Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Khalanibe Okhulupilika ku Ufumu wa Mulungu

Khalanibe Okhulupilika ku Ufumu wa Mulungu

“Iwo sali mbali ya dziko.”—YOH. 17:16.

NYIMBO: 63, 129

1, 2. (a) N’cifukwa ciani n’kofunika kuti Akhristu azikhala okhulupilika kwa Mulungu? Nanga amafunika kucita bwanji pa nkhani za kukonda dziko? (Onani cithunzi pamwambapa.) (b) Ndi kukhulupilika kotani komwe kwafala m’dzikoli? Ndipo kumakhala ndi zotulukapo zotani?

KUKHALA wokhulupilika ndi kusatengako mbali mundale ndi nkhani imene imakhudza Akristu nthawi zonse ngakhale pamene kulibe nkhondo. N’cifukwa ciani? N’cifukwa cakuti munthu aliyense wodzipeleka kwa Yehova anamulonjeza kukhala wokhulupilika, womvela ndiponso kumukonda. (1 Yoh. 5:3) Ndipo tonse timafuna kutsatila mfundo zolungama za Mulungu mosasamala kanthu za kumene timakhala, kumene tinakulila, dziko lathu kapena mtundu wathu. Kukhala okhulupilika kwa Yehova ndi Ufumu wake kumaposa mmene timakondela cinthu cina ciliconse. (Mat. 6:33) Kuti Akristu akhale okhulupilika afunika kupewa kutengako mbali mu mikangano ndi m’zocitika zina za m’dzikoli.—Yes. 2:4; ŵelengani Yohane 17:11, 15, 16.

2 Anthu ambili m’dzikoli amaona kuti afunika kukhala okhulupilika kwambili ku dziko lao, mtundu wao, kapena cikhalidwe cao, ngakhalenso ku timu yamaseŵela ya m’dziko lao. Anthu ena pofuna kukhala okhulupilika ku mtundu wao amapikisana, kudana ngakhale kuvulazana ndi kuphana. Popeza kuti tikukhala m’dziko lino, zilizonse zimene anthu angacite pofuna kuthetsa nkhani zimenezi zingakhudze ife kapena mabanja athu. Cifukwa cakuti tinapangidwa m’cifanizilo ca Mulungu, timakonda cilungamo. Conco malamulo amene maboma a anthu amapanga nthawi zina angatikhumudwitse. (Gen. 1:27; Deut. 32:4) Kodi tiyenela kucita ciani zimenezi zikaticitikila? Tiyenela kukhala wosamala kuti tisatengemo mbali m’zocitika za m’dzikoli ndi kuyamba mikangano.

3, 4. (a) N’cifukwa ciani Akristu satengamo mbali m’mikangano ya m’dzikoli? (b) Tikambilana ciani m’nkhani ino?

3 Pakabuka mikangano, maboma ena amalimbikitsa nzika zao kutenga mbali m’ndale. Akristu oona sangacite zimenezo. Sititengamo mbali m’ndale za dziko ndipo sitinyamula malupanga. (Mat. 26:52) Sitilola kunyengeleledwa ndi dziko la Satana kuti titengemo mbali m’ndale. (2 Akor. 2:11) Conco, cifukwa cosakhala mbali ya dziko sitiloŵelela m’mikangano ya dziko.—Ŵelengani Yohane 15:18, 19.

4 Cifukwa ca kupanda ungwilo, mwina ena a ife timavutika kuthetsa khalidwe la tsankho limene tinali nalo poyamba. (Yer. 17:9; Aef. 4:22-24) M’nkhani ino tikambilana mfundo zimene zingatithandize kuthetsa khalidwe la tsankho. Tikambilananso zimene tingacite kuti maganizo ndi cikumbumtima cathu zizitithandiza kukhala okhulupilika ku Ufumu wa Mulungu.

CIFUKWA CAKE SITITENGAMO MBALI M’ZOCITIKA ZA M’DZIKOLI

5, 6. Kodi Yesu anali kucita ciani ndi mikangano ya anthu a m’nthawi yake? Ndipo n’cifukwa ciani?

5 Ngati pacitika zina zake ndipo simukudziŵa coyenela kucita, kungakhale kwanzelu kudzifunsa kuti, ‘Kodi Yesu akanacita ciani pamenepa?’ M’dziko limene Yesu anali kukhala munali anthu ocokela m’madela osiyanasiyana monga a ku Yudeya, Galileya, Samariya ndi kumadela ena. Baibulo limanena kuti anthu a m’madela amenewa anali kukangana. (Yoh. 4:9) Afarisi ndi Asaduki anali kukangana kwambili. (Mac. 23:6-9) Anthu ena anali kudana ndi okhometsa msonkho. (Mat. 9:11) Ndipo anthu odziŵa cilamulo anali kuona anthu osadziŵa Cilamulo kukhala otembeleledwa. (Yoh. 7:49) M’nthawi ya atumwi, Aisiraeli anali kudana kwambili ndi Aroma amene anali kuwalamulila. Ngakhale kuti Yesu anali kuphunzitsa coonadi ndipo anali kudziŵa kuti cipulumutso cikucokela kwa Ayuda, sanalimbikitse atumwi ake kudana ndi mitundu ina. (Yoh. 4:22) M’malomwake, anawalimbikitsa kukonda anthu onse monga anansi ao.—Luka 10:27.

6 N’cifukwa ciani Yesu sanali kulimbikitsa Ayuda kudana ndi anthu ena? N’cifukwa cakuti iye ndi Atate ake saloŵelela m’mikangano ya m’dzikoli. Colinga ca Yehova pamene analenga anthu kudzela mwa Yesu cinali cakuti adzaze dziko lonse. (Gen. 1:27, 28) Mulungu analenga anthu m’njila yakuti azitha kubeleka anthu a mitundu yosiyanasiyana. Yehova ndi Yesu saona kuti mtundu wina, dziko lina, kapena cinenelo cina ndi zapamwamba kuposa zina. (Mac. 10:34, 35; Chiv. 7:9, 13, 14) Ifenso tiyenela kutsanzila citsanzo cao cabwino cimeneci.—Mat. 5:43-48.

7, 8. (a) Ndi nkhani iti imene Akristu ayenela kutengamo mbali? (b) Kodi Akristu ayenela kudziŵa ciani pankhani yothetsa mikangano?

7 Koma nkhani imene tiyenela kutengamo mbali ndi yokhudza ulamulilo wa Yehova wa cilengedwe conse. Satana anayambitsa mkangano mu Edeni pamene anatsutsa ulamulilo wa Yehova. Conco, aliyense afunika kusankha kuti wolamulila wabwino ndi uti pakati pa Mulungu ndi Satana. Kodi mumasankha kukhala ku mbali ya Yehova mwa kumvela malamulo ndi mfundo zake m’malo mocita zinthu mmene mukufunila? Kodi mumaona kuti Ufumu wake ndiwo wokha umene udzathetsa mavuto onse a anthu? Kapena mumakhulupilila kuti anthu akhoza kudzilamulila okha?—Gen. 3:4, 5.

8 Mayankho anu pa mafunso amenewa angaonetse zimene mudzacite anthu akadzakupemphani kuti munenepo maganizo anu pa nkhani za mikangano. Anthu andale kwa nthawi yaitali akhala akufunafuna njila zimene angathetsele mikangano. N’zoona kuti amacita zimenezi ndi zolinga zabwino. Koma Akristu oona amadziŵa kuti ndi Ufumu wa Mulungu wokha umene udzathetsa mavuto onse a anthu ndi kubweletsa cilungamo ceniceni. Komanso tonse timatsatila malangizo a Yehova m’malo moti aliyense azicita zimene aona kuti ndiye zabwino. N’cifukwa cake ndife ogwilizana.

9. Ndi vuto lotani limene linabuka mumpingo wa ku Korinto? Nanga Paulo anawauza ciani pofuna kuthetsa vuto limenelo?

9 Onani mmene Akristu akale anacitila pamene mumpingo wao munabuka mikangano. Anthu a ku Korinto anali kunena kuti: “‘Ine ndine wa Paulo,’ ena amati, ‘Ine ndine wa Apolo,’ enanso amati ‘Ine ndine wa Kefa’, pamene ena amati, ‘Ine ndine wa Khristu.’” Sitikudziŵa cimene cinayambitsa mkanganowo, koma Paulo mokhumudwa anawauza kuti: ‘Kristu wakhala wogawanika’ pakati panu. Kodi vuto limenelo likanathetsedwa bwanji? Paulo analangiza Akristuwo kuti: “Tsopano ndikukudandaulilani abale, m’dzina la Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti nonse muzilankhula mogwilizana ndi kuti pasakhale magaŵano pakati panu, koma kuti mukhale ogwilizana pokhala ndi mtima umodzi ndi maganizo amodzi.” Conco, masiku ano mumpingo wacikristu simuyenela kukhala magaŵano a mtundu uliwonse.—1 Akor. 1:10-13; ŵelengani Aroma 16:17, 18.

10. Ndi citsanzo cotani cimene mtumwi Paulo anapeleka coonetsa cifukwa cake Akristu sayenela kutengamo mbali m’mikangano ya m’dzikoli?

10 Paulo analangiza Akristu odzozedwa kuti ayenela kuika maganizo ao pa kukhala nzika zakumwamba osati pa zinthu za dziko lapansi. (Afil. 3:17-20) * Iwo anafunikila kucita zinthu monga akazembe m’malo mwa Kristu. Akazembe saloŵelela m’zocitika za m’dziko limene atumidwa kukatumikilako. Iwo amafunikila kukhala okhulupilika ku dziko lao. (2 Akor. 5:20) Akristu amene ali ndi ciyembekezo codzakhala pano pa dziko lapansi naonso ndi nzika za Ufumu wa Mulungu. Conco, sayenela kutengamo mbali m’mikangano ya m’dzikoli.

PHUNZILANI KUKHALA OKHULUPILIKA KWA YEHOVA

11, 12. (a) Ndi zinthu zotani zimene zingacititse Akristu kuvutika kukhalabe okhulupilika ku Ufumu wa Mulungu? (b) Ndi vuto lotani limene Mkristu wina anakumana nalo? Ndipo anacita ciani kuti alithetse?

11 M’madela ambili padziko lapansi, anthu amagwilizana kwambili cifukwa cokhala ndi mbili yofanana, cikhalidwe ndi cinenelo cofanana ndipo zimenezi amazinyadila. Akristu amene ali m’madela amenewo amafunika kuphunzitsa maganizo ao ndi cikumbumtima cao kuti azicita zinthu mwanzelu ngati pabuka mikangano pakati pa mitundu yosiyana. Kodi angacite bwanji zimenezi?

12 Ganizilani citsanzo ca mlongo wina dzina lake Mirjeta * amene amakhala ku dziko limene poyamba linali Yugoslavia. Kucokela ali mwana iye anaphunzitsidwa kuzonda anthu a ku dziko la Serbia. Ataphunzila kuti Yehova alibe tsankho ndi kuti Satana ndiye amacititsa kuti anthu a mitundu yosiyana azidana, anayesetsa kuthetsa maganizo a tsankho. Koma pamene anthu m’dela lake anayamba kucita ciwawa cifukwa cosiyana mitundu, maganizo a tsankho anayambanso kukula mumtima mwake. Izi zinacititsa kuti Mirjeta azivutika kulalikila anthu a ku Serbia. Iye anaona kuti afunika kucitapo kanthu kuti athetse maganizo olakwika amenewa. Conco anacondelela Yehova kuti amuthandize kuthetsa vutoli ndi kuonjezela utumiki wake kuti ayenelele kukhala mpainiya wa nthawi zonse. Iye anati “Kunena zoona kuika maganizo pa utumiki kwandithandiza kwambili kuthetsa vuto limenelo. Ndikakhala muutumiki, ndimayesetsa kutsanzila makhalidwe acikondi a Yehova ndipo maganizo anga olakwikawo anathelatu.”

13. (a) N’ciani cinacititsa Mkristu wina kukhumudwa? Koma anacita ciani? (b) Kodi zimene zinacitikila Zoila zikutiphunzitsa ciani?

13 Ganizilaninso citsanzo ca Zoila. Iye anabadwila m’dziko lina la ku Mexico, koma tsopano amasonkhana mumpingo wina ku Ulaya. Iye ananena kuti abale ena a mumpingowo ocokela ku Latin America anali kunena mau oipa okhudza dziko limene iye anabadwila, cikhalidwe ca kwao ngakhalenso nyimbo za m’dzikolo. Kodi mukanakhala inu mukanacita ciani? N’zomveka kuti mau amenewo anali kumukhumudwitsa Zoila. Koma iye anapempha Yehova kuti amuthandize kuthetsa maganizo olakwika amene anayamba kukhala nao mumtima mwake. N’zoonekelatu kuti ena a ife tikali kulimbana ndi maganizo a tsankho. Sitiyenela kukamba kapena kucita zinthu zimene zingayambitse magaŵano ndi kulimbikitsa mzimu watsankho pakati pathu.—Aroma 14:19; 2 Akor. 6:3.

14. Kodi Akristu angaphunzitse bwanji maganizo ao ndi cikumbumtima cao kuti apewe tsankho?

14 Kodi mmene munaleledwela kapena malo amene mumakhala zinali kukucititsani kukonda kwambili dela kapena dziko lanu? Kodi mukali ndi maganizo otelo? Akristu sayenela kulola tsankho kuwacititsa kuona anthu ena molakwika. Nanga bwanji ngati mwadziŵa kuti muli ndi maganizo olakwika ponena za anthu a m’dziko lina, a cikhalidwe ndi cinenelo cina kapena a fuko lina? Kuti muthetse vuto limeneli, muyenela kusinkhasinkha mmene Yehova amaonela khalidwe la tsankho. Muyenelanso kuphunzila nkhani imeneyi ndi zina zokhudzana ndi imeneyi pa phunzilo lanu laumwini kapena pa kulambila kwa pabanja. Ndipo muzicondelela Yehova kuti akuthandizeni kutsatila mfundo zake pankhaniyi.—Ŵelengani Aroma 12:2.

Kukhala okhulupilika kwa Yehova kumafuna kucita zinthu molimba mtima anthu akatiopseza (Onani ndime 15 ndi 16)

15, 16. (a) Kodi anthu ena adzacita ciani akaona kuti ndife okhulupilika kwa Mulungu? (b) Kodi makolo angathandize bwanji ana ao kukhala okhulupilika akakumana ndi ziyeso?

15 Nthawi ina iliyonse, mtumiki wa Yehova angakumane ndi ciyeso, ndipo angafunike kucita zinthu mosiyana ndi anzake a kunchito, a kusukulu, acibanja, ndi ena. (1 Pet. 2:19) Inde, tifunikadi kukhala osiyana ndi dzikoli. Sitiyenela kudabwa tikaona kuti dziko likudana nafe cifukwa ca zimene timakhulupilila popeza kuti Yesu anaticenjezelatu za zimenezi. Adani athu sadziŵa kapena kumvetsetsa cifukwa cake sititengamo mbali m’zinthu za dzikoli. Koma kwa ife nkhaniyi ndi yofunika kwambili.

16 Kukhala okhulupilika kwa Yehova kumafuna kucita zinthu molimba mtima anthu akatiopseza. (Dan. 3:16-18) Anthu a msinkhu uliwonse angaope akaopsezedwa, koma acicepele ndi amene amaopa kwambili kucita zinthu mosiyana ndi anzao. Ngati ana anu akukumana ndi ziyeso monga kuuzidwa kuimba nao nyimbo yafuko kapena kucita zikondwelelo za dziko, muyenela kuwathandiza mwamsanga. Pa Kulambila kwa Pabanja, muzithandiza ana anu kumvetsa nkhani zimenezi n’colinga cakuti azicita zinthu molimba mtima akayesedwa kuti acite zimenezi. Athandizeni kuti azitha kufotokoza zimene amakhulupilila momveka bwino ndiponso mwaulemu. (Aroma 1:16) Muziyesetsa kukambilana ndi aphunzitsi ao za nkhani zimenezi ngati m’pofunika kutelo.

MUZIKONDA ZONSE ZIMENE YEHOVA ANAPANGA

17. Ndi maganizo ati amene tiyenela kupewa? Nanga n’cifukwa ciani?

17 N’zomveka kuti mwacibadwa timakonda malo athu, cikhalidwe ndi cinenelo cathu, kapenanso zakudya za m’dziko limene tinakulila. Komabe, tiyenela kupewa maganizo akuti, “Zinthu zanga ndi za m’dziko langa ndiye zabwino kuposa zonse.” Yehova analenga zinthu za mitundu yosiyanasiyana n’colinga cakuti tizisangalala. (Sal. 104:24; Chiv. 4:11) Conco n’kupanda nzelu kuganiza kuti zimene ife timacita ndiye zabwino kuposa zimene ena amacita.

18. Kodi kuona zinthu mmene Yehova amazionela kumabweletsa madalitso otani?

18 Mulungu afuna kuti anthu a mitundu yonse adziŵe coonadi molondola ndi kuti adzasangalale ndi moyo wosatha. (Yoh. 3:16; 1 Tim. 2:3, 4) Kulemekeza maganizo a anthu ena kudzatithandiza kusunga mgwilizano wathu wacikristu. Pamene tipitilizabe kukhala okhulupilika kwa Yehova tifunika kupewa kutengamo mbali m’mikangano ya m’dzikoli. Akristu sayenela kucilikiza kapena kuloŵa m’zipani za ndale. Ndife oyamikila kuti Yehova akutithandiza kupewa zinthu zoyambitsa magaŵano, kunyada ndi mpikisano zimene zafala m’dziko la Satanali. Tiyeni tiyesetse kukhala amtendele, ndipo tidzamva monga mmene wamasalimo anamvela pamene ananena kuti: “Taonani! Ndi zabwino komanso zosangalatsa kwambili Abale akakhala pamodzi mogwilizana!”—Sal. 133:1.

^ par. 10 Filipi linali dela lolamulidwa ndi ufumu wa Roma. Zioneka kuti Akristu ena mumpingo wa kumeneko anapatsidwa mwai wokhala nzika za Roma. Cifukwa cakuti anakhala nzika anali ndi mwai wocita zinthu zina zimene abale ena sanaloledwe kucita.

^ par. 12 Maina ena asinthidwa.