Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

‘Mvelani ndi Kumvetsa Tanthauzo Lake’

‘Mvelani ndi Kumvetsa Tanthauzo Lake’

“Mvelani kuno nonsenu, ndipo mumvetse tanthauzo lake.”—MALIKO 7:14.

1, 2. N’cifukwa ciani anthu ambili amene anamva Yesu akulankhula analephela kumvetsetsa tanthauzo la zimene iye anali kukamba?

MUNTHU akamva zimene winawake akulankhula, angazindikile kuti munthuyo wakondwela kapena ai malinga ndi mmene mauwo akumvekela. Koma zimakhala zovuta kudziŵa tanthauzo la zimene munthu akulankhula ngati zimene akunena sitikuzimvetsetsa. (1 Akor. 14:9) Mofananamo, anthu ambili anamva zimene Yesu anali kunena. Iye anali kugwilitsila nchito mau osavuta kumva. Ngakhale ndi telo, ndi anthu ocepa cabe amene anali kumvetsetsa tanthauzo la mau a Yesu. Pa cifukwa cimeneci, Yesu anauza anthu amene anali kulankhula nao kuti: “Mvelani kuno nonsenu, ndipo mumvetse tanthauzo lake.”—Maliko 7:14.

2 N’cifukwa ciani anthu ambili analephela kumvetsetsa tanthauzo la mau a Yesu? Anthu ena anali ndi maganizo olakwika ndiponso zolinga zolakwika. Ponena za anthuwo, Yesu anati: “Mocenjela, mumakankhila pambali malamulo a Mulungu kuti musunge mwambo wanu.” (Maliko 7:9) Anthuwo sanali kucita khama kuti adziŵe tanthauzo la mau a Yesu. Iwo sanafune kusintha zocita zao ndi maganizo ao. Ngakhale kuti anali kumva, mitima yao inali youma kwambili. (Ŵelengani Mateyu 13:13-15.) Nanga n’ciani cimene ife tiyenela kucita kuti tisaumitse mitima yathu n’colinga cakuti tipindule ndi zimene Yesu anali kuphunzitsa?

 ZIMENE TINGACITE KUTI TIPINDULE NDI ZIPHUNZITSO ZA YESU

3. N’cifukwa ciani ophunzila anali kutha kumvetsetsa zimene Yesu anali kukamba?

3 Tiyenela kutengela citsanzo ca ophunzila a Yesu odzicepetsa. Ponena za io, Yesu anati: “Ndinu odala cifukwa maso anu amaona, komanso makutu anu amamva.” (Mat. 13:16) N’cifukwa ciani ophunzila a Yesu anali kumvetsetsa zimene iye anali kuphunzitsa pamene ena anali kulephela? Coyamba, io anali kufunsa ngati sanamvetsetse, ndipo anali kucita khama kuti azindikile tanthauzo la zimene Yesu anali kukamba. (Mat. 13:36; Maliko 7:17) Caciŵili, io anali okonzeka kuphunzila zambili kuonjezela pa zimene anali kudziŵa kale. (Ŵelengani Mateyu 13:11, 12.) Cacitatu, anali ofunitsitsa kugwilitsila nchito paumoyo wao zimene anaphunzila ndiponso kuzigwilitsila nchito pothandiza anthu ena.—Mat. 13:51, 52.

4. Ndi zinthu zitatu ziti zimene tiyenela kucita kuti tizimvetsetsa mafanizo a Yesu?

4 Tiyenela kutengela citsanzo ca ophunzila a Yesu okhulupilika kuti tizimvetsetsa tanthauzo la mafanizo ake. Kuti zimenezi zitheke, pali zinthu zitatu zimene tiyenela kucita. Coyamba, tiyenela kukhala ofunitsitsa kupatula nthawi yophunzila ndi kusinkhasinkha zimene Yesu anakamba, kufufuza ndi kufunsa mafunso oyenelela. Tikatelo tidzakhala ndi cidziŵitso. (Miy. 2:4, 5) Caciŵili, tiyenela kugwilizanitsa zimene taphunzila ndi zimene tikudziŵa kale ndi kuona mmene zingatipindulitsile. Zimenezo zidzatithandiza kumvetsa zinthu. (Miy. 2:2, 3) Comaliza, zimene taphunzila tiyenela kuzigwilitsila nchito paumoyo wathu. Tikatelo tidzasonyeza kuti tili ndi nzelu.Miy. 2:6, 7.

5. Pelekani citsanzo cosonyeza kusiyana pakati pa cidziŵitso, kumvetsa zinthu, ndi nzelu.

5 Kodi pali kusiyana kotani pakati pa cidziŵitso, kumvetsa zinthu, ndi nzelu? Kuti timvetsetse kusiyana kwake, tiyeni tiyelekezele motele: Tinene kuti mwaima pakati pa mseu, ndipo kutsogolo kukubwela basi. Coyamba, mwazindikila kuti galimoto imene ikubwelayo ndi basi. Cimeneco ndi cidziŵitso. Kenako, mukuzindikila kuti ngati simucoka pakati pamseupo, mugundidwa ndi basiyo. Kumeneko ndi kumvetsa zinthu. Pamapeto pake, mukuthawa pakati pamseupo mwamsanga. Kutelo ndiko nzelu. M’pomveka kuti Baibulo limatilimbikitsa ‘kusunga nzelu zopindulitsa,’ cifukwa zimatanthauza moyo kwa ife.—Miy. 3:21, 22; 1 Tim. 4:16.

6. Ndi mafunso anai ati amene tidzakambilana pamene tikupenda mafanizo 7 a Yesu? ( Onani kabokosi.)

6 M’nkhani ino ndi yotsatila, tidzakambilana mafanizo 7 a Yesu. Pamene tikukambilana fanizo lililonse, tiyenela kupeza mayankho a mafunso awa: Kodi fanizo limeneli limatanthauza ciani? (Kuyankha funso limeneli kutithandiza kukhala ndi cidziŵitso.) N’cifukwa ciani Yesu anagwilitsila nchito fanizo limeneli? (Kudziŵa cifukwa cake kutithandiza kukhala omvetsa zinthu.) Kodi mfundo zimenezi tingazigwilitsile nchito bwanji paumoyo wathu ndiponso pothandiza ena? (Kucita zimenezo ndi nzelu.) Yomaliza ndi yakuti, kodi zimenezi zikutiphunzitsa ciani ponena za Yehova ndi Yesu?

FANIZO LA KANJELE KA MPILU

7. Kodi fanizo la kanjele ka mpilu limatanthauza ciani?

7 Ŵelengani Mateyu 13:31, 32. Kodi fanizo la Yesu la kanjele ka mpilu limatanthauza ciani? Kanjele ka mpilu kamaimila uthenga wa Ufumu ndiponso mpingo wacikristu umene ulipo cifukwa colalikila uthenga umenewu. Mofanana ndi kanjele ka mpilu kamene “ndi kakang’ono kwambili mwa njele zonse,” mpingo wacikristu unali waung’ono kwambili pamene unayamba mu 33 C.E. Koma pambuyo pa zaka zocepa, mpingowo unakula mofulumila ndiponso modabwitsa kwambili. (Akol. 1:23) Kukula kumeneku kunali kopindulitsa cifukwa cakuti Yesu anakamba kuti ‘mbalame zam’mlengalenga zinabwela  kudzapeza malo okhala munthambi zake.’ Mbalame zophiphilitsila zimenezi zimaimila anthu a mitima yabwino amene amapeza cakudya cakuuzimu, mthunzi, ndi malo okhala mkati mwa mpingo wacikristu.—Yelekezelani Ezekieli 17:23.

8. N’cifukwa ciani Yesu anagwilitsila nchito fanizo la kanjele ka mpilu?

8 N’cifukwa ciani Yesu anagwilitsila nchito fanizo limeneli? Iye anakamba za kukula kodabwitsa kwa kanjele ka mpilu poonetsa mphamvu imene Ufumu wa Mulungu uli nayo yokulitsa, kuteteza ndi kugonjetsa mavuto onse. Kuyambila mu 1914, mbali ya padziko lapansi ya gulu la Mulungu yakhala ikukula modabwitsa. (Isa. 60:22) Anthu amene amagwilizana ndi gulu limeneli ndi otetezeka mwakuuzimu. (Miy. 2:7; Yes. 32:1, 2) Kuonjezela pamenepo, zinthu za Ufumu zikupitabe patsogolo ngakhale kuti anthu ena akhala akutsutsa komanso kuzunza atumiki a Mulungu.—Yes. 54:17.

9. (a) Ndi phunzilo lotani limene tikuphunzilapo pa fanizo la kanjele ka mpilu? (b) Kodi fanizoli likutiphunzitsa ciani ponena za Yehova ndi Yesu?

9 N’ciani cimene tikuphunzilapo pa fanizo la kanjele ka mpilu? Mwina kumene timakhala kulibe Mboni zambili kapena ndi anthu ocepa cabe amene amalabadila uthenga wathu. Koma kukumbukila kuti Ufumu wa Mulungu ungathe kugonjetsa zopinga zonse, kungatithandize kupilila. Mwacitsanzo, pamene M’bale Edwin Skinner anafika ku India mu 1926, m’dzikolo munali Mboni zocepa kwambili. Poyamba nchito yolalikila inali kuoneka kukhala “yovuta kwambili” cifukwa cakuti sinali kupita patsogolo. Koma m’baleyo anapitilizabe kulalikila ndipo anaona mmene uthenga wa Ufumu unagonjetsela zopinga zazikulu. Pali pano, ku India kuli Mboni za Yehova zacangu zoposa 37,000, ndipo anthu oposa 108,000 anapezeka pa Cikumbutso caka catha. Komanso onani citsanzo cina cosonyeza mmene nchito ya Ufumu yapitila patsogolo mocititsa cidwi. Caka cimodzimodzi cimene m’bale Skinner anafika ku India, ndi pamene nchito yolalikila inali itangoyamba muno mu Zambia. Panopa mu Zambia muli ofalitsa oposa 170,000, ndipo anthu oposa 763,915 anapezeka pa Cikumbutso mu 2013. Ciŵelengelo cimeneci cikuonetsa kuti pa anthu 18 alionse mu Zambia, munthu mmodzi anapezeka pa Cikumbutso. Zimenezi zikusonyeza kupita patsogolo kocititsa cidwi.

 FANIZO LA ZOFUFUMITSA

10. Kodi fanizo la zofufumitsa limatanthauza ciani?

10 Ŵelengani Mateyo 13:33. Kodi fanizo la zofufumitsa limatanthauza ciani? Fanizo limeneli limatanthauzanso uthenga wa Ufumu ndi zotsatilapo za nchitoyo. “Mtanda wonsewo” wa ufa umaimila mitundu yonse, ndipo kufufuma kumaimila kufalikila kwa uthenga wa Ufumu kudzela m’nchito yolalikila. Mosiyana ndi kanjele ka mpilu kamene kukula kwake kumaonekela mosavuta, kufalikila kwa zofufumitsa sikuonekela nthawi yomweyo. Kukula kwake kumayamba kuonekela pakapita nthawi.

11. N’cifukwa ciani Yesu anagwilitsila nchito fanizo limeneli?

11 N’cifukwa ciani Yesu anagwilitsila nchito fanizo limeneli? Mwa kugwilitsila nchito fanizoli, iye anali kuonetsa kuti uthenga wa Ufumu uli ndi mphamvu yofalikila paliponse ndi kusintha anthu. Uthenga wa Ufumu wafalikila “mpaka kumalekezelo a dziko lapansi.” (Mac. 1:8) Koma kusintha kumene kumacitika cifukwa ca uthengawu nthawi zina sikumaonekela, ndipo zotsatila zina za nchito yolalikila sizionekela nthawi yomweyo. Koma kusintha kumakhalapo, ndipo kumaonekela osati cabe mwa ziŵelengelo, koma mwa kuona mmene anthu amene alandila uthenga wa Ufumu amasinthila umunthu wao.—Aroma 12:2; Aef. 4:22, 23.

12, 13. Mogwilizana ndi fanizo la zofufumitsa, pelekani zitsanzo zoonetsa mmene nchito yolalikila Ufumu yapitila patsogolo.

12 Zotsatilapo za nchito yolalikila kaŵilikaŵili zimaonekela pambuyo pa zaka zambili nchitoyo itagwilidwa. Mwacitsanzo, Franz ndi Margit, amene akutumikila ku nthambi ina, anatumikilako ku nthambi ya ku Brazil mu 1982. Panthawi imeneyo io analalikilapo ku dela lina la ku midzi. Pakati pa anthu amene anayamba kuphunzila nao Baibulo panthawiyo, panali mayi wina ndi ana ake anai. Mwana wina wa mayiyu anali mnyamata wa zaka 12, ndipo anali wamanyazi kwambili cakuti anali kukonda kubisala phunzilo lisanayambe. Franz ndi Margit anasamukila ku dela lina cifukwa ca utumiki ndipo sanapitilize kuphunzila ndi banja lija. Koma pambuyo pa zaka 25, io anapita kukaceza kudela limenelo. N’ciani cimene anapeza atafika kumeneko? Anapeza kuti ku delalo kuli mpingo wokhala ndi ofalitsa 69, apainiya a nthawi zonse 13, ndipo onse anali kusonkhanila m’Nyumba ya Ufumu yatsopano. Nanga bwanji za mnyamata wamanyazi uja? Anapeza kuti ndi amene tsopano akutumikila monga mgwilizanitsi wa bungwe la akulu. Mofanana ndi zofufumitsa za m’fanizo la Yesu, uthenga wa Ufumu unakula ndi kusintha miyoyo ya anthu ambili, ndipo Franz ndi Margit akusangalala kwambili.

13 Mphamvu yosaoneka yosintha anthu imene uthenga wa Ufumu uli nayo, imaonekela bwino m’maiko amene nchito ya Ufumu ndi yoletsedwa mwalamulo. Zimakhala zovuta kudziŵa kuti uthenga wa Ufumu wafika pati m’maiko amenewo, koma tingadabwe tikaona zotsatilapo zake. Mwacitsanzo, uthenga wa Ufumu unafika m’dziko ka Cuba mu 1910, ndipo M’bale Russell anapita kukaceza m’dzikolo mu 1913. Poyamba nchito yolalikila siinali kupita patsogolo m’dzikolo. Nanga zinthu zili bwanji masiku ano ku Cuba? Kuli ofalitsa 96,000 amene akulalikila uthenga wabwino, ndipo anthu 229,726 anapezeka pa Cikumbutso mu 2013. Ciŵelengelo cimeneci cikusonyeza kuti munthu mmodzi pa anthu 48 alionse ku Cuba anapezeka pa Cikumbutso. Ngakhale m’maiko amene mulibe ziletso, uthenga wa Ufumu umafika ku madela akutali kumene Mboni zakumaloko zimaona kuti n’zosatheka kufikako. *Mlal. 8:7; 11:5.

14, 15. (a) Tingapindule bwanji ndi fanizo la Yesu la zofufumitsa? (b) Kodi fanizoli likutiphunzitsa ciani ponena za Yehova ndi Yesu?

14 Tingapindule bwanji ndi zimene Yesu  anatiphunzitsa m’fanizo la zofufumitsa? Tikamasinkhasinkha za tanthauzo la fanizo la Yesu limeneli, timazindikila kuti sitiyenela kudela nkhawa kwambili kuti uthenga wa Ufumu udzafikila bwanji mamiliyoni a anthu amene sanalandilebe uthengawo. Yehova adzasamalila zimenezo. Koma kodi nchito yathu ndi yotani? Mau a Mulungu amayankha kuti: “Bzala mbewu zako m’mawa, ndipo dzanja lako lisapume mpaka madzulo, cifukwa sukudziŵa pamene padzacite bwino, kaya pano kapena apo, kapena ngati zonsezo zidzacite bwino.” (Mlal. 11:6) Koma panthawi imodzimodzi, sitiyenela kuiwala kupemphela kuti nchito yolalikila ipitebe patsogolo, makamaka m’maiko amene nchitoyo ndi yoletsedwa.—Aef. 6:18-20.

15 Kuonjezela pamenepo, tisataye mtima ngati taona kuti nchito yathu siikubeleka zipatso mwamsanga. Ndiponso sitiyenela kupeputsa nchito yathu ‘cifukwa cakuti tinayamba kumanga ndi zinthu zocepa.’ (Zek. 4:10) M’kupita kwa nthawi, tikhoza kukhala ndi zosatilapo zabwino kwambili kuposa mmene tinali kuganizila poyamba.—Sal. 40:5; Zek. 4:7.

FANIZO LA WAMALONDA WOYENDAYENDA NDI LA CUMA COBISIKA

16. Kodi mafanizo amene Yesu anakamba onena za wamalonda woyendayenda ndi cuma cobisika amatanthauza ciani?

16 Ŵelengani Mateyu 13:44-46. Yesu anakamba fanizo la wamalonda woyendayenda ndi la cuma cobisika. Kodi mafanizo amenewa amatanthauza ciani? M’nthawi za Yesu, amalonda ena anali kuyenda mpaka kufika ku nyanja ya Indian n’colinga cokapeza ngale zamtengo wapatali. Wamalonda mu fanizo ili amaimila anthu oona mtima amene amacita khama kuti apeze zosoŵa zao za kuuzimu. “Ngale imodzi yamtengo wapatali” imaimila coonadi ca Ufumu camtengo wapatali. Atazindikila kuti ngaleyo ndi yamtengo wapatali, wamalonda uja “mwamsanga” anali wofunitsitsa kugulitsa zinthu zonse zimene anali nazo kuti akagule ngaleyo. Yesu anafotokozanso za munthu wina amene anapeza cuma “cobisika” pogwila nchito m’munda. Mosiyana ndi wamalonda uja, munthu ameneyu sanali kufunafuna cuma. Koma mofanana ndi wamalonda uja, iyenso anali wofunitsitsa kugulitsa “zinthu zonse” ndi kugula mundawo.

17. N’cifukwa ciani Yesu anagwilitsila nchito fanizo la wamalonda woyendayenda ndi la cuma cobisika?

17 N’cifukwa ciani Yesu anagwilitsila nchito mafanizo aŵiliwa? Iye anali kusonyeza kuti coonadi tingacipeze m’njila zosiyanasiyana. Anthu ena akufunafuna coonadi, ndipo akucita ciliconse cimene angathe kuti acipeze. Ena sanacite kufunafuna coonadi, io anacipeza mwina cifukwa cakuti munthu wina anawalalikila. Ngakhale kuti anthu a m’fanizoli anapeza cumaco m’njila zosiyanasiyana, onse aŵili anazindikila kuti zimene anapezazo zinali zamtengo wapatali, ndipo onse anali ofunitsitsa kudzimana zinthu zina kuti apeze cumaco.

18. (a) Tingapindule bwanji ndi mafanizo aŵiliwa? (b) Kodi mafanizowa akutiphunzitsa ciani ponena za Yehova ndi Yesu?

18 Tingapindule bwanji ndi mafanizo aŵiliwa? (Mat. 6:19-21) Dzifunseni kuti: ‘Kodi ndili ndi mzimu wofanana ndi amuna amenewo? Kodi ndimaona coonadi kukhala camtengo wapatali mofanana ndi io? Kodi ndine wofunitsitsa kudzimana zinthu zina kuti ndipeze coonadi, kapena ndimalola zinthu zina monga nchito yanga kundilepheletsa kupeza coonadi?’ (Mat. 6:22-24, 33; Luka 5:27, 28; Afil. 3:8) Kukhala ndi cimwemwe cacikulu tikapeza coonadi kudzatithandiza kudzimana zinthu zina ndi kukhala wotsimikiza mtima kuika coonadi patsogolo pa umoyo wathu.

19. Tidzakambilana ciani m’nkhani yotsatila?

19 Tiyenela kuonetsa mwa zocita zathu kuti tamvela ndi kumvetsetsa tanthauzo la mafanizo a Ufumu amenewa. Musaiŵale kuti sitiyenela kudziŵa tanthauzo la mafanizo amenewa cabe, koma tiyenelanso kugwilitsila nchito zimene taphunzila m’mafanizo amenewa. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana mafanizo ena atatu ndi kuona zimene tikuphunzilapo.

^ par. 13 Zocitika zofanana ndi zimenezi zinacitikanso ku Argentina (Yearbook ya 2001, tsamba 186); East Germany (Yearbook ya 1999, tsamba 83); Papua New Guinea (Yearbook ya 2005, tsamba 63); ndi Robinson Crusoe Island (Nsanja ya Olonda ya June 15, 2000, tsamba 9).