Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

‘Mverani Ndipo Mumvetse Tanthauzo Lake’

‘Mverani Ndipo Mumvetse Tanthauzo Lake’

“Mverani kuno nonsenu, ndipo mumvetse tanthauzo lake.”—MALIKO 7:14.

1, 2. N’chifukwa chiyani anthu ena sankamvetsa tanthauzo la mawu a Yesu?

MUNTHU akhoza kumva wina akulankhula komanso mmene akulankhulira koma osadziwa tanthauzo la zimene akunena. Zikatero ndiye kuti mawuwo sangamuthandize. (1 Akor. 14:9) N’chimodzimodzi ndi zimene Yesu ankaphunzitsa. Anthu ambirimbiri ankamva mawu ake m’chilankhulo chawo koma si onse amene ankamvetsa tanthauzo lake. N’chifukwa chake Yesu anauza anthu amene ankamumvetsera kuti: “Mverani kuno nonsenu, ndipo mumvetse tanthauzo lake.”—Maliko 7:14.

2 N’chifukwa chiyani ambiri sanamvetse tanthauzo la mawu a Yesu? Vuto la ena linali loti anali ndi maganizo awoawo komanso zolinga zolakwika. Ponena za anthu amenewa, Yesu anati: “Mochenjera, mumakankhira pambali malamulo a Mulungu kuti musunge mwambo wanu.” (Maliko 7:9) Anthuwa sankayesetsa kuti amvetse tanthauzo la mawu a Yesu. Iwo sankafuna kusintha maganizo ndiponso zochita zawo. Ankamva Yesu akulankhula koma sankalola kuti ziwafike pamtima. (Werengani Mateyu 13:13-15.) Kodi ifeyo tingatani kuti mawu a Yesu azitifika pamtima n’kutithandiza?

KODI TINGATANI KUTI MAWU A YESU ATITHANDIZE?

3. N’chifukwa chiyani ophunzira a Yesu ankamvetsa tanthauzo la mawu ake?

3 Tiyenera kutsatira chitsanzo cha ophunzira a Yesu amene anali odzichepetsa. Iye anawauza kuti: “Ndinu odala chifukwa maso anu amaona, komanso makutu anu amamva.” (Mat. 13:16) N’chifukwa chiyani ophunzirawo ankamvetsa mawu a Yesu pomwe ena sankawamvetsa? Choyamba, iwo ankafunsa mafunso ndiponso kuyesetsa kumvetsa tanthauzo la mawu ake. (Mat. 13:36; Maliko 7:17) Chachiwiri, iwo ankayesetsa kuona kugwirizana pakati pa zimene akuphunzira ndi zimene ankadziwa kale. (Werengani Mateyu 13:11, 12.) Chachitatu, ankayesetsa kugwiritsa ntchito zimene ankaphunzira pa moyo wawo komanso kuti athandize anthu ena.—Mat. 13:51, 52.

4. Kodi tiyenera kuchita zinthu zitatu ziti kuti timvetse bwino mafanizo a Yesu?

4 Ngati tikufuna kumvetsa mafanizo a Yesu, tiyenera kutsatira chitsanzo cha ophunzira ake okhulupirika. Ifenso tiyenera kuchita zinthu zitatu. Choyamba, tiyenera kuphunzira ndiponso kufufuza mwakhama zimene Yesu ananena. Pochita zimenezi, tiyenera kudzifunsa mafunso oyenera. Tikatero tidzadziwa tanthauzo la mawuwo. (Miy. 2:4, 5) Chachiwiri, tiyenera kuona kugwirizana pakati pa zimene taphunzirazo ndi zimene timadziwa kale komanso kuona mmene zingatithandizire. Tikachita zimenezi ndiye kuti tidzamvetsa tanthauzo la mawuwo. (Miy. 2:2, 3) Chachitatu, tiyenera kugwiritsa ntchito zimene taphunzirazo. Zimenezi zidzasonyeza kuti ndife anzeru.Miy. 2:6, 7.

5. Perekani chitsanzo chosonyeza kusiyana pakati pa kudziwa zinthu, kumvetsa zinthu komanso nzeru.

5 Kodi kudziwa zinthu, kumvetsa zinthu komanso nzeru zimasiyana bwanji? Kuti tiyankhe funsoli, tiyerekezere kuti mwaima pamsewu ndipo galimoto ikubwera mofulumira. Choyamba, mumadziwa kuti kukubwera galimoto. Kenako mumazindikira kuti mukaimabe pamsewupo ndiye kuti mugundidwa. Apa tingati mwamvetsa tanthauzo la zimene zikuchitika. Ndiyeno mukathawa pamsewupo m’pamene mudzasonyeza kuti ndinu anzeru. M’pake kuti Baibulo limanena kuti tiyenera ‘kusunga nzeru zopindulitsa.’ Nzeru zimenezi zingatithandize kukhala ndi moyo.—Miy. 3:21, 22; 1 Tim. 4:16.

6. Kodi tizikambirana mafunso ati pa mafanizo 7 a Yesu? (Onani  bokosi patsamba 8.)

6 M’nkhaniyi ndiponso yotsatira tikambirana mafanizo 7 a Yesu. Tikamakambirana mafanizowa tizipeza mayankho a mafunso awa: Kodi fanizoli limatanthauza chiyani? N’chifukwa chiyani Yesu analinena? Kodi tingagwiritse ntchito bwanji mfundozi pa moyo wathu komanso pothandiza anthu ena? Funso loyamba litithandiza kudziwa bwino fanizolo, lachiwiri litithandiza kumvetsa mfundo zake ndipo lachitatu litithandiza kuchita zinthu mwanzeru. Ndiyeno, funso lomaliza ndi lakuti: Kodi fanizoli likutiphunzitsa chiyani za Yehova ndi Yesu?

FANIZO LA KANJERE KA MPIRU

7. Kodi fanizo la kanjere ka mpiru limatanthauza chiyani?

7 Werengani Mateyu 13:31, 32. Kodi fanizoli limatanthauza chiyani? Kanjere ka mpiru kamaimira uthenga wa Ufumu komanso mpingo wachikhristu, umene unayamba chifukwa cha ntchito yolalikira uthengawu. Kanjere ka mpiru kamakhala “kakang’ono kwambiri.” Mpingo wachikhristu unalinso waung’ono kwambiri pamene unkayamba mu 33 C.E. Koma patapita zaka, unakula kwambiri kuposa mmene anthu ankaganizira. (Akol. 1:23) Kukula kumeneku kunali kothandiza kwambiri chifukwa chakuti Yesu ananena kuti “mbalame zam’mlengalenga zimabwera kudzapeza malo okhala munthambi zake.” Mbalamezi zikuimira anthu ofuna kuphunzira Baibulo amene tingati amapeza chakudya chauzimu, mthunzi komanso malo okhala mumpingo wachikhristu.—Yerekezerani ndi Ezekieli 17:23.

8. N’chifukwa chiyani Yesu ananena fanizo la kanjere ka mpiru?

8 N’chifukwa chiyani Yesu ananena fanizoli? Iye analigwiritsa ntchito pofuna kusonyeza kuti Ufumu wa Mulungu uli ndi mphamvu yogonjetsa chilichonse, yoteteza anthu a Yehova komanso yothandiza kuti gulu lake likule kwambiri. Kuyambira mu 1914, mbali yapadziko lapansi ya gulu la Mulungu yakhala ikukula kwambiri. (Yes. 60:22) Anthu amene ali m’gululi akhala akutetezedwanso kuti ubwenzi wawo ndi Yehova usasokonezeke. (Miy. 2:7; Yes. 32:1, 2) Palibenso chilichonse chimene chaimitsa ntchito ya gulu la Yehova.—Yes. 54:17.

9. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizo la kanjere ka mpiru? (b) Kodi zimenezi zikutiphunzitsa chiyani za Yehova ndi Yesu?

9 Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizo la kanjere ka mpiru? Mwina panopa kudera limene mukukhala kulibe a Mboni ambiri kapena anthu safuna kuphunzira Baibulo. Koma kukumbukira kuti Ufumu wa Mulungu uli ndi mphamvu yogonjetsa vuto lililonse kungakuthandizeni kuti musagwe mphwayi. Mwachitsanzo, m’bale wina dzina lake Edwin Skinner anapita ku India mu 1926. Atafika, anapeza kuti kuli Mboni zochepa kwambiri ndipo ntchito yolalikira sinkayenda bwino kwenikweni. Koma iye ankalalikirabe ndipo anaona uthenga wa Ufumu ukufalikira ngakhale kuti kunali zinthu zambiri zimene zikanalepheretsa ntchitoyi. Panopa, ku India kuli Mboni zoposa 37,000 ndipo anthu oposa 108,000 anafika pa Chikumbutso mu 2013. Zimene zachitikanso ku Zambia zikusonyeza kuti ntchito ya Ufumu yakhala ikuyenda bwino kwambiri. Tikutero chifukwa chakuti pamene M’bale Skinner ankapita ku India, ntchitoyi inali itangoyamba kumene ku Zambia. Koma panopa kuli ofalitsa oposa 170,000 ndipo anthu 763,915 anafika pa Chikumbutso mu 2013. Izi zikusonyeza kuti munthu mmodzi pa anthu 18 alionse ku Zambia anafika pa mwambowu.

FANIZO LA ZOFUFUMITSA

10. Kodi fanizo la zofufumitsa limatanthauza chiyani?

10 Werengani Mateyu 13:33. Kodi fanizoli limatanthauza chiyani? Fanizoli limaimiranso uthenga wa Ufumu komanso zimene zimachitika chifukwa cha ntchito yolalikira uthengawu. ‘Mtanda wonse’ wotchulidwa pa lembali umaimira mitundu yonse ya anthu ndipo kufalikira kwa zofufumitsa kumaimira kufalikira kwa uthenga wa Ufumu chifukwa cha ntchito yolalikira. Kukula kwa kanjere ka mpiru kumaonekera bwinobwino pomwe kufalikira kwa zofufumitsa sikumaonekera poyamba. Koma pakapita nthawi, anthu amaona kuti mtanda wonse wafufuma.

11. N’chifukwa chiyani Yesu ananena fanizo la zofufumitsa?

11 N’chifukwa chiyani Yesu ananena fanizoli? Iye ankasonyeza kuti uthenga wa Ufumu umafalikira kwambiri komanso umasintha zinthu. Mwachitsanzo, panopa uthenga wa Ufumu wafika “mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Ngakhale kuti poyamba sitingaone zinthu zonse zimene zikusintha chifukwa cha uthengawu, pakapita nthawi zimaonekera. Chiwerengero chimawonjezeka komanso anthu amasintha makhalidwe awo chifukwa chomva uthengawu.—Aroma 12:2; Aef. 4:22, 23.

12, 13. Perekani zitsanzo zosonyeza kuti uthenga wa Ufumu wafalikira kwambiri mogwirizana ndi fanizo la zofufumitsa.

12 Nthawi zambiri zinthu zimene zikusintha chifukwa cha ntchito yolalikira zimaonekera pakapita zaka zambiri. Mwachitsanzo, Franz ndi mkazi wake Margit amene panopa akutumikira kunthambi ina, mu 1982 ankatumikira kunthambi ya ku Brazil. Ndiyeno anakalalikira m’tauni yaing’ono m’dziko lomweli. Iwo anayambitsa phunziro ndi mayi wina ndi ana ake 4. Pa nthawiyo, mnyamata wamkulu anali wazaka 12 ndipo anali wamanyazi kwambiri moti ankabisala pa nthawi ya phunzirolo. Banjali silinapitirize kuphunzira nawo chifukwa chopemphedwa kukatumikira kwina. Koma patapita zaka 25, anapitanso kutauniyi. Anapeza kuti kunali mpingo wa ofalitsa 69 ndipo 13 anali apainiya. Iwo ankasonkhana m’Nyumba ya Ufumu yatsopano. Anapezanso kuti mnyamata wamanyaziyo ndi amene anali wogwirizanitsa ntchito za akulu. Mofanana ndi zofufumitsa m’fanizo la Yesu, uthenga wa Ufumu unafalikira komanso kusintha moyo wa anthu ambiri. Banjalo linasangalala kwambiri kuona zimenezi.

13 Umboni wakuti uthenga wa Ufumu uli ndi mphamvu yosintha anthu m’njira yosaonekera tingaupeze m’mayiko amene ntchito yolalikira ndi yoletsedwa. Nthawi zambiri sitidziwa mmene uthenga ukufalikira m’mayiko amenewa koma timangodabwa ndi zotsatira zake. Chitsanzo pa nkhaniyi ndi dziko la Cuba. Uthenga wa Ufumu unafika m’dzikoli mu 1910 ndipo M’bale Russell anapitako mu 1913. Komabe ntchito yolalikira sinkayenda bwino poyamba. Koma panopa kuli ofalitsa oposa 96,000 ndipo anthu 229,726 anafika pa Chikumbutso mu 2013. Apa tingati munthu mmodzi pa anthu 48 alionse m’dzikoli anafika pa mwambowu. N’kutheka kuti m’mayiko amene ntchito yathu si yoletsedwa, uthenga wa Ufumu wafikanso m’madera amene abale ndi alongo amaganiza kuti sungafikeko bwinobwino. *Mlal. 8:7; 11:5.

14, 15. (a) Kodi zimene taphunzira pa fanizo la Yesu la zofufumitsa zingatithandize bwanji? (b) Kodi mfundo za mu fanizoli zikutiphunzitsa chiyani za Yehova ndi Yesu?

14 Kodi tikuphunzira chiyani pa fanizo la Yesu la zofufumitsa? Kuganizira tanthauzo la fanizoli kungatithandize kuti tisamadere nkhawa za anthu ambirimbiri amene panopa sanamve uthenga wa Ufumu. Tizikumbukira kuti Yehova ndi amene akutsogolera zinthu. Ndiyeno kodi choyenera kuchita n’chiyani? Mawu a Mulungu amati: “Bzala mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo, chifukwa sukudziwa pamene padzachite bwino, kaya pano kapena apo, kapena ngati zonsezo zidzachite bwino.” (Mlal. 11:6) Komabe sitiyenera kusiya kupempha Yehova kuti ntchito yolalikira iziyenda bwino, makamaka m’mayiko amene ntchitoyi ndi yoletsedwa.—Aef. 6:18-20.

15 Sitiyeneranso kukhumudwa ngati poyamba sitikuona zotsatira za ntchito yathu. Tisanyoze “zinthu zochepa” zimene zikuchitika chifukwa tikhoza kudzadabwa ndi zotsatira zake.—Zek. 4:10; Sal. 40:5; Zek. 4:7.

FANIZO LA WAMALONDA WOYENDAYENDA NDIPONSO LA CHUMA CHOBISIKA

16. Kodi fanizo la wamalonda woyendayenda ndiponso la chuma chobisika limatanthauza chiyani?

16 Werengani Mateyu 13:44-46. Kodi mafanizowa amatanthauza chiyani? M’nthawi ya Yesu, anthu ena amalonda ankayenda mpaka kukafika kunyanja yakutali kwambiri (Indian Ocean) kukafufuza ngale zabwino. Mu fanizo la Yesu limeneli, wamalonda woyendayenda akuimira anthu amene amachita khama kwambiri pofufuza mwayi woti adziwe bwino uthenga wa m’Baibulo. “Ngale imodzi yamtengo wapatali” ikuimira uthenga wa Ufumu. Wamalonda woyendayenda uja atazindikira kuti ngale imene wapeza ndi yamtengo wapatali anapita “mwamsanga” kukagulitsa zinthu zake zonse kuti agule ngaleyo. Yesu ananenanso za munthu amene anapeza “chuma chobisika” m’munda. Mosiyana ndi wamalonda uja, munthuyu sankafufuza chumacho koma anangochipeza. Koma mofanana ndi wamalonda uja, nayenso anakagulitsa ‘zinthu zake zonse’ kuti apeze chumacho.

17. N’chifukwa chiyani Yesu anapereka fanizo la wamalonda woyendayenda ndi la chuma chobisika?

17 N’chifukwa chiyani Yesu ananena mafanizo awiriwa? Iye ankafuna kusonyeza zinthu zosiyanasiyana zimene zimachitika kuti anthu amve uthenga wabwino. Ena amafufuza mwakhama kuti apeze uthengawu. Pomwe ena safufuza koma amangoupeza, mwina pamene anthu awafikira n’kuwalalikira. Koma anthu onsewa amazindikira kufunika kwake ndipo amalolera kusiya zinthu zambiri n’cholinga choti adziwe bwino uthengawo.

18. (a) Kodi tikuphunzira chiyani pa mafanizo awiri a Yesuwa? (b) Kodi mafanizowa akutiphunzitsa chiyani za Yehova ndi Yesu?

18 Kodi tikuphunzira chiyani pa mafanizo awiriwa? (Mat 6:19-21) Tiyenera kudzifunsa kuti: ‘Kodi ineyo ndimaona kuti uthenga wabwino ndi wamtengo wapatali ngati mmene anthu a m’mafanizowa anachitira? Kodi ndimalolera kusiya zinthu zambiri n’cholinga choti ndiudziwe bwino n’kumautsatira? Kapena kodi ndimalola zinthu zina pa moyo wanga kundisokoneza?’ (Mat. 6:22-24, 33; Luka 5:27, 28; Afil. 3:8) Tikamayamikira kwambiri mwayi wodziwa uthenga wa m’Baibulo tidzayesetsa kuika uthengawo pa malo oyamba.

19. Kodi tidzakambirana chiyani m’nkhani yotsatira?

19 Tiyeni tizisonyeza kuti tamva mafanizo okhudza Ufumu amenewa komanso kumvetsa bwino tanthauzo lake. Koma tisaiwale kuti kungomvetsa tanthauzo lake si kokwanira. Tiyeneranso kutsatira zimene taphunzira m’mafanizowo. M’nkhani yotsatira tidzakambirana mafanizo ena atatu n’kuonanso zimene tikuphunzirapo.

^ ndime 13 Nkhani zoterezi zachitikanso m’mayiko monga ku Argentina (onani Buku Lapachaka lachingelezi la 2001, tsamba 186); ku East Germany (onani Buku Lapachaka lachingelezi la 1999, tsamba 83); ku Papua New Guinea (onani Buku Lapachaka lachingelezi la 2005, tsamba 63) ndiponso kuchilumba cha Robinson Crusoe (onani Nsanja ya Olonda ya June 15, 2000, tsamba 9).