Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Mmene Akulu Angathandizile Ena Kukhala Oyenelela Maudindo

Mmene Akulu Angathandizile Ena Kukhala Oyenelela Maudindo

“Zinthu zimene unazimva kwa ine . . . , uziphunzitse kwa anthu okhulupilika.”—2 TIM. 2:2.

1. (a) Kuyambila kale, n’ciani cimene atumiki a Mulungu amadziŵa pankhani yophunzitsa ena? Nanga zimenezi zikugwila nchito bwanji masiku ano? (b) Tikambilana ciani m’nkhani ino?

KUYAMBILA kalekale atumiki a Mulungu akhala akudziŵa kuti kuphunzila kumapindulitsa. Mwacitsanzo, Abulamu “anasonkhanitsa anyamata ake odziŵa kumenya nkhondo” kuti akapulumutse Loti, ndipo anyamatawo anapambana. (Gen. 14:14-16) M’nthawi ya Mfumu Davide anthu amene anali kuimba pa nyumba ya Mulungu ‘anaphunzitsidwa kuimba’ nyimbo zotamanda Yehova. (1 Mbiri 25:7) Masiku ano, tikumenya nkhondo yakuuzimu yolimbana ndi Satana ndi otsatila ake. (Aef. 6:11-13) Ndiponso timacita zilizonse zimene tingathe kuti titamande Yehova mwa zocita zathu. (Aheb. 13:15,16) Conco mofanana ndi atumiki a Mulungu akale, nafenso tiyenela kuphunzitsidwa kuti titamande Mulungu mwa zocita zathu ndi kupambana pa nkhondo yathu yakuuzimu. Ndiye cifukwa cake Yehova wapatsa akulu udindo wophunzitsa ena mumpingo. (2 Tim. 2:2) Ndi njila zotani zimene akulu aluso amagwilitsila nchito pophunzitsa abale kuti ayenelele kusamalila nkhosa?

THANDIZANI WOPHUNZILA KUKULA MWAKUUZIMU

2. N’ciani cimene mkulu angacite asanaphunzitse m’bale maluso enaake? Nanga n’cifukwa ciani?

2 Monga mkulu, mungayelekezedwe ndi mlimi. Asanabyale mbeu mlimi amaona ngati n’kofunika kuthila manyowa m’nthaka kuti akolole zambili. Mofanana ndi zimenezi, musanaphunzitse m’bale maluso enaake, mungacite bwino kukambilana naye mfundo zolimbikitsa za m’Malemba. Kucita zimenezi kungamuthandize kukhala wokonzeka kumvetsela malangizo amene mudzamupatse.—1 Tim. 4:6.

3. (a) Kodi mau a Yesu opezeka pa Maliko 12:29, 30 angagwilitsidwe nchito bwanji pokambilana ndi wophunzila? (b) Nanga pemphelo limene mkulu angapeleke lingamukhudze bwanji wophunzila?

3 Kuti mudziŵe mmene coonadi ca Ufumu casinthila maganizo ndi zocita za wophunzila, mungamufunse kuti, ‘Kodi kudzipeleka kwanu kwa Yehova kwakhudza bwanji mmene mumagwilitsila nchito moyo wanu?’ Kufunsa funso limeneli kungamuthandize kudziŵa zimene angacite kuti atumikile Mulungu ndi mtima wonse. (Ŵelengani Maliko 12:29, 30) Mwina pambuyo pokambilana mungapeleke pemphelo, ndi kupempha Yehova kuti apatse wophunzilayo mzimu woyela kuti umuthandize kugwilitsila nchito zimene adzaphunzila. Kunena zoona m’baleyo adzalimbikitsidwa kwambili ndi pemphelo lanu locokela pansi pamtima.

4. (a) Pelekani zitsanzo za m’Baibulo zimene zingalimbikitse wophunzila kuti akule mwakuuzimu. (b) Kodi akulu amakhala ndi colinga cotani akamaphunzitsa ena?

4 Paciyambi pa maphunzilo anu, muzikambilana zocitika za m’Baibulo zimene zingathandize wophunzila kuona ubwino wokhala wodzipeleka, wodalilika ndiponso wodzicepetsa. (1 Maf. 19:19-21; Neh. 7:2; 13:13; Mac. 18:24-26) Makhalidwe amenewa ndi ofunika kwambili kwa ophunzila mofanana ndi manyowa m’nthaka, cifukwa amacititsa munthu kukula msanga mwakuuzimu. Mkulu wina wa ku France dzina lake Jean-Claude anati: “Ndikamaphunzitsa wophunzila, colinga canga cimakhala kumuthandiza kukonda zinthu zakuuzimu. Ndimayesetsa kupeza nthawi yoyenela yakuti tiŵelengele pamodzi lemba lina lake kuti ndimuthandize ‘kutsegula maso ake ndi kuona zinthu zodabwitsa’ zopezeka m’mau a Mulungu.’ (Sal. 119:18) Ndi njila zina ziti zimene mungagwilitsile nchito pothandiza wophunzila?

MUUZENI ZOLINGA ZIMENE ANGASANKHE NDI CIFUKWA CAKE

5. (a) Kodi kukamba ndi wophunzila nkhani ya zolinga za kuuzimu kuli ndi ubwino wotani? (b) N’cifukwa ciani akulu ayenela kuphunzitsa abale acinyamata? (Onani mau a munsi.)

5 Funsani wophunzila kuti, ‘Ndi zolinga zotani zimene muli nazo?’ Ngati alibe zolinga zenizeni muthandizeni kupanga zolinga zabwino zimene angakwanitse. Muuzeni colinga cimene munali naco, ndipo mufotokozeleni mogwila mtima cisangalalo cimene munapeza mutakwanilitsa colingaco. Njila imeneyi ingaoneke yosafunika kwenikweni, koma ndi yothandiza kwambili. Mkulu wina amenenso ndi mpainiya dzina lake Victor anati: “Pamene ndinali wacinyamata mkulu wina anandifunsa mafunso ocepa ndiponso osankhidwa bwino okhudza zolinga zanga. Mafunsowo anandicititsa kuyamba kuganizila kwambili za utumiki wanga.” Akulu aluso amaonanso kuti n’kofunika kuyamba kuphunzitsa abale acinyamata mwa kuwapatsa zocita mumpingo molingana ndi msinkhu wao. Maphunzilo amenewo adzathandiza acinyamata kuikabe maganizo ao pa zinthu za kuuzimu makamaka akamakula ndi kukumana ndi zoceukitsa.—Ŵelengani Salimo 71:5,17. *

Fotokozelani wophunzila cifukwa cake afunika kucita zimene mwam’pempha, ndipo muyamikileni cifukwa ca khama lake poyesetsa kucita zimenezo. (Onani ndime 5 mpaka 8)

6. Ndi mbali iti imene inali yofunika kwambili kwa Yesu pophunzitsa?

6 Simuyenela kungomuuza zimene afunika kucita koma muyenela kumuuzanso cifukwa cake ayenela kucita zimenezo. Mukatelo mudzathandiza wophunzila kukhala wofunitsitsa kutumikila Mulungu, ndipo mudzaonetsa kuti mumatsatila Yesu, Mphunzitsi Wamkulu. Mwacitsanzo asanapatse atumwi ake nchito yopanga ophunzila, Yesu anawauza cifukwa cake anafunika kugwila nchito imeneyo. Iye anati: “Ulamulilo wonse wapelekedwa kwa ine kumwamba ndi padziko lapansi.” Ndipo anaonjezela kuti: “Conco pitani mukaphunzitse anthu a mitundu yonse.” (Mat. 28:18, 19) Kodi mungatsatile bwanji kaphunzitsidwe ka Yesu?

7, 8. (a) Kodi akulu angatsanzile bwanji kaphunzitsidwe ka Yesu? (b) N’cifukwa ciani kuyamikila wophunzila n’kofunika? (c) Ndi malangizo ati amene akulu angagwilitsile nchito pophunzitsa ena? (Onani bokosi lakuti “ Mmene Tingaphunzitsile Ena.”)

7 Fotokozelani wophunzila cifukwa ca m’Malemba pa zimene mwamupempha kucita. Mwa njila imeneyo mudzamuthandiza kugwilitsila nchito mfundo za m’Baibulo. Tiyelekeze kuti mwapempha m’bale kuti ayeletse pakhomo la nyumba ya Ufumu ndi kukonza zinthu zimene zingapangitse ngozi. Mungaŵelenge naye lemba la Tito 2:10 ndi kumufotokozela kuti Nyumba ya Ufumu ifunika kukhala yaukhondo n’colinga cakuti ‘ikometsele ciphunzitso ca Mpulumutsi wathu Mulungu.’ Mungamuthandizenso kuganizila mmene kucita zimenezi kudzapindulitsila okalamba. Kukambilana zinthu ngati zimenezi kudzathandiza wophunzila kuti asamangoganizila za nchito yake koma aziganizila kwambili mmene anthu ena angapindulile ndi nchitoyo. Adzakhala wosangalala kuona mmene nchito yake yapindulitsila abale ndi alongo mumpingo.

8 Kuonjezela apo, onetsetsani kuti mukuyamikila wophunzilayo cifukwa ca khama lake poyesetsa kutsatila zimene munamuuza kucita. N’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika? Monga mmene madzi amathandizila mbeu kukula bwino, kuyamikila wophunzila mocokela pansi pa mtima kudzamuthandiza kukula mwakuuzimu.—Yelekezelani ndi Mateyu 3:17.

VUTO LINA

9. (a) Pankhani yophunzitsa ena, ndi vuto liti limene akulu akukumana nalo m’maiko olemela? (b) N’cifukwa ciani acinyamata ena sanaike coonadi patsogolo m’moyo wao?

9 M’maiko olemela, akulu akukumana ndi vuto lina la mmene angathandizile abale obatizidwa a zaka za m’ma 20 kapena za m’ma 30 kutengako mbali m’nchito za mumpingo. Tinafunsa akulu amene atumikila kwa zaka zambili ocokela m’maiko 20 a azungu kuti atiuze cifukwa cake abale acinyamata amakana maudindo mumpingo. Yankho limene ambili anapeleka ndi lakuti acinyamata ena pamene anali ana sanali kulimbikitsidwa kukhala ndi zolinga za kuuzimu. Ndiponso acinyamata ena anali kufuna kukhala ndi zolinga za kuuzimu, koma makolo ao anawalimbikitsa kucita maphunzilo apamwamba. Conco pamene anali acinyamata, io sanaphunzitsidwe kuika coonadi patsogolo m’moyo wao.—Mat. 10:24.

10, 11. (a) Kodi mkulu angathandize bwanji m’bale amene aoneka kuti safuna kukalamila maudindo? (b) Ndi mfundo za m’Malemba ziti zimene mkulu angakambilane ndi m’bale amene safuna kukalamila maudindo? Nanga n’cifukwa ciani? (Onani mau a munsi.)

10 Ngati m’bale aoneka kuti safuna kukalamila maudindo, n’zotheka kumuthandiza kusintha maganizo koma pamafunika khama ndi kuleza mtima. Monga mmene mlimi amaongolela mbeu zimene zapindika cifukwa ca cimphepo, inunso mungathandize abale ena kusintha maganizo kuti ayambe kukalamila maudindo mumpingo. Kodi mungacite bwanji zimenezi?

11 Coyamba yesetsani kukhala naye paubwenzi m’baleyo. Muthandizeni kudziŵa kuti ndi wofunika kwambili mumpingo. Ndiyeno, m’kupita kwa nthawi kambilanani naye malemba ena ndi kumuthandiza kuganizila kwambili za kudzipeleka kwake kwa Yehova. (Mlal. 5:4; Yes. 6:8; Mat. 6:24, 33; Luka 9:57-62; 1 Akor. 15:58; 2 Akor. 5:15; 13:5) Mwina mungamufunse kuti: ‘Kodi munamulonjeza ciani Mulungu pamene munadzipeleka kwa iye?’ Yesani kumufunsa funso lokhudza mtima lakuti: ‘Muganiza kuti Yehova anamva bwanji pamene munabatizidwa?’ (Miy. 27:11) ‘Nanga Satana anamva bwanji? (1 Pet. 5:8) Dziŵani kuti m’bale angakhudzidwe kwambili ndi Malemba osankhidwa bwino amene mungaŵelenge naye.—Ŵelengani Aheberi 4:12. *

OPHUNZILA, KHALANI OKHULUPILIKA

12, 13. (a) Monga wophunzila, ndi mtima wotani umene Elisa anali nao? (b) Kodi Yehova anadalitsa bwanji Elisa cifukwa cokhala wokhulupilika?

12 Nanga bwanji inu acinyamata amene mufunika kuthandiza mpingo? Ndi mtima wotani umene muyenela kukhala nao kuti muyenelele maudindo? Kuti tiyankhe funso limeneli, tiyeni tikambilane citsanzo ca wophunzila wina wakale.

13 Pafupifupi zaka 3,000 zapitazo, mneneli Eliya anaitana Elisa amene anali wacinyamata kuti akhale mtumiki wake. Mwamsanga, Elisa anavomela ndipo anayamba kutumikila Eliya wokalambayo mokhulupilika mwa kugwila nchito zooneka ngati zotsika. (2 Maf. 3:11) Elisa ataphunzitsidwa kwa zaka 6 anazindikila kuti nchito ya Eliya mu Isiraeli inali pafupi kutha. Ndiyeno Eliya anauza mtumiki wake wophunzitsidwa bwino ameneyu kuti aleke kumutsatila, koma Elisa anamuuza katatu konse kuti: “Sindikusiyani.” Iye anali wofunitsitsa kukhalabe ndi mphunzitsi wake mulimonse mmene zikanakhalila. Motelo Yehova anadalitsa Elisa cifukwa ca kukhulupilika kwake mwa kumulola kuona zimene zinacitika pamene Eliya anatengedwa modabwitsa.—2 Maf. 2:1-12.

14. (a) Kodi ophunzila masiku ano angatsanzile bwanji Elisa? (b) N’cifukwa ciani wophunzila afunika kukhala wokhulupilika?

14 Kodi mungatsanzile bwanji Elisa masiku ano? Mukapatsidwa zocita, muzivomela mwamsanga ngakhale zioneke kuti ndi zotsika. Muziona aphunzitsi anu ngati bwenzi lanu ndipo muzionetsa kuti mumayamikila kuyesayesa kwao pokuthandizani. Mukamatelo mumakhala ngati mukuwauza kuti “sindikusiyani”. Koposa zonse, muzigwila mokhulupilika nchito iliyonse imene mwapatsidwa. N’cifukwa ciani kucita zimenezi n’kofunika? Cifukwa cakuti mukamaonetsa kuti ndinu okhulupilika ndiponso odalilika, akulu adzadziŵa kuti Yehova afuna kukupatsani maudindo ena oonjezeleka mumpingo.—Sal. 101:6; ŵelengani 2 Timoteyo. 2:2.

MUZISONYEZA ULEMU

15, 16. (a) Kodi Elisa anasonyeza bwanji ulemu kwa mphunzitsi wake? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.) (b) Kodi Elisa anacita ciani cimene cinapangitsa kuti aneneli anzake ayambe kumudalila?

15 Cocitika ca Elisa amene analowa m’malo Eliya cimaonetsanso mmene abale masiku ano angasonyezele ulemu kwa akulu amene atumikila kwa zaka zambili. Pambuyo pocezela aneneli a ku Yeriko, Eliya ndi Elisa anapita kumtsinje wa Yorodano. Atafika kumeneko, “Eliya anatenga covala cake cauneneli n’kucipinda. Atatelo anamenya naco madzi a mtsinjewo, ndipo pang’onopang’ono madzi onsewo anagawanika.” Atadutsa panthaka youma pakati pa mtsinje wa Yorodano, io anapitiliza ‘kuyenda akumalankhulana.’ N’zoonekelatu kuti Elisa sanaganize kuti tsopano wadziŵa zonse. Elisa anapitiliza kusunga zonse zimene mphunzitsi wake, Eliya, anamuuza mpaka pamene Eliyayo anacoka. Kenako Eliya anatengedwa mumphepo yamkuntho. Patapita nthawi, Elisa anabwelela ku mtsinje wa Yorodano ndipo anatenga covala cauneneli ca Eliya n’kumenya madzi a mtsinjewo, n’kunena kuti: “Ali kuti Yehova Mulungu wa Eliya?” Ndiyeno, madziwo anayambanso kugawanika.—2 Maf. 2:8-14.

16 Kodi mwaona kuti cozizwitsa comaliza cimene Eliya anacita ndiye cinali cozizwitsa coyamba cimene Elisa anacita? N’cifukwa ciani zimenezi n’zocititsa cidwi? Mwacionekele, Elisa sanadzimve kuti popeza kuti iye tsopano ndiye anali mtsogoleli anafunika kusintha zinthu mwamsanga. M’malomwake, iye anaonetsa ulemu kwa Eliya mwa kupitiliza kucita zinthu mmene Eliya anali kucitila, ndipo zimenezi zinathandiza kuti aneneli anzake ayambe kumudalila. (2 Maf. 2:15) Mkati mwa utumiki wake wa zaka 60 monga mneneli, Yehova anathandiza Elisa kucita zozizwitsa zambili kuposa zimene Eliya anacita. Kodi ophunzila masiku ano mukutengapo phunzilo lotani?

17. (a) Kodi ophunzila angatengele bwanji citsanzo ca Elisa masiku ano? (b) M’kupita kwa nthawi, kodi Yehova angagwilitsile nchito bwanji ophunzila okhulupilika?

17 Mukangolandila maudindo mumpingo musaganize kuti tsopano mufunika kusintha zinthu zonse. Musasinthe zinthu cifukwa cofuna kungotsatila zofuna zanu koma cifukwa cofuna kusamalila bwino mpingo ndi kutsatila malangizo amene gulu la Yehova limapeleka. Elisa anaonetsa ulemu kwa Eliya mwa kupitiliza kucita zinthu zimene Eliya anali kucita, ndipo izi zinacititsa kuti aneneli anzake ayambe kum’dalila. Inunso ophunzila muyenela kusonyeza ulemu kwa akulu amene atumikila kwa zaka zambili mwa kupitiliza kutsatila njila za m’Malemba zimene anali kugwilitsila nchito. Mukatelo, abale ndi alongo mumpingo adzayamba kukudalilani. (Ŵelengani 1 Akorinto 4:17.) Komabe, pamene mukukulitsa luso pa udindo wanu, mosakaikila mungathandize kusintha zinthu zina mumpingo kuti uziyendela limodzi ndi gulu la Yehova. Ndipo monga mmene zinalili ndi Elisa, inu ophunzila okhulupilika, Yehova angakuthandizeni kucita zinthu zazikulu kuposa aphunzitsi anu.—Yoh. 14:12.

18. N’cifukwa ciani kuphunzitsa abale mumpingo n’kofunika kwambili masiku ano?

18 Tikukhulupilila kuti malangizo amene takambilana m’nkhani ino ndi m’nkhani yapita, athandize akulu kupeza nthawi yophunzitsa ena. Tikupemphanso abale onse amene angayenelele maudindo kuti akhale ofunitsitsa kuphunzila ndi kugwilitsa nchito zimene aphunzitsidwa pothandiza kusamalila nkhosa za Yehova. Kucita izi kudzalimbitsa mipingo yonse padziko lapansi ndi kuthandiza aliyense wa ife kukhala okhulupilika makamaka pa nthawi yapadela imene ikubwela.

^ par. 5 Ngati m’bale wacinyamata akuonetsa kukula mwakuuzimu, ndipo ndi wodzicepetsa komanso akukwanilitsa ziyeneletso zina za m’Malemba, akulu angamuyamikile kuti aikidwe kukhala mtumiki wothandiza ngakhale kuti sanakwanitse zaka 20 zakubadwa.—1 Tim. 3:8-10, 12; onani Nsanja ya Olonda ya July 1, 1989, tsamba 29.

^ par. 11 Mukamakambilana mungagwilitsile nchito mfundo zopezeka mu Nsanja ya Olonda ya April 15, 2012, tsamba 14 mpaka 16, ndime 8 mpaka 13; ndi buku lakuti: “Khalanibe M’cikondi ca Mulungu,” nkhani  16, ndime 1 mpaka 3.