Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

KALE LATHU

Zinthu Zinkayenda Bwino Chifukwa cha Chikondi

Zinthu Zinkayenda Bwino Chifukwa cha Chikondi

TIMASANGALALA kwambiri pa misonkhano yathu. Timasonkhana pamodzi kuti tiphunzitsidwe ndi Yehova ndipo chakudya chimene timadya chimangowonjezera chisangalalo chathu.

Mu September 1919, Ophunzira Baibulo anachita msonkhano wa masiku 8 mumzinda wa Cedar Point ku Ohio, m’dziko la United States. Alendo anafunika kugona ndiponso kudya m’mahotela, koma kunabwera anthu ambiri zedi kuposa amene anaitanidwa. Zimenezi zinachititsa kuti ogawa chakudya anyanyale ntchito yawo. Ndiyeno woyang’anira zakudya anapempha abale achinyamata kuti athandize kugawa chakudya ndipo ambiri anavomera. Mlongo wina dzina lake Sadie Green anali m’gululo ndipo anati: “Kanali koyamba kugwira ntchito yogawa chakudya. Koma tinasangalala kwambiri.”

Ku Sierra Leone mu 1982

M’zaka zotsatira abale ndi alongo ambiri anali ndi mwayi wogwira ntchito yophika ndiponso kugawira anthu chakudya pa misonkhano. Izi zinathandiza achinyamata ambiri kuganizira zowonjezera utumiki wawo. Mlongo Gladys Bolton, anagwira ntchito yogawa chakudya pa msonkhano wachigawo mu 1937 ndipo iye anati: “Ndinakumana ndi anthu ochokera m’madera osiyanasiyana ndipo ankandifotokozera mmene akupirira mavuto awo. Zimenezi zinandipangitsa kuti ndifune kuyamba upainiya.”

Mlongo Beulah Covey anati: “Popeza abalewo ankagwira ntchito mwakhama, zinthu zinkayenda mofulumira zedi.” Koma ntchitoyi inali ndi mavuto ake. M’bale Angelo Manera anachita nawo msonkhano ku Los Angeles mu 1969. Iye atangofika ku msonkhanowu anauzidwa kuti aziyang’anira ntchito yokonza ndi kugawa chakudya. Iye anati: “Ndinadabwa kwambiri.” Kuti ntchitoyi iyende bwino panafunika kukumba ngalande yotalika mamita 400 kuti tidutsitsemo mapaipi a gasi wophikira.

Ku Frankfurt m’dziko la Germany mu 1951

Mu 1982, abale ongodzipereka anagwira ntchito yolambula malo ochitirapo msonkhano ku Sierra Leone ndiponso anamanga khitchini. Mu 1951 mumzinda wa Frankfurt ku Germany, abale ankagwiritsa ntchito mpweya wotentha wochokera musitima kuti aphikire zinthu m’mapoto okwana 40. Mbale za chakudya zokwana 30,000 zinkagawidwa pa ola. Pofuna kuchepetsa ntchito ya abale 576 otsuka mbale, abale ankapemphedwa kuti pobwera azitenga mipeni ndiponso mafoloko awo. Abale ophika pa msonkhano wa ku Yangon m’dziko la Myanmar ankaganizira alendo ochokera kumayiko ena ndipo sankaika tsabola wambiri m’chakudya chawo.

“AMADYA CHOIMIRIRA”

Mu 1950, mlongo wina dzina lake Annie Poggensee, anapita ku msonkhano ku United States. Iye anaima pamzere kwa nthawi yaitali koma anaona kuti umenewu unali mwayi wake. Iye anati: “Ndinkacheza ndi alongo awiri a ku Ulaya amene anabwera pa boti.” Aliyense ananena mmene Yehova anamuthandizira kuti apezeke pa msonkhanowo. Annie anati: “Alongowo anali osangalala kuposa aliyense pa msonkhanowo. N’zoona kuti tinaima kwanthawi yaitali ndipo kunkatentha koma zonsezi sizinali vuto kwa iwo.”

Ku Seoul, m’dziko la Korea mu 1963

M’malo ambiri a misonkhano, munkaikidwa matebulo ataliatali kuti athu azidya choimirira. Izi zinkathandiza kuti adye mwamsanga n’kupereka mpata kwa anzawo kuti adyenso. Njira imeneyi inathandiza kuti anthu masauzande ambiri adye nthawi yopuma isanathe. Munthu wina yemwe sanali Mboni anati: “Chipembedzo ichi n’chodabwitsa kwambiri. Eti anthu ake amadya choimirira.”

Ngakhale akuluakulu a boma ndiponso asilikali anachita chidwi ndi mmene zinthu zinkayendera. Mkulu wa asilikali a ku United States anafika pa msonkhano wa ku Yankee Stadium mumzinda wa New York ndipo analimbikitsa mkulu wa asilikali a ku Britain kuti adzaone zimene abalewo ankachita. Iye anamvera n’kupita pa msonkhano wina umene unachitika mu 1955 ku England. Ataona zimene zinkachitika, ananena kuti zinthu zinkayenda bwino chifukwa cha chikondi.

Kwa zaka zambiri abale ndi alongo ankapemphedwa kugwira ntchito yopereka chakudya kwa anthu pa msonkhano. Koma izi zinkachititsa kuti anthu ena agwire ntchito kwa maola ambiri ndipo ena analibe mpata womvetsera msonkhano wonse. Choncho pofika m’ma 1970, zinthu zinasintha m’mayiko ambiri kuti pasamakhale ntchito yaikulu. Pofika mu 1995, anthu anayamba kuuzidwa kuti azitenga chakudya chawo popita ku msonkhano. Izi zachepetsa ntchito komanso zathandiza kuti aliyense azisangalala ndi msonkhano komanso kucheza ndi Akhristu anzake. *

Yehova amayamikira kwambiri anthu amene amadzipereka kuti athandize anzawo. Anthu ena amalakalakabe atamagwira ntchito yoperekera chakudya pa msonkhano. Koma mfundo ndi yakuti: Chikondi chimaonekerabe pa misonkhano yathu.—Yoh. 13:34, 35.

^ ndime 12 Koma pali ntchito zina m’madipatimenti a pa msonkhano zofunika kuti anthu azidziperekabe n’kuzigwira.