Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi ‘Mudzakhalabe Maso’?

Kodi ‘Mudzakhalabe Maso’?

“Cotelo khalanibe maso cifukwa simukudziŵa tsiku kapena ola lake”—MAT. 25:13.

1, 2. (a) Kodi Yesu anakamba ciani za masiku otsiliza? (b) Ndi mafunso ati amene tikambilane?

TAYELEKEZANI kuti mukuona Yesu atakhala pa Phiri la Maolivi, ndipo akuyang’ana kacisi amene ali mu Yerusalemu. Iye ali limodzi ndi atumwi ake anai, Petulo, Andireya, Yakobo, ndi Yohane. Iwo akuchela khutu kwambili pamene Yesu akuwafotokozela za ulosi wocititsa cidwi wokhudza tsogolo. Ulosiwo ukunena zimene zidzacitika m’masiku otsiliza a dziko loipa lino Yesu akadzayamba kulamulila mu Ufumu wa Mulungu. Yesu akuwauza kuti m’masiku otsiliza, “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” adzaimila iye padziko lapansi, ndipo azidzapatsa otsatila ake cakudya cakuuzimu panthawi yake yoyenela.Mat. 24:45-47.

2 Kenako, mu ulosi umodzimodziwo, Yesu akufotokozanso fanizo la anamwali 10. (Ŵelengani Mateyu 25:1-13.) Tiyeni tikambilane mafunso atatu awa: (1) Ndi uthenga wanji womwe uli m’fanizo limeneli? (2) Kodi odzozedwa okhulupilika akhala akugwilitsila nchito bwanji uphungu wa m’fanizo limeneli? Nanga zotsatilapo zake ndi zotani? (3) Kodi aliyense wa ife angapindule bwanji ndi fanizo la Yesu limeneli masiku ano?

NDI UTHENGA WANJI WOMWE ULI M’FANIZOLI?

3. Kodi kale zofalitsa zathu zinali kufotokoza bwanji fanizo la anamwali 10? Nanga zotsatilapo zinali zotani?

3 M’nkhani yapita, tinaphunzila kuti m’zaka zaposacedwapa, kapolo wokhulupilika wasintha mofotokozela nkhani zina za m’Baibulo. Masiku ano, kapolo wokhulupilika akufotokoza kwambili zimene tikuphunzilapo pa nkhanizo m’malo molongosolo zimene ulosiwo kapena nkhaniyo ikutanthauza. Mwacitsanzo, taganizilani za fanizo la Yesu la anamwali 10. Kale, zofalitsa zathu zinali kufotokoza kuti nyali, mafuta, ndi mabotolo a mafuta amaimila zinthu zinazake kapena winawake. Kodi n’kutheka kuti uthenga womveka bwino ndiponso wofunika kwambili womwe uli m’fanizoli unali kuphimbika ndi zinthu zing’onozing’ono zimenezo? Yankho la funsoli ndi lofunika kwambili.

4. Malinga ndi fanizo la Yesu, (a) kodi mkwati ndani? (b) nanga anamwali ndani?

4 Tiyeni tikambilane uthenga wofunika womwe uli m’fanizo la Yesu limeneli. Coyamba, ganizilani za anthu amene akuchulidwa m’fanizoli. Kodi mkwati ndani m’fanizoli? Mwacionekele, Yesu anali kukamba za iye mwini, cifukwa cakuti panthawi ina iye anakamba kuti ndi mkwati. (Luka 5:34, 35) Nanga bwanji za anamwali? M’fanizo limeneli, Yesu anakamba kuti anamwali anayenela kukhala okonzeka, ndipo nyali zao zinafunika kukhala zoyaka mpaka mkwati atafika. Yesu anapatsa malangizo ofanana ndi amenewa ku “kagulu ka nkhosa” ka otsatila ake odzozedwa. Iye anati: “Mangani m’ciuno mwanu ndipo nyale zanu zikhale ciyakile. Inuyo mukhale ngati anthu amene akuyembekezela kubwela kwa mbuye wao kucokela ku ukwati.” (Luka 12:32, 35, 36) Komanso, mtumwi Paulo ndi mtumwi Yohane mouzilidwa anayelekezela otsatila a Kristu odzozedwa ndi anamwali oyela. (2 Akor. 11:2; Chiv. 14:4) Apa n’zoonekelatu kuti Yesu anali kupeleka uphungu ndiponso cenjezo kwa otsatila ake odzozedwa pamene anali kufotokoza fanizo lopezeka pa Mateyu 25:1-13.

5. Kodi Yesu anaonetsa bwanji za nthawi pamene ulosi wake udzakwanilitsidwa?

5 Kodi uphungu wa Yesu unali kunena za nthawi iti? Zimene Yesu anakamba kumapeto kwa fanizolo zingatithandize kudziŵa nthawi imeneyo. Iye anati: “Mkwati anafika.” (Mat. 25:10) Mu Nsanja ya Mlonda ya July 1, 2013, tinaphunzila kuti mu ulosi wopezeka pa Mateyu caputala 24 ndi 25, Yesu anachula za ‘kubwela’ kapena kufika kwake nthawi zokwanila 8. Pamene Yesu anakamba za ‘kubwela’ kapena kufika kwake, anali kutanthauza za nthawi ya cisautso cacikulu pamene iye adzabwela kudzaweluza ndi kuononga dziko loipali. Conco, tingakambe kuti fanizo la Yesu likunena za masiku otsiliza ndi kuti adzabwela panthawi ya cisautso cacikulu.

6. Malinga ndi zimene Yesu anakamba, kodi uthenga wofunika umene uli m‘fanizo lake ndi wotani?

6 Kodi uthenga wofunika umene uli m’fanizoli ndi wotani? Musaiŵale zimene Yesu anali kukamba pochula mfundo imeneyi. M’caputala 24 ca buku la Mateyu, Yesu anafotokoza za “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu.” Kapolo ameneyo anali kudzakhala kagulu ka amuna odzozedwa amene anali kudzatsogolela otsatila a Kristu m’masiku otsiliza. Yesu anacenjeza amunawo kuti ayenela kupitiliza kukhala okhulupilika. M’caputala cotsatila, Yesu anagwilitsila nchito fanizo la anamwali 10 polangiza otsatila ake onse odzozedwa a m’masiku otsiliza. Uthenga wake unali wakuti io ayenela ‘kukhalabe maso’ kuti asataye mphoto yao ya mtengo wapatali. (Mat. 25:13) Tiyeni tikambilane za fanizo limenelo ndi kuona mmene odzozedwa agwilitsila nchito uphungu umenewu.

KODI ODZOZEDWA AGWILITSILA NCHITO BWANJI UPHUNGU WA M’FANIZO LIMENELI?

7, 8. (a) N’cifukwa ciani anamwali anzelu anali okonzeka? (b) Nanga odzozedwa aonetsa bwanji kuti ndi okonzeka?

7 Fanizo la Yesu likugogomeza mfundo yakuti anamwali anzelu anali okonzeka za kubwela kwa mkwati kusiyana ndi anamwali opusa. N’cifukwa ciani? Cifukwa cakuti anaonetsa makhalidwe aŵili awa:kukonzeka ndi kukhala maso. Anamwali onse 10 anafunika kukhala maso, ndipo nyali zao zinafunika kupitiliza kukhala zoyaka usiku. Mosiyana ndi anamwali opusa, anamwali asanu anali okonzekadi cifukwa anali ndi mafuta ena m’mabotolo ao kuonjezela pa mafuta amene anali kale m’nyali zao. Kodi Akristu odzozedwa okhulupilika aonetsa bwanji kuti ndi okonzeka kubwela kwa Yesu?

8 Odzozedwa ndi okonzeka kukwanilitsa utumiki wao mpaka mapeto. Amadziŵa kuti kutumikila Mulungu kumafuna kuti akhale umoyo wosalila zambili m’dziko lino la Satana, ndipo ndi ofunitsitsa kucita zimenezi. Iwo ndi otsimikiza mtima kutumikila Yehova mokhulupilika cifukwa cakuti amam’konda, ndi kukondanso Mwana wake, ndipo amatelo osati cifukwa cakuti mapeto ali pafupi. Iwo ndi okhulupilika ndipo amapewa mzimu wokonda cuma, ciwelewele, ndi kudzikonda. Mofanana ndi anamwali anzelu amene anali okonzeka ndi nyali zao, odzozedwa akupitilizabe kuwala ndi kuyembekezela moleza mtima kubwela kwa Mkwati, ngakhale angaoneke kuti akucedwa.Afil. 2:15.

9. (a) Ndi cenjezo lotani limene Yesu anapeleka ponena za kuodzela? (b) Kodi odzozedwa aonetsa bwanji kuti alabadila mau akuti: “Mkwati uja wafika”? (Onaninso mau amunsi.)

9 Khalidwe laciŵili limene linathandiza anamwali anzelu kukhala okonzeka ndilo kukhala maso. Kodi n’zotheka kuti Mkristu wodzozedwa alephele kukhala maso panthawi imene akuyembekeza kubwela kwa Kristu ? Inde n’zotheka. Yesu anakamba kuti anamwali 10 “onse anayamba kuwodzela kenako anagona” pamene anaona kuti mkwati akucedwa. Yesu anali kudziŵa kuti ngakhale munthu wofunitsitsa kukhala maso angagone thupi likafooka. Odzozedwa okhulupilika akhala akutsatila cenjezo limenelo ndi kucita khama kuti apitilizebe kukhala maso. M’fanizo limenelo, anamwali onse anadzuka pamene anamva kufuula usiku kuti: “Mkwati uja wafika!” Koma ndi anamwali anzelu okha amene anakhalabe maso. (Mat. 25:5, 6; 26:41) Mofananamo, Akristu odzozedwa okhulupilika m’masiku otsiliza ano alabadila mau akuti “Mkwati uja wafika!” Iwo acita zimenezi mwa kukhulupilila umboni woonekelatu wakuti Yesu ali pafupi kubwela, ndipo ndi okonzeka ponena za kubwela kwake. * Komabe, tiyeni tikambilane mbali yomaliza ya fanizo la Yesu, imene ikukhudza kwambili nthawi inayake yapadela.

ANZELU AFUPIDWA NDIPO OPUSA ALANGIDWA

10. Ndi funso liti limene tingafunse ponena za makambilano a pakati pa anamwali anzelu ndi anamwali opusa?

10 Cakumapeto kwa fanizo la Yesu, anamwali opusa akupempha anamwali anzelu mafuta oika m’nyali zao. Koma anamwali anzelu akukana kuwathandiza. (Ŵelengani Mateyu 25:8, 9.) Kodi Akristu odzozedwa okhulupilika anakanapo kuthandiza anzao? Kuti tipeze yankho, tiyenela kudziŵa kuti fanizoli likunena za nthawi iti. Yesu amene ndi Mkwati, adzabwela kudzapeleka ciweluzo cisautso cacikulu cikatsala pang’ono kutha. Conco, zikuoneka kuti makambilano a anamwaliwo akuonetsa zimene zidzacitike cisautso cacikulu cikatsala pang’ono kutha. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti panthawiyo odzozedwa adzakhala atalandila cidindo cao comaliza.

11. (a) N’ciani cidzacitika cisautso cacikulu cikatsala pang’ono kuyamba? (b) N’ciani cimene anamwali anzelu anatanthauza pamene anauza anamwali opusa kuti apite kukagula mafuta ao?

11 Motelo, Cisautso cacikulu cisanayambe, odzozedwa onse okhulupilika amene adzakhala akali padziko lapansi adzalandila cidindo cao cotsiliza. (Chiv. 7:1-4) Cidindo cimeneco cidzakhala umboni wakuti adzapitadi kumwamba. Nanga n’ciani cidzacitika kwa odzozedwa amene adzalephela kukhala maso ndi kukhala okhulupilika cisautso cacikulu cisanayambe? Iwo sadzalandila mphoto yao ya kumwamba. Panthawiyo, Akristu ena okhulupilika adzakhala atadzozedwa. Cisautso cacikulu cikadzayamba, odzozedwa a m’gulu la anamwali opusa adzadabwa kwambili akadzaona kuonongedwa kwa Babulo Wamkulu. Mwina panthawiyo ndi pamene adzazindikila kuti sanakonzekele kubwela kwa Yesu. N’ciani cidzacitika akadzapempha thandizo panthawi imeneyo? Yankho tikulipeza m’fanizo la Yesu. Anamwali anzelu anakana kugaŵila mafuta ao anamwali opusa. M’malo mwake, anawauza kuti apite kukagula ao kwa ogulitsa. Popeza kuti panali “pakati pa usiku,” zinali zovuta kupeza anthu ogulitsa mafutawo cifukwa munali m’mbuyo mwa alendo.

12. (a) Panthawi ya cisautso cacikulu, n’ciani cidzacitikila aliyense amene kale anali wodzozedwa koma n’kukhala wosakhulupilika asanalandile cidindo cotsiliza? (b) Nanga n’ciani cidzacitikila omwe adzakhala ngati anamwali opusa?

12 Panthawi ya cisautso cacikulu, odzozedwa okhulupilika sadzathandizanso aliyense wosakhulupilika. Sadzatelo cifukwa mudzakhala m’mbuyo mwa alendo. Motelo, n’ciani cidzacitikila osakhulupilika amenewo? Onani zimene zinacitika pamene anamwali opusa anapita kukagula mafuta a m’nyali. Baibulo limati: “Mkwati anafika, ndipo anamwali okonzekelawo analoŵa naye limodzi m’nyumba imene munali phwando laukwati, ndipo citseko cinatsekedwa.” Pamene Yesu adzabwela mu ulemelelo wake cisautso cacikulu citatsala pang’ono kutha, iye adzasonkhanitsila odzozedwa okhulupilika kumwamba. (Mat. 24:31; 25:10; 1 Ates. 4:17) Citseko cidzatsekedwadi kuti osakhulupilikawo, amene adzakhala ngati anamwali opusa asaloŵe. Iwo adzafuula kuti: “Ambuye, ambuye, titsegulileni!” Koma adzalandila yankho lofanana ndi limene anthu ambili amene ali ngati mbuzi adzalandila panthawi yaciweluzo. Iye adzati: “Kunena zoona, sindikukudziŵani inu.” Zimenezo zidzakhaladi zomvetsa cisoni.Mat. 7:21-23; 25:11, 12.

13. (a) N’cifukwa ciani sitiyenela kuganiza kuti odzozedwa ambili a Kristu adzakhala osakhulupilika? (b) N’cifukwa ciani tingakambe kuti fanizo la Yesu limaonetsa kuti iye ali ndi cidalilo mwa Akristu odzozedwa? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

13 Kodi Yesu anali kutanthauza kuti odzozedwa ambili adzakhala osakhulupika, ndi kuti adzafunika kuloŵedwa m’malo ndi ena? Iyai. Kumbukilani kuti Yesu anacenjeza “kapolo wokhulupilika ndi wanzelu” kuti sayenela kukhala kapolo woipa. Zimenezo sizitanthauza kuti Yesu anali kuyembekezela kuti kapoloyo adzakhaladi woipa. M’fanizo la anamwali 10 muli cenjezo lamphamvu. Malinga ndi fanizoli, anamwali asanu anali anzelu ndipo asanu anali opusa. Zimenezi zikusonyeza kuti wodzozedwa aliyense ali ndi ufulu wosankha kukhala wokonzeka ndi kukhala maso, kapena kukhala wopusa ndi wosakhulupilika. Mtumwi Paulo anapeleka cenjezo lofanana ndi limeneli kwa abale ndi alongo ake odzozedwa. (Ŵelengani Aheberi 6:4-9; yelekezelani ndi Deuteronomo 30:19) Cenjezo lake linali lacindunji, koma iye analinso ndi cidalilo cakuti io adzalandila mphoto yao. Cenjezo limene lili m’fanizo la anamwali 10 limaonetsa kuti Yesu nayenso anali ndi cidalilo cakuti odzozedwa adzalandila mphoto yao. Iye amadziŵa kuti mtumiki wake wodzozedwa aliyense angakhalebe wokhulupilika ndi kulandila mphoto ya mtengo wapatali imeneyi.

NANGA A “NKHOSA ZINA” ZA KRISTU AMAPINDULA BWANJI?

14. N’cifukwa ciani a “nkhosa zina” naonso angapindule ndi fanizo la anamwali 10?

14 Popeza kuti uthenga womwe uli m’fanizo la Yesu umakhudza otsatila ake odzozedwa, kodi tinganene kuti a “nkhosa zina” sangapindule ndi fanizo limeneli? (Yoh. 10:16) Kutalitali! Musaiŵale kuti uthenga waukulu womwe uli m’fanizo limeneli ndi wakuti: “Khalani maso.” Kodi uthengawu ukukhudza odzozedwa okha? Yesu anati: “Zimene ndikuuza inuzi ndikuuza onse, Khalani maso.” (Maliko 13:37) Yesu amafuna kuti ophunzila ake onse azikhala okonzeka komanso kukhala maso. Akristu onse amatengela citsanzo ca odzozedwa pankhaniyi, ndipo amaika utumiki wao patsogolo. Tisaiŵale kuti anamwali opusa anapempha anamwali anzelu kuti awagaŵileko mafuta. Zimenezo zikutikumbutsa kuti aliyense payekha ayenela kukhala wokhulupilika kwa Mulungu, wokonzeka, ndiponso kukhala maso. Aliyense adzaziyankhila mlandu pamaso pa Woweluza wolungama, Yesu Kristu, amene wasankhidwa ndi Yehova. Tifunika kukhala okonzeka cifukwa afika posacedwapa.

Kupempha mafuta kumene anamwali opusa anacita kumatikumbutsa kuti aliyense payekha ayenela kukhalabe maso komanso kukhala wokhulupilika

15. N’cifukwa ciani Akristu onse oona akusangalala kudziŵa za cikwati ca pakati pa Kristu ndi mkwatibwi?

15 Akristu onse ndi okondwela kudziŵa za cikwati cochulidwa m’fanizo la Yesu. Mtsogolomu, pambuyo pa nkhondo ya Aramagedo, Akristu odzozedwa adzakhala mkwatibwi wa Kristu. (Chiv. 19:7-9) Aliyense amene adzakhala ndi moyo padziko lapansi adzapindula ndi cikwati ca kumwamba cimeneco, cifukwa cikwatico ndi citsimikizo ca boma labwino. Kaya tikuyembekeza kudzakhala ndi moyo wosatha kumwamba kapena padziko lapansi, tiyeni tikhale otsimikiza mtima kupitiliza kukhala okonzeka ndi kukhala maso. Tikatelo, tidzasangalala ndi tsogolo labwino limene Yehova watikonzela.

^ par. 9 M’fanizo limeneli, pali nyengo ya nthawi kucokela pamene mau akuti “Mkwati uja wafika!” akumveka (vesi 6) ndi kubwela kapena kufika kwa mkwati (vesi 10). M’masiku otsiliza ano, odzozedwa apitilizabe kukhala maso. Iwo aona cizindikilo ca kukhalapo kwa Yesu, ndipo akudziŵa kuti iye akulamulila monga Mfumu ya Ufumu wa Mulungu. Ngakhale zili conco, io afunika kukhalabe maso mpaka iye atabwela kapena kufika.