Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | N’CHIYANI CHINGATITHANDIZE TIKAKHALA NDI NKHAWA?

Kuda Nkhawa Chifukwa cha Zinthu Zoopsa

Kuda Nkhawa Chifukwa cha Zinthu Zoopsa

Alona ananena kuti: “Ndikangomva phokoso la masayilini, ndimachita mantha kwambiri ndipo ndimathamangira m’chipinda chobisalirako mabomba akamaphulika. Ngakhale nditabisala kumeneko ndimakhalabe ndi nkhawa. Koma ndimakhala ndi nkhawa kwambiri ndikamamva kulira kwa masayilini ndili kwina. Tsiku lina ndikuyenda mumsewu, ndinayamba kumva kulira kwa sayilini ndipo ndinayamba kulira mpaka kubanika. Panatenga maola ambiri kuti mtima wanga ukhale m’malo ndipo posakhalitsa masayilini aja anayambiranso kulira.”

Alona

Pali zinthu zinanso zambiri zimene zingatidetse nkhawa. Mwachitsanzo, mukadziwa kuti inuyo kapena wachibale wanu akudwala matenda oopsa, mungayambe kuda nkhawa kwambiri. Koma anthu ena amada nkhawa chifukwa choopa zimene zingadzawachitikire m’tsogolo. Iwo amaganiza kuti, ‘Kodi ana athu ndi zidzukulu zathu adzakhalabe m’dziko la nkhondo, matenda oopsa, loonongeka chifukwa cha kusintha kwa nyengo, komanso limene anthu ambiri ndi osamvera malamuloli?’ Kodi tingatani ngati tili ndi nkhawa chifukwa cha zinthu zimenezi?

Ngakhale kuti palibe chimene tingachite kuti zinthu zoipa zisamachitike Baibulo limati, “wochenjera amene waona tsoka amabisala.” (Miyambo 27:12) Mofanana ndi mmene timatetezera thupi lathu kuti lisavulale, tizitetezanso maganizo ndi mtima wathu ku zinthu zoipa. Kuona zinthu zachiwawa komanso nkhani za pa TV zosonyeza zithunzi zoopsa kungapangitse kuti ifeyo komanso ana athu tikhale ndi nkhawa. Tikamapewa kuona zithunzi zoopsa, sizitanthauza kuti sitidera nkhawa anthu amene akukumana ndi zoopsawo. Kungoti anthufe sitinalengedwe kuti tizingoona zinthu zoopsa. Choncho m’malo moganizira zinthu zoopsa, tiyenera kumaganizira “zinthu zilizonse zoona, . . . zilizonse zolungama, zilizonse zoyera, zilizonse zachikondi.” Tikamachita zimenezi, “Mulungu wamtendere” adzatipatsa mtendere wa m’maganizo ndi wa mumtima.—Afilipi 4:8, 9.

PEMPHERO NDI LOTHANDIZA

Kukhulupirira kwambiri Mulungu kumatithandiza kuti tisamakhale ndi nkhawa kwambiri. Baibulo limatilimbikitsa kuti: “Khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphera.” (1 Petulo 4:7) Tizipempha Mulungu kuti atithandize, atipatse nzeru komanso mphamvu kuti tikhale olimba mtima pothana ndi mavuto athu. Tizikhulupirira ndi mtima wonse kuti iye “amatimvera tikapempha chilichonse.”—1 Yohane 5:15.

Ndi mwamuna wake dzina lake Avi

Baibulo limanena kuti Satana ndiye “wolamulira wa dzikoli” osati Mulungu. Limanenanso kuti “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (Yohane 12:31; 1 Yohane 5:19) Mpake kuti Yesu anati tizipemphera kuti: “Mutilanditse kwa woipayo.” (Mateyu 6:13) Alona ananena kuti: “Ndikamva kulira kwa masayilini, ndimapemphera kuti Yehova andithandize kuti mtima ukhale m’malo. Komanso amuna anga amabwera pafupi n’kupemphera nane. Pemphero limathandiza kwambiri. N’chifukwa chake Baibulo limati: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanira pa iye. Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’choonadi.”—Salimo 145:18.

ZINTHU ZABWINO ZIMENE TIKUZIYEMBEKEZERA

Pa Ulaliki wa Paphiri, Yesu anaphunzitsa otsatira ake kuti azipemphera kuti: “Ufumu wanu ubwere.” (Mateyu 6:10) Ufumu wa Mulungu udzachotseratu zinthu zonse zimene zimatidetsa nkhawa. Mulungu adzagwiritsa ntchito Yesu yemwe ndi “Kalonga Wamtendere” kuti adzathetse “nkhondo mpaka kumalekezero a dziko lapansi.” (Yesaya 9:6; Salimo 46:9) “Mulungu adzakhala woweruza pakati pa mitundu yambiri ya anthu . . . Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunziranso nkhondo. . . . Sipadzakhala wowaopsa.” (Mika 4:3, 4) Mabanja azidzakhala mosangalala ndipo “adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.” (Yesaya 65:21) Ndipotu “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: ‘Ndikudwala.’”—Yesaya 33:24.

Masiku ano, pali zinthu zambiri zothandiza anthu kudziwiratu zinthu zoopsa zimene zingachitike. Koma n’zosatheka kupeweratu “zinthu zosayembekezereka” kapena kupewa kukhala malo olakwika pa nthawi yolakwikanso. (Mlaliki 9:11) Kwa zaka zambiri, ngakhale anthu osalakwa akhala akufa chifukwa cha nkhondo, chiwawa komanso matenda. Kodi anthu amenewa adzakhalanso ndi moyo?

Anthu amene anafa ndi ochuluka kwambiri ndipo Mulungu yekha ndi amene akudziwa chiwerengero chawo. Onsewa adzakhalanso ndi moyo. Panopa zili ngati akugona, ndipo Mulungu amawakumbukirabe mpaka pa tsiku limene “onse ali m’manda achikumbutso . . . adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29) Pa nkhani ya kuuka kwa akufa, Baibulo limatitsimikizira kuti: “Chiyembekezo chimene tili nachochi chili ngati nangula wa miyoyo yathu ndipo n’chotsimikizika ndiponso chokhazikika.” (Aheberi 6:19) Ndipo Mulungu “wapereka chitsimikizo kwa anthu onse mwa kumuukitsa [Yesu] kwa akufa.”—Machitidwe 17:31.

Panopa, aliyense kuphatikizapo amene amayesetsa kusangalatsa Mulungu amakhala ndi nkhawa. Paul, Janet, ndi Alona amakhalabe osangalala ngakhale kuti anakumanapo ndi zinthu zodetsa nkhawa kwambiri. Izi zatheka chifukwa amachita zinthu zothandiza kuchepetsa nkhawa, amapemphera kwa Mulungu ndiponso amakhulupirira kwambiri zimene Mulungu analonjeza m’Baibulo kuti adzachita m’tsogolo. Ngati inunso muli ndi nkhawa, “Mulungu amene amapereka chiyembekezo akudzazeni ndi chimwemwe chonse ndi mtendere wonse chifukwa cha kukhulupirira kwanu.”—Aroma 15:13.