Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

N’chifukwa chiyani anthu ambiri amakhulupirira kuti pali winawake amene analenga zonse?

Moyo ndi wodabwitsa

Zaka 3,000 zapitazo, wolemba ndakatulo wina anati: “Munandipanga modabwitsa ndipo zimenezi zimandichititsa mantha.” (Salimo 139:14) Anthu ambiri amachita chidwi akaganizira mmene mwana amayambira m’mimba mwa mayi ake. Zimenezi zimawachititsa kuti aziona kuti pali winawake amene analenga zamoyo zonse.—Werengani Salimo 139:13-17; Aheberi 3:4.

Mulungu ndi amene analenga zinthu zamoyo, dziko lapansi komanso zina zonse. (Salimo 36:9) Amalankhula nafe kudzera m’Baibulo ndipo watiuza zokhudza iyeyo.—Werengani Yesaya 45:18.

Kodi anthufe tinachokera ku nyama?

Mmene thupi lathu linapangidwira limafanana kwambiri ndi thupi la nyama. Zimenezi zili choncho chifukwa Mulungu analenga anthufe komanso nyama kuti tizikhala padziko lapansi. Munthu woyambirira sanachokere ku nyama koma Mulungu anachita kumulenga kuchokera ku dothi.—Werengani Genesis 1:24; 2:7.

Koma anthu amasiyana ndi nyama m’njira ziwiri. Yoyamba, anthufe timatha kudziwa, kukonda komanso kulemekeza Mulungu. Yachiwiri, anthufe tinalengedwa kuti tisamafe pomwe nyama sanazilenge kuti zizikhala ndi moyo mpaka kalekale. Koma panopa timafa chifukwa choti tinatengera uchimo kuchokera kwa anthu awiri oyambirira, omwe sanamvere Mulungu.—Werengani Genesis 1:27; 2:15-17.