Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Pitirizani Kukhala Okhulupirika kwa Mulungu

Pitirizani Kukhala Okhulupirika kwa Mulungu

“Iwo sali mbali ya dziko.”—YOH. 17:16.

NYIMBO: 63, 129

1, 2. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala okhulupirika kwa Mulungu? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife okhulupirika kwa Mulungu? (Onani chithunzi pamwambapa.) (c) Kodi anthu ena amakonda kwambiri zinthu ziti ndipo zimabweretsa mavuto otani?

AKHRISTU ayenera kukhala okhulupirika kwa Mulungu nthawi zonse ndipo sayenera kulowerera nkhani zimene zimasokoneza mgwirizano wa anthu. Tikutero chifukwa chakuti munthu amene wadzipereka kwa Yehova amalonjeza kuti azimukonda ndiponso kumumvera nthawi zonse. (1 Yoh. 5:3) Timafunika kumvera malangizo a Yehova mosatengera kumene timakhala, mtundu wathu kapena chikhalidwe chathu. Tiyenera kukonda Yehova ndiponso Ufumu wake kuposa munthu aliyense kapena chinthu chilichonse. (Mat. 6:33) Kuti zimenezi zitheke, Akhristu ayenera kupewa kulowerera m’mikangano yonse ya m’dzikoli.—Yes. 2:4; werengani Yohane 17:11, 15, 16.

2 Anthu omwe si atumiki a Yehova amakonda kwambiri dziko lawo, mtundu wawo, chikhalidwe chawo ngakhalenso timu yamasewera ya dziko lawo. Zimenezi zimachititsa kuti anthu azipikisana, kudana kapena kuphana kumene. Ndiyeno zimene amachita pothetsa mavutowa zingatikhudzenso popeza tili m’dzikoli. Mwachibadwa, anthufe timafuna chilungamo moti nthawi zina zimene maboma amachita zingatikhumudwitse ndithu. (Gen. 1:27; Deut. 32:4) Zimenezi zikachitika n’zosavuta kuti tiyambe kulowerera m’mikangano ya m’dzikoli.

3, 4. (a) N’chifukwa chiyani Akhristu salowerera m’mikangano ya m’dzikoli? (b) Kodi tikambirana chiyani m’nkhaniyi?

3 Nthawi zina maboma kapena mabungwe amakakamiza anthu kuti azilowerera m’mikangano. Koma Akhristufe sitilowerera ndale kapena kumenya nawo nkhondo. (Mat. 26:52) Sititengekanso ndi zimene anthu amachita pofuna kusonyeza kuti dziko lawo ndi lofunika kuposa la ena. (2 Akor. 2:11) Paja Baibulo limati Akhristu oona sayenera kukhala mbali ya dziko.—Werengani Yohane 15:18, 19.

4 Popeza ndife anthu ochimwa, mwina tikulimbana ndi maganizo olakwika amene tinali nawo tisanaphunzire za Yehova. (Yer. 17:9; Aef. 4:22-24) M’nkhaniyi tikambirana mfundo zina zimene zingatithandize kuthetsa maganizo olakwikawo. Tikambirananso zimene tingachite kuti tidziphunzitse kukhala okhulupirika kwa Yehova ndi Ufumu wake.

TISALOLE KUTI DZIKO LITIGAWANITSE

5, 6. N’chifukwa chiyani Yesu sankadana ndi anthu ena?

5 Ngati zikukuvutani kudziwa zochita pa nkhani inayake, muyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi akanakhala Yesu akanachita chiyani?’ M’dziko limene Yesu ankakhala munali anthu ochokera m’madera osiyanasiyana monga Yudeya, Galileya ndi Samariya. Baibulo limasonyeza kuti anthu ochokera m’maderawa sankagwirizana. (Yoh. 4:9) Panalinso kusagwirizana pakati pa Afarisi ndi Asaduki, anthu wamba ndi okhometsa misonkho komanso anthu ophunzira ndi osaphunzira. (Mac. 23:6-9; Mat. 9:11; Yoh. 7:49) Chinanso n’chakuti pa nthawiyo Aisiraeli ankalamuliridwa ndi Aroma ndipo sankagwirizana nawo. N’zoona kuti Yesu ankauza anthu molimba mtima za Yehova ndipo ankadziwa kuti Aisiraeli anali anthu ake apadera. Koma sankaphunzitsa ophunzira ake kuti iwo anali abwino kuposa anthu ena. (Yoh. 4:22) M’malomwake, ankawaphunzitsa kuti azikonda anthu onse.—Luka 10:27.

6 N’chifukwa chiyani Yesu sankadana ndi anthu ena ngati mmene Ayuda ambiri ankachitira? Chifukwa chakuti iye ndi Atate wake salowerera m’mikangano ya m’dzikoli. Pamene Yehova analenga anthu awiri oyamba, ankafuna kuti iwo adzaze dziko lonse. (Gen. 1:27, 28) Mulungu analenga anthu kuti azitha kubereka ana a mitundu yosiyanasiyana. Choncho Yehova ndi Yesu saona kuti anthu a mtundu wina kapena a chilankhulo china ndi apamwamba kuposa ena. (Mac. 10:34, 35; Chiv. 7:9, 13, 14) Ndiyetu tingachite bwino kutsatira chitsanzo chawo.—Mat. 5:43-48.

7, 8. (a) Kodi Akhristu ayenera kusankha mbali pa nkhani iti? (b) Kodi Akhristu ayenera kuzindikira chiyani pa nkhani yothetsa mavuto m’dzikoli?

7 Koma kodi tonsefe tiyenera kusankha mbali pa nkhani iti? Nkhani yake ndi imene Satana anayambitsa m’munda wa Edeni. Iye anatsutsa zoti Yehova ndi woyenera kulamulira chilengedwe chonse. Panopa anthu onse ayenera kusankha pakati pa ulamuliro wa Yehova ndi wa Satana. Kodi mumasonyeza kuti mwasankha ulamuliro wa Yehova pomumvera m’malo mochita zimene mukufuna? Kodi mumakhulupiriradi kuti Ufumu wake wokha ndi umene ungathetse mavuto a anthu? Kapena kodi mumaona kuti anthu akhoza kudzilamulira okha bwinobwino?—Gen. 3:4, 5.

8 Mayankho anu pa mafunsowa angakuthandizeni kudziwa zimene mungachite anthu akakufunsani maganizo pa nkhani za m’dzikoli. Anthu andale kapena amabungwe akhala akuyesetsa kuthetsa mikangano ya m’dzikoli. N’kutheka kuti iwo akufunitsitsa kuthandiza anthu. Koma Akhristu amadziwa kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene ungathetse mavuto n’kukhazikitsa chilungamo. Ngati Mkhristu aliyense atati alimbikitse anthu kutsatira njira imene akuona kuti ingathetse mavuto, mgwirizano ukhoza kusokonekera mumpingo. Choncho tiyenera kusiya nkhaniyi m’manja mwa Yehova.

9. (a) Kodi mpingo wa ku Korinto unali ndi vuto liti? (b) Kodi mtumwi Paulo anawapatsa malangizo ati?

9 Tiyeni tione zimene Akhristu oyambirira anachita pamene ena mumpingo anayamba kugawikana. Mumpingo wa ku Korinto anthu ena ankanena kuti: ‘“Ine ndine wa Paulo,” ena ankati, “Ine ndine wa Apolo,” enanso ankati “Ine ndine wa Kefa,” pamene ena ankati, “Ine ndine wa Khristu.”’ Kaya ankanena zimenezi chifukwa chiyani, mtumwi Paulo sanasangalale nazo ndipo anati “Khristu wakhala wogawanika.” Ndiyeno anauza Akhristuwo kuti: “Tsopano ndikukudandaulirani abale, m’dzina la Ambuye wathu Yesu Khristu, kuti nonse muzilankhula mogwirizana ndi kuti pasakhale magawano pakati panu, koma kuti mukhale ogwirizana pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.” Masiku anonso sitiyenera kulola kuti nkhani zina zitilekanitse.—1 Akor. 1:10-13; werengani Aroma 16:17, 18.

10. Kodi mtumwi Paulo anasonyeza bwanji kuti Akhristu sayenera kulowerera m’mikangano ya m’dzikoli?

10 Paulo analimbikitsa Akhristu odzozedwa kuti azikumbukira kuti iwo ndi nzika zakumwamba osati zapadzikoli. (Afil. 3:17-20) * Anayenera kuchita zinthu ngati akazembe oimira Khristu. Paja akazembe salowerera m’nkhani za m’dziko limene akugwira ntchito chifukwa si dziko lawo. (2 Akor. 5:20) Nawonso Akhristu amene akuyembekezera kudzakhala padziko lapansi ndi nzika za Ufumu wa Mulungu. Choncho iwonso sayenera kulowerera m’mikangano ya m’dzikoli.

TIYENERA KUDZIPHUNZITSA KUKHALA OKHULUPIRIKA KWA YEHOVA

11, 12. (a) Kodi ndi zinthu ziti zimene tiyenera kupewa kuti tikhalebe okhulupirika kwa Mulungu? (b) Kodi mlongo wina anali ndi vuto liti? (c) Kodi anathana nalo bwanji vutolo?

11 M’madera ambiri, anthu amagwirizana chifukwa choti mbiri yawo ndi yofanana komanso ali ndi chikhalidwe ndiponso chilankhulo chimodzi. Iwo amanyadira zinthu zimenezi. Koma Akhristu ayenera kudziphunzitsa kuti asakhale ndi mbali pa nkhani zimene zingalekanitse anthu. Ndiyeno kodi angadziphunzitse bwanji?

12 Kuti tiyankhe funsoli, tiyeni tikambirane nkhani ya mlongo wina dzina lake Mirjeta. * Mlongoyu anachokera m’dziko limene linkatchedwa Yugoslavia ndipo anaphunzitsidwa kuti anthu a ku Serbia ndi oipa. Kenako anaphunzira kuti Yehova alibe tsankho koma Satana ndi amene amayambitsa zosankhana mitundu. Zitatero, anayamba kuyesetsa kuti asamakhale ndi tsankho. Koma kenako m’dera limene ankakhala munayambika zipolowe chifukwa cha tsankho. Izi zinachititsa kuti mlongoyu ayambenso kuipidwa ndi anthu a ku Serbia moti zinkamuvuta kwambiri kuti aziwalalikira. Koma iye anazindikira kuti ayenera kuyesetsa kusintha chifukwa tsankho lakelo silikanatha palokha. Iye anapempha Yehova kuti amuthandize kuthetsa vutoli komanso kuti azilimbikira kulalikira n’cholinga choti ayenerere kukhala mpainiya. Mlongoyu anati: “Ndazindikira kuti kuchita khama pa ntchito yolalikira n’kothandiza kwambiri. Ndikakhala mu utumiki ndimayesetsa kuona anthu mmene Yehova amawaonera ndipo izi zandithandiza kuti ndizikonda aliyense.”

13. (a) Kodi mlongo wina anakumana ndi vuto liti? (b) Kodi anathetsa bwanji vutolo? (c) Nanga ife tikuphunzirapo chiyani?

13 Chitsanzo china ndi cha mlongo wina dzina lake Zoila. Iye anasamuka ku Mexico kupita ku Europe. Ndiyeno mumpingo umene akusonkhana muli abale ena ochokera ku Latin America omwe ananena zinthu zina zonyoza dziko limene mlongoyu amachokera. Ananenanso zinthu zokhudza chikhalidwe ndiponso nyimbo za m’dzikolo. Kodi mukanakhala inuyo mukanatani? Mlongoyu sankamva bwino mumtima mwake. Koma chosangalatsa n’chakuti iye anapempha Yehova kuti amuthandize kuti asamaipidwe nazo. N’zoona kuti enafe tikuvutikabe kuthetseratu mtima wokhumudwa ngati anthu anena zinthu zokhudza kwathu. Choncho tiyeni tizipewa kulankhula kapena kuchita zinthu zimene zingatilekanitse ndi anzathu mumpingo kapena kwina kulikonse.—Aroma 14:19; 2 Akor. 6:3.

14. Kodi Akhristu angadziphunzitse bwanji kuti apewe tsankho kapena mtima wokonda kwambiri dziko lawo?

14 Kodi inuyo mumavutika ndi mtima wa tsankho chifukwa cha kumene munakulira? Kapena kodi mumakonda kwambiri dziko kapena dera lanu? Akhristu sayenera kulola zinthu ngati zimenezi kusokoneza mgwirizano wawo ndi anthu ena. Ndiyeno kodi mungatani ngati mukuona kuti muli ndi kamtima koipidwa ndi anthu amene mukusiyana nawo mayiko, chikhalidwe, chilankhulo kapena mtundu? Ndi bwino kuganizira mmene Yehova amaonera nkhani ya tsankho kapena yokonda kwambiri dziko linalake. Mwina mungafufuze nkhani zimenezi m’mabuku athu n’kumaziphunzira pa Kulambira kwa Pabanja kapena pophunzira Baibulo panokha. Ndiyeno muyenera kupempha Yehova kuti akuthandizeni kukhala ndi maganizo ake pa nkhaniyi.—Werengani Aroma 12:2.

Kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova, tiyenera kukhala olimba mtima zivute zitani (Onani ndime 15 ndi 16)

15, 16. (a) Kodi anthu ena angatani akaona kuti sitikuchita nawo zinthu zina? (b) Kodi makolo angathandize bwanji ana awo kuti akhale okhulupirika kwa Mulungu?

15 Mtumiki wa Yehova aliyense ayenera kudziwa kuti nthawi zina anthu ena angafune kuti iye achite zinthu zosemphana ndi zimene amakhulupirira. Izi zikhoza kuchitika kuntchito, kusukulu, kunyumba kapena kwina kulikonse. (1 Pet. 2:19) Zikatero sitiyenera kuopa kuchita zinthu zosiyana ndi ena. Anthu ena amatida chifukwa cha zimenezi. Koma sitiyenera kudabwa chifukwa Yesu ananeneratu kuti tidzadedwa. Anthu ambiri amene amatitsutsa samvetsa chifukwa chake sitilowerera m’zochitika za m’dzikoli. Koma ife timadziwa kuti nkhaniyi ingasonyeze ngati tili okhulupirika kwa Mulungu kapena ayi.

16 Kuti tikhalebe okhulupirika kwa Yehova, tiyenera kukhala olimba mtima. (Dan. 3:16-18) Aliyense akhoza kuyamba kuopa anthu. Koma achinyamata ndi amene amavutika kwambiri kuchita zinthu zosiyana ndi anzawo. Choncho makolo ayenera kuthandiza ana awo kudziwa zochita ngati atauzidwa kuti aimbe nawo nyimbo yafuko kapena achite zinthu zina zosonyeza kukonda kwambiri dziko lawo. Akhoza kukambirana zimenezi pa Kulambira kwa Pabanja kuti anawo adziwe bwino nkhaniyi n’cholinga choti azitha kuyankha molimba mtima. Ayenera kuwathandizanso kuti azifotokoza zimene amakhulupirira momveka bwino komanso mwaulemu. (Aroma 1:16) Makolo angachitenso bwino kulankhula ndi aphunzitsi a ana awo nkhani ngati zimenezi.

ZINTHU ZONSE ZIMENE YEHOVA ANALENGA N’ZABWINO

17. Kodi tiyenera kupewa maganizo ati? Perekani chifukwa.

17 Mwachibadwa, anthufe timakonda kumene tinachokera, chilankhulo chathu kapena chakudya chimene tinazolowera. Koma tiyenera kupewa maganizo akuti zathuzo n’zabwino kuposa za ena. Yehova analenga zinthu zosiyanasiyana n’cholinga choti tizisangalala. (Sal. 104:24; Chiv. 4:11) Ndiye palibe chifukwa choganizira kuti zina ndi zabwino kapena zapamwamba kuposa zina.

18. Kodi kuona zinthu mmene Yehova amazionera kungatithandize bwanji?

18 Yehova amafuna kuti anthu a mtundu uliwonse adziwe choonadi molondola kuti adzapeze moyo wosatha. (Yoh. 3:16; 1 Tim. 2:3, 4) Kunena zoona, zimakhala zosangalatsa ngati tilolera maganizo osasemphana ndi mfundo za m’Baibulo amene anthu osiyanasiyana angakhale nawo. Izi zimathandizanso kuti tizigwirizana. Tiyeni tiziyesetsa kupewa mikangano ya m’dzikoli n’kumakhalabe okhulupirika kwa Yehova. Si bwino kulola kuti zinthu zina zitilekanitse. Timayamikira kwambiri kuti Yehova amatithandiza kupewa maganizo a m’dziko la Satanali amene amachititsa anthu kukhala atsankho, onyada ndiponso okonda kupikisana. Tiyeni tonse tiziyesetsa kukhala mwamtendere ndi anzathu. Tizitsanzira wamasalimo amene ananena kuti: “Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambiri abale akakhala pamodzi mogwirizana!”—Sal. 133:1.

^ ndime 10 Anthu a ku Filipi ankalamuliridwa ndi Aroma. Ndiyeno mwina anthu ena mumpingo anali nzika za Roma. Choncho iwo ankakhala ndi ufulu wina umene Akhristu anzawo analibe.

^ ndime 12 Mayina ena asinthidwa.