Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Zimene Tiphunzilapo pa Fanizo la Matalente

Zimene Tiphunzilapo pa Fanizo la Matalente

“Woyamba anam’patsa ndalama zokwana matalente asanu, waciŵili anam’patsa matalente aŵili, ndipo wacitatu anam’patsa talente imodzi.”—MAT. 25:15.

1, 2. N’cifukwa ciani Yesu anafotokoza fanizo la matalente?

M’FANIZO la matalente, Yesu anafotokoza momveka bwino za udindo umene otsatila ake odzozedwa ali nao. Tiyenela kumvetsa zimene fanizoli limatanthauza, cifukwa cakuti limakhudza Akristu onse oona, kaya akuyembekezela kudzalandila mphoto yao kumwamba kapena padziko lapansi.

2 Yesu anafotokoza fanizo la matalente poyankha zimene ophunzila ake anafunsa ponena za “cizindikilo ca kukhalapo kwake ndi ca mapeto a nthawi ino.” (Mat. 24:3) Conco, fanizo limeneli likukwanilitsidwa masiku ano, ndipo lili mbali ya cizindikilo ca kukhalapo kwa Yesu ndi kuti akulamulila monga Mfumu.

3. Tiphunzilapo ciani pa mafanizo opezeka pa Mateyu caputala 24 ndi 25?

3 Fanizo la matalente ndi limodzi mwa mafanizo anai opezeka pa Mateyu 24:45 mpaka 25:46. Mafanizo ena atatu ndi okhudza kapolo wokhulupilika ndi wanzelu, anamwali 10, ndi nkhosa ndi mbuzi. Koma onse ali mbali ya yankho la Yesu lokhudza cizindikilo ca kukhalapo kwake. M’mafanizo onse anai, Yesu anafotokoza zinthu zimene zinali kudzasiyanitsa otsatila ake oona m’masiku otsiliza ano. Fanizo la kapolo wokhulupilika, la anamwali 10, ndi la matalente, onsewa amakhudza otsatila ake odzozedwa. M’fanizo lokhudza kapolo wokhulupilika, Yesu anatsindika mfundo yakuti odzozedwa ocepa amene apatsidwa nchito yodyetsa anchito apakhomo m’masiku otsiliza ayenela kukhala okhulupilika ndiponso anzelu. M’fanizo la anamwali, Yesu anagogomezela mfundo yakuti odzozedwa ake onse ayenela kukhala okonzeka komanso kukhala maso podziŵa kuti Yesu adzabwela pa tsiku kapena ola limene sakuyembekezela. M’fanizo la matalente, Yesu anaonetsa kuti odzozedwa afunika kucita khama kuti akwanitse maudindo ao acikristu. Pofotokoza fanizo lake lothela la nkhosa ndi mbuzi, Yesu analunjika mfundo yake kwa anthu amene ali ndi ciyembekezo ca padziko lapansi. Iye anatsindika mfundo yakuti io ayenela kukhala okhulupilika ndiponso kuthandiza abale a Yesu odzozedwa padziko lapansi. * Tsopano, tiyeni tikambilane fanizo la matalente.

MBUYE APATSA AKAPOLO AKE CUMA

4, 5. Kodi munthu, kapena mbuye amaimila ndani? Nanga talente imodzi inali yoculuka bwanji?

4 Ŵelengani Mateyu 25:14-30. Kwa zaka zambili, zofalitsa zathu zakhala zikufotokoza kuti munthu, kapena mbuye wa m’fanizoli ndi Yesu, ndi kuti anapita ku dziko lakutali pamene anakwela kumwamba mu 33 C.E. M’fanizo lake loyamba, Yesu anakamba kuti colinga cake copitila ku dziko lakutali ndi cakuti “akalandile ufumu.” (Luka 19:12) Yesu sanalandile mphamvu zonse monga mfumu atangofika kumwamba. * M’malo mwake, iye “anakhala pansi kudzanja lamanja la Mulungu. Kuyambila pamenepo, akuyembekezela kufikila pamene adani ake adzaikidwe monga copondapo mapazi ake.”—Aheb. 10:12, 13.

5 Munthu wa m’fanizoli anali ndi matalente 8, cimene cinali cuma cambili panthawiyo. * Iye anagaŵila akapolo ake cuma cake asanapite ku dziko lakutali, ndipo anali kuyembekezela kuti akapolo onse adzagwilitsila nchito cumaco kucita malonda iye akali ku dziko lakutali. Mofanana ndi munthuyo, Yesu asanapite kumwamba, anali ndi cinthu ca mtengo wapatali. Kodi cinali ciani? Yankho la funso limeneli likukhudza nchito imene iye amakonda kwambili.

6, 7. Kodi matalente amaimila ciani?

6 Yesu anali wodzipeleka kwambili panchito yake yolalikila ndi kuphunzitsa. Cifukwa ca nchito yake yolalikila, anthu ambili anakhala ophunzila ake. (Ŵelengani Luka 4:43.) Koma anali kudziŵa kuti panali nchito yaikulu imene inali kufunika kucitidwa, ndi kuti anthu ambili adzalandila uthenga wabwino. Panthawi ina, iye anauza ophunzila ake kuti: “Kwezani maso anu muone m’mindamo, mwayela kale ndipo m’mofunika kukolola.” (Yoh. 4:35-38) Mofanana ndi mlimi wabwino, Yesu sakanasiya munda umene unali kufunika kukololedwa. Ndiye cifukwa cake atangoukitsidwa, koma asanapite kumwamba, iye anapatsa ophunzila ake udindo waukulu. Iye anati: “Conco pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse kuti akhale ophunzila anga.” (Mat. 28:18-20) Mwakutelo, Yesu anapatsa ophunzila ake cuma camtengo wapatali, cimene ndi utumiki wacikristu.—2 Akor. 4:7.

7 Mofanana ndi munthu amene anapatsa akapolo ake ndalama, Yesu anapatsa otsatila ake odzozedwa nchito yopanga ophunzila. (Mat. 25:14) Conco, matalente amaimila nchito yolalikila ndi kupanga ophunzila.

8. Ngakhale kuti kapolo aliyense analandila ciŵelengelo ca matalente cosiyana, kodi mbuye wao anali kufuna ciani?

8 Mogwilizana ndi fanizo la matalente, mbuye anapatsa kapolo woyamba matalente asanu, kapolo waciŵili matalente aŵili, ndipo kapolo wacitatu anam’patsa talente imodzi. (Mat. 25:15) Ngakhale kuti mbuye anapatsa akapolo ciŵelengelo ca matalente cosiyana, iye anali kufuna kuti akapolo onse acite khama pogwilitsila nchito matalentewo. Mofananamo, Yesu anali kufuna kuti otsatila ake odzozedwa azicita khama panchito yolalikila. (Mat. 22:37; Akol. 3:23) Pa Pentekosite mu 33 C.E., otsatila a Yesu anayamba kuphunzitsa anthu a mitundu yonse kukhala ophunzila. Timaona mosavuta mmene anagwilila nchito yolalikila mwakhama tikamaŵelenga buku la Machitidwe m’Baibulo. *Mac. 6:7; 12:24; 19:20.

KUCITA MALONDA NDI MATALENTE M’NTHAWI YA MAPETO

9. (a) Kodi akapolo aŵili okhulupilika anacita ciani ndi matalente? Nanga zimenezo zikusonyeza ciani? (b) Ndi udindo wotani umene a “nkhosa zina” ali nao?

9 M’nthawi ya mapeto, makamaka kuyambila mu 1919, akapolo odzozedwa a Kristu ndiponso okhulupilika padziko lapansi, akhala akucita malonda ndi matalente a Mbuye wao. Mofanana ndi akapolo aŵili oyamba aja, abale ndi alongo odzozedwa akhala akucita khama pa nchito yao yolalikila. Palibe cifukwa cofuna kudziŵila kuti ndani analandila matalente asanu kapena ndani analandila aŵili. M’fanizolo, akapolo onse aŵili anaculukitsa cuma cimene mbuye wao anawasiila. Conco onse aŵili anali a khama. Nanga anthu amene ali ndi ciyembekezo cokhala padziko lapansi ali ndi udindo wotani? Iwo ali ndi udindo wofunika kwambili. Fanizo la Yesu la nkhosa ndi mbuzi limatiphunzitsa kuti amene ali ndi ciyembekezo ca padziko lapansi ali ndi mwai wocilikiza abale odzozedwa a Yesu mokhulupilika panchito yolalikila ndi kuphunzitsa. Mkati mwa masiku ano otsiliza, magulu onse aŵili amagwilila nchito pamodzi yopanga ophunzila mwacangu monga “gulu limodzi.”—Yoh. 10:16.

10. Ndi mbali iti ya cizindikilo imene ikusonyeza kuti tikukhala m’nthawi ya mapeto?

10 Yesu amafuna kuti otsatila ake onse azicita khama kuti aphunzitse anthu ambili kukhala ophunzila. Izi ndi zimene ophunzila ake anacita m’nthawi ya atumwi. Pamene fanizo la Yesu la matalente likukwanilitsidwa nthawi ino ya mapeto, kodi otsatila ake akuigwiladi nchito imeneyi? Inde akuigwila, ndipo masiku ano anthu ambili amva uthenga wabwino ndi kukhala ophunzila kuposa kale. Otsatila a Yesu akugwila nchito imeneyi mwakhama, ndipo pa cifukwa cimeneci, anthu ambilimbili akubatizidwa caka ciliconse. Anthuwo amayamba kugwila nafe nchito yolalikila. Nchito yolalikila komanso zotsatilapo zake zabwino ndi mbali ya cizindikilo cimene Yesu anapeleka cosonyeza kuti tikukhala m’nthawi ya mapeto. Mosakaikila, Yesu ndi wokondwela kwambili ndi anchito ake.

Kristu wapatsa atumiki ake udindo wolalikila umene ndi wamtengo wapatali (Onani ndime 10)

KODI MBUYE ADZABWELA LITI KUDZAŴELENGELA CUMA CAKE?

11. Timadziŵa bwanji kuti Yesu adzabwela pa cisautso cacikulu kudzaŵelengela cuma cake?

11 Yesu adzabwela kudzaŵelengela cuma cake comwe anasiila akapolo ake ku mapeto kwa cisautso cacikulu. Tikudziŵa bwanji zimenezi? Mu ulosi wake wopezeka pa Mateyu caputala 24 ndi 25, Yesu anachula za kubwela kwake mobwelezabweleza. Ponena za ciweluzo cimene cidzacitika mkati mwa cisautso cacikulu, Yesu anakamba kuti anthu “adzaona Mwana wa munthu akubwela pamitambo ya kumwamba.” Iye analimbikitsa otsatila ake amene adzakhala ndi moyo m’masiku otsiliza kuti ayenela kukhala maso pamene anati: “Simukudziŵa tsiku limene Ambuye wanu adzabwele,” ndipo “pa ola limene simukuliganizila, Mwana wa munthu adzabwela.” (Mat. 24:30, 42, 44) Motelo, pamene Yesu anakamba kuti “mbuye wa akapolowo anabwela ndi kuŵelengelana nao ndalama,” iye anali kutanthauza nthawi imene iye adzabwela kuweluza anthu ndi kuononga dziko la Satana. *Mat. 25:19.

12, 13. (a) Kodi mbuye adzauza ciani akapolo aŵili oyamba? Nanga cifukwa ciani? (b) Kodi odzozedwa adzadindidwa liti cidindo cao comaliza? (Muonenso kabokosi ka mutu wakuti “ Aweluzidwa Kukhala Oyenela Akafa.”) (c) Kodi amene anali kucilikiza odzozedwa adzalandila mphoto yotani?

12 Mogwilizana ndi fanizolo, pamene mbuye anabwela, anapeza kuti kapolo amene anapatsidwa matalente asanu, anaonjezelanso ena asanu, ndipo kapolo amene anali ndi matalente aŵili, anaonjezelanso ena aŵili. Mbuye anauza akapolo onse aŵili kuti: “Wacita bwino kwambili, kapolo wabwino ndi wokhulupilika iwe! Unakhulupilika pa zinthu zocepa. Ndikuika kuti udziyang’anila zinthu zambili.” (Mat. 25:21, 23) Kodi Ambuye wathu, Yesu, adzacita ciani akadzabwela mtsogolo?

13 Cisautso cacikulu cikadzatsala pang’ono kuyamba, Mulungu adzadinda cidindo comaliza odzozedwa a khama amene adzakhala akali padziko lapansi. (Chiv. 7:1-3) Kenako, Aramagedo isanacitike, Yesu adzawapatsa mphoto yao ya kumwamba. Nanga bwanji za amene ali ndi ciyembekezo codzakhala padziko lapansi, amene anacilikiza odzozedwa pa nchito yolalikila? Iwo adzakhala ataweluzidwa kuti ndi nkhosa, ndipo adzapatsidwa mphoto yokhala ndi moyo padziko lapansi mu ulamulilo wa Ufumu wa Mulungu.—Mat. 25:34.

KAPOLO WOIPA NDI WAULESI

14, 15. Kodi Yesu anali kutanthauza kuti abale ake ambili odzozedwa adzakhala oipa ndi aulesi? Fotokozani.

14 M’fanizoli, mulinso kapolo amene anali ndi talente imodzi. Iye sanaigwilitsile nchito kuti aonjezele ndalama za mbuye wake, kapena kuisungitsa kwa osunga ndalama kuti apeze ciongoladzanja. M’malo mwake, iye anabisa talente yake pansi. Mbuye anakamba kuti kapoloyo anali “woipa ndi waulesi.” Mbuyeyo analanda kapolo woipa talente yake ndi kupatsa kapolo woyamba. Ndiyeno anaponya kapolo woipa uja “kunja kumdima,” ndipo kumeneko analila ndi kukukuta mano.—Mat. 25:24-30; Luka 19:22, 23.

15 Pamene Yesu anakamba kuti kapolo mmodzi pa akapolo atatu aja anali woipa ndi waulesi, iye sanali kutanthauza kuti odzozedwa ena adzakhala monga kapolo ameneyo. Timadziŵa zimenezo tikafananitsa fanizoli ndi mafanizo ena aŵili. M’fanizo la kapolo wokhulupilika ndi wanzelu, Yesu anachula za kapolo woipa amene anali kuzunza akapolo anzake. M’fanizoli, Yesu sanali kutanthauza kuti ena amene ali m’gulu la kapolo wokhulupilika ndi wanzelu adzakhala oipa. M’malo mwake, iye anali kucenjeza odzozedwa kuti sayenela kukhala ngati kapolo woipa. Kenako m’fanizo la anamwali 10, Yesu anakamba kuti anamwali asanu anali opusa. Pochula mfundo imeneyi, Yesu sanali kutanthauza kuti hafu ya odzozedwa adzakhala opusa. M’malo mwake, Yesu anali kuwacenjeza za zimene zingadzawacitikile ngati angalephele kukhala okonzeka ndi kukhala maso. * Mofananamo, pofotokoza fanizo la matalente, Yesu sanali kutanthauza kuti odzozedwa ambili m’masiku otsiliza adzakhala oipa ndi aulesi. Koma iye anali kucenjeza otsatila ake odzozedwa kuti afunika kupitiliza kucita khama kapena ‘kucita malonda ndi matalente ao’ ndi kupewa kukhala monga kapolo woipa.—Mat. 25:16.

16. (a) Ndi mfundo ziŵili ziti zimene tikuphunzila m’fanizo la matalente? (b) Kodi nkhani ino yatithandiza bwanji kumvetsa fanizo la matalente? (Onani bokosi la mutu wakuti, “ Kumvetsa Fanizo la Matalente”)

16 Ndi mfundo ziŵili ziti zimene tikuphunzila m’fanizo la matalente? Mfundo yoyamba ndi yakuti Yesu anapatsa ophunzila ake odzozedwa udindo wofunika kwambili wolalikila ndi kuphunzitsa anthu kuti akhale ophunzila. Udindowu uli ngati cuma camtengo wapatali. Mfundo yaciŵili ndi yakuti, Yesu amafuna kuti tonse tizicita khama pogwila nchito yolalikila. Tikamagwila nchito imeneyi mwakhama ndi kukhalabe omvela ndi okhulupilika kwa Yesu, iye adzatifupadi.—Mat. 25:21, 23, 34.

^ par. 3 Nsanja ya Mlonda ya July 1, 2013, tsamba 28, ndime 8-10 inafotokoza yemwe ali kapolo wokhulupilika ndi wanzelu. Nkhani yapita m’magazini ino inafotokoza kuti anamwali amaimila ndani. Fanizo la nkhosa ndi mbuzi linafotokozedwa mu Nsanja ya Olonda ya October 15, 1995, tsamba 23 mpaka 28 ndiponso mu nkhani yotsatila m’magazini ino.

^ par. 5 M’nthawi ya Yesu, talente imodzi inali kulemela madinari pafupifupi 6,000. Ngati wanchito wamba anali kulandila dinari imodzi patsiku, ndiye kuti akanafunika kugwila nchito zaka 20 kuti alandile talente imodzi.

^ par. 8 Pambuyo poti atumwi afa, mpatuko unafalikila mumipingo yonse. Kwa zaka zambili, nchito yolalikila sinali kugwilidwa mwakhama. Koma mkati mwa nthawi “yokolola” kapena kuti nthawi ya mapeto, nchito yolalikila inali kudzayambanso kugwilidwa mwakhama. (Mat. 13:24-30, 36-43) Onani Nsanja ya Mlonda ya July 1, 2013, tsamba 15-18.

^ par. 11 Onani Nsanja ya Mlonda ya July 1, 2013, tsamba 13-14, ndime 14-18.

^ par. 15 Onani ndime 13 m’nkhani yakuti: “Kodi ‘Mudzakhalabe Maso’?” yomwe ili m’magazini ino.