya anthu ikhale pamodzi. Ndani pakati pawo amene anganene zimenezi? Kapena ndani amene angatiuze zinthu zimene zidzayambirire kuchitika? Abweretse mboni zawo kuti akhale olungama ndipo mbonizo zimve ndi kunena kuti, ‘Zimenezo ndi zoona!’”—Yes. 43:9.

15 Ndiyeno milunguyo inakanika kupereka mboni chifukwa chakuti inali mafano  osalankhula ongofunika kunyamulidwa. (Yes. 46:5-7) Koma Yehova anauza Aisiraeli kuti: “Inu ndinu mboni zanga, . . . ndinu mtumiki wanga amene ndakusankhani kuti mundidziwe ndi kundikhulupirira, komanso kuti mumvetse kuti ine sindinasinthe. Ine ndisanakhaleko kunalibe Mulungu amene anapangidwa, ndipo pambuyo panga palibenso wina. Ine ndine Yehova. Popanda ine palibenso mpulumutsi wina. . . . Choncho inuyo ndinu mboni zanga, ndipo ine ndine Mulungu.”—Yes. 43:10-12.

16 Apatu anthu a Yehova anali ndi mwayi wopereka umboni pa mlandu wa m’chilengedwe chonse n’kutsimikizira zoti Yehova ndi Mulungu weniweni. Iye anati Aisiraeliwo anali ‘anthu amene anawapanga kuti akhale anthu ake komanso kuti anene za ulemerero wake.’ (Yes. 43:21) Anthuwo ankadziwikanso ndi dzina lake. Popeza Yehova anawapulumutsa ku Iguputo, iwo anayenera kumumvera, kumulemekeza komanso kukhala ku mbali ya ulamuliro wake. Iwo anayenera kukhala ndi maganizo amene Mika anafotokoza polemba za anthu a Mulungu a m’nthawi yathu. Iye anati: “Mtundu uliwonse wa anthu udzayenda m’dzina la mulungu wake. Koma ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu mpaka kalekale, inde mpaka muyaya.”—Mika 4:5.

MTUNDUWO UNASIYA YEHOVA

17. N’chifukwa chiyani Yehova anayerekezera Aisiraeli ndi mtengo wa mpesa wachabechabe?

17 Koma chomvetsa chisoni n’chakuti Aisiraeli anasiya Yehova. Iwo anayamba kutengera mitundu ina imene inkalambira milungu yochita kusema. Cha m’ma 700 B.C.E., mneneri Hoseya analemba kuti: “Isiraeli ndi mtengo wa mpesa umene ukuwonongeka . . . wachulukitsa maguwa ansembe . . . Mtima wawo wakhala wachinyengo. Tsopano iwo adzapezeka ndi mlandu.” (Hos. 10:1, 2) Ndiyeno patapita zaka pafupifupi 150, Yeremiya anayerekezeranso Aisiraeliwo ndi mtengo wa mpesa. Iye anati: “Ndinakubzala ngati mtengo wa mpesa wofiira, wabwino kwambiri. Mtengo wonsewo unali mbewu yeniyeni yabwino. Ndiye wandisinthira bwanji kukhala mphukira yachabechabe ya mtengo wa mpesa wachilendo? Kodi milungu yako imene wadzipangira ili kuti? Imeneyo ibwere kwa iwe ngati ingathe kukupulumutsa pa nthawi ya tsoka . . . Anthu anga andiiwala.”—Yer. 2:21, 28, 32.

18, 19. (a) Kodi Yehova analosera bwanji kuti adzakhala ndi mtundu watsopano? (b) Kodi tidzakambirana mafunso ati m’nkhani yotsatira?

18 Aisiraeli sankabereka zipatso zabwino chifukwa sankalambira Yehova moyenera kapena kukhala mboni zake zokhulupirika. M’malomwake iwo ankalambira mafano. N’chifukwa chake Yesu anauza atsogoleri achiyuda kuti: “Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu n’kuperekedwa kwa mtundu wobala zipatso zake.” (Mat. 21:43) Yehova anauza Yeremiya kuti alosere za “pangano latsopano.” Ndiyeno anthu amene ali m’panganolo ndi amene angakhale mu mtundu watsopanowu, womwe ndi Isiraeli wauzimu. Ponena za anthu amene adzakhale m’pangano latsopanolo, Yehova analosera kuti: “Ine ndidzakhala Mulungu wawo ndipo iwo adzakhala anthu anga.”—Yer. 31:31-33.

19 Pamene Aisiraeli anasiya Yehova, iye anasankha Aisiraeli auzimu kuti akhale anthu ake. Izi zinachitika m’nthawi ya atumwi. Koma kodi masiku ano anthu ake padzikoli ndi ndani? Kodi anthu angadziwe bwanji atumiki enieni a Yehova? Tidzakambirana mafunsowa m’nkhani yotsatira.