Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kuyankha Mafunso a m’Baibulo

Kuyankha Mafunso a m’Baibulo

N’ciani cimacititsa anthu ambili kuganizila zakuti kuli Mlengi?

Kodi zamoyo si zodabwitsa?

Zaka 3,000 zapitazo, wolemba ndakatulo wina anati: “Munandipanga modabwitsa ndipo zimenezi zimandicititsa mantha.” (Salimo 139:14) Kodi sizimakucititsani mantha mukaganizila mmene mwana wakhanda amakulila kucokela ku selo limodzi? Anthu ambili amakamba kuti pali Mlengi amene anapanga zamoyo.—Ŵelengani Salimo 139:13-17; Aheberi 3:4.

Amene analenga cilengedwe conse ndi kupanga dziko lapansi ndi amene analenganso zamoyo zonse. (Salimo 36:9) Iye analankhula ndi anthu ndipo anatiuza zinthu zokhudza iye.—Ŵelengani Yesaya 45:18.

Kodi tinacokela ku nyama?

Matupi athu ndi ofanana ndi a nyama m’mbali zambili. Izi zili conco, cifukwa cakuti anthu ndi nyama anapangidwa ndi Mlengi kuti azikhala padziko lapansi. Mulungu sanapange munthu woyamba kucokela ku nyama koma ku fumbi lapansi.—Ŵelengani Genesis 1:24; 2:7.

Anthu amasiyana ndi nyama m’njila ziŵili zazikulu. Yoyamba, anthu amatha kudziŵa zinthu, kuonetsa cikondi ndi kulemekeza Mlengi. Yaciŵili, nyama sizinalengedwe kuti zizikhala kosatha, koma anthu analengedwa kuti azitelo. Anthu onse amafa cifukwa cakuti munthu woyamba anakana kutsogoleledwa ndi Mlengi.—Ŵelengani Genesis 1:27; 2:15-17.