Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

‘Tsopano Ndinu Anthu a Mulungu’

‘Tsopano Ndinu Anthu a Mulungu’

“Kale simunali mtundu, koma tsopano ndinu mtundu wa anthu a Mulungu.”—1 PET. 2:10.

1, 2. N’ciani cinacitika pa Pentekosite wa mu 33 C.E? Nanga ndani anakhala mtundu watsopano wa Yehova? (Onani cithunzi pamwamba.)

PA Pentekosite wa mu 33 C.E., panacitika cinthu capadela m’mbili ya anthu a Yehova padziko lapansi. Zinthu zinasintha mwadzidzidzi. Patsiku limeneli, Yehova, kupyolela mwa mzimu wake, anakhazikitsa mtundu watsopano, umene ndi Isiraeli wa kuuzimu, kapena kuti “Isiraeli wa Mulungu.” (Agal. 6:16) Paulo analemba kuti anthu amene amapanga mtundu watsopano safunika kudulidwa, monga mmene zinalili ndi mbadwa za Abulahamu. M’malo mwake, ‘mdulidwe wao ndi wa mumtima wocitidwa ndi mzimu.’—Aroma 2:29.

2 Anthu oyamba kupanga mtundu watsopano wa Mulungu anali atumwi ndi ophunzila ena a Kristu oposa mahandiledi. Anthu amenewa anasonkhana m’cipinda capamwamba ku Yerusalemu. (Mac. 1:12-15) Iwo analandila mzimu woyela umene unawapangitsa kukhala ana auzimu a Mulungu. (Aroma 8:15, 16; 2 Akor. 1:21) Izi zinapeleka umboni wakuti pangano latsopano layamba kugwila nchito, limene Kristu ndiye Mkhalapakati cifukwa ca magazi ake. (Luka 22:20; ŵelengani Aheberi 9:15.) Motelo, ophunzila amenewa anapanga mtundu watsopano wa Yehova. Ndipo mzimu woyela unawathandiza kulalikila m’zinenelo zosiyanasiyana za Ayuda ndi za anthu otembenukila  kuciyuda ocokela m’madela a Ufumu wa Roma. Anthu amenewa anabwela ku Yerusalemu kudzacita cikondwelelo ca Ayuda. Iwo anamvetsetsa m’zinenelo zao pamene Akristu odzozedwa anali kulalikila “zinthu zazikulu za Mulungu.”—Mac. 2:1-11.

MTUNDU WATSOPANO WA ANTHU A MULUNGU

3-5. (a) N’ciani cimene Petulo anauza Ayuda patsiku la Pentekosite? (b) Kodi mtundu watsopano unakula motani m’nthawi ya atumwi?

3 Yehova kupyolela mwa mtumwi Petulo, anapeleka mwai kwa Ayuda ndi anthu otembenukila kuciyuda kuti akhale mtundu watsopano, umene ndi mpingo wacikristu. Pa Pentekosite, Petulo anauza Ayuda molimba mtima kuti afunika kukhulupilila Yesu, munthu amene io ‘anamukhomelela pamtengo,’ popeza “Mulungu anamuika kukhala Ambuye ndi Kristu.” Pamene anthuwo anafunsa Petulo zimene ayenela kucita, iye anawayankha kuti: “Lapani, ndipo aliyense wa inu abatizidwe m’dzina la Yesu Kristu kuti macimo anu akhululukidwe. Mukatelo mudzalandila mphatso yaulele ya mzimu woyela.” (Mac. 2:22, 23, 36-38) Tsiku limenelo, mtundu watsopano wa Isiraeli wa kuuzimu unaonjezeka ndi anthu pafupifupi 3,000. (Mac. 2:41) Pambuyo pake, atumwi anapitiliza kugwila nchito yolalikila mwakhama ndi kubala zipatso. (Mac. 6:7) Ndithudi, mtundu watsopano umenewu unali kukulilakulila.

4 Ndiyeno, uthenga wabwino unafalikila kwa Asamariya, ndipo panakhala zotsatilapo zabwino. Anthu ambili anabatizidwa ndi mlaliki Filipo, koma io sanalandile mzimu woyela nthawi imeneyo. Motelo, bungwe lolamulila ku Yerusalemu linatumiza mtumwi Petulo ndi Yohane kwa Asamariya otembenukila kuciyuda. Atumwi amenewo “anayamba kuika manja ao pa anthuwo, ndipo analandila mzimu woyela.” (Mac. 8:5, 6, 14-17) Conco, Asamaliya amenewo naonso anadzozedwa kukhala Isiraeli wa kuuzimu.

Petulo analalikila Koneliyo ndi banja lake (Onani ndime 5)

5 Mu 36 C.E., Mulungu anagwilitsilanso nchito Petulo kupeleka mwai kwa ena kuti akhale mtundu watsopano wa Isiraeli wa kuuzimu. Anacita zimenezi pamene analalikila kwa kazembe waciroma Koneliyo, pamodzi ndi acibale ndi mabwenzi ake. (Mac. 10:22, 24, 34, 35) Baibulo limati: “Pamene Petulo anali kulankhula . . . , mzimu woyela unagwa pa onse [anthu akunja] amene anali kumvela mau amenewo. Ndipo okhulupilika amene anabwela ndi Petulo, amene anali odulidwa anadabwa, cifukwa mphatso yaulele ya mzimu woyela inalinso kuthilidwa pa anthu a mitundu ina.” (Mac. 10:44, 45) Conco, kuyambila nthawi imeneyo, anthu akunja osadulidwa anayamba kupatsidwa mwai wokhala Isiraeli wa kuuzimu.

“ANTHU ODZIŴIKA NDI DZINA LAKE”

6, 7. N’ciani cimene mtundu watsopano wa anthu unali kudzacita pokhala “anthu odziŵika ndi dzina [la Yehova]”? Nanga anacita zimenezo kufika pati?

6 Pamsonkhano wa bungwe lolamulila la Akristu a m’nthawi ya atumwi umene unacitika mu 49 C.E., wophunzila Yakobo anati:  “Sumeoni [Petulo] wafotokoza bwino mmene Mulungu anaceukila anthu a mitundu ina kwa nthawi yoyamba, kuti mwa io atengemo anthu odziŵika ndi dzina lake.” (Mac. 15:14) Mtundu watsopano umenewu wochedwa ndi dzina la Yehova, unapangidwa ndi Ayuda ndiponso anthu akunja okhulupilila. (Aroma 11:25, 26a) Pambuyo pake, Petulo analemba kuti: “Kale simunali mtundu, koma tsopano ndinu mtundu wa anthu a Mulungu.” (1 Pet. 2:10) Pofotokoza colinga ca mtundu watsopano umenewu, Petulo anati: “Inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe acifumu, mtundu woyela mtima, anthu a mwini wake, kotelo kuti mukalalikile zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, muloŵe kuunika kwake kodabwitsa.” (1 Pet. 2:9, 10) Conco, colinga ca mtunduwo cinali kukhala mboni za Yehova zolimba mtima, mwa kulengeza poyela kuti iye ndi Mfumu ya Cilengedwe Conse.

7 Monga mmene zinalili ndi Isiraeli wakuthupi, Isiraeli wa kuuzimu ndi anthu amene Yehova anakamba kuti “anthu amene ndinawapanga kuti akhale anga, anene za ulemelelo wanga.” (Yes. 43:21) Molimba mtima Akritsu oyambilila anali kulengeza kuti Yehova ndi Mulungu yekha woona, ndi kuti milungu yonse ndi yonama. (1 Ates. 1:9) Iwo anacitila umboni za Yehova ndi Yesu “mu Yerusalemu, ku Yudeya konse ndi ku Samariya, mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.”—Mac. 1:8; Akol. 1:23.

8. Mtumwi Paulo anapeleka cenjezo liti kwa anthu a Mulungu m’nthawi ya atumwi?

8 Mtumwi Paulo anali mmodzi wa anthu olimba mtima ndiponso ‘odziŵika ndi dzina [la Yehova]’ m’nthawi ya atumwi. Paulo ataimilila pamaso pa anthu amene anali kuphunzitsa nzelu za anthu, iye molimba mtima anaikila kumbuyo ulamulilo wa Yehova, ‘Mulungu amene anapanga dzikoli ndi zinthu zonse zili mmenemo, amene ndi Ambuye wakumwamba ndi dziko.’ (Mac.17:18, 23-25) Ndipo kumapeto kwa ulendo wake wacitatu wa umishonale, Paulo anacenjeza anthu ochedwa ndi dzina la Mulungu kuti: “Ndikudziŵa kuti ine ndikacoka, mimbulu yopondeleza idzafika pakati panu ndipo sidzasamalila gulu la nkhosa mwacikondi. Ndipo pakati panu anthu ena adzayamba kulankhula zinthu zopotoka kuti apatutse ophunzila aziwatsatila.” (Mac. 20:29, 30) Mpatuko wonenedwelatu umenewu unaonekela kwambili pamene atumwi onse anamwalila.—1 Yoh. 2:18, 19.

9. N’ciani cinacitika kwa anthu a Mulungu atumwi atamwalila?

9 Pambuyo pakuti atumwi onse amwalila, mpatuko umenewo unafalikila, ndipo unayambitsa Machalichi Acikristu. M’malo mokhala “anthu odziŵika ndi dzina [la Yehova],” Akristu ampatuko amenewa acotsa dzina la Mulungu m’ma Baibulo ao ambili. Iwo atengela miyambo yacikunja. Ndipo salemekeza Mulungu mwa kuphunzitsa nzelu za anthu, kumenya nkhondo zimene amati ndi ‘zopatulika,’ ndi kucita ciwelewele. Conco, kwa zaka zambili, Yehova anali cabe ndi alambili okhulupilika ocepa padziko lapansi, koma analibe gulu la “anthu odziŵika ndi dzina lake.”

KUBADWANSO KWA ANTHU A MULUNGU

10, 11. (a) M’fanizo lake la tiligu ndi namsongole, Yesu anakambilatu za ciani? (b) Kodi fanizo la Yesu linakwanilitsidwa motani pambuyo pa 1914? Nanga panakhala zotsatilapo zotani?

10 M’fanizo lake lonena za tiligu ndi namsongole, Yesu anakambilatu za mdima wa kuuzimu umene unali kudzacititsidwa ndi ampatuko. Iye anakamba kuti pamene ‘anthu anali m’tulo,’ Mdyelekezi anafesa namsongole m’munda umene Mwana wa munthu anafesamo tiligu. Zonse zinali kudzakulila pamodzi kufikila “mapeto a nthawi ino.” Yesu anafotokoza kuti “mbeu  yabwino” imaimila “ana a Ufumu.” Ndipo “namsongole” amaimila “ana a woipayo.” Panthawi ya mapeto, Mwana wa munthu adzatumiza “okololawo,” amene ndi angelo, kudzalekanitsa tiligu wophiphilitsa ndi namsongole. Ndiyeno, ana a Ufumu adzasonkhanitsidwa pamodzi. (Mat. 13:24-30, 36-43) Kodi ulosi umenewu unakwanilitsidwa motani? Nanga unathandiza bwanji kuti Yehova akhalenso ndi gulu la alambili ake padziko lapansi?

11 “Mapeto a nthawi ino” anayamba mu 1914. Panthawi ya nkhondo m’caka cimeneco, Akristu odzozedwa masauzande ocepa, amene ndi “ana a Ufumu,” anali mu ukapolo wa kuuzimu wa Babulo Wamkulu. Koma mu 1919, Yehova anawamasula ndipo anaonetsa bwino kwambili kusiyana pakati pa io ndi “namsongole,” kapena kuti Akristu onyenga. Iye anasonkhanitsa “ana a Ufumu” kukhala gulu la anthu, pokwanilitsa ulosi wa Yesaya wakuti: “Kodi dziko limatulutsidwa ndi zoŵaŵa za pobeleka tsiku limodzi lokha? Kapena kodi mtundu umabadwa nthawi imodzi? Pakuti Ziyoni wamva zoŵaŵa za pobeleka ndipo wabeleka ana ake aamuna.” (Yes. 66:8) Ziyoni, amene ndi gulu la Yehova la zolengedwa zauzimu, anabala ana auzimu ndi kuwapanga kukhala mtundu.

12. Kodi odzozedwa aonetsa bwanji kuti ndi “anthu odziŵika ndi dzina [la Yehova]” masiku ano?

12 Mofanana ndi Akristu oyambilila, odzozedwa amene ndi “ana a Ufumu,” anali kudzakhala Mboni za Yehova. (Ŵelengani Yesaya 43:1, 10, 11.) Iwo anali kudzakhala osiyana ndi anthu ena cifukwa ca khalidwe lao labwino, ndi nchito yao yolalikila ‘uthenga wabwino wa Ufumu . . . kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.’ (Mat. 24:14; Afil. 2:15) Zimenezi zathandiza anthu ambili kuti akhale olungama pamaso pa Yehova.—Ŵelengani Danieli 12:3.

“TIPITA NANU LIMODZI”

13, 14. Kuti alambile Yehova ndi kum’tumikila movomelezeka, kodi anthu amene si Aisiraeli a kuuzimu afunika kucita ciani? Nanga zimenezi zinanenedwelatu motani m’Baibulo?

13 M’nkhani yapita, tinakambilana kuti  m’nthawi ya Aisiraeli, anthu amitundu ina analoledwa kulambila Yehova. Koma kuti acite zimenezo, io anafunika kugwilizana ndi anthu a Yehova. (1 Maf. 8:41-43) Mofananamo, masiku ano anthu amene si Aisiraeli a kuuzimu afunika kugwilizana ndi anthu a Yehova, amene ndi “ana a Ufumu,” kapena kuti Mboni za Yehova zodzozedwa.

14 Anthu ambili masiku ano akukhamukila kwa Yehova kuti am’lambile pamodzi ndi anthu ake. Izi zinanenedwelatu ndi aneneli aŵili akale. Yesaya analosela kuti: “Anthu ocokela m’mitundu yosiyanasiyana adzabwela n’kunena kuti: ‘Bwelani anthu inu. Tiyeni tipite kukakwela phili la Yehova. Tipite kunyumba ya Mulungu wa Yakobo. Iye akatiphunzitsa njila zake, ndipo ife tidzayenda m’njila zakezo.’ Pakuti mu Ziyoni mudzatuluka malamulo ndipo mau a Yehova adzatuluka mu Yerusalemu.” (Yes. 2:2, 3) Mofananamo, mneneli Zekariya anakambilatu kuti “anthu ambili a mitundu ina ndiponso mitundu yamphamvu ya anthu idzabweladi kudzafunafuna Yehova wa makamu mu Yerusalemu.” Iye anakamba kuti “amuna 10 ocokela m’zilankhulo zonse za anthu a mitundu ina,” amene mophiphilitsa adzagwila covala ca Mwiisiraeli wa kuuzimu, ndi kukamba kuti: “Anthu inu tipita nanu limodzi, cifukwa tamva kuti Mulungu ali ndi inu.”—Zek. 8:20-23.

15. Ndi nchito iti imene a “nkhosa zina” amathandiza Isiraeli wa kuuzimu?

15 A “nkhosa zina” amathandiza Isiraeli wa kuuzimu pa nchito yolalikila uthenga wabwino wa Ufumu. (Maliko 13:10) Iwo akhala mbali ya anthu a Mulungu, ndipo akhala “gulu limodzi” ndi odzozedwa, lotsogoleledwa ndi “m’busa wabwino,” Kristu Yesu.—Ŵelengani Yohane 10:14-16.

PEZANI CITETEZO PAKATI PA ANTHU A YEHOVA

16. Kodi Yehova adzacita ciani cimene cidzatsogolela ku Aramagedo?

16 Pambuyo pakuti Babulo Wamkulu waonongedwa, anthu a Yehova adzaukilidwa. Panthawi imeneyi, tidzafunika kukhala m’malo acitetezo amene Yehova adzapeleka kwa atumiki ake. Panthawi yake yoikika, Yehova adzaloŵelelapo pa zocitika za padziko lapansi, ndipo zimenezi zidzacititsa kuti anthu ake aukilidwe. Ndiyeno, kuukila kumeneku kudzayambitsa Aramagedo, imene ndi mbali yotsiliza ya “cisautso cacikulu.” (Mat. 24:21; Ezek. 38:2-4) Panthawiyo, Gogi adzaukila “anthu amene anasonkhanitsidwa pamodzi kucokela ku mitundu ina,” amene ndi anthu a Yehova. (Ezek. 38:10-12) Zimenezi zikadzacitika, mwamsanga Yehova adzacitapo kanthu mwa kuukila Gogi ndi anthu ake. Motelo, Yehova adzakweza ulamulilo wake ndi kuyeletsa dzina lake, popeza iye anati: ‘Ndidzacititsa kuti mitundu yambili ya anthu indidziŵe, ndipo io adzadziŵa kuti ine ndine Yehova.’—Ezek. 38:18-23.

Panthawi ya “cisautso cacikulu,” tidzafunika kugwilizana kwambili ndi mipingo yathu (Onani ndime 16-18)

17, 18. (a) Kodi anthu a Yehova adzalandila malangizo otani Gogi akadzawaukila? (b) Tifunika kucita ciani kuti tikatetezedwe ndi Yehova?

17 Gogi akadzayamba kuukila kwake, Yehova adzauza atumiki ake kuti: “Inu anthu anga, pitani mukaloŵe m’zipinda zanu zamkati ndipo mukatseke zitseko. Mukabisale kwa kanthawi mpaka mkwiyo utadutsa.” (Yes. 26:20) Panthawi yovuta imeneyo, Yehova adzatipatsa malangizo kuti tikatetezeke. Ndipo mwina ‘zipinda zathu zamkati’ ndi mipingo yathu.

18 Conco, kuti Yehova akatiteteze pa cisautso cacikulu, tifunika kudziŵa kuti iye ali ndi anthu ake padziko lapansi, ndipo anthuwo ali m’mipingo. Motelo, tifunika kupitilizabe kukhala pakati pao ndi kugwilizana kwambili ndi mipingo yathu. Ndipo ndi mtima wathu wonse, tiyeni tinene mofanana ndi wamasalimo kuti: “Cipulumutso cimacokela kwa Yehova. Madalitso anu ali pa anthu anu.”—Sal. 3:8.