Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

Mafunso Ocokela kwa Aŵelengi

Kale, mabuku athu anali kufotokoza kwambili nkhani za m’Baibulo ndi zimene zikuimila. Koma m’zaka zaposacedwapa, mabuku athu safotokoza kwambili zimenezo. N’cifukwa ciani?

Nsanja ya Olonda yacingelezi ya September 15, 1950, inafotokoza kuti nthawi zina munthu, cocitika, kapena cinthu cinacake m’Baibulo cinali kuimila cinthu cina cacikulu mtsogolo. Kale, mabuku athu anali kufotokoza kuti amuna ndi akazi okhulupilika monga Debora, Elihu, Yefita, Yobu, Rahabi, Rabeka, ndi ena ambili, anali kuimila odzozedwa kapena “khamu lalikulu.” (Chiv. 7:9) Mwacitsanzo, Yefita, Yobu, ndi Rabeka anali kukambidwa kuti anali kuimila odzozedwa, pamene Debora ndi Rahabi anali kuimila khamu lalikulu. Komabe, m’zaka zaposocedwapa, tasiya kufotokoza pa zimene nkhani za m’Baibulo zimaimila. N’cifukwa ciani zakhala conco?

COCITIKA

Nkhosa ya pasika imene Aisiraeli anali kupha inali kuimila cinacake.—Num. 9:2

ZIMENE CINALI KUIMILA

Paulo anakamba kuti Kristu “wapelekedwa monga nsembe yathu ya pasika.”—1 Akor. 5:7

Malemba amaonetsa kuti anthu ena ochulidwa m’Baibulo anali kuimila cinthu cina cacikulu codzacitika mtsogolo. Mwacitsanzo, pa Agalatiya 4:21-31, mtumwi Paulo anafotokoza za “tanthauzo lophiphilitsila” lokhuza akazi aŵili. Mkazi woyamba ndi Hagara amene anali wanchito wa Abulahamu. Paulo anafotokoza kuti Hagara anali kuimila mtundu wa Aisiraeli, umene unacita pangano ndi Yehova kupyolela m’Cilamulo ca Mose. Koma Sara, amene anali mfulu, anali kuimila mkazi wa Mulungu, limene ndi mbali yakumwamba ya gulu lake. Paulo anachulanso kufanana pakati pa mfumu komanso Melekizedeki ndi Yesu. (Aheb. 6:20; 7:1-3) Ndiponso, Paulo anayelekezela mneneli Yesaya ndi ana ake aamuna kuti anali kuimila Yesu ndi otsatila ake odzozedwa. (Aheb. 2:13, 14) Yehova ndiye anauzila Paulo kulemba nkhani zonsezi, ndipo ndife otsimikiza mtima kuti n’zolondola.

Ngakhale kuti Baibulo limaonetsa kuti munthu wina anali kudzaimila munthu winawake mtsogolo, sitiyenela kuganiza kuti nkhani iliyonse kapena cocitika ciliconse cimaimila cinthu cacikulu codzacitika mtsogolo. Mwacitsanzo, Paulo anakamba kuti Melekizedeki anali kuimila Yesu, koma sanakambe ciliconse pankhani yakuti panthawi ina Melekizedeki anapatsa Abulahamu mkate ndi vinyo kuti asangalale pambuyo pogonjetsa mafumu anai. Conco, palibe cifukwa ca m’Malemba cofuna kudziŵila ngati cocitikaci cili ndi tanthauzo lobisika.—Gen. 14:1, 18.

Olemba nkhani zakale amene anakhalako pambuyo pa imfa ya Kristu, anali kufufuza zinthu zilizonse kuti adziŵe zimene zimatanthauza. Pofotokoza ziphunzitso za Origen, Ambrose, ndi Jerome, buku lina linati: “Iwo anali kufufuza zocitika zilizonse za m’Malemba ndi zimene zinali kuimila ngakhale kuti zinali zosafunika kwenikweni. Anafufuzanso ngakhale zinthu zing’onozing’ono zimene zinali zofala panthawiyo zimene anaona kuti zikubisa coonadi . . . , kuphatikizapo ciŵelengelo ca nsomba zimene ophunzila anagwila usiku umene Mpulumutsi woukitsidwa anaonekela kwa io. Ena amakamba kuti ciŵelengelo ca nsombazo cinali 153.”

Katswili wina wacipembedzo dzina lake Augustine, anafotokoza mwatsatanetsatane za nkhani ya Yesu imene timaŵelenga yakuti anadyetsa amuna pafupifupi 5,000 ndi mikate isanu ya balele komanso nsomba ziŵili. Popeza kuti anthu anali kuona balele kukhala cakudya cotsika poyelekezela ndi tiligu, Augustine anafotokoza kuti mikate isanu iyenela kuti inali kuimila mabuku asanu olembedwa ndi Mose (“balele” wotsika anali kuona kuti akuimila “Cipangano Cakale”) Nanga bwanji za nsomba ziŵili? Iye anaziyelekezela ndi mfumu ndi wansembe pa zifukwa zosadziŵika bwino. Katswili wina wofufuza zimene nkhani za m’Baibulo zimaimila anakamba kuti zimene Yakobo anacita pogula ukulu wa Esau ndi cakudya cofiila, zinaimila coloŵa ca kumwamba cimene Yesu anagulila anthu pogwilitsila nchito magazi ake ofiila.

Vuto ndi lakuti matembenuzidwe amenewa alibe maziko. Anthu sangathe kuzindikila kuti ndi nkhani ziti za m’Baibulo zimene zimaimila zinthu zodzacitika mtsogolo kapena ai. Mfundo imene sitiyenela kuiŵala ndi yakuti: Sitimatsutsa ngati Malemba akamba kuti munthu winawake, cocitika cinacake, kapena cinthu cinacake, cimaimila cinthu cina mtsogolo. Koma timapewa kunena kuti munthu winawake kapena nkhani inayake imaimila cinacake ca mtsogolo ngati palibe umboni wa m’Malemba wosonyeza zimenezo.

Nanga tingapindule bwanji ndi zocitika ndiponso zitsanzo za m’Malemba? Pa Aroma 15:4, mtumwi Paulo anati: “Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize, zimatipatsa ciyembekezo cifukwa malembawa amatithandiza kupilila ndiponso amatilimbikitsa.” Apa Paulo anali kutanthauza kuti abale ake odzozedwa a m’nthawi ya atumwi akanapindula ndi nkhani zimene zinalembedwa m’Malemba. Komabe, kuyambila kale anthu onse a Mulungu, kaya ndi odzozedwa kapena a “nkhosa zina,” akhala akupindula ndi “zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale.”—Yoh. 10:16; 2 Tim. 3:1.

M’malo moona kuti nkhani zimenezi zimangogwila nchito ku gulu limodzi la anthu, anthu Mulungu kuyambila kale, kaya ndi odzozedwa kapena ai akhala akugwilitsila nchito mfundo zambili zimene amaphunzila m’nkhani za m’Baibulo. Motelo, sitiyenela kuona kuti mfundo za m’buku la Yobu zimangogwila nchito kwa odzozedwa amene anapilila panthawi ya Nkhondo Yoyamba ya Padziko Lonse. Atumiki ambili a Mulungu, amuna ndi akazi, odzozedwa ndi a khamu lalikulu, akumanapo ndi mavuto monga a Yobu, ndipo ‘aona zimene Yehova anamupatsa, aona kuti Yehova ndi wacikondi cacikulu ndi wacifundo.’—Yak. 5:11.

Ganizilani izi: M’mipingo yathu masiku ano, muli akazi acikulile okhulupilika monga Debora, acinyamata anzelu monga Elihu amene akutumikila monga akulu, apainiya olimba mtima ndipo acangu ngati Yefita, ndiponso amuna ndi akazi okhulupilika ndipo oleza mtima monga Yobu. Timayamikila kwambili kuti Yehova anasunga “zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale,” kuti tikhale ndi “ciyembekezo cifukwa malembawa amatithandiza kupilila ndiponso amatilimbikitsa.”

Conco, pa zifukwa zimenezi, mabuku athu a m’zaka zino amagogomezela kwambili mfundo zimene tikuphunzilapo pa nkhani za m’Baibulo, m’malo mofotokoza zinthu zimene nkhanizo zimaimila.