Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kodi Mukumbukila?

Kodi Mukumbukila?

Kodi mwaŵelenga mosamala magazini aposacedwapa a Nsanja ya Mlonda kapena a Nsanja ya Olonda? Yesani kuyankha mafunso otsatilawa:

Kodi Akristu ayenela kupemphela kwa Yesu Kristu?

Iyai. Yesu anatiphunzitsa kuti tizipemphela kwa Yehova ndipo anatipatsa citsanzo popeleka pemphelo kwa Atate wake. (Mat. 6:6-9; Yoh. 11:41; 16:23) Otsatila ake oyambilila anapemphela kwa Mulungu osati kwa Yesu. (Mac. 4:24, 30; Akol. 1:3)—1/1, tsamba 14.

Kodi Tingakonzekele bwanji cikumbutso ca imfa ya Yesu caka ciliconse?

Cinthu coyamba cimene tingacite ndi kutsatila ndandanda ya kuŵelenga Baibulo pa nyengo ya Cikumbutso. Tingaonjezelenso utumiki wathu pa nyengo imeneyi. Tingasinkhesinkhe mwapemphelo za ciyembekezo cimene Mulungu watipatsa.—1/15, masamba 14-16.

Kodi akaidi aŵili a ku Iguputo amene anafotokozela Yosefe maloto ovuta, zinthu zinawayendela bwanji?

Yosefe anauza wopelekela cikho kuti Farao adzam’tulutsa ndi kumubwezela pa nchito yake yakale. Iye anauzanso wophika mkate kuti maloto ake anatanthauza kuti Farao adzamutulutsa ndi kum’dula mutu ndipo adzam’pacika pamtengo. Zonse zimene Yosefe anakamba zinacitikadi. (Gen. 40:1-22) —3/1, masamba 12-14.

Kodi abale a ku Japan analandila mphatso yosangalatsa yotani?

Analandila buku limene lili ndi Uthenga Wabwino wa Mateyu wocokela m’Baibulo la Dziko Latsopano. Buku limeneli akuligaŵila mu ulaliki ndipo anthu ambili amene sadziŵa Baibulo akusangalala nalo.—2/15, tsamba 3.

Ndi zinthu zotani zimene zinathandiza kuti uthenga wabwino ufalikile m’nthawi ya Atumwi?

Panthawi yochedwa Mtendele wa Aroma (Pax Romana) panalibe nkhondo. Ophunzila oyambilila anali kuyenda m’njila zabwino zimene Aroma anapanga. Panthawiyo cinenelo ca Cigiliki cinali cofala kwambili. Pa cifukwa cimeneci, atumiki a Mulungu anali kulankhula ndi anthu osiyanasiyana, kuphatikizapo Ayuda amene anali mu Ufumu wonse wa Roma ndipo izi zinathandiza kuti uthenga wabwino ufalikile. Ophunzilawo anali kugwilitsila nchito lamulo la Aroma pofuna kuteteza uthenga wabwino.—2/15, masamba 20-23.

Kodi Akristu ayenela kukondwelela Isitala?

Yesu anauza otsatila ake kukumbukila imfa yake osati kuukitsidwa kwake. (Luka 22:19, 20)—3/1, tsamba 8.

Kale, mabuku athu anali kufotokoza kwambili nkhani za m’Baibulo ndi zimene zikuimila. Koma m’zaka zaposacedwapa mabuku athu safotokoza kwambili zimenezo. N’cifukwa ciani?

Malemba amaonetsa kuti anthu ena ochulidwa m’Baibulo anali kuimila cinthu cina cacikulu codzacitika mtsogolo. Cimodzi mwa zitsanzo zimenezi cikupezeka pa Agalatiya 4:21-31. Komabe sitiyenela kuganiza kuti nkhani iliyonse kapena cocitika ciliconse cimaimila cinthu cacikulu codzacitika mtsogolo. Conco, tingaone zimene tikuphunzilapo pa nkhani ndi zocitika zochulidwa m’Baibulo, m’malo mofotokoza zinthu zimene nkhanizo zimaimila. (Aroma 15:4)—3/15, masamba 17-18.

N’cifukwa ciani tiyenela kucita cidwi ndi zidutswa zopezeka pa zinyalala zakale za ku Iguputo?

Kwa zaka 100 zapitazo, anthu ena anapeza zidutswa za Uthenga Wabwino wa Yohane. Patapita zaka zingapo Yohane atalemba buku lake, zolembedwa pa zidutswazo zinagwilizana ndi zimene zili m’Baibulo masiku ano. Zimenezi zikusonyeza kuti Baibulo ndi lodalilika.—4/1, masamba 10-11.

N’cifukwa ciani kucotsa munthu wosalapa mumpingo ndi makonzedwe acikondi?

Baibulo limafotokoza makonzedwe a kucotsa munthu mumpingo kumene kumakhala ndi zotsatilapo zosangalatsa. (1 Akor. 5:11-13) Kucotsa wolakwa mumpingo kumacititsa kuti dzina la Yehova lilemekezedwe, kumateteza mpingo woyela wacikristu ndipo kungamuthandize kuzindikila chimo lake. —4/15, masamba 29-30