Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi

Mafunso Ocokela Kwa Aŵelengi

Kodi Yeremiya anali kutanthauza ciani pamene ananena kuti Rakele anali kulilila ana ake?

Pa Yeremiya 31:15 pamati: “Yehova wanena kuti, ‘Mau amveka ku Rama. Kwamveka kulila mofuula ndiponso momvetsa cisoni. Rakele akulilila ana ake. Iye wakana kutonthozedwa pamene akulilila ana ake, cifukwa ana akewo kulibenso.’”

Rakele anamwalila ana ake aŵili asanamwalile. Conco, zimene Yeremiya analemba zaka 1,000 Rakele atafa kale zingamveke ngati si zolondola.

Mwana woyamba wa Rakele anali Yosefe. (Gen. 30:22-24) Pambuyo pake, Rakele anabeleka mwana wina wamwamuna, ndipo anamucha Benjamini. Koma Rakele anamwalila pamene anali kubeleka mwana waciŵiliyo. Motelo pakubuka funso lakuti: N’cifukwa ciani lemba la Yeremiya 31:15 limanena kuti iye anali kulila cifukwa ana ake “kulibenso”?

N’zocititsa cidwi kuti m’kupita kwa nthawi, mwana woyamba wa Rakele, Yosefe, anakhala ndi ana aŵili aamuna Manase ndi Efuraimu. (Gen. 41:50-52; 48:13-20) M’kupita kwa zaka, fuko la Efuraimu linakhala lochuka ndi lamphamvu kwambili mu ufumu wakumpoto wa Isiraeli, ndipo linayamba kuimila mafuko onse 10 a ufumuwo. Ku mbali ina, fuko la Benjamini, limene linali mbadwa za mwana waciŵili wa Rakele, linakhala mbali ya ufumu wa kumwela, pamodzi ndi fuko la Yuda. Conco, tinganene kuti Rakele anali monga cizindikilo ca amai onse a mtundu wa Isiraeli, a mu ufumu wa kumpoto ndi mu ufumu wa kumwela.

Panthawi imene buku la Yeremiya linali kulembedwa, ufumu wakumpoto wa mafuko 10 unali utagonja kale kwa Asuri, ndipo anthu ambili a mu ufumuwo anali atatengedwela ku ukapolo. Komabe, n’kutheka kuti ena mwa mbadwa za Efuraimu anathaŵila m’dela la Yuda. Mu 607 B.C.E., Ababulo anagonjetsa ufumu wakumwela wa Yuda umene unali ndi mafuko aŵili. Zikuoneka kuti panthawi imene Ababulo anali kuukila Yuda, akapolo ambili anawasonkhanitsa ku Rama. Dela limeneli linali pamtunda wa makilomita 8 kumpoto kwa Yerusalemu. (Yer. 40:1) Mwina ena mwa akapolowo anaphedwa kumeneko m’dela la Benjamini, kumenenso Rakele anaikidwa m’manda. (1 Sam. 10:2) Motelo n’kutheka kuti mau akuti Rakele analilila ana ake amatanthauza kulila kwake kophiphilitsa cifukwa ca kuphedwa kwa anthu a fuko la Benjamini kapena anthu a ku Rama. N’kuthekanso kuti mauwa amasonyeza kuti amai onse a anthu a Mulungu analila cifukwa ca kuphedwa kwa Aisiraeli kapena cifukwa ca amene anatengedwa ku ukapolo.

Mulimonse mmene zilili, mau a Yeremiya onena za kulila kwa Rakele, ndi ulosi wokamba za nthawi pamene anthu anacita ciwembu kuti aphe Yesu pamene anali mwana. Zimenezi zinacitika zaka zambili Yeremiya atanena mau amenewa. Mfumu Herodi inalamula kuti ana onse aamuna a ku Betelehemu a zaka ziŵili kapena kucepelapo aphedwe. Mzinda wa Betelehemu unali kumwela kwa Yerusalemu. Motelo anawo kunalibenso cifukwa cakuti anaphedwa. Amai a ku Betelehemu analila kwambili cifukwa ca kuphedwa kwa ana ao. Zinali ngati kuti kulila kwao kunamveka ku Rama, dela limene linali kumpoto kwa Yerusalemu.—Mat. 2:16-18.

Conco, m’nthawi ya Yeremiya ndiponso m’nthawi ya Yesu, mau akuti Rakele analilila ana ake anali oyenelela ponena za cisoni cimene amai aciyuda anamva cifukwa ca kuphedwa kwa ana ao. Komabe, anthu amene anafa ndi kupita ku “kudziko la mdani” wathu imfa adzamasuka ku ukapolo wa mdani ameneyu pamene akufa adzaukitsidwa.—Yer. 31:16; 1 Akor. 15:26.