Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Yehova Akutsogolera Ntchito Yolalikira Padziko Lonse

Yehova Akutsogolera Ntchito Yolalikira Padziko Lonse

“Ine Yehova ndine Mulungu wanu, amene ndimakuphunzitsani kuti zinthu zikuyendereni bwino, amene ndimakuchititsani kuti muyende m’njira imene muyenera kuyendamo.”YES. 48:17.

1. Kodi Akhristu anakumana ndi mavuto ati m’zaka za m’ma 1800 ndi 1900?

M’ZAKA za m’ma 1800 ndi 1900, Ophunzira Baibulo * ankakumana ndi mavuto osiyanasiyana. Mofanana ndi nthawi ya atumwi, anthu ambiri sankasangalala ndi uthenga wawo. Akhristuwo anali ochepa ndipo anthu ambiri ankawaona kuti ndi osaphunzira. Nayenso Satana Mdyerekezi anadzakhala ndi “mkwiyo waukulu” n’kuyamba kulimbana nawo. (Chiv. 12:12) Iwo anayeneranso kugwira ntchitoyi ‘m’masiku otsiriza’ omwe ndi ovuta kwambiri.2 Tim. 3:1.

2. Kodi Yehova watithandiza bwanji kuti tigwire bwino ntchito yolalikira?

2 Cholinga cha Yehova ndi chakuti uthenga wabwino ulalikidwe padziko lonse ndipo palibe chimene chingamulepheretse. Kale, Yehova anapulumutsa Aisiraeli ku Babulo. Masiku anonso, iye wapulumutsa atumiki ake mu “Babulo Wamkulu” amene akuimira zipembedzo zonyenga zonse. (Chiv. 18:1-4) Yehova akutiphunzitsa kuti zinthu zitiyendere bwino, watithandiza kukhala mwamtendere komanso kuti tiziphunzitsa anthu ena. (Werengani Yesaya 48:16-18.) Koma izi sizikutanthauza kuti Yehova amaoneratu chilichonse n’kukonza zinthu zonse padzikoli kuti ntchito yolalikira iziyenda bwino. N’zoona kuti pali zinthu zina m’dzikoli zimene zathandiza pa ntchito yathuyi. Koma popeza dzikoli lili m’manja mwa Satana, timazunzidwa komanso kukumana ndi mavuto ena. Choncho pakanapanda thandizo la Yehova, sitikanakwanitsa kugwirabe ntchito yathuyi.Yes. 41:13; 1 Yoh. 5:19.

3. N’chiyani chikusonyeza kuti anthu ‘adziwa zinthu zambiri zoona’?

3 Yehova anauza Danieli kulemba kuti nthawi ya mapeto, anthu “adzadziwa zinthu zambiri zoona.” (Werengani Danieli 12:4.) Yehova anathandiza Ophunzira Baibulo kumvetsa mfundo zimene zinabisika chifukwa cha mabodza amene zipembedzo zonyenga zimaphunzitsa. Panopa, iye akugwiritsa ntchito anthu ake kuti aziphunzitsa anthu padziko lonse moti ulosi wa Danieli ukukwaniritsidwa. Anthu pafupifupi 8 miliyoni aphunzira uthenga wa m’Baibulo ndipo akulalikira padziko lonse. Koma kodi ndi zinthu zina ziti zimene zathandiza kuti ntchito yolalikira iziyenda bwino?

NTCHITO YOMASULIRA BAIBULO

4. Kodi m’zaka za m’ma 1800, Baibulo linamasuliridwa bwanji?

4 Kumasulira Baibulo m’zilankhulo zambiri kunathandiza kuti ntchito yolalikira iziyenda bwino. Kwa zaka zambiri, atsogoleri a matchalitchi akhala akuletsa anthu awo kuwerenga Baibulo moti anapha anthu ena amene analimasulira. M’zaka za m’ma 1800, mabungwe ena anamasulira Baibulo lonse kapena mbali zake m’zilankhulo pafupifupi 400. Choncho pofika chakumapeto kwa zakazi, anthu ambiri anali ndi Baibulo komabe sankamvetsa mfundo zake molondola.

5. Kodi a Mboni za Yehova achita chiyani pa ntchito yomasulira Baibulo?

5 Ophunzira Baibulo ankadziwa kuti ayenera kulalikira ndipo ankagwira ntchitoyi mwakhama kwambiri. Kuwonjezera pamenepa, atumiki a Yehova akhala akugwiritsa ntchito Mabaibulo osiyanasiyana ndiponso kuwagawira kwa anthu. Koma kuyambira mu 1950, anayamba kufalitsa Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika kapena mbali zake m’zilankhulo zoposa 120. Baibulo la Dziko Latsopano lachingelezi linakonzedwanso kuti likhale losavuta kumva ndipo linatulutsidwa mu 2013. Baibuloli likuthandiza kuti ntchito yomasulira Mabaibulo ndiponso yolalikira ikhale yosavuta.

MTENDERE WATITHANDIZA

6, 7. (a) Kodi masiku ano pakhala pakuchitika nkhondo zochuluka bwanji? (b) Kodi mtendere wa m’mayiko ena wathandiza bwanji pa ntchito yolalikira?

6 Pa zaka 100 zapitazi, pamenyedwa nkhondo zambirimbiri ndipo ziwiri zinali zapadziko lonse. Anthu mamiliyoni ambiri anaphedwa pa nkhondozi. Choncho kodi tinganenedi kuti pakhala mtendere umene watithandiza kulalikira? Pamene nkhondo yachiwiri ya padziko lonse inkamenyedwa, Nathan Knorr ankatsogolera ntchito ya Mboni za Yehova. Pa msonkhano wina mu 1942, iye anakamba nkhani yamutu wakuti, “Kodi Padzikoli Padzakhala Mtendere?” Nkhaniyi inafotokoza ulosi wa m’chaputala 17 cha Chivumbulutso ndipo inasonyeza kuti pambuyo pa nkhondoyo padzakhala nthawi ya mtendere osati Aramagedo.Chiv. 17:3, 11.

7 Koma sikuti panali mtendere padziko lonse nkhondoyo itatha. Kafukufuku wina amasonyeza kuti kuchokera pamene nkhondoyo inatha, padzikoli pachitika nkhondo 331 ndipo anthu ambiri aphedwa. Komabe pa zaka zimenezi, m’mayiko ambiri munali mtendere ndipo izi zinathandiza kuti atumiki a Yehova azilalikira uthenga wabwino. Kodi pakhala zotsatirapo zotani? M’chaka cha 1944, panali ofalitsa osakwana 110,000 padziko lonse. Koma masiku ano pali ofalitsa pafupifupi 8,000,000. (Werengani Yesaya 60:22.) Kunena zoona timatha kulalikira anthu ambirimbiri pa nthawi za mtendere.

KAYENDEDWE KABWINO

8, 9. (a) N’chifukwa chiyani tinganene kuti masiku ano kayendedwe n’kabwino? (b) Kodi kayendedwe kabwino katithandiza bwanji pa ntchito yathu?

8 Kayendedwe kabwino ka masiku ano kathandizanso kuti tizilalikira uthenga wabwino. M’chaka cha 1900, zaka pafupifupi 21 pambuyo poti Nsanja ya Olonda yoyamba inasindikizidwa, ku United States kunali magalimoto okwana 8,000 basi. Kunalinso misewu yabwino yochepa kwambiri. Koma masiku ano padziko lonse pali magalimoto oposa 1.5 biliyoni komanso misewu yabwino yambirimbiri. Izi zimathandiza kuti tizikalalikira uthenga wabwino kwa anthu okhala kumadera akutali. Komabe ngakhale kuti nthawi zina tiyenera kuyenda wapansi mtunda wautali, timayesetsa kukalalikira kwa anthu onse.Mat. 28:19, 20.

9 Mayendedwe enanso athandiza pa ntchito yathu yolalikira. Mwachitsanzo, malole, sitima zapamadzi ndiponso zapamtunda zathandiza kuti mabuku ofotokoza Baibulo azitumizidwa mwamsanga kumadera akutali. Ndege zimathandizanso kuti oyang’anira madera, abale a m’Komiti ya Nthambi, amishonale ndiponso anthu ena akafike mwamsanga ku misonkhano ikuluikulu kapena kumipingo. Nawonso abale a m’Bungwe Lolamulira ndiponso abale ena ochokera kulikulu amakwera ndege popita kumayiko ena kuti akalimbikitse Akhristu anzawo. Choncho kayendedwe kabwino kathandiza kuti anthu a Yehova azigwirizana padziko lonse.Sal. 133:1-3.

CHILANKHULO CHATITHANDIZA

10. Kodi anthu ambiri padziko lonse amagwiritsa ntchito bwanji Chingelezi?

10 M’nthawi ya atumwi, anthu ambiri ankalankhula Chigiriki m’mayiko olamulidwa ndi Aroma. Masiku ano anthu ambiri amalankhula Chingelezi. Mwachitsanzo, buku lina linanena kuti: “Pa dzikoli, anthu 25 mwa anthu 100 alionse amalankhula bwino Chingelezi.” Ambiri amaphunzira Chingelezi pofuna kukambirana ndi anthu a m’mayiko ena nkhani zokhudza malonda, ndale, sayansi ndiponso zinthu zina.

11. Kodi Chingelezi chathandiza bwanji pa ntchito yathu?

11 Chingelezichi chathandizanso kuti anthu ambiri amve uthenga wabwino. Kwa zaka zambiri, magazini a Nsanja ya Olonda ndiponso mabuku ena ankayamba kutuluka m’Chingelezi. Chilankhulochi n’chimene chimagwiritsidwanso ntchito ku likulu la padziko lonse la Mboni za Yehova. Ndipo nthawi zambiri amachigwiritsa ntchito ku sukulu zophunzitsa Baibulo ku Patterson.

12. Kodi ntchito yomasulira mabuku yafika pati, nanga zinthu monga makompyuta zathandiza bwanji?

12 Tili ndi udindo wothandiza anthu a mitundu yonse kumva uthenga wabwino. Choncho tamasulira mabuku athu m’zilankhulo pafupifupi 700. Makompyuta ndiponso mapulogalamu ena apakompyuta athandiza kwambiri pa ntchito imeneyi. Zonsezi zathandiza kuti ntchito yathu yolalikira iziyenda bwino komanso kuti tizigwirizana padziko lonse. Koma timagwirizana kwambiri chifukwa chakuti timalankhula “chilankhulo choyera” kapena kuti timamvetsa ndi kutsatira mfundo zoona za m’Baibulo.Werengani Zefaniya 3:9.

MALAMULO AMENE ATHANDIZA

13, 14. Kodi malamulo ndiponso makhoti athandiza bwanji Akhristu masiku ano?

13 M’nkhani yapita ija, tinakambirana zoti malamulo achiroma anathandiza Akhristu. Masiku anonso malamulo ena amathandiza Akhristu. Mwachitsanzo, m’dziko la United States, komwe kuli likulu lathu, kuli ufulu wa chipembedzo, wolankhula ndiponso wochita misonkhano. Izi zathandiza kuti abale m’dzikoli azisonkhana momasuka n’kumaphunzira Baibulo komanso kuphunzitsa ena. Koma nthawi zina ankapita kukhoti kuti ateteze ufulu wawo. (Afil. 1:7) Makhoti ena akawaphera ufuluwu iwo ankachita apilo kumakhoti akuluakulu ndipo ankawina milanduyo.

14 Makhoti a m’mayiko ena athandizanso kuti tikhale ndi ufulu wolambira komanso wolalikira. M’mayiko ena milandu sinkatiyendera bwino moti tinkachita apilo kumakhoti oona za ufulu wa anthu m’mayiko ambiri. Mwachitsanzo, pofika mu June 2014, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya linaweruza motikomera milandu yokwana 57. Zimene linagamula zimagwira ntchito m’mayiko onse amene ali m’Bungwe la Mayiko a ku Ulaya. Anthu ambiri amatida koma makhoti a m’mayiko ambiri amatipatsa ufulu wolambira.Mat. 24:9.

ZINTHU ZINA ZIMENE ZATHANDIZA

Timagawira mabuku ofotokoza Baibulo kwa anthu padziko lonse

15. Kodi makina osindikizira a masiku ano amatha kuchita chiyani ndipo zimenezi zatithandiza bwanji?

15 Makina osindikizira athandizanso pa ntchito yolalikira uthenga wabwino. M’chaka cha 1450, Johannes Gutenberg anapanga makina ena osindikizira ndipo anthu anawagwiritsa ntchito kwa zaka zambirimbiri. Koma pa zaka 200 zapitazi, zinthu zasintha kwambiri pa nkhani yosindikiza mabuku. Makina a masiku ano ndi aakulu kwambiri, amagwira ntchito mwamsanga komanso amatha kuchita zambiri. Kupanga mapepala ndi mabuku n’kotchipanso masiku ano. Makina atsopanowa athandiza kuti maonekedwe a mabuku ndiponso zithunzi zikhale zabwino kwambiri. Kodi zonsezi zathandiza bwanji pa ntchito yathu? Nsanja ya Olonda yoyamba imene inatuluka mu July 1879 inali m’Chingelezi chokha. Inalibe zithunzi ndipo magazini 6,000 okha anasindizidwa. Koma masiku ano magazini oposa 50,000,000 a Nsanja ya Olonda iliyonse amasindikizidwa. Magaziniwa amakhala ndi zithunzi zokongola kwambiri ndipo amapezeka m’zilankhulo zoposa 200.

16. Kodi ndi zinthu ziti zimene zatithandiza kulalikira padziko lonse? (Onani chithunzi patsamba 24.)

16 Pali zinthu zambiri zimene zapangidwa pa zaka 200 zapitazi zomwe zathandiza pa ntchito yolalikira. Tatchula kale sitima zapamadzi, magalimoto ndiponso ndege. Koma pali zinthu zinanso monga njinga, makina otayipira, makina opangira mabuku a anthu osaona, mafoni, makamera, makina ojambula mavidiyo, wailesi, TV, mafilimu, makompyuta ndiponso Intaneti. Zinthu zimenezi zatithandiza kwambiri kuti tizigwira bwino ntchito yolalikira. Timagwiritsa ntchito zinthu zambiri zatsopano kuti tizifalitsa Baibulo ndiponso mabuku ena m’zilankhulo zambiri. Izi zikukwaniritsa ulosi wakuti anthu a Yehova ‘adzayamwa mkaka wa mitundu ya anthu.’Werengani Yesaya 60:16.

17. N’chifukwa chiyani Yehova amatipatsa mwayi wokhala “antchito anzake”?

17 Zikuonekeratu kuti Mulungu akudalitsa ntchito yathu. N’zoona kuti Yehova akhoza kukwaniritsa cholinga chake popanda ifeyo. Koma Atate wathu wakumwamba amatipatsa mwayi wokhala “antchito anzake.” Zimenezi zimatipatsa mpata wosonyeza kuti timamukonda kwambiri komanso timakonda anthu anzathu. (1 Akor. 3:9; Maliko 12:28-31) Choncho tiyeni tizichita zonse zimene tingathe polalikira uthenga wa Ufumu chifukwa ntchitoyi ndi yofunika kwambiri. Tiyeni tizisonyeza kuti timayamikira kwambiri kuti Yehova akutsogolera ndiponso kudalitsa ntchito yathu yophunzitsa anthu padziko lonse.

^ ndime 1 Mu 1931, Ophunzira Baibulo anayamba kudziwika ndi dzina loti Mboni za Yehova.Yes. 43:10.