Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Thandizani Kukongoletsa Paladaiso Wauzimu

Thandizani Kukongoletsa Paladaiso Wauzimu

“Ine ndidzalemekeza malo oikapo mapazi anga.”—YES. 60:13.

NYIMBO: 102, 75

1, 2. Kodi mau akuti “copondapo mapazi” amaimila ciani m’Malemba Aciheberi?

YEHOVA MULUNGU anati: “Kumwamba ndiko mpando wanga wacifumu, ndipo dziko lapansi ndilo copondapo mapazi anga.” (Yes. 66:1) Ponena za “copondapo mapazi” ake, iye ananenanso kuti: “Ine ndidzalemekeza malo oikapo mapazi anga.” (Yes. 60:13) Kodi iye amacita bwanji zimenezi? Nanga zimenezi zikutikhudza bwanji ife amene tikukhala pa “copondapo mapazi” ca Mulungu?

2 Liu lakuti “copondapo mapazi” limanena za dziko lino, koma limagwilitsidwanso nchito m’Malemba Aciheberi pofotokoza mophiphilitsa za kacisi wakale amene Aisiraeli anali kugwilitsila nchito. (1 Mbiri 28:2; Sal. 132:7) Kacisi ameneyo anali kugwilitsidwa nchito monga malo olambililapo Mulungu woona. Cifukwa ca zimenezi, kacisiyo anali wokongola kwambili pamaso pa Yehova, ndipo anali kukongoletsa malo oikapo mapazi ake.

3. Kodi kacisi wamkulu wauzimu wa Mulungu n’ciani? Nanga anakhazikitsidwa liti?

3 Masiku ano, padziko lapansi palibe kacisi weniweni amene ndi cimake ca kulambila koona. Koma pali kacisi wauzimu amene amalemekeza Yehova kuposa nyumba iliyonse. Kacisi ameneyu ndi dongosolo limene Yehova anakonza lotithandiza kukhala naye paubwenzi kudzela m’nsembe ya Yesu Kristu amenenso ndi wansembe. Makonzedwe amenewo anakhazikitsidwa mu 29 C.E. pa ubatizo wa Yesu pamene iye anadzozedwa kukhala Mkulu wa Ansembe pa kacisi wamkulu wauzimu wa Yehova.—Aheb. 9:11, 12.

4, 5. (a) Malinga ndi Salimo 99, n’ciani cimene atumiki a Yehova amakonda kucita? (b) Ndi funso liti limene aliyense ayenela kudzifunsa?

4 Posonyeza kuyamikila makonzedwe a kacisi wauzimu, timatamanda Yehova ndi kumukweza mwa kulengeza dzina lake cifukwa anatipatsa dipo mwa cifundo cake. N’zosangalatsa kwambili kudziŵa kuti Akristu oona oposa 8 miliyoni akutamanda Yehova mwacangu masiku ano. Mosiyana ndi anthu ena amene amakhulupilila bodza lakuti adzatamanda Mulungu akadzapita kumwamba, Mboni za Yehova panthawi ino zikutamanda Mulungu pano padziko lapansi.

5 Mwa kucita zimenezi, timatsatila citsanzo ca Akristu okhulupilika amene akufotokozedwa pa Salimo 99:1-3, 5. (Ŵelengani.) Monga mmene lembali lasonyezela, Mose, Aroni, ndi Samueli anacilikiza mokwanila makonzedwe a kulambila koona. (Sal. 99:6, 7) Masiku ano, otsalila odzozedwa asanapite kumwamba kukatumikila monga ansembe pamodzi ndi Yesu, amatumikila mokhulupilika m’bwalo la padziko lapansi la kacisi wauzimu. Ndipo anthu mamiliyoni ambili a “nkhosa zina” amawacilikiza mokhulupilika. (Yoh. 10:16) Ngakhale kuti a nkhosa zina ndiponso odzozedwa ali ndi ziyembekezo zosiyana, io amalambila Yehova mogwilizana pano padziko lapansi. Komabe aliyense payekha ayenela kudzifunsa kuti: ‘Kodi ndimacilikiza mokwanila makonzedwe a Yehova okhudza kulambila koona?’

KUDZIŴA AMENE AKUTUMIKILA PA KACISI WAUZIMU WA MULUNGU

6, 7. Ndi vuto liti limene linabuka pakati pa Akristu oyambilila? Ndipo n’ciani cinacitika patapita zaka zambili?

6 Patapita zaka pafupifupi 100 mpingo wacikristu utakhazikitsidwa, mpatuko unabuka pakati pa Akristu monga mmene Malemba ananenela. (Mac. 20:28-30; 2 Ates. 2:3, 4) Ndipo zinali zovuta kudziŵa amene anali kutumikiladi Mulungu pa kacisi wake wauzimu. Patapita zaka zambili, nthawi inakwana yoti Yehova akonze zinthu kudzela mwa Yesu Kristu, Mfumu yatsopano imene iye anaika.

7 Podzafika mu 1919, anthu amene anali kutumikiladi Yehova pa kacisi wake wauzimu anadziŵika. Iye anawayeletsa mwakuuzimu kuti utumiki wao kwa Yehova ukhale wovomelezeka. (Yes. 4:2, 3; Mal. 3:1-4) Conco, zinthu zimene mtumwi Paulo anaona m’masomphenya ake zinayamba kukwanilitsidwa.

8, 9. Kodi “paladaiso” amene Paulo anaona amatanthauza zinthu zitatu ziti?

8 Lemba la 2 Akorinto 12:1-4 (Ŵelengani.) limafotokoza za masomphenya amene Paulo anaona. Masomphenya amene Paulo anaona anali okhudza zinthu zamtsogolo osati zimene zinali kucitika m’nthawi yake. Ndi “paladaiso” uti amene Paulo anaona pamene “anakwatulidwila kumwamba kwacitatu”? Paladaiso ameneyu angatanthauze Paladaiso weniweni wa padziko lapansi amene akubwela posacedwapa. (Luka 23:43) Angatanthauzenso paladaiso wauzimu amene adzafika pacimake m’dziko latsopano. Kuonjezela pamenepo, angatanthauzenso madalitso a kumwamba amene ali “m’paladaiso wa Mulungu.”—Chiv. 2:7.

9 Nanga n’cifukwa ciani Paulo ananena kuti “anamva mau osachulika, amene sikololeka munthu kuwanena”? Cifukwa cakuti siinali nthawi yoti afotokoze zinthu zonse zodabwitsa zimene anaona m’masomphenya ake. Koma masiku ano n’kololeka kukamba za madalitso amene anthu a Mulungu ali nao.

10. N’cifukwa ciani mau akuti “paladaiso wauzimu” ndi akuti “kacisi wauzimu” ndi osiyana?

10 Mau akuti “paladaiso wauzimu” timawagwilitsila nchito kwambili m’gulu lathu. Paladaiso ameneyu ndi mkhalidwe wauzimu wapadela umene umacititsa Akristu kukhala pamtendele ndi Mulungu ndiponso Akristu anzao. Koma mau akuti “paladaiso wauzimu” ndi akuti “kacisi wauzimu” satanthauza zinthu zofanana. Kacisi wauzimu ndi makonzedwe a Mulungu okhudza kulambila koona. Paladaiso wauzimu amatithandiza kudziŵa bwino anthu amene amalambiladi Mulungu ndi kumutumikila pa kacisi wake wauzimu masiku ano.—Mal. 3:18.

11. Ponena za paladaiso wauzimu, ndi mwai wotani umene tili nao?

11 N’zosangalatsa kwambili kudziŵa kuti kuyambila mu 1919, Yehova wapatsa anthu opanda ungwilo mwai wogwila naye nchito yopanga paladaiso wauzimu, kuulimbitsa, ndi kuukulitsa pano padziko lapansi. Kodi inu mumatengako mbali pa nchitoyi? Kodi mumaona kuti ndi mwai wanu kugwilila nchito limodzi ndi Yehova pokongoletsa ‘malo oikapo mapazi ake?’

GULU LA YEHOVA LIKUPITILIZABE KUKONGOLA

12. Kodi kukwanilitsidwa kwa lemba la Yesaya 60:17 kumatipangitsa kutsimikiza za ciani? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

12 Lemba la Yesaya 60:17. (Ŵelengani.) linanenelatu za kusintha kocititsa cidwi kwa mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova. Akristu acinyamata kapena anthu ena amene aphunzila coonadi posacedwapa adziŵa za kusintha kumeneku pambuyo poŵelenga kapena kuuzidwa ndi anthu ena. Koma abale ndi alongo amene atumikila kwa zaka zambili ali ndi mwai waukulu cifukwa adzionela okha mmene gulu lasinthila. Ndiye cifukwa cake io ndi otsimikiza kuti Yehova akutsogoleladi gulu lake kudzela mwa Mfumu Yesu Kristu. Iwo sakaikila zimenezi cifukwa ali ndi umboni wokwanila ndipo n’zimene tonsefe timakhulupilila. Kumvetsela pamene akusimba za cisangalalo cimene ali naco kungalimbitse cikhulupililo ndi cidalilo canu mwa Yehova.

13. Ndi udindo wotani umene tili nao wopezeka pa Salimo 48:12-14?

13 Kaya takhala nthawi yaitali m’coonadi kapena ai, tifunika kuuzako ena za gulu la Yehova. Paladaiso wauzimu amene tili naye ndi cozizwitsa m’dziko loipali lomwe lilibe cikondi. Tifunika kuuzako “m’badwo wam’tsogolo” zinthu zocititsa cidwi za gulu la Yehova kapena kuti “Ziyoni,” ndiponso coonadi ponena za paladaiso wauzimu.—Ŵelengani Salimo 48:12-14.

14, 15. Ndi kusintha kotani kokhudza gulu lathu kumene kunapangidwa ca m’ma 1970? Ndipo kusintha kumeneko kwatipindulitsa bwanji?

14 Kwa zaka zambili, acikulile amene ali pakati pathu aona kusintha kwina kumene kwakongoletsa mbali ya padziko lapansi ya gulu la Yehova. Iwo amakumbukila kuti kale mipingo inali kutsogoleledwa ndi mtumiki wa mpingo m’malo mwa bungwe la akulu, nthambi ya m’dziko lililonse inali kuyang’anilidwa ndi mtumiki wa nthambi m’malo mwa komiti ya nthambi, ndipo malangizo anali kupelekedwa ndi pulezidenti wa Watch Tower Society m’malo mwa Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova. Ngakhale kuti abale okhulupilika amenewa anali ndi atumiki ena amene anali kuwathandiza, m’bale mmodzi ndi amene anali ndi udindo wopanga zosankha kaya ndi pa mpingo, pa nthambi kapena ku likulu lathu. M’zaka za m’ma 1970 panali kusintha kwakuti mipingo, nthambi, ndiponso likulu lathu ziziyang’anilidwa ndi gulu la abale oyenelela osati ndi munthu mmodzi.

15 Kodi kusintha kumeneku ndi kopindulitsa? Inde. N’cifukwa ciani tikutelo? Cifukwa cakuti kusintha kumeneku kunapangidwa potsatila zimene Malemba amasonyeza. M’malo motsatila maganizo a mkulu mmodzi, akulu onse omwe ndi “mphatso za amuna” zocokela kwa Mulungu amathandizana popanga zosankha zimene zimapindulitsa gulu la Yehova.—Aef. 4:8; Miy. 24:6.

Yehova akupeleka malangizo othandiza kwa munthu aliyense (Onani ndime 16 ndi 17)

16, 17. Ndi kusintha kuti kwaposacedwapa kumene kumakusangalatsani kwambili? Ndipo n’cifukwa ciani?

16 Ganizilani za kusintha kumene kunapangidwa posacedwapa, monga kusintha kwa kaonekedwe ka zofalitsa zathu, nkhani zimene zimafalitsidwa, ndi kagaŵilidwe ka zofalitsazo. N’zosangalatsa kwambili kugaŵila zofalitsa zokongola ndiponso zothandiza zimenezi mu utumiki. Ndipo tikamagwilitsila nchito zinthu zamakono monga webusaiti yathu ya jw.org pofalitsa coonadi, timasonyeza kuti tikutsanzila Yehova amene amafunitsitsa kupeleka malangizo othandiza kwa munthu aliyense.

17 Ndipo timayamikilanso kusintha kokhudza misonkhano kumene kunapangidwa cifukwa kunatithandiza kuti tizikhala ndi nthawi yocita Kulambila kwa Pabanja ndi phunzilo laumwini. Timayamikilanso kusintha kwina kumene kunapangidwa kokhudza mapulogilamu a pa msonkhano wadela ndi wacigawo. Ndiye cifukwa cake timanena kuti misonkhano yathu imakhala yosangalatsa caka ciliconse. Ndipo timapindula ndi maphunzilo oonjezeleka amene timalandila m’masukulu athu osiyanasiyana. Kusintha kumeneku kumasonyeza kuti Yehova ndiye akutsogolela gulu lathu. Iye akukongoletsa kwambili gulu lake ndiponso paladaiso wauzimu amene tikusangalala naye masiku ano.

ZIMENE MUNGACITE KUTI MUCILIKIZE PALADAISO WAUZIMU

18, 19. Tingathandize bwanji kukongoletsa paladaiso wauzimu?

18 Kunena zoona, ndi mwai wamtengo wapatali kuthandiza Yehova pa nchito yokongoletsa paladaiso wauzimu. Ndipo timacita zimenezi mwa kulalikila mwakhama uthenga wabwino ndi kupanga ophunzila. Tikathandiza munthu kuphunzila mpaka kufika pobatizidwa ndiye kuti tathandiza kukulitsa paladaiso wauzimu.—Yes. 26:15; 54:2.

19 Njila ina imene tingathandizile kukongoletsa paladaiso wauzimu ndi mwa kukonza umunthu wathu. Kucita zimenezi kumacititsa kuti anthu ena azikopeka ndi paladaiso wauzimu ameneyu. Nthawi zambili makhalidwe athu abwino monga ciyelo ndi mtendele ndi amene amacititsa anthu kuyandikila Mulungu ndi Kristu ndiponso kubwela m’gulu la Yehova.

Tingathandize panchito yokulitsa paladaiso wauzimu (Onani ndime 18 ndi 19)

20. Malinga ndi Miyambo 14:35, kodi tiyenela kucita ciani?

20 Masiku ano, Yehova ndi Yesu amasangalala kwambili akaona paladaiso wathu wauzimu. Cisangalalo cimene timakhala naco pothandiza kukongoletsa paladaiso wauzimu, cimaonetsa cisangalalo cacikulu cimene tidzakhala naco mtsogolo pokonza paladaiso weniweni pano padziko lapansi. Tiyeni nthawi zonse tizikumbukila mau amene ali pa Miyambo 14:35 akuti: “Mfumu imasangalala ndi wanchito wocita zinthu mozindikila.” Tiyeni tizicita zinthu mozindikila pamene tikuthandiza pa nchito yongokoletsa paladaiso wauzimu.