Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | KODI MAPETO A DZIKOLI ALI PAFUPI?

Ambili Adzapulumuka—Nanga Bwanji Inuyo?

Ambili Adzapulumuka—Nanga Bwanji Inuyo?

Baibulo limatiuza kuti mapeto adzaphatikizapo cionongeko. Ilo limati: “Pa nthawiyo kudzakhala cisautso cacikulu cimene sicinacitikepo kucokela pa ciyambi ca dziko mpaka tsopano . . . Kunena zoona, masikuwo akanapanda kufupikitsidwa, palibe amene akanapulumuka.” (Mateyu 24:21, 22) Ndipo Mulungu amatilonjeza kuti ambili adzapulumuka. Baibulo limati: “Dziko likupita . . . , koma wocita cifunilo ca Mulungu adzakhala kosatha.”—1 Yohane 2:17.

Kodi mungatani kuti mudzapulumuke ndi ‘kukhala kosatha’ pamene dzikoli lizidzaonongedwa? Kodi mufunika kuyamba kusunga zinthu kapena kudzikonzekeletsa mwa kuthupi? Ai. Baibulo limatiuza kuti tifunika kucita zinthu zina zofunika kwambili. Limati: “Popeza zinthu zonsezi zidzasungunuka, ganizilani za mtundu wa munthu amene muyenela kukhala. Muyenela kukhala anthu akhalidwe loyela ndipo muzicita nchito zosonyeza kuti ndinu odzipeleka kwa Mulungu. Muzicita zimenezi poyembekezela ndi kukumbukila nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.” (2 Petulo 3:10-12) Malinga ndi mmene nkhaniyi ikuonetsela, “zinthu zonsezi” zimene zidzasungunuka zikuphatikizapo olamulila a dziko loipali ndiponso anthu amene amasankha ulamulilowo m’malo mwa ulamulilo wa Mulungu. Apa n’zoonekelatu kuti kusunga cuma kapena zinthu za kuthupi sikungatipulumutse.

Conco, kuti tikapulumuke tifunika kukhala odzipeleka kwa Yehova Mulungu, kukhala ndi makhalidwe abwino ndiponso kucita zinthu zimene iye amakondwela nazo. (Zefaniya 2:3) Motelo, sitifunika kutsatila gulu la anthu ndi kunyalanyaza zizindikilo zoonetsa kuti tili m’masiku otsiliza, m’malomwake ‘tizikumbukila nthawi zonse kukhalapo kwa tsiku la Yehova.’ Mwa kugwilitsila nchito Baibulo, Mboni za Yehova zingakuthandizeni kudziŵa zimene mungacite kuti mukapulumuke pa tsiku limenelo.