Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Mafunso Ochokera kwa Owerenga

Kodi Yeremiya ankatanthauza chiyani ponena kuti Rakele akulirira ana ake?

Lemba la Yeremiya 31:15 limati: “Yehova wanena kuti, ‘Mawu amveka ku Rama. Kwamveka kulira mofuula ndiponso momvetsa chisoni. Rakele akulirira ana ake. Iye wakana kutonthozedwa pamene akulirira ana ake, chifukwa ana akewo kulibenso.’”

Rakele anamwalira ana ake adakali moyo. Choncho zimene Yeremiya analemba zaka 1,000 Rakele atamwalira, zingaoneke kuti si zoona.

Mwana woyamba wa Rakele anali Yosefe. (Gen. 30:22-24) Kenako anabereka Benjamini ndipo Rakele anamwalira atangobereka mwana wachiwiriyu. Choncho funso ndi lakuti: N’chifukwa chiyani lemba la Yeremiya 31:15 limanena kuti Rakele ankalirira ana ake chifukwa “kulibenso”?

Patapita nthawi, Yosefe anabereka Manase ndi Efuraimu. (Gen. 41:50-52; 48:13-20) Fuko la Efuraimu linadzakhala lalikulu kwambiri mu ufumu wakumpoto wa Isiraeli ndipo linkaimira mafuko onse 10. Koma fuko la Benjamini linadzakhala mu ufumu wakum’mwera limodzi ndi fuko la Yuda. Choncho tinganene kuti Rakele ankaimira amayi onse a mu ufumu wa Isiraeli, wakumpoto komanso wakum’mwera.

Pamene buku la Yeremiya linkalembedwa, Asuri anali atagonjetsa ufumu wakumpoto wa Isiraeli ndipo anthu ake anali atatengedwa ku ukapolo. Koma mwina anthu ena a fuko la Efuraimu anathawira ku Yuda. Mu 607 B.C.E., Ababulo anagonjetsa ufumu wakum’mwera wa Yuda. Zikuoneka kuti anthu ambiri amene anagwidwa anapita nawo kumzinda wa Rama m’dera la Benjamini, womwe unali pamtunda wa makilomita 8 kumpoto kwa Yerusalemu. (Yer. 40:1) N’kutheka kuti anthu ambiri anaphedwa m’dera limeneli ndipo n’kumenenso Rakele anaikidwa. (1 Sam. 10:2) Choncho mawu akuti Rakele akulirira ana ake angaimire kulirira anthu onse a ku Benjamini kapena anthu amene anaphedwa ku Rama. N’kuthekanso kuti mawuwo akusonyeza kuti amayi onse a mu Isiraeli ankalirira Aisiraeli amene anaphedwa kapena kutengedwa ku ukapolo.

Koma zimene tikudziwa n’zakuti mawuwo anasonyeza zimene zinadzachitika patapita zaka zambirimbiri pamene Mfumu Herode inkafuna kupha Yesu. Herode analamula kuti ana onse aamuna amene anali asanakwanitse zaka ziwiri ku Betelehemu aphedwe. Ana onsewa anaphedwa ndipo ‘kunalibenso.’ Tangoganizirani mmene amayi a anawo analirira mumzinda wa Betelehemu womwe unali kum’mwera kwa Yerusalemu. Zinali ngati kulira kwa amayiwo kunamvekanso mumzinda wa Rama umene unali kumpoto kwa Yerusalemu.—Mat. 2:16-18.

Choncho mawu akuti Rakele akulirira ana ake akufotokoza bwino zimene zinachitika pa nthawi ya Yeremiya komanso ya Yesu pamene amayi achiyuda ankalirira ana awo amene anaphedwa. Koma anthu onse amene anaphedwa, kapena kuti anapita “kudziko la mdani,” akhoza kudzaukitsidwa m’tsogolo.—Yer. 31:16; 1 Akor. 15:26.