Pitani ku nkhani yake

Pitani ku mitu ya nkhani

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

Kuyankha Mafunso a M’Baibulo

N’chiyani chimachititsa kuti anthu azichita zoipa?

Kodi ndi ndani amene anayesa Yesu kuti achite zoipa?—Mateyu 4:8-10

Anthufe timafuna titamachita zinthu mwamtendere, moona mtima komanso mwachifundo. Nanga n’chifukwa chiyani padzikoli pamachitika zinthu zopanda chilungamo, zachiwawa komanso anthu amachitirana nkhanza? Nthawi zambiri timamva zokhudza zinthu zoopsa monga nkhondo kapenanso kuzionera pa TV. Kodi pali winawake amene amapangitsa kuti anthu azichita zoipa?—Werengani 1 Yohane 5:19.

Kodi Mulungu anatilenga anthufe ndi maganizo ofuna kuchita zoipa? Ayi, chifukwa Baibulo limati Yehova Mulungu analenga anthu m’chifaniziro chake. Izi zimapangitsa kuti tizitha kusonyeza chikondi ngati mmene iye amachitira. (Genesis 1:27; Yobu 34:10) Komatu Mulungu anatipatsa ufulu wosankha ndipo zimenezi zimasonyeza kuti amatilemekeza. Makolo athu oyambirira anasankha molakwika chifukwa sanamvere Mulungu. Zimenezi zinapangitsa kuti asamakwanitsenso kutsanzira makhalidwe abwino a Mulungu popanda kulakwitsa chilichonse. N’chifukwa chake anthufe timachita zoipa.—Werengani Deuteronomo 32:4, 5.

Kodi anthu adzasiya kuchita zoipa?

Mulungu amafuna kuti tizichita zinthu zabwino osati zoipa. (Miyambo 27:11) Choncho amatiphunzitsa zimene tingachite kuti tizipewa kuchita zoipa komanso kuti tikhale osangalala. Koma panopa, sitingathe kutsanzira bwinobwino chikondi cha Mulungu.—Werengani Salimo 32:8.

Ngakhale kuti zinthu zoipa zachuluka masiku ano, Mulungu wazilola kwa kanthawi ndithu kuti aliyense aone zotsatira za kuchita zinthu zoipa. (2 Petulo 3:7-9) Posachedwapa, padziko lonse padzakhala anthu osangalala komanso omvera Mulungu.—Werengani Salimo 37:9-11.