Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Nkhawa Zokhudza Ngozi

Nkhawa Zokhudza Ngozi

“Nditamva belo locenjeza, ndinacita mantha ndipo ndinathaŵila kumalo obisalamo kukaphulika bomba. Koma ngakhale kuti ndinabisala, ndinali kucitabe mantha. Ndimacita mantha kwambili ndikakhala panja pamene palibe malo obisalako. Tsiku lina pamene ndinali kuyenda pamseu, belo locenjeza linalilanso. Ndinayamba kulila ndipo ndinalephela kupuma bwinobwino. Panatenga maola ambili kuti mtima wanga ukhazikike.” Anasimba motelo Alona.

Alona

Nkhondo ndi imodzi mwa zinthu zimene zimacititsa ngozi. Mwacitsanzo, tikadziŵa kuti munthu amene timakonda kapena ifeyo tili ndi matenda oopsa, timamva ngati kuti taphulitsidwa ndi bomba. Anthu ena akamaganizila za tsogolo lao, amakhala ndi nkhawa kwambili. Amadzifunsa kuti: ‘Kodi ana ndi adzukulu athu adzakhala m’dziko limene muli nkhondo, ciwawa, kuonongedwa kwa cilengedwe, kusintha kwa nyengo ndi milili?’ Tingalimbane bwanji ndi nkhawa zimenezi?

Kudziŵa kuti zinthu zoipa zimacitika, kumacititsa munthu ‘wocenjela amene waona tsoka kubisala.’ (Miyambo 27:12) Monga mmene timatetezela umoyo wathu, tifunika kucita zimene tingathe kuti titeteze maganizo athu ndi mtima wathu. Zosangulutsa zoipa ndiponso mabuku amene ali ndi zithunzi zoopsa, zimacititsa ana ndi acikulile kukhala ndi nkhawa. Kupewa kupenyelela zithunzi zaciwawa sikutanthauza kuti tikunyalanyaza zinthu zenizeni. Mulungu sanatipange kuti tiziganizila zinthu zoipa. Ndiye cifukwa cake tiyenela kudzaza maganizo athu ndi “zinthu zilizonse zoona,  . . .  zolungama, . . . zoyela, . .  .  zacikondi.” Tikacita zimenezi, “Mulungu wa mtendele” adzatipatsa mtendele wa mumtima.—Afilipi 4:8, 9.

KUFUNIKA KWA PEMPHELO

Kukhala ndi cikhulupililo ceniceni kumatithandiza kulimbana ndi nkhawa. Baibulo limatilimbikitsa kuti, “khalani maso kuti musanyalanyaze kupemphela.” (1 Petulo 4:7) Mwacidalilo timapempha Mulungu kuti atithandize, atipatse nzelu ndi kukhala olimba mtima polimbana ndi mavuto, popeza kuti “amatimvela tikapempha ciliconse.”—1 Yohane 5:15.

Ali ndi Avi, mwamuna wake

Baibulo limafotokoza kuti Satana ndi “wolamulila wa dzikoli” osati Mulungu. Ndipo limati “dziko lonse lili m’manja mwa woipayo.” (Yohane 12:31; 1 Yohane 5:19) Yesu sanakaikile zakuti Satana alikodi ndi zakuti Yehova amapulumutsa. N’cifukwa cake anatiphunzitsa kupempha kuti: “Mutilanditse kwa woipayo.” (Mateyu 6:13) Alona anati: “Nthawi zonse belo locenjeza likalila, ndimapempha Yehova kuti andithandize kukhazika mtima pansi. Komanso mwamuna wanga amandiitana kuti tipemphele pamodzi. Kukamba zoona, kupemphela kumathandiza kwambili.” Tikamapemphela, timamva mmene Baibulo limanenela kuti: “Yehova ali pafupi ndi onse oitanila pa iye. Iye ali pafupi ndi onse amene amamuitana m’coonadi.”—Salimo 145:18.

CIYEMBEKEZO CATHU CA MTSOGOLO

Pa ulaliki wake wa pa Phili, Yesu anaphunzitsa otsatila ake kupemphela kuti: “Ufumu wanu ubwele.” (Mateyu 6:10) Ufumu wa Mulungu udzacotsa nkhawa zonse kwamuyaya. Mulungu adzaletsa “nkhondo mpaka kumalekezelo a dziko lapansi” kudzela mwa Yesu, amene ndi “Kalonga Wamtendele.” (Yesaya 9:6; Salimo 46:9) Baibulo limati: “Mulungu adzakhala woweluza pakati pa mitundu yambili ya anthu  . . . Mtundu wa anthu sudzanyamula lupanga kuti umenyane ndi mtundu unzake, ndipo anthuwo sadzaphunzilanso nkhondo. . . . ndipo sipadzakhala wowaopsa.” (Mika 4: 3,  4) Mabanja acimwemwe “adzamanga nyumba n’kukhalamo. Adzabzala minda ya mpesa n’kudya zipatso zake.” (Yesaya 65:21) Komanso “palibe munthu wokhala m’dzikolo amene adzanene kuti: “Ndikudwala.’”—Yesaya 33:24.

Masiku ano, n’zosatheka kupewelatu “zinthu zosayembekezeleka” kapena kupewa kupezeka pamalo olakwika komanso panthawi yolakwika. (Mlaliki 9:11) Kwa zaka zambili, nkhondo, ciwawa ndi matenda zapitiliza kupha anthu abwino. Kodi anthu osalakwa amenewa ali ndi ciyembekezo cotani?

Anthu mamiliyoni ambili amene anamwalila, adzakhalanso ndi moyo. Palipano, tingati Mulungu akuwakumbukila, kufikila “pamene onse ali m’manda acikumbutso . . . adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29) Ponena za kuuka kwa akufa, Baibulo limatitsimikizila kuti: “Ciyembekezo cimene tili nacoci cili ngati nangula wa miyoyo yathu ndipo n’cotsimikizika ndiponso cokhazikika.” (Aheberi 6:19) Ndipo Mulungu “wapeleka citsimikizo kwa anthu onse mwa kumuukitsa [Yesu] kwa akufa.”—Machitidwe 17:31.

Ngakhale anthu amene akuyesetsa kukondweletsa Mulungu masiku ano, amakhala ndi nkhawa. Kuyandikila Mulungu m’pemphelo, ndi kulimbitsa cikhululipilo pa malonjezo a m’Baibulo a m’tsogolo, kumathandiza Paul, Janet, ndi Alona kulimbana ndi nkhawa. Monga mmene Iye wathandizila anthu amenewa, “Mulungu amene amapeleka ciyembekezo akudzazeni ndi cimwemwe conse ndi mtendele wonse cifukwa ca kukhulupilila kwanu.”—Aroma 15:13.