Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi ‘Mudzakhalabe Maso’?

Kodi ‘Mudzakhalabe Maso’?

“Khalanibe maso chifukwa simukudziwa tsiku kapena ola lake.”—MAT. 25:13.

1, 2. (a) Kodi Yesu anafotokoza zotani zokhudza masiku otsiriza? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?

YESU ali ndi ophunzira ake paphiri la Maolivi anawafotokozera ulosi wochititsa chidwi. Munthu akakhala paphirilo ankatha kuona kachisi wa ku Yerusalemu. Mosakayikira, Petulo, Andireya, Yakobo ndi Yohane ankamvetsera mwatcheru pamene Yesu ankafotokoza zinthu zodzachitika m’tsogolo. Anawafotokozera ulosi wonena za masiku otsiriza a dziko loipali ndiponso nthawi ya ulamuliro wake. Ananenanso kuti m’masiku otsirizawo, iye adzagwiritsa ntchito “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti azipereka chakudya pa nthawi yoyenera kwa atumiki ake.—Mat. 24:45-47.

2 Kenako mu ulosi womwewu, Yesu anafotokoza fanizo la anamwali 10. (Werengani Mateyu 25:1-13.) Tsopano tiyeni tikambirane mafunso otsatirawa: (1) Kodi mfundo yaikulu ya mu fanizoli ndi iti? (2) Kodi odzozedwa atsatira bwanji mfundo ya mu fanizo limeneli, nanga yawathandiza bwanji?(3) Kodi tonsefe tikuphunzira chiyani pa fanizoli?

KODI MFUNDO YAKE YAIKULU NDI ITI?

3. (a) Kodi m’mbuyomu mabuku athu ankafotokoza bwanji fanizo la anamwali 10? (b) Kodi mwina zimenezi zinkabweretsa vuto liti?

3 M’nkhani yapita ija tanena kuti masiku ano kapolo wokhulupirika nthawi zambiri safotokoza kuti nkhani inayake ikuphiphiritsira zakutizakuti koma akutsindika kwambiri zimene tikuphunzira pa nkhanizo. M’mbuyomu mabuku athu ankasonyeza kuti zinthu zonse zotchulidwa mu fanizo la anamwali 10 monga nyale, mafuta ndi mabotolo zinkaphiphiritsira zinazake. Komatu n’kutheka kuti zimenezi zinkachititsa kuti anthu asaganizire kwambiri mfundo yaikulu ya mu fanizoli. Tiyeni tione chifukwa chake tikunena choncho.

4. (a) Kodi mkwati akuimira ndani ndipo tikudziwa bwanji zimenezi? (b) Kodi anamwali akuimira ndani ndipo tikudziwa bwanji zimenezi?

4 Kodi mfundo yaikulu ya mu fanizoli ndi iti? Choyamba, tiyeni tikambirane za anthu otchulidwa mu fanizoli. Kodi mkwati akuimira ndani? N’zosachita kufunsa kuti Yesu ankatanthauza kuti iyeyo ndi mkwati. Tikutero chifukwa chakuti pa nthawi ina ananenanso kuti iye ndi mkwati. (Luka 5:34, 35) Nanga anamwali akuimira ndani? Yesu ananena kuti anamwaliwo ayenera kukhala okonzeka ndipo nyale zawo ziyenera kukhala zikuyaka pa nthawi imene mkwati akufika. Yesu anaperekanso malangizo ngati amenewa kwa “kagulu ka nkhosa” kapena kuti Akhristu odzozedwa. Iye anati: “Mangani m’chiuno mwanu ndipo nyale zanu zikhale chiyakire. Inuyo mukhale ngati anthu amene akuyembekezera kubwera kwa mbuye wawo kuchokera ku ukwati.” (Luka 12:32, 35, 36) Mtumwi Paulo komanso mtumwi Yohane anauziridwanso kulemba kuti Akhristu odzozedwa ali ngati anamwali oyera. (2 Akor. 11:2; Chiv. 14:4) Choncho m’pomveka kunena kuti malangizo komanso machenjezo amene Yesu anapereka mu fanizo lake la pa Mateyu 25:1-13 anali opita kwa Akhristu odzozedwa.

5. Kodi malangizo a Yesu mu fanizoli ndi okhudza nthawi iti? Fotokozani.

5 Chachiwiri, tiyeni tikambirane nthawi yake. Kodi malangizo a Yesu mu fanizoli ndi okhudza nthawi iti? Fanizoli likunena za masiku otsiriza ndipo kubwera kwa mkwati kudzachitika pa chisautso chachikulu. Tikutero chifukwa chakuti chakumapeto kwa fanizoli, Yesu ananena mawu amene angatithandize kudziwa za nthawiyi. Iye anati: “Mkwati anafika.” (Mat. 25:10) Nsanja ya Olonda ya July 15, 2013, inanena kuti ulosi wa Yesu pa Mateyu 24 ndi 25 umanena maulendo 8 za ‘kubwera’ kapena kuti ‘kufika’ kwake. Mawu achigiriki amene anagwiritsidwa ntchito m’maulendo onsewa ndi ofanana. Ndipo ulendo uliwonse umene Yesu anagwiritsa ntchito mawuwa, ankanena za kubwera kwake pa chisautso chachikulu kudzaweruza anthu komanso kudzawononga dziko loipali.

6. Kodi mfundo yaikulu mu fanizo la Yesu ndi iti ndipo tikudziwa bwanji zimenezi?

6 Ndiyeno kodi mfundo yaikulu ya mu fanizoli ndi iti? Kuti tiyankhe, tiyenera kukumbukira kuti iye anapereka fanizoli atangomaliza kunena za kapolo wokhulupirika ndi wanzeru. Kapoloyu akuimira kagulu ka Akhristu odzozedwa kamene kakutsogolera Akhristu onse m’masiku otsiriza. Yesu anachenjeza kagulu kameneka kuti kayenera kukhala kokhulupirika. Kenako ananena fanizoli ndipo mfundo yake yaikulu ndi yoti odzozedwa onse ayenera ‘kukhalabe maso’ m’masiku otsiriza chifukwa kupanda kutero sangalandire mphoto yawo. (Mat. 25:13) Tiyeni tsopano tikambirane bwinobwino fanizoli n’kuona zimene odzozedwa achita potsatira malangizo ake.

KODI ODZOZEDWA ATSATIRA BWANJI MFUNDO YA MU FANIZOLI?

7, 8. (a) N’chiyani chinathandiza anamwali ochenjera kuti asasiye kuyembekezera? (b) Kodi odzozedwa asonyeza bwanji kuti ndi okonzeka?

7 Fanizo la Yesu limeneli likusonyeza kuti anamwali ena anali ochenjera koma ena anali opusa. Anamwali ochenjerawo anali okonzeka komanso atcheru ndipo izi zinawathandiza kuti asasiye kuyembekezera. Anamwali onse anayenera kuyembekezera nthawi yaitali usiku kuti mkwati afike. Choncho iwo anayenera kukhala maso ndiponso kuonetsetsa kuti nyale zawo zikuyaka mpaka mkwati atafika. Mosiyana ndi anamwali opusa, anamwali 5 anali okonzeka kwambiri chifukwa anabweretsa mafuta ena m’mabotolo. Kodi odzozedwa okhulupirika akhalanso okonzeka?

8 M’masiku otsiriza ano, nawonso Akhristu odzozedwa akhala okonzeka kuti agwire ntchito yawo mokhulupirika. Iwo amadziwa kuti ayenera kudzimana zinthu zambiri za m’dziko la Satanali kuti achite zimenezi. Odzozedwawa amadzipereka kwa Yehova kuti azimutumikira ndi moyo wawo wonse. Amachita zimenezi chifukwa chokonda Yehova ndi Mwana wake osati pongofuna kupeza mphoto. Iwo amakhalabe okhulupirika kwa Yehova ndipo amakana kutengera mtima wa anthu a m’dzikoli amene ndi odzikonda, okonda chuma ndiponso amakhalidwe oipa. Odzozedwawa amakhalabe okonzeka nthawi zonse, amawalabe monga zounikira m’dzikoli ndipo satopa podikira kuti Mkwati afike.—Afil. 2:15.

9. (a) N’chifukwa chiyani Yesu anachenjeza za kuwodzera? (b) Kodi odzozedwa achita chiyani pozindikira kuti mkwati watsala pang’ono kufika? (Onaninso mawu a m’munsi.)

9 Monga tanenera kale, anamwali ochenjera anali atcheru. Koma kodi n’zotheka kuti odzozedwa ena ayambe kusinza chifukwa chodikira nthawi yaitali usiku? Inde, paja Yesu ananena kuti anamwali onse 10 “anayamba kuwodzera kenako anagona” pamene ankaona kuti mkwati akuchedwa. Yesu ankadziwa bwino kuti munthu angakhale wofunitsitsa kuchita zinthu zina koma n’kulephera chifukwa chofooka. Odzozedwa okhulupirika azindikira mfundo imeneyi ndipo ayesetsa kwambiri kuti akhalebe atcheru. Mu fanizoli, anamwali onse anadzuka atamva mawu akuti: “Mkwati uja wafika!” Koma anamwali atcheru okha ndi amene anapirira mpaka pa mapeto. (Mat. 25:5, 6; 26:41) Kodi masiku anonso odzozedwa ali tcheru? M’masiku otsiriza ano, iwo akhala tcheru n’kuzindikira umboni wosonyeza kuti mkwati watsala pang’ono kufika. Akhalanso opirira ndiponso okonzeka podikira kuti Mkwati afike. * Koma kodi mu fanizoli n’chiyani chinachitika mkwati atafika?

OCHENJERA ADZALANDIRA MPHOTO KOMA OPUSA ADZALANGIDWA

10. N’chifukwa chiyani tinganene kuti mawu amene ali chakumapeto kwa fanizoli ndi ovuta kumvetsa?

10 Koma mbali yovuta kumvetsa ya mu fanizoli ndi yokhudza mawu amene anamwali ochenjera ndi opusa ankalankhulana chakumapeto kwa fanizoli. (Werengani Mateyu 25:8, 9.) Mbaliyi ndi yovuta kumvetsa chifukwa munthu sangadziwe kuti ndi liti pamene odzozedwa okhulupirika adzakane kuthandiza ena. Koma kuti tidziwe tiyenera kuganizira za nthawi yomwe fanizoli likukwaniritsidwa. Pajatu tanena kuti Yesu kapena kuti Mkwati adzafika chakumapeto kwa chisautso chachikulu kudzapereka chiweruzo. Choncho zikuoneka kuti kulankhulana kuja kudzachitika nthawi yachiweruzo itatsala pang’ono kuyamba. Tikutero chifukwa chakuti pa nthawi imeneyi odzozedwa adzakhala atadindidwa chidindo komaliza.

11. (a) Kodi n’chiyani chidzachitike chisautso chachikulu chitatsala pang’ono kuyamba? (b) Kodi anamwali ochenjera ankatanthauza chiyani pamene ankauza anamwali opusa kuti akagule mafuta?

11 Chisautso chachikulu chisanayambe, odzozedwa onse okhulupirika adzakhala atadindidwa chidindo komaliza. (Chiv. 7:1-4) Izi zidzawatsimikizira kuti apitadi kumwamba. Koma kodi n’chiyani chidzachitikire odzozedwa omwe alephera kukhala tcheru ndiponso sanali okhulupirika? Iwo sadzakhalanso ndi mwayi wopita kumwamba ndipo sadzadindidwa chidindo chomaliza. Chisautso chachikulu chisanayambe, anthu ena okhulupirika adzakhala atadzozedwa kuti alowe m’malo mwawo. Ndiyeno chisautso chachikulu chikadzayamba, n’kutheka kuti odzozedwa osakhulupirikawo adzadabwa Babulo Wamkulu akadzawonongedwa. Mwina pa nthawiyi m’pamene adzazindikire kuti sanakonzekere kufika kwa Mkwati. Kodi iwo akadzapempha thandizo pa nthawiyi, zidzawathera bwanji? Fanizo la Yesu lija limayankha funsoli. Limanena kuti anamwali ochenjera anakana kupereka mafuta awo kwa anamwali opusa ndipo anawauza kuti apite kukagula. Powauza zimenezi ankatanthauza kuti achedwa kwambiri. Kumbukirani kuti izi zinachitika “pakati pa usiku.” Pa nthawiyi zinali zosatheka kukapeza anthu ogulitsa mafuta.

12. (a) Pa nthawi ya chisautso chachikulu, kodi n’chiyani chidzachitikire odzozedwa osakhulupirika? (b) Kodi Yesu adzanena chiyani kwa anthu okhala ngati anamwali opusa?

12 Zimenezi zikusonyeza kuti pa nthawi ya chisautso chachikulu, odzozedwa okhulupirika sadzathandiza odzozedwa osakhulupirika. Izitu zidzakhala chonchi chifukwa nthawi idzakhala itatha kale. Ndiyeno odzozedwa osakhulupirikawo zidzawathera bwanji? Mu fanizo lija Yesu anafotokoza zimene zinachitikira anamwali opusa. Iye anati: “Mkwati anafika, ndipo anamwali okonzekerawo analowa naye limodzi m’nyumba imene munali phwando laukwati, ndipo chitseko chinatsekedwa.” Chakumapeto kwa chisautso chachikulu, Yesu adzafika mu ulemerero wake ndipo adzasonkhanitsa odzozedwa okhulupirika n’kupita nawo kumwamba. (Mat. 24:31; 25:10; Yoh 14:1-3; 1 Ates. 4:17) Apatu chitseko chidzatsekedwa ndipo odzozedwa osakhulupirika adzafanana ndi anamwali opusa aja. Tingati adzafuula kuti: “Ambuye, ambuye, titsegulireni!” Pa nthawi yachiweruzoyi, Yesu adzawayankha mofanana ndi mmene adzayankhire anthu okhala ngati mbuzi. Iye adzati: “Kunena zoona, sindikukudziwani inu.” Izitu zidzakhala zomvetsa chisoni kwambiri.—Mat. 7:21-23; 25:11, 12.

13. (a) N’chifukwa chiyani sitiyenera kuganiza kuti odzozedwa ambiri adzakhala osakhulupirika? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti mawu a Yesu mu fanizo lake sakusonyeza kuti ankakayikira odzozedwa? (Onani chithunzi patsamba 12.)

13 Kodi pamenepa Yesu ankatanthauza chiyani? Kodi odzozedwa ambiri adzakhala osakhulupirika ndipo padzafunika kuti anthu ena adzozedwe n’kulowa m’malo mwawo? Ayi si choncho. Paja Yesu anali atangopereka kumene chenjezo kwa “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” kuti asakhale kapolo woipa. Ponena zimenezi, sankatanthauza kuti kapoloyu adzasinthadi n’kukhala woipa. N’chimodzimodzi ndi fanizo la anamwali 10. Yesu anapereka chenjezo kwa odzozedwa kuti asakhale ngati anamwali opusa. Mu fanizoli, anamwali 5 anali opusa ndipo anamwali 5 anali ochenjera. Izi zikusonyeza kuti wodzozedwa aliyense ayenera kusankha pakati pa zinthu ziwiri. Angasankhe kukhala wokonzeka ndiponso watcheru kapena kukhala wopusa ndiponso wosakhulupirika. Nayenso mtumwi Paulo analemba mfundo yofanana ndi imeneyi kwa odzozedwa anzake. (Werengani Aheberi 6:4-9; yerekezerani ndi Deuteronomo 30:19.) N’zoona kuti mtumwi Paulo anawachenjeza mwamphamvu koma sankawakayikira. Tikutero chifukwa chakuti ananenanso kuti iwo akuyembekezera “zinthu zabwino kwambiri.” Mu fanizo lake, nayenso Yesu ankachenjeza odzozedwa mwachikondi ndipo ankakhulupirira kuti adzamvera chenjezoli. Iye akudziwa kuti wodzozedwa aliyense akhoza kukhalabe wokhulupirika mpaka kudzalandira mphoto yake.

KODI A “NKHOSA ZINA” AKUPHUNZIRAPO CHIYANI?

14. Kodi a “nkhosa zina” akuphunzirapo chiyani pa fanizo la anamwali 10?

14 M’nkhaniyi taona kuti Yesu anapereka fanizo la anamwali 10 pochenjeza odzozedwa. Kodi izi zikutanthauza kuti a “nkhosa zina” sangaphunzirepo chilichonse? (Yoh. 10:16) Ayi si choncho. Paja mfundo yaikulu mu fanizoli ndi yakuti: “Khalanibe maso.” Kodi malangizo amenewa ndi opita kwa odzozedwa okha? Pa nthawi ina, Yesu ananena kuti: “Zimene ndikuuza inuzi ndikuuza onse, Khalani maso.” (Maliko 13:37) Yesu amafuna kuti Akhristu onse akhale okonzeka kutumikira Yehova mokhulupirika komanso akhale maso. Choncho Mkhristu aliyense ayenera kutsanzira odzozedwa n’kumaika kutumikira Mulungu pa malo oyamba. Mfundo ina imene tiyenera kuiganizira ndi yoti anamwali opusa anapempha anamwali ochenjera kuti awagawire mafuta koma sizinatheke. Izi zikutikumbutsa kuti palibe amene angatichitire zinthu monga kukhala okhulupirika, kukhalabe m’gulu la Yehova kapena kukhala maso. Aliyense adzayankha yekha mlandu kwa Woweruza wachilungamo amene Yehova wasankha. Choncho tiyenera kukhala okonzeka chifukwa Woweruzayo akubwera mwamsanga.

Zinali zosatheka kugawira ena mafuta choncho palibe amene angatichitire zinthu monga kukhalabe okhulupirika ndiponso kukhala maso

15. N’chifukwa chiyani Mkhristu aliyense amayembekezera mwachidwi ukwati wa Khristu ndi odzozedwa?

15 Fanizo la Yesuli kwenikweni likunena za ukwati womwe udzathandiza Akhristu onse. Tonsefe tikuyembekezera mwachidwi ukwati umenewu. Choyamba, odzozedwa onse adzapita kumwamba ndipo pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo, ukwatiwu udzachitika. (Chiv. 19:7-9) Ukwati umenewu udzachititsa kuti pakhale boma labwino kwambiri limene lidzathandiza aliyense amene adzakhale padziko lapansi. Kaya tikuyembekezera kupita kumwamba kapena kudzakhala padzikoli, tiyenera kuphunzirapo kanthu pa fanizo la anamwali 10. Tiyeni tonsefe tikhale okonzeka mumtima mwathu, tikhalebe okhulupirika ndiponso atcheru. Tikatero tidzalandira madalitso amene Yehova watikonzera.

^ ndime 9 Mu fanizoli, kufuula kuti, “Mkwati uja wafika!” kuli mu vesi 6 koma kufika kwake kwenikweni kuli mu vesi 10. Izi zikusonyeza kuti panadutsa nthawi kuchokera pamene anafuula kufika pamene anafikadi. M’masiku otsiriza ano, odzozedwa atcheru azindikira kuti Yesu akulamulira. Koma iwo ayenera kukhalabe maso mpaka iye atafika.