Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kukonzekeletsa Anthu ‘Kuphunzila Zokhudza Yehova’

Kukonzekeletsa Anthu ‘Kuphunzila Zokhudza Yehova’

“Bwanamkubwa uja . . . anakhala wokhulupilila, pakuti anadabwa kwambili ndi zimene anaphunzila zokhudza Yehova.”—MAC. 13:12.

1-3. N’cifukwa ciani zinali zovuta kuti ophunzila a Yesu alalikile uthenga wabwino “ku mitundu yonse”?

YESU KRISTU anapatsa otsatila ake nchito yaikulu. Iye anawalamula kuti: “Pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga.” Iwo anafunika kulalikila ‘uthenga wabwino wa ufumu padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse.’—Mat. 24:14; 28:19.

2 Ophunzilawo anali kukonda Yesu ndi uthenga wabwino. Koma popeza anali ocepa kwambili, io ayenela kuti sanali kudziŵa kuti adzakwanitsa bwanji kugwila nchitoyo. Yesu, amene io anali kulengeza kuti ndi Mwana wa Mulungu, anali ataphedwa. Ndipo ophunzila ake anali kuonedwa kuti ndi “osaphunzila ndiponso anthu wamba.” (Mac. 4:13) Atsogoleli a cipembedzo aciyuda anaphunzila miyambo yacipembedzo ku masukulu ophunzitsa zacipembedzo, koma ophunzilawo sanaphunzile zimenezo. Uthenga umene ophunzilawo anali kulalikila sunagwilizane ndi miyambo yaciyuda imene atsogoleli acipembedzo anali kuphunzitsa kwa zaka zambili. Komanso, ophunzilawo anali kuonedwa kukhala osafunika m’dziko lao. Mtundu wa Isiraeli sunali  kanthu poyelekezela ndi Ufumu wa Roma umene unali wochuka.

3 Yesu anali atacenjeza ophunzila ake kuti adzadedwa, adzazunzidwa, ndipo ena adzaphedwa kumene. (Luka 21:16, 17) Anafunika kulimbana ndi anthu osakhulupilika, aneneli onyenga, ndi kuonjezeka kwa kusamvela malamulo. (Mat. 24:10-12) Ngakhale kuti anthu kulikonse anali kudzamvetsela uthenga wao, kodi io akanakwanitsa bwanji kulalikila “mpaka kumalekezelo a dziko lapansi”? (Mac. 1:8) Poganizila mavuto amenewa, ophunzilawo ayenela kuti anakaikila ngati adzakwanitsa nchitoyo.

4. Kodi nchito yolalikila inawayendela bwanji ophunzila a m’nthawi ya atumwi?

4 Ngakhale kuti ophunzilawo anadziŵa kuti kugwila nchitoyo kudzakhala kovuta, io anamvelabe lamulo la Yesu, ndipo analalikila mu Yesusalemu, ku Samariya, ndi kumaiko ena. Mosasamala kanthu za mavuto amene ophunzilawo anakumana nao, uthenga wabwino “unalalikidwa m’cilengedwe conse ca pansi pa thambo,” pa zaka 30 cabe, ndipo ‘unabala zipatso ndi kuwonjezeka m’dziko lonse.’ (Akol. 1:6, 23) Mwacitsanzo, mtumwi Paulo atalalikila pa cilumba ca Kupuro, bwanamkubwa wa Roma dzina lake Serigio Paulo, “anakhala wokhulupilila, pakuti anadabwa kwambili ndi zimene anaphunzila zokhudza Yehova.”—Ŵelengani Machitidwe 13:6-12.

5. (a) N’ciani cimene Yesu analonjeza ophunzila ake? (b) Kodi buku lina linakamba ciani ponena za nthawi ya atumwi?

5 Ophunzila a Yesu anali kudziŵa kuti sakanakwanitsa nchito yolalikila mwa mphamvu zao zokha. Yesu anali atawalonjeza kuti iye adzakhala nao, ndi kuti mzimu woyela udzawathandiza. (Mat. 28:20) Mmenenso zinthu zinalili padziko panthawiyo ziyenela kuti zinapangitsa kuti nchito yolalikila Ufumu iyende bwino. Buku lina lofotokoza za mbili yakale linakamba kuti nthawi ya atumwi iyenela kuti inali nthawi yabwino kwambili ya Akristu kuyamba kulalikila, ndi kuti Akristuwo anaona kuti Mulungu anali atawakonzelatu njila.

6. N’ciani cimene tikambilane (a) m’nkhani ino (b) m’nkhani yotsatila?

6 Kodi Yehova anasintha zocitika za padziko n’colinga cakuti Akristu akwanitse kulalikila m’nthawi ya atumwi? Baibulo silinena ciliconse pankhaniyi. Koma cimene tidziŵa n’cakuti Yehova anafuna kuti anthu ake alalikile uthenga wabwino, ndipo Satana sanakwanitse kuwalepheletsa kucita zimenezo. M’nkhani ino, tikambilana zocitika zina za m’nthawi ya atumwi zimene zinapangitsa ophunzilawo kulalikila popanda zovuta. M’nkhani yotsatila, tidzakambilana zinthu zina zimene zatithandiza kulalikila uthenga wabwino padziko lonse masiku ano.

PAMENE AROMA ANALI PAMTENDELE

7. Kodi Mtendele wa Aroma unali ciani? Nanga unasiyana bwanji ndi nthawi ina iliyonse m’mbili ya anthu?

7 M’nthawi ya atumwi, Ufumu wa Roma unali pamtendele. Zimenezi zinathandiza ophunzilawo kulalikila popanda zovuta. Nthawiyo inali kuchedwa Mtendele wa Aroma. Panthawiyo, boma la Roma linaletselatu kuukila boma kulikonse. N’zoona kuti nthawi zina panali kucitika nkhondo monga mmene Yesu anakambila. (Mat. 24:6) Aroma anaononga Yerusalemu mu 70 C.E., ndipo anamenyanso nkhondo zing’onozing’ono ndi maufumu amene anali oyandikana nao. Ngakhale ndi conco, mbali yaikulu ya ufumuwo munali mtendele, ndipo ophunzilawo anali kuyenda ndi kulalikila popanda zovuta. Nthawi yamtendele imeneyo inali ya zaka pafupifupi 200. Buku lina linakamba kuti  m’mbili ya anthu, palibe nthawi yaitali imene anthu anakhalapo pamtendele kuposa nthawiyo.

8. Kodi Akristu oyambilila anapindula bwanji panthawi ya mtendele?

8 Patapita zaka pafupifupi 300 pambuyo pa Kristu, katswili wina wochedwa Origen analemba za nthawi ya mtendele imeneyi. Iye anakamba kuti Aroma anali kulamulila m’maiko ambili, ndipo pa cifukwa cimeneci kunali kosavuta kuti ophunzilawo alalikile m’maiko onsewo. Anthu sanali kumenya nkhondo kuti ateteze dziko lao, koma anali kukhala m’midzi mwao mwamtendele. Pa cifukwa cimeneci, anthu ambili anali ndi mpata womvetsela zimene ophunzilawo anali kulalikila ponena za cikondi ndi mtendele. Ngakhale kuti ophunzilawo anazunzidwa, io anagwilitsila nchito bwino nthawi ya mtendele mwa kulalikila uthenga wabwino kulikonse.—Ŵelengani Aroma 12:18-21.

MAYENDEDWE ANALI OSAVUTA

9, 10. N’cifukwa ciani zinali zosavuta kuti ophunzila azipanga maulendo mu Ufumu wa Aroma?

9 Akristu anapindula ndi miseu yabwino ya Aroma. Kuti ateteze ndi kupitiliza kulamulila nzika zake, dziko la Roma linali ndi gulu la nkhondo la mphamvu. Miseu yabwino inali yofunika kuti asilikali aziyenda mofulumila, ndipo Aroma anali akatswili popanga miseu imeneyo. Akatswili opanga miseu aciroma anapanga miseu yosiyanasiyana ndipo yonse pamodzi inakwana makilomita 80,000. Miseu imeneyi inali yopita ku madela osiyanasiyana a dzikolo, ndipo inali kudutsa m’nkhalango, m’zipululu, ndi m’mapili.

10 Kuonjezela pa miseu imeneyi, Aroma analinso kugwilitsila nchito zombo zambili. Iwo anali kuyenda pamitsinje ikuluikulu ndiponso panyanja kuti afike ku madoko onse mu ufumuwo. Aroma anali ndi miseu ya pamadzi yoposa 900. Conco, Akristu naonso anali kugwilitsila nchito zombo poyenda m’madela ambili. Iwo sanali kufunika kugwilitsila nchito ziphaso monga mapasipoti, kuti aloŵe m’dziko lina. Pa miseu yao panalibe akuba ambili cifukwa anali kudziŵa kuti Aroma anali kulanga moopsa akuba. Kuyendanso panyanja sikunali koopsa cifukwa asilikali aciroma anali kuteteza nyanjazo kwa anthu acifwamba. Ngakhale kuti combo cinamswekelapo kangapo Paulo, ndipo anakumana ndi zoopsa panyanja, Malemba sakamba mwacindunji kuti pa maulendo akewo anakumanapo ndi acifwamba.—2 Akor. 11:25, 26.

CINENELO CA CIGILIKI

Kunali kosavuta kupeza lemba pogwilitsila nchito codex (Onani ndime 12)

11. N’cifukwa ciani ophunzila anali kugwilitsila nchito Cigiliki?

11 Anthu ambili anali kulankhula Cigiliki, ndipo zimenezi zinathandiza kuti mipingo izicita zinthu mogwilizana. Alexander Wamkulu atagonjetsa madela ambili, Cigiliki cinakhala cinenelo cofala. Pa cifukwa cimeneci, atumiki a Mulungu anali okhoza kulankhula ndi anthu osiyanasiyana, ndipo izi zinathandiza kuti uthenga wabwino ufalikile. Kuonjezela apo, Ayuda amene anali kukhala ku Iguputo anali atamasulila Malemba Aciheberi kupita m’Cigiliki. Anthu anali kulidziŵa Baibulo lacigiriki la Septuagint, ndipo otsatila oyambilila a Kristu anali kuligwila mau mosavuta. Olemba Baibulo anagwilitsilanso nchito Cigiliki polemba malemba ena a m’Baibulo. Cineneloci cinali ndi mau ambili ndi othandiza pofotokoza mfundo za coonadi.

12. (a) Kodi buku lochedwa codex linali ciani? Nanga linali kusiyana bwanji ndi mpukutu? (b) Ndi liti pamene Akristu anayamba kugwilitsila nchito kwambili codex?

12 Kodi Akristu a m’nthawi ya atumwi anali kugwilitsila nchito ciani kuti aphunzitse Malemba mu utumiki? Iwo anali  kugwilitsila nchito mipukutu. Koma mipukutuyo inali yovuta kunyamula. Mkristu akafuna kupeza lemba, anali kufunikila kutambasula mpukutuwo ndiyeno akamaliza kuŵelenga anali kuupindanso. Ndipo kaŵilikaŵili, mau pampukutupo anali kulembedwa mbali imodzi. Mwacitsanzo, Uthenga Wabwino wa Mateyu unali kudzaza mpukutu umodzi. Koma m’zaka za m’ma 100 C.E, io anayamba kugwilitsila nchito mabuku ochedwa codex, cifukwa masamba ake anali kuikidwa pamodzi monga buku. Munthu anali kutsegula bukulo ndi kupeza lemba limene akufuna mosavuta. Olemba mbili yakale amakamba kuti Akristu anayamba kugwilitsila nchito mabuku amenewo mwamsanga, cakuti pambuyo pa zaka za m’ma 100 C.E., Akristu ambili anali kugwilitsila nchito mabuku amenewo.

MMENE LAMULO LA AROMA LINATHANDIZILA

13, 14. (a) Kodi Paulo anagwilitsila nchito motani ufulu wake wokhala nzika ya Roma? (b) Kodi Akristu anapindula bwanji ndi lamulo la Aroma?

13 Lamulo la Aroma linali kugwila nchito mu ufumu wonsewo, ndipo anthu amene anali nzika za Roma anali kupatsidwa ufulu ndiponso kutetezedwa. Paulo anagwilitsila nchito ufulu wake monga nzika ya Roma pa zocitika zingapo. Pamene mtumwiyu anakumana ndi mazunzo ku Yerusalemu, iye anafunsa mkulu wa asilikali wa Aroma kuti: “Kodi anthu inu, malamulo amakulolani kukwapula munthu amene ndi Mroma, mlandu wake usanazengedwe?” Zimene io anacita zinali zosaloleka. Paulo atafotokoza kuti anali nzika ya Roma, ndipo unzika wake unali wocita kubadwa nao, “amuna amene anafuna kumufufuza mwa kumuzunza aja anacoka n’kumusiya yekha. Nayenso mkulu wa asilikali uja anacita mantha atadziŵa kuti [Paulo] ndi Mroma ndiponso kuti anamumanga.”—Mac. 22:25-29.

14 Popeza kuti Paulo anali nzika ya Roma, zimenezi zinakhudza mmene anthu a ku Filipi anayenela kucitila naye. (Mac. 16:35-40) Pamene cigulu ca anthu aukali cinafuna kuvulaza Akristu ena ku Efeso, ndipo woyang’anila mzinda atakhalitsa cete anthuwo, iye anawakumbutsa zimene malamulo a Roma amanena. (Mac. 19:35-41) Pambuyo pake, Paulo ali ku Kaisareya, anapempha kuti agwilitsile nchito ufulu wake mwa kukaonekela kwa mfumu ya Aroma. Atapita kumeneko, anateteza uthenga wabwino. (Mac. 25:8-12) Conco,  lamulo la Aroma linathandiza “pa kuteteza uthenga wabwino ndi kukhazikitsa mwalamulo nchito ya uthenga wabwino.”—Afil. 1:7.

AYUDA OKHALA M’MAIKO ENA

15. Ndi kuti kumene Ayuda ambili anali kukhala m’nthawi ya atumwi?

15 Kugwila nchito yolalikila kunali kosavuta kwa Akristu cifukwa Ayuda anali kukhala m’madela ambili amene anali kulamulidwa ndi Aroma. Zaka zambili m’mbuyomo, Asuri ndiponso pambuyo pake Ababulo anali atatenga Ayuda kupita nao ku ukapolo. Kuyambila zaka za m’ma 400 B.C.E., panali Ayuda amene anali kukhala m’zigawo 127 mu Ufumu wa Perisiya. (Esitere 9:30) Pamene Yesu anali padziko lapansi, Ayuda ena anali kukhala ku Iguputo ndi madela ena a kumpoto kwa Africa, ngakhalenso ku Greece, Asia Minor ndi Mesopotamiya. Zikuoneka kuti pa anthu 60 miliyoni amene anali kukhala mu ufumu wa Aroma, anthu oposa 4 miliyoni anali Ayuda. Ngakhale kuti Ayudawo anali kukhala m’madela osiyanasiyana, io anapitilizabe ndi cipembedzo cao.—Mat. 23:15.

16, 17. (a) Kodi anthu osakhala Ayuda anapindula motani cifukwa ca Ayuda okhala m’madela ena? (b) Ndi citsanzo citi ca Ayuda cimene Akristu amatsatila?

16 Cifukwa cakuti Ayuda anali kukhala m’madela ambili, anthu amene sanali Ayuda anayamba kudziŵa Malemba Aciheberi. Anthuwo anaphunzila kuti pali Mulungu mmodzi woona, ndi kuti amene amam’tumikila ayenela kutsatila mfundo zake za makhalidwe abwino. Ndipo Malemba Aciheberi anali ndi maulosi ambili onena za Mesiya. (Luka 24:44) Motelo, pamene Akristu anali kulalikila uthenga wabwino, Ayuda ndiponso anthu osakhala Ayuda anali kudziŵa kale zinthu zina zimene Akristuwo anali kulalikila. Paulo anali kufuna kupeza anthu omwe akanamvetsela uthenga wabwino. Iye nthawi zonse anali kupita m’masunagoge, kumene Ayuda anali kulambilila Mulungu, ndipo anali kukambilana nao za m’Malemba.—Ŵelengani Machitidwe 17:1, 2.

17 Nthawi zonse Ayuda anali kukumana m’masunagoge kapena pabwalo kuti alambile Mulungu. Iwo anali kuimba nyimbo, kupemphela, ndi kukambilana Malemba. Akristu a m’nthawi ya atumwi anali kutsatila citsanzo cimeneco, ndipo ifenso timatsatila citsanzo cimeneco.

YEHOVA ANAWATHANDIZA KULALIKILA

18, 19. (a) Kodi zocitika za m’nthawi ya atumwi zinatheketsa ciani? (b) Kodi mfundo zimene takambilana zakucitsani kumva bwanji ponena za Yehova?

18 Conco, zocitika zapadela zimene takambilanazi zinathandiza kuti nchito yolalikila uthenga wabwino iyende bwino. Mtendele wa Aroma, mayendedwe osavuta, cinenelo cofala, lamulo la Aroma, ndiponso Ayuda okhala m’maiko ena, zinathandiza ophunzila a Yesu kupitiliza kugwila nchito yolalikila imene Mulungu anawapatsa.

19 Zaka za m’ma 400, katswili wina wacigiliki dzina lake Plato, m’buku lake lina anati: “N’zovuta kwambili kudziŵa amene anapanga ndiponso tate wa cilengedwe cathu. Ngakhale titam’dziŵa, zingakhale zosatheka kuuzako aliyense za iye.” Komabe, Yesu anati: “Zinthu zosatheka ndi anthu n’zotheka ndi Mulungu.” (Luka 18:27) Mlengi wa cilengedwe conse akufuna kuti anthu am’peze ndi kumudziŵa. Kuonjezela pamenepo, Yesu anauza otsatila ake kuti: “Mukaphunzitse anthu a mitundu yonse.” (Mat. 28:19) N’zotheka kukwanilitsa nchito imeneyi ndi thandizo la Yehova Mulungu. Nkhani yotsatila idzafotokoza mmene nchitoyi ikucitikila masiku ano.