Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mphatso Yosangalatsa ya Anthu a ku Japan

Mphatso Yosangalatsa ya Anthu a ku Japan

PA April 28, 2013, mumzinda wa Nagoya, ku Japan munali msonkhano wapadela. Anthu anasangalala pamene M’bale Anthony Morris wa m’Bungwe Lolamulila analengeza za kutulutsidwa kwa buku lochedwa The Bible—The Gospel According to Matthew (Baibulo—Uthenga Wabwino wa Mateyu) m’Cijapanizi. Anthu oposa 210,000 amene anali pamalopo ndiponso amene anamvetsela kupyolela pa Intaneti, anakondwela kwambili cakuti anaomba m’manja kwa nthawi yaitali.

Buku la masamba 128 la Uthenga Wabwino wa Mateyu n’lapadela, ndipo linasindikizidwa kucoka ku Baibulo la Dziko Latsopano m’Cijapanizi. M’bale Morris anafotokoza kuti bukuli linakonzedwela “anthu a ku Japan.” Kodi buku la m’Baibulo limeneli linalembedwa bwanji? Nanga n’cifukwa ciani linalembedwa? Ndipo anthu anamva bwanji atalilandila?

KODI LINALEMBEDWA BWANJI?

Anthu anacita cidwi ndi mmene buku la Uthenga Wabwino wa Mateyu linalembedwela. Zilembo za Cijapanizi zingalembedwe kucoka pamwamba kupita pansi kapena kucoka kumanzele kupita kulamanja. Mabuku ambili kuphatikizapo zofalitsa zathu zaposacedwapa zakhala zikulembedwa kucoka kumanzele kupita kulamanja. Komabe, m’buku latsopanoli zilembo zake zinalembedwa kucoka pamwamba kupita pansi potengela kalembedwe kofala ka m’manyuzipepala ndi mabuku ena a Cijapanizi. Anthu ambili ku Japan amakonda kalembedwe kameneka cifukwa n’kosavuta kuŵelenga. Kuonjezela pamenepa, mitu ya nkhani sinalembedwe pamwamba pa masamba, koma inalembedwa monga tumitu tung’onotung’ono mkati mwa nkhani kuti anthu asamavutike kupeza mfundo zazikulu poŵelenga.

Mosataya nthawi, abale ndi alongo a ku Japan anayamba kugwilitsila nchito buku la Uthenga Wabwino wa Mateyu limene linalembedwa mosavuta kuŵelenga. Mlongo wina wazaka za m’ma 80 anati: “Ndaŵelengapo buku la Uthenga Wabwino wa Mateyu nthawi zambili, koma kalembedwe aka ndiponso mmene tumitu twa nkhani tunalembedwela zandithandiza kumvetsetsa kwambili ulaliki wa pa phili.” Mlongo wina wacitsikana analemba kuti: “Ndinamaliza kuŵelenga buku lonse la Uthenga Wabwino wa Mateyu panthawi imodzi. Ndinazoloŵela kuŵelenga kucoka kumanzele kupita kulamanja, koma anthu a ku Japan amakonda kuŵelenga malembo amene amayambila pamwamba kupita pansi.”

LINALEMBEDWELA ANTHU A KU JAPAN

N’cifukwa ciani buku la m’Baibulo limeneli n’lothandiza kwa anthu a ku Japan? Ngakhale kuti anthu ambili a ku Japan salidziŵa bwino Baibulo, io ali ndi cidwi cofuna kuliŵelenga. Buku la Uthenga Wabwino wa Mateyu lidzapatsa anthu amene sanaonepo Baibulo mwai wonyamula ndi kuŵelenga mbali ya malemba opatulika imeneyi.

N’cifukwa ciani anasankha kusindikiza buku la Uthenga Wabwino wa Mateyu? Anthu ambili a ku Japan akamva liu lakuti “Baibulo” amaganizila za Yesu Kristu. Motelo, bukuli linasankhidwa cifukwa cakuti limafotokoza za banja limene Yesu anabadwilamo, ulaliki wake  wochuka wa pa phili, komanso ulosi wocititsa cidwi wokhudza masiku otsiliza. Anthu a ku Japan amacita cidwi ndi nkhani zimenezi.

Ofalitsa Ufumu ku Japan anayamba kugaŵila bukuli mokangalika kunyumba ndi nyumba ndi pa maulendo obwelelako. Mlongo wina analemba kuti: “Tsopano ndili ndi mipata yambili yogaŵila Mau a Mulungu kwa anthu a m’gawo lathu. Masana a tsiku la msonkhano wapadela umenewo ndinagaŵila buku la Uthenga Wabwino wa Mateyu limeneli.”

KODI ANTHU AMAMVA BWANJI?

Kodi ofalitsa amagaŵila bwanji bukuli? Anthu ambili a ku Japan anamvapo mau akuti “pacipata copapatiza,” “kuponyela nkhumba ngale,” ndi akuti “musamade nkhawa za tsiku lotsatila.” (Mat. 6:34; 7:6, 13) Iwo amacita cidwi akadziŵa kuti amene analankhula mauwa ndi Yesu Kristu. Akaona mau amenewa mu Uthenga Wabwino wa Mateyu, ambili amakamba kuti: “Ndakhala ndikufunitsitsa kuŵelenga Baibulo ngakhale kamodzi kokha.”

Ofalitsa akapita ku maulendo obwelelako kwa anthu amene anasiila buku la Uthenga Wabwino wa Mateyu, kaŵilikaŵili amapeza kuti eninyumba ayamba kuŵelenga bukulo kapena alimaliza. Mwamuna wina wa zaka za m’ma 60 anauza wofalitsa wina kuti: “Ndaŵelenga bukuli nthawi zambili ndipo landitonthoza. Ndiphunzitseni zoonjezeleka zokhudza Baibulo.”

Buku la Uthenga Wabwino wa Mateyu akuligwilitsilanso nchito pocita ulaliki wapoyela. Pocita ulaliki umenewu, mlongo wina anapatsa adilesi ya imelo yake kwa mtsikana wina amene analandila bukuli. Patapita ola limodzi, mtsikanayo anatumiza uthenga kwa mlongoyo pa imelo ndi kumuuza kuti ayamba kuŵelenga bukuli ndipo akufuna kudziŵa zambili. Pambuyo pa mlungu umodzi, mtsikanayo anayamba kuphunzila Baibulo, ndipo mosataya nthawi anayamba kusonkhana.

Makope oposa 1,600,000 a buku lochedwa Uthenga Wabwino wa Mateyu amatumizidwa m’mipingo ya ku Japan, ndipo ofalitsa amagaŵila makope masauzande ambili mwezi uliwonse. Mau oyamba a m’bukuli amafotokoza colinga ca ofalitsa bukuli kuti: “Tikhulupilila kuti kuŵelenga bukuli kudzakuthandizani kukulitsa cidwi cofuna kuphunzila Baibulo.”