Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

Kodi akulu ndi atumiki othandiza amaikidwa bwanji pa udindo mumpingo?

M’nthawi ya atumwi, mtumwi Paulo anauza akulu mumpingo wa ku Efeso kuti: “Mukhale chelu ndi kuyang’anila gulu lonse la nkhosa, limene mzimu woyela wakuikani pakati pao kukhala oyang’anila, kuti muŵete mpingo wa Mulungu, umene anaugula ndi magazi a Mwana wake weniweni.” (Mac. 20:28) Kodi mzimu woyela umathandiza bwanji pa kuikidwa kwa akulu ndi atumiki othandiza masiku ano?

Coyamba, mzimu woyela unatsogolela olemba Baibulo kuti alembe ziyeneletso za akulu ndi atumiki othandiza. Pa lemba la 1 Timoteyo 3:1-7, pali ziyeneletso zosiyanasiyana za akulu zokwanila 16. Ndipo ziyeneletso zina zipezeka pa Tito 1:5-9, ndi pa Yakobo 3:17, 18. Ndiponso, ziyeneletso za atumiki othandiza zipezeka pa 1 Timoteyo 3:8-10, 12, 13. Caciŵili, akulu amene amapenda ziyeneletso ndi kuika abale pa udindo amapempha mzimu wa Yehova kuti uwathandize kudziŵa ngati m’bale akukwanilitsa ziyeneletso za m’Malemba. Cacitatu, m’bale amene akalamila udindo afunika kuonetsa makhalidwe amene mzimu woyela wa Mulungu umatulutsa. (Agal. 5:22, 23) Conco, mzimu wa Mulungu umathandiza panchito yoika abale pa udindo.

Koma ndani kwenikweni amene amaika abale pa udindo? Kale, ziyamikilo zonse zokhudza kuika akulu ndi atumiki othandiza pa udindo zinali kutumizidwa ku ofesi ya nthambi ya m’dzikolo. Ku nthambi kumeneko, abale amene anasankhidwa ndi Bungwe Lolamulila anali kubwelelamo m’ziyamikilo zimenezo ndi kusankha woyenelela. Ndiyeno, ofesi ya nthambi inali kudziŵitsa bungwe la akulu za abale amene anasankhidwa. Ndipo naonso akulu anali kudziŵitsa abale amene ayamikilidwa kumene, ndi kuwafunsa ngati ndi okonzeka ndi oyenelela kulandila udindo umenewo. Pambuyo pake, anali kulengeza mumpingo za kuikidwa kwao.

Nanga kodi abale anali kuikidwa bwanji pa udindo m’nthawi ya atumwi? Nthawi zina, atumwi anali kuika abale mwacindunji. Mwacitsanzo, amuna 7 anawaika kuti aziyang’anila nchito yogaŵila cakudya ca tsiku ndi tsiku kwa akazi amasiye. (Mac. 6:1-6) Komabe, amuna amenewo ayenela kuti anali kale akulu asanapatsidwe udindo woonjezeleka umenewu.

Ngakhale kuti Malemba safotokoza mwatsatanetsatane mmene anali kuikila abale pa udindo, tingathe kuona mmene zimenezi zinali kucitikila.  Timauzidwa kuti pamene Paulo ndi Baranaba anatsiliza ulendo wao woyamba wa umishonale, “anawaikila akulu mumpingo uliwonse, ndipo atapemphela ndi kusala kudya, anawapeleka kwa Yehova yemwe anamukhulupilila.” (Mac 14:23) Patapita zaka, Paulo analembela Tito amene anali kuyenda naye kuti: “Ndinakusiya ku Kerete kuti ukonze zinthu zosalongosoka ndi kuti uike akulu mumzinda uliwonse, malinga ndi malangizo amene ndinakupatsa.” (Tito 1:5) Mofananamo, Timoteyo, amene anali kuyenda ndi mtumwi Paulo pa maulendo aatali, ayenela kuti anapatsidwa udindo umodzimodziwo. (1 Tim. 5:22) Conco, n’zoonekelatu kuti oyang’anila oyendela ndi amene anali kuika abale pa udindo, osati atumwi kapena akulu ku Yerusalemu.

Potengela citsanzo ca m’Baibulo cimeneci, Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova lapanga masinthidwe okhudza kuika akulu ndi atumiki othandiza pa udindo. Kuyambila pa September 1, 2014, kuika abale pa udindo kukucitika motele: Woyang’anila dela aliyense amapenda mosamalitsa ziyamikilo za abale a m’dela lake. Pamene iye acezela mpingo adzayesetsa kuwadziŵa bwino abale amene asankhidwa kuti aikidwe pa udindo, ndi kuseŵenza nao mu ulaliki ngati n’kotheka. Pambuyo pokambilana ziyamikilo za abalewo ndi bungwe la akulu, woyang’anila dela ali ndi udindo woika akulu ndi atumiki othandiza mumpingo. Makonzedwe amenewa ndi ofanana ndi a m’nthawi ya atumwi.

Akulu akambilana ndi woyang’anila dela ziyeneletso za m’Malemba za m’bale (Malawi)

Nanga ndani amene amagwila nchito yaikulu imeneyi? Monga mwa nthawi zonse, “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” ndiye ali ndi udindo waukulu wopeleka cakudya kwa anchito apakhomo. (Mat. 24:45-47) Motsogoleledwa ndi mzimu woyela, amafufuza Malemba kuti apeleke malangizo oyenela a mmene gulu lifunika kuyendela pogwilitsila nchito mfundo za m’Baibulo. Ndiponso, kapolo wokhulupilika amaika oyang’anila dela ndi abale a m’Komiti ya Nthambi. Ndipo ofesi ya nthambi imatithandiza kugwilitsila nchito malangizo ocokela kwa kapolo wokhulupilika. Bungwe la akulu lililonse lili ndi udindo wopenda mosamalitsa ziyeneletso za m’Malemba za abale amene asankhidwa kuti aikidwe pa udindo mumpingo. Nayenso woyang’anila dela ali ndi udindo waukulu wopenda mosamalitsa ndiponso mwapemphelo ziyamikilo zocokela kwa akulu, ndi kuika pa udindo abale amene akwanilitsa ziyeneletso.

Tikadziŵa mmene kuika abale pa udindo kumacitikila, tidzamvetsetsa mmene mzimu woyela umagwilila nchito pankhani imeneyi. Ndipo tidzadalila kwambili ndi kulemekeza abale amene aikidwa pa udindo mumpingo wacikristu.—Aheb. 13:7, 17.

 Kodi mboni ziŵili zochulidwa pa Chivumbulutso caputala 11 ndani?

Lemba la Chivumbulutso 11:3 limanena za mboni ziŵili zimene zinali kudzalosela kwa masiku 1,260. Ndiyeno nkhaniyo imati, cilombo “cidzazigonjetsa ndi kuzipha.” Koma pambuyo pa “masiku atatu ndi hafu,” mboni ziŵili zimenezi zidzaukitsidwa. Ndipo zimenezi zidzadabwitsa anthu onse oona.—Chiv. 11:7, 11.

Kodi mboni ziŵili zimenezi ndani? Nkhani yonse ya m’caputala cimeneci itithandiza kudziŵa mboni zimenezi. Coyamba, tikuuzidwa kuti mboni zimenezi “zikuimilidwa ndi mitengo iŵili ya maolivi, ndi zoikapo nyale ziŵili.” (Chiv. 11:4) Zimenezi zitikumbutsa zoikapo nyale ndi mitengo iŵili ya maolivi, yochulidwa mu ulosi wa Zekariya. Mitengo ya maolivi imeneyo inaimila “odzozedwa aŵili,” Bwanamkubwa Zerubabele ndi Mkulu wa Ansembe Yoswa, amene ‘anaimilila kumbali iyi ndi mbali inayi ya Ambuye wa dziko lonse lapansi.’ (Zek. 4:1-3, 14) Caciŵili, mboni ziŵili zimenezi zikufotokozedwa kuti zikucita zizindikilo zofanana ndi zimene Mose ndi Eliya anacita.—Yelekezelani Chivumbulutso 11:5, 6 ndi Numeri 16:1-7, 28-35 ndiponso 1 Mafumu 17:1; 18:41-45.

Kodi malifalensi aŵili amenewa akugwilizana motani? Kugwilizana kwake ndi kwakuti nkhani iliyonse imachula za odzozedwa a Mulungu, amene anali kutsogolela panthawi zovuta. Conco, pa kukwanilitsidwa kwa Chivumbulutso caputala 11, abale odzozedwa amene anali kutsogolela pamene Ufumu wa Mulungu unakhazikitsidwa kumwamba mu 1914, analalikila kwa zaka zitatu ndi hafu atavala “ziguduli.”

Atatsiliza kulalikila m’ziguduli, odzozedwa amenewa mophiphilitsila anaphedwa mwa kuikidwa m’ndende kwa kanthawi. Kanthawi kameneka kanaimila masiku atatu ndi hafu. Kwa adani a anthu a Mulungu, nchito ya mboni zimenezo inali ngati yaphedwa, ndipo adani ao anakondwela kwambili.—Chiv. 11:8-10.

Komabe, mogwilizana ndi kukwanilitsidwa kwa ulosi umenewu, pamapeto pa masiku atatu ndi hafu, mboni ziŵili zimenezo zinaukitsidwa. Sikuti odzozedwa amenewa anangomasulidwa m’ndende cabe, koma amene anakhalabe okhulupilika analandila udindo wapadela wocokela kwa Mulungu kupyolela mwa Mbuye wao Yesu Kristu. Mu 1919, io pamodzi ndi odzozedwa ena anaikidwa kukhala “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” kuti asamalile zosoŵa za kuuzimu za anthu a Mulungu m’masiku otsiliza.—Mat. 24:45-47; Chiv. 11:11, 12.

N’zokondweletsa kuti zocitika za pa lemba la Chivumbulutso 11:1, 2 zimagwilizana ndi nthawi pamene kacisi wa kuuzimu anali kudzayezedwa, kapena kupimidwa. Mofananamo, Malaki caputala 3 amachula za kuyendela kacisi wa kuuzimu, ndiyeno pambuyo pake kuuyeletsa. (Mal. 3:1-4) Kodi nchito yoyendela ndi yoyeletsa imeneyo inatenga utali wotani? Nchito imeneyi inayamba mu 1914, mpaka kuciyambi kwa 1919. Nthawi imeneyi imaphatikizapo masiku 1,260 (kapena miyezi 42) ndi masiku atatu ndi hafu ophiphilitsa ochulidwa pa Chivumbulutso caputala 11.

Ndithudi, ndife okondwa kuti Yehova anakonza zakuti pakhale nchito yoyenga mwa kuuzimu kuti ayeletse anthu apadela kuti acite nchito zabwino. (Tito 2:14) Ndiponso, timayamikila citsanzo ca Akristu odzozedwa okhulupilika, amene anatsogolela panthawi zovuta, ndi kutumikila monga mboni ziŵili zophiphilitsa. *

^ par. 18 Kuti mudziŵe zambili, onani Nsanja ya Mlonda ya July 1, 2013 masamba 28 ndi 29, ndime 12.