Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizichita Zinthu Mogwirizana ndi Pemphero la Ambuye—Gawo 1

Tizichita Zinthu Mogwirizana ndi Pemphero la Ambuye—Gawo 1

“Dzina lanu liyeretsedwe.”—MAT. 6:9.

1. Kodi pemphero la pa Mateyu 6:9-13 timaligwiritsa ntchito bwanji mu utumiki?

ANTHU ambiri amadziwa bwino mawu a m’pemphero la Ambuye. Tikamalalikira timakonda kugwiritsa ntchito pempheroli pothandiza anthu kudziwa kuti Ufumu wa Mulungu ndi boma limene lidzathetse mavuto padzikoli. Nthawi zina timagwiritsa ntchito pempheroli pothandiza anthu kudziwa kuti Mulungu ali ndi dzina ndipo liyenera kuyeretsedwa.—Mat. 6:9.

2. Kodi tikudziwa bwanji kuti Yesu sankafuna kuti popemphera tizinena mawu a mu pemphero la Ambuye ndendende?

2 Kodi Yesu ankatanthauza kuti tiyenera kuloweza pempheroli n’kumatchula mawu ake ndendende tikamapemphera? Ayi. Tikutero chifukwa chakuti asananene pempheroli ananena kuti: “Iwe popemphera, usanene zinthu mobwerezabwereza.” (Mat. 6:7) Pa nthawi ina, ananenanso pempheroli koma anasintha mawu ena. (Luka 11:1-4) Choncho Yesu ankangofuna kutithandiza kudziwa zimene tingatchule m’pemphero. M’pake kuti pempheroli limatchedwanso kuti pemphero lachitsanzo.

3. Kodi tiyenera kudzifunsa mafunso ati tikamakambirana nkhaniyi?

3 M’nkhaniyi ndiponso yotsatira, tikambirana zinthu zina zotchulidwa m’pemphero lachitsanzo. Tikamakambirana nkhanizi, tizidzifunsa mafunso awa: ‘Kodi pempheroli lingandithandize bwanji kuti mapemphero anga azikhala abwino? Kodi ndikuchita zinthu mogwirizana ndi pemphero limeneli?’

“ATATE WATHU WAKUMWAMBA”

4. (a) Kodi mawu akuti “Atate wathu” akutikumbutsa za chiyani? (b) N’chifukwa chiyani tinganene kuti Yehova ndi “Atate” wa anthu amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi?

4 Yesu anayamba pempheroli ndi mawu akuti “Atate wathu” osati “Atate wanga.” Zimenezi zikutikumbutsa kuti tili m’gulu la abale ambiri omwe amakondana. (1 Pet. 2:17) Umenewutu ndi mwayi waukulu kwambiri. Akhristu ena asankhidwa ndi Mulungu kuti akhale ana ake ndiponso kuti apite kumwamba. Iwo ndi oyenereradi kunena kuti Yehova ndi “Atate” wawo. (Aroma 8:15-17) Koma Akhristu amene akuyembekezera kudzakhala padzikoli anganenenso kuti Yehova ndi “Atate” wawo. Tikutero chifukwa chakuti Yehova ndi amene anawapatsa moyo ndipo amawapatsanso zinthu zonse zofunika. M’tsogolomu, iwonso adzakhala ana enieni a Mulungu. Izi zidzachitika akadzakhala angwiro komanso akadzadutsa bwinobwino mayesero omaliza.—Aroma 8:21; Chiv. 20:7, 8.

5, 6. (a) Kodi makolo ayenera kuthandiza bwanji ana awo? (b) Kodi ana ali ndi udindo wotani? (Onani chithunzi patsamba 20.)

5 Makolo ayenera kuphunzitsa ana awo kupemphera ndiponso kuwathandiza kuona kuti Yehova ndi Atate wawo wachikondi kwambiri. M’bale wina amene panopa ndi woyang’anira dera ku South Africa anati: “Kuyambira pamene ana athu anabadwa, ndinkapemphera nawo usiku uliwonse ndikakhala pakhomo. Ana athu amanena kuti sakumbukira bwinobwino mawu amene ndinkanena m’mapempherowo. Koma amakumbukira kuti pamene tinkapemphera, mtima wawo unkakhala m’malo komanso ankaona kuti akulankhuladi ndi Mulungu. Atafika msinkhu woti akhoza kupemphera okha, ndinkawalimbikitsa kuti azipemphera mokweza kuti ndidziwe zimene zili mumtima mwawo komanso mmene amaonera Yehova. Zimenezi zinandithandiza kuti ndiziwaphunzitsa pang’onopang’ono kupereka mapemphero abwino okhala ndi mfundo za m’pemphero lachitsanzo.”

6 M’pake kuti ana a m’baleyu anakula bwino n’kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova. Panopa ali pa banja ndipo akuchita utumiki wa nthawi zonse limodzi ndi amuna awo. Kuthandiza ana anu kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova n’kofunika kwambiri kuposa kuwapatsa mphatso iliyonse. Koma mwana aliyense ali ndi udindo wopitiriza kulimbitsa ubwenziwu, kukonda dzina la Mulungu ndiponso kulilemekeza kwambiri.—Sal. 5:11, 12; 91:14.

“DZINA LANU LIYERETSEDWE”

7. Kodi ifeyo tili ndi mwayi uti, nanga tiyenera kuchita chiyani?

7 Ifeyo tili ndi mwayi wodziwa dzina la Mulungu komanso wokhala “anthu odziwika ndi dzina lake.” (Mac. 15:14; Yes. 43:10) Timapempha Yehova kuti dzina lake liyeretsedwe. Koma tiyenera kumupemphanso kuti azitithandiza kupewa chilichonse chimene chinganyozetse dzinalo. Sitifuna kufanana ndi anthu ena a m’nthawi ya atumwi amene zochita zawo zinkasemphana ndi zimene ankalalikira. Mtumwi Paulo anauza anthuwo kuti: “Dzina la Mulungu likunyozedwa pakati pa anthu amitundu chifukwa cha inu.”—Aroma 2:21-24.

8, 9. Perekani chitsanzo chosonyeza kuti Yehova amadalitsa anthu amene amafuna kuti dzina lake liyeretsedwe.

8 Timafunitsitsa kuchita zinthu zimene zingalemekeze dzina la Mulungu. Mlongo wina wa ku Norway anavutika kwambiri mwamuna wake atamwalira. Anamusiya ndi mwana wazaka ziwiri ndipo mlongoyo anati: “Nthawi imeneyi inali yovuta kwambiri. Ndinkapemphera tsiku lililonse mwinanso ola lililonse kuti Yehova azindikhazika mtima m’malo. Sindinkafuna kuti Satana azitonza Yehova chifukwa choti ndachita zosayenera. Ndinkafuna kulemekeza dzina la Yehova ndiponso kuthandiza mwana wanga kuti adzakumane ndi bambo ake m’Paradaiso.”—Miy. 27:11.

9 Yehova anayankha pemphero la mlongoyu. Popeza iye ankakonda kucheza ndi abale ndi alongo, iwo ankamulimbikitsa kwambiri. Patapita zaka 5, anakwatiwa ndi mkulu. Panopa mwana wake uja ali ndi zaka 20 ndipo anabatizidwa. Mlongoyu anati: “Ndikusangalala kwambiri kuti mwamuna wanga watsopanoyu wandithandiza kulera bwino mwanayu.”

10. N’chiyani chiyenera kuchitika kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe?

10 N’chiyani chiyenera kuchitika kuti dzina la Mulungu liyeretsedwe? Yehova ayenera kuchotsa aliyense amene amakana ulamuliro wake. (Werengani Ezekieli 38:22, 23.) Kenako anthu onse adzathandizidwa kuti akhale angwiro. Timalakalaka kwambiri nthawi imene aliyense adzaganiza, kulankhula komanso kuchita zinthu zolemekeza dzina la Mulungu. Pamapeto pake, Atate wathu wakumwamba adzakhala “zinthu zonse kwa aliyense.”—1 Akor. 15:28.

“UFUMU WANU UBWERE”

11, 12. Kodi Akhristu odzozedwa anathandizidwa kuzindikira chiyani mu 1876?

11 Yesu asanapite kumwamba, ophunzira ake anafunsa kuti: “Ambuye, kodi mubwezeretsa ufumu kwa Isiraeli pa nthawi ino?” Zimene Yesu anayankha zinasonyeza kuti sinali nthawi yoti ophunzirawo adziwe pamene Ufumu wa Mulungu udzayambe kulamulira. Koma anawathandiza kuika maganizo awo pa ntchito yolalikira chifukwa inali yofunika kwambiri. (Werengani Machitidwe 1:6-8.) Komabe Yesu anaphunzitsa ophunzira ake kuti aziyembekezera kubwera kwa Ufumu wa Mulungu. Kuyambira nthawi ya atumwi, Akhristu akhala akupemphera kuti Ufumuwu ubwere.

12 Ndiyeno patapita zaka, Yehova anathandiza atumiki ake kudziwa nthawi imene Yesu adzayambe kulamulira kumwamba. Anachita zimenezi nthawiyo itatsala pang’ono kukwana. M’chaka cha 1876, Charles Taze Russell analemba nkhani yofotokoza zimenezi m’magazini inayake. Nkhani yake inali yakuti: “Kodi Nthawi za Anthu a Mitundu Ina Zidzatha Liti?” Nkhaniyi inafotokoza kuti “nthawi zokwanira 7” zotchulidwa mu ulosi wa Danieli zikufanana ndi ‘nthawi zoikidwiratu za anthu a mitundu ina’ zimene Yesu anatchula. Nkhaniyo inafotokozanso kuti nthawizi zidzatha mu 1914. *Dan. 4:16; Luka 21:24.

13. (a) N’chiyani chinachitika mu 1914? (b) Kodi zimene zakhala zikuchitika kuyambira mu 1914 zikusonyeza chiyani?

13 Mu 1914, ku Ulaya kunayambika nkhondo imene inafalikira padziko lonse lapansi. Pamene nkhondoyi inkatha mu 1918, panali njala m’madera ambiri. Panalinso matenda a chimfine choopsa omwe anapha anthu ambiri kuposa amene anaphedwa pa nkhondoyo. Apa “chizindikiro” chakuti Yesu wayamba kulamulira kumwamba chinayamba kuonekera. (Mat. 24:3-8; Luka 21:10, 11) Pali umboni wokwanira wosonyeza kuti Yesu Khristu “anapatsidwa chisoti chachifumu” mu 1914 ndipo ‘anapita kukagonjetsa adani ake.’ (Chiv. 6:2) Yesu anathamangitsa Satana ndi ziwanda zake kumwamba n’kuwaponyera padziko lapansi. Kuyambira nthawi imeneyo, ulosi wina wa m’Baibulo wakhala ukukwaniritsidwa. Ulosiwu umati: “Tsoka dziko lapansi ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, ndipo ali ndi mkwiyo waukulu podziwa kuti wangotsala ndi kanthawi kochepa.”—Chiv. 12:7-12.

14. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kupempherabe kuti Ufumu wa Mulungu ubwere? (b) Tchulani ntchito yofunika kwambiri imene tiyenera kugwira.

14 N’chifukwa chiyani mavuto anachuluka kwambiri padzikoli Yesu atayamba kulamulira kumwamba? Ulosi wa pa Chivumbulutso 12:7-12 umafotokoza bwino chifukwa chake. Ngakhale kuti Yesu anayamba kulamulira kumwamba, Satana akulamulirabe dziko lapansi. Choncho tidzapitirizabe kupemphera kuti Ufumu wa Mulungu ubwere mpaka pamene Yesu adzathetse zoipa zonse padzikoli. Komanso tiziyesetsa kugwira nawo ntchito yolalikira. Ntchitoyi ikukwaniritsa ulosi wa Yesu wakuti: “Uthenga wabwino uwu wa ufumu udzalalikidwa padziko lonse lapansi kumene kuli anthu, kuti ukhale umboni ku mitundu yonse, kenako mapeto adzafika.”—Mat. 24:14.

‘CHIFUNIRO CHANU CHICHITIKE PANSI PANO’

15, 16. Kodi tingachite bwanji zinthu mogwirizana ndi pemphero lakuti chifuniro cha Mulungu chichitike padzikoli?

15 Pafupifupi zaka 6,000 zapitazo, chifuniro cha Mulungu chinkachitika padzikoli. M’pake kuti Yehova anaona kuti “zonse zimene anapanga zinali zabwino kwambiri.” (Gen. 1:31) Koma kenako Satana anasiya kumvera Mulungu. Kuyambira nthawi imeneyo, anthu ochepa okha akhala akumvera Mulungu padzikoli. Koma masiku ano, pali a Mboni oposa 8 miliyoni amene amapemphera kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padziko lapansi komanso akuyesetsa kuchita zinthu mogwirizana ndi pempheroli. Iwo amayesetsa kukhala ndi khalidwe labwino ndipo amagwira mwakhama ntchito yophunzitsa anthu za Ufumu wa Mulungu.

Kodi mukuthandiza ana anu kuti azichita zinthu mogwirizana ndi pemphero lakuti chifuniro cha Mulungu chichitike padzikoli? (Onani ndime 16)

16 Chitsanzo pa nkhaniyi ndi mlongo wina amene akuchita umishonale ku Africa. Iye ali ndi zaka 80 ndipo anabatizidwa mu 1948. Mlongoyu anati: “Ndimakonda kupemphera kuti tipeze anthu onse okhala ngati nkhosa n’kuwathandiza kuti adziwe Yehova mapeto asanafike. Komanso ndikafuna kulalikira munthu wina ndimapempha kaye nzeru kuti ndithe kumufika pamtima. Ndimapempheranso kuti Yehova atidalitse pamene tikuyesetsa kuthandiza anthu amene tawapeza kale.” M’pake kuti zinthu zimamuyendera bwino mlongoyu mu utumiki ndipo wathandiza anthu ambirimbiri kuti ayambe kutumikira Yehova. Mwina inunso mumadziwa anthu ena amene amachita zonse zimene angathe potumikira Mulungu ngakhale kuti ndi okalamba.—Werengani Afilipi 2:17.

17. Kodi mukumva bwanji mukaganizira zimene Yehova adzachite padzikoli m’tsogolo?

17 Tidzapitiriza kupemphera kuti chifuniro cha Mulungu chichitike padzikoli mpaka nthawi imene adani onse a Ufumu wa Mulungu adzachotsedwe. Pa nthawiyo, tidzaona chifuniro cha Mulungu chikuchitika kwambiri padzikoli ndipo anthu mabiliyoni ambiri adzaukitsidwa. Paja Yesu anati: “Musadabwe nazo zimenezi, chifukwa idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu [anga] ndipo adzatuluka.” (Yoh. 5:28, 29) Tidzasangalala kwambiri kulandira anzathu amene adzaukitsidwe. Mulungu ‘adzapukutadi misozi yonse m’maso mwathu.’ (Chiv. 21:4) Ambiri amene adzaukitsidwe adzakhala anthu “osalungama” omwe anamwalira asanadziwe bwino Yehova Mulungu ndi Mwana wake. Tidzakhala ndi mwayi waukulu wowathandiza kuphunzira za Mulungu kuti akhale oyenerera kulandira “moyo wosatha.”—Mac. 24:15; Yoh. 17:3.

18. Kodi anthu amafunikira kwambiri zinthu ziti?

18 Ufumu wa Mulungu ukabwera udzayeretsa dzina la Yehova ndipo padziko lonse padzakhala mtendere ndiponso mgwirizano. Choncho Mulungu akadzayankha mbali zitatu zoyambirira za pemphero la Ambuye, adzathandiza anthu kuti akhale ndi zinthu zofunika kwambiri. Komabe pali zinthu zina zofunika zimene Yesu anatchulanso m’pemphero lachitsanzo. Tidzakambirana zinthuzi m’nkhani yotsatira.

^ ndime 12 Kuti mumvetse bwinobwino zoti ulosiwu unakwaniritsidwa mu 1914, onani buku lakuti Kodi Baibulo Limaphunzitsa Chiyani Kwenikweni? tsamba 215 mpaka 218.