Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

“Kuzindikira Kumachititsa Munthu Kubweza Mkwiyo”

“Kuzindikira Kumachititsa Munthu Kubweza Mkwiyo”

Kochi wa masewera a mpira anachotsedwa ntchito chifukwa chopsa mtima.

Mwana wina anapsa mtima makolo ake atakana kum’patsa zomwe ankafuna ndipo anayamba kulira kwambiri.

Mayi anakangana kwambiri ndi mwana wake wamwamuna chifukwa choti mwanayo ankangosiya zinthu zili mbwe kuchipinda kwake.

AMBIRIFE tinaonapo anthu atapsa mtima ndipo n’zosachita kufunsa kuti nafenso nthawi ina tinapsapo mtima. Anthufe timadziwa kuti si bwino kupsa mtima, koma munthu akatikhumudwitsa, timapsa mtima poganiza kuti tili ndi zifukwa zomveka zochitira zimenezi. Nkhani ya m’magazini ina inati: “Mwachibadwa munthu aliyense amapsa mtima ndipo palibe vuto ndi zimenezi.”—American Psychological Association.

Zimenezi zingaoneke ngati zomveka, makamakanso tikaganizira zimene mtumwi Paulo ananena. Iye ankadziwa kuti nthawi zina munthu akhoza kupsa mtima. Choncho anati: “Kwiyani, koma musachimwe. Dzuwa lisalowe muli chikwiyire.” (Aefeso 4:26) Koma kodi pamenepa Paulo ankatanthauza chiyani? Kodi ankatanthauza kuti tisamaugwire mtima munthu akatilakwira, kapena ankatanthauza kuti tiziyesetsa kuugwira mtima?

KODI KUKWIYA N’KULAKWA?

Pamene Paulo ankapereka malangizo amene taona m’ndime yapitayi, ayenera kuti ankaganizira zimene munthu wina amene analemba nawo Masalimo ananena. Iye anati: “Ngati mwakwiya, musachimwe.” (Salimo 4:4) Kodi Paulo ankatanthauza chiyani pamene ankapereka malangizowa? Ambiri angaganize kuti Paulo ankalimbikitsa kuti anthu azipsa mtima kapena kukwiya. Komatu izi si zoona chifukwa Paulo anapitiriza kunena kuti: “Kuwawidwa mtima konse kwa njiru, kupsa mtima, mkwiyo, kulalata ndiponso mawu achipongwe zichotsedwe mwa inu limodzi ndi zoipa zonse.” (Aefeso 4:31) Apa Paulo ankalimbikitsa Akhristu anzake kuti munthu wina akawakhumudwitsa, aziyesetsa kuugwira mtima. Nkhani ya m’magazini ija inanenanso kuti: “Kafukufuku amasonyeza kuti kusaugwira mtima kumapangitsa kuti munthu akwiye kwambiri ndiponso kuti achite zoipa . . . komanso sikuthetsa vutolo.”

Ndiye kodi ‘tingachotse’ bwanji kupsa mtima kuti tipewe mavuto amene amabwera chifukwa cha kupsa mtimako? Solomo, yemwe anali mfumu yanzeru analemba kuti: “Kuzindikira kumachititsa munthu kubweza mkwiyo wake, ndipo kunyalanyaza cholakwa kumam’chititsa kukhala wokongola.” (Miyambo 19:11) Kodi “kuzindikira” kungathandize bwanji munthu akakhumudwa ndi zinazake?

KODI KUZINDIKIRA KUMATHANDIZA BWANJI MUNTHU KUBWEZA MKWIYO?

Kuzindikira ndi luso lotha kudziwa zambiri pa nkhani inayake. Munthu wozindikira samangoona zinthu pamwambamwamba koma amaganizira zinthu zosiyanasiyana zokhudza nkhaniyo. Kodi kuzindikira kungatithandize bwanji, munthu wina akatilakwira kapena kutikhumudwitsa?

Nthawi zambiri munthu akatichitira zinthu zopanda chilungamo, timakhumudwa. Komabe, ndi bwino kuugwira mtima chifukwa kupsa mtima kungapangitse kuti tichite zinthu zomwe zingabweretse mavuto kwa ifeyo komanso anthu ena. Monga mmene moto ungawonongere nyumba, kupsa mtima kungawononge mbiri yathu, ubwenzi wathu ndi anthu ena komanso ndi Mulungu. Choncho zina zikatikhumudwitsa, ndi bwino kuganizira zinthu zosiyanasiyana zokhudza nkhaniyo. Kuchita zimenezi kungatithandize kuti tithe kuugwira mtima.

Davide, yemwe anali bambo ake a Solomo, pa nthawi ina anangotsala pang’ono kupha anthu chifukwa cha zimene munthu wina dzina lake Nabala anachita. Koma mwamwayi Abigayeli, mkazi wa Nabala, anamuthandiza kuti aonenso nkhaniyo bwinobwino, ndipo izi zinachititsa kuti augwire mtima. Zomwe zinachitika n’zoti, pa nthawi ina Davide ndi atumiki ake anateteza nkhosa za Nabala m’chipululu cha Yudeya. Ndiyeno itafika nthawi yometa ubweya wa nkhosa, Davide anatumiza anyamata ake kuti akapemphe chakudya kwa Nabala. Koma Nabala anayankha kuti: “Ine nditenge mkate wanga, madzi ndi nyama imene ndaphera anyamata anga ometa ubweya wa nkhosa n’kupereka kwa amuna amene sindikudziwa m’pang’ono pomwe kumene achokera?” Umenewutu unali mwano waukulu. Davide atamva zimenezi, anatenga atumiki ake 400 n’kuyamba ulendo wopita kukapha Nabala ndi onse a m’banja lake.—1 Samueli 25:4-13.

Abigayeli atamva izi anapita kukakumana ndi Davide. Atafika, anagwada pamaso pa Davide ndi anyamata ake, ndipo anati: “Chonde, lolani kapolo wanu wamkazi alankhule nanu ndipo mvetserani mawu a kapolo wanu.” Kenako anauza Davide kuti Nabala ndi munthu wopanda nzeru. Anamuuzanso kuti si bwino kuti abwezere chipongwe cha Nabala komanso kupha anthu, chifukwa adzanong’oneza nazo bondo.—1 Samueli 25:24-31.

Kodi zimene Abigayeli ananenazi zinathandiza bwanji Davide? Choyamba zinamuthandiza kuzindikira kuti mwachibadwa, Nabala anali munthu wopanda nzeru. Anazindikiranso kuti akabwezera, akhala ndi mlandu wa magazi. Mofanana ndi Davide, nanunso mungakwiye ndi zimene munthu wina wachita. Kodi zikatere mungatani? Nkhani ina yomwe inalembedwa ndi ogwira ntchito pachipatala china chotchedwa Mayo, inati: “Muzisiya kaye kuganiza za nkhaniyo n’kupuma mokoka mpweya, kenako n’kuwerenga ka 10.” Apa mfundo ndi yakuti, muyenera kuganizira zimene zachititsa vutolo komanso zimene zingachitike mukabwezera. Kuganizira mofatsa za nkhaniyo kungathandize kuti mtima wanu utsike mwinanso kuti mkwiyo wanu uthe.—1 Samueli 25:32-35.

Mofanana ndi Davide, anthu ambiri masiku ano aphunzira kuugwira mtima. Mwachitsanzo, mnyamata wina wazaka 23, dzina lake Sebastian, yemwe pa nthawi ina anali m’ndende ya ku Poland, anayamba kuugwira mtima chifukwa chophunzira Baibulo. Iye anati: “Choyamba ndimaganizira zomwe zachititsa vutolo. Kenako ndimayesetsa kugwiritsa ntchito malangizo a m’Baibulo. Ndimaona kuti malangizo a m’Baibulo ndi othandiza kwambiri.”

Kutsatira malangizo a m’Baibulo kungakuthandizeni kuti muziugwira mtima

Nayenso Setsuo amachita chimodzimodzi. Iye anati: “Poyamba munthu akandikhumudwitsa kuntchito, ndinkamukalipira. Koma panopa chifukwa choti ndaphunzira Baibulo, munthu akandikhumudwitsa ndimadzifunsa kuti: ‘Kodi pamenepa wolakwa ndani? Kodi n’kutheka kuti ineyo ndi amene ndachititsa vutoli?’” Kuganizira mafunso amenewa kunkamuthandiza kuugwira mtima.

Malangizo a m’Baibulo angathandize munthu amene wakhumudwitsidwa kuti asakwiye kwambiri. Kutsatira malangizowa komanso kupempha Mulungu kuti akuthandizeni kungachititse kuti mukhale ozindikira. Ndipo kuzindikira kungakuthandizeni kuti muziugwira mtima.