Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Muzisinkhasinkha za Cikondi Cosatha ca Yehova

Muzisinkhasinkha za Cikondi Cosatha ca Yehova

“Ndidzasinkhasinkha za nchito zanu zonse.”—SAL. 77:12.

NYIMBO: 18, 61

1, 2. (a) N’cifukwa ciani simukaikila kuti Yehova amakonda anthu ake? (b) Kodi anthu mwacibadwa amafuna ciani?

N’CIFUKWA ciani ndinu wotsimikiza mtima kuti Yehova amakonda anthu ake? Musanayankhe funsoli, ganizilani zitsanzo izi: Kwa zaka zambili, Akristu ena anali kulimbikitsa mlongo wina dzina lake Taylene kuti asamadzikaikile koma kuti azicita zimene angakwanitse. Iye anati: “Ndikuona kuti Yehova amandikonda kwambili, n’cifukwa cake anandipatsa malangizo mobwelezabweleza.” Mlongo winanso dzina lake Brigitte, amene analela yekha ana aŵili pambuyo pakuti mwamuna wake wamwalila anati: “Kulela ana m’dziko la Satanali n’cimodzi mwa zinthu zovuta kwambili makamaka ngati ukuwalela wekha. Koma sindikaikila kuti Yehova amandikonda cifukwa ananditsogolela ngakhale pa nthawi zovuta kwambili. Sanandilole kuti ndiyesedwe kufika pamene sindingapilile.” (1 Akor. 10:13) Sandra nayenso akuvutika ndi matenda osacilitsika. Pa msonkhano wina wacigawo, mlongo wina anam’citila zinthu zabwino. Mwamuna wa Sandra anakamba kuti: “Ngakhale kuti mlongoyu sitinali kumudziŵa bwino, zinthu zimene anaticitila zinatisangalatsa kwambili. Abale ndi alongo akaticitila zinthu zabwino ngakhale n’zocepa, zimandionetsa kuti Yehova amatikonda.”

2 Anthu mwacibadwa amafuna kukonda ena ndiponso kukondedwa. Komabe, zimakhala zosavuta kukhumudwa cifukwa ca matenda, kusoŵa ndalama, kapena cifukwa cakuti sitikupeza anthu acidwi mu ulaliki. Ngati tayamba kuona kuti Yehova satikonda, tiyenela kukumbukila kuti ndife a mtengo wapatali kwa Yehova, ndiponso kuti iye ‘wagwila dzanja lathu lamanja’ kuti atithandize. Iye sadzatiiŵala ngati ndife okhulupilika kwa iye.—Yes. 41:13; 49:15.

3. N’ciani cingatithandize kukhala otsimikiza mtima kuti cikondi ca Yehova kwa ife n’cosatha?

3 Alongo amene tawachula m’ndime zapitazi sakukaikila kuti Mulungu anali nao panthawi ya mavuto. Nafenso tifunika kukhulupilila kuti Mulungu ali kumbali yathu. (Sal. 118:6, 7) Nkhani ino ifotokoza zinthu zinai zimene zionetsa kuti Mulungu amatikonda. Zinthu zimenezi ndi (1) cilengedwe cake, (2) Mau ake ouzilidwa, (3) pemphelo, ndi (4) dipo. Kusinkhasinkha pa zinthu zabwino zimene Yehova waticitila kudzatithandiza kuyamikila kwambili cikondi cake cosatha.—Ŵelengani Salimo 77:11, 12.

MUZISINKHASINKHA ZA CILENGEDWE CA YEHOVA

4. Kodi cilengedwe cimatiphunzitsa ciani ponena za Yehova? (Onani cithunzi kuciyambi kwa nkhani ino.)

4 Tikayang’ana cilengedwe ca Yehova, timaona umboni wakuti iye amatikonda kwambili. (Aroma 1:20) Iye analenga dzikoli m’njila yakuti tizisangalala ndi moyo. Koma kuti tipitilizebe kukhala ndi moyo, timafunika cakudya. Yehova analenga zipatso ndi zakudya zina za mitundumitundu ndiponso zokoma kuti tizidya. Ndipo si zokhazo ai, iye anatilenganso m’njila yakuti tizitha kusangalala ndi zakudya. (Mlal. 9:7) Mlongo wina wa ku Canada dzina lake Catherine, amasangalala kwambili kuyang’ana cilengedwe, makamaka m’nyengo imene zinthu zimaphukila. Iye ananena kuti: “Panthawiyi ndimacita cidwi kwambili kuona maluwa akuphukila, mbalame zikubwelela kucoka kutali kumene zinapita, kuphatikizapo kambalame kakang’ono kooneka ngati kacoso (kasongwe) kamene kamabwela kudzadyela panyumba panga. Ndikaona zonsezi, ndimadziŵa kuti Yehova amatikonda kwambili.” Atate wathu wakumwamba ndi wacikondi. Iye amasangalala ndi zinthu zimene analenga, ndipo amafuna kuti nafenso tizisangalala nazo.—Mac. 14:16, 17.

5. Kodi cikondi ca Yehova cimaonekela bwanji ndi mmene analengela anthu?

5 Yehova anatilenga m’njila yakuti tizitha kugwila nchito mwakhama kuti tizisangalala ndi moyo. (Mlal. 2:24) Colinga cake cinali cakuti anthu aculuke, adzaze dziko lapansi, ayang’anile nsomba, mbalame, ndi zamoyo zonse. (Gen. 1:26-28) N’zosangalatsa kwambili kuti Yehova anatilenganso ndi makhalidwe amene amatithandiza kumutsanzila.—Aef. 5:1.

MUZIKONDA MAU A MULUNGU

6. N’cifukwa ciani tifunika kuyamikila kwambili Mau a Mulungu?

6 Mulungu waonetsa kuti amatikonda kwambili mwa kutipatsa Mau ake ouzilidwa. Mau ake amatiuza za iye ndiponso mmene amacitila zinthu ndi anthu. Mwacitsanzo, Malemba amatiuza mmene anali kucitila zinthu ndi Aisiraeli ngakhale kuti nthawi zambili io sanali kumumvela. Lemba la Salimo 78:38 limati: “Anawamvela cifundo. Anali kukhululukila macimo ao ndipo sanali kuwaononga. Nthawi zambili anali kubweza mkwiyo wake, ndipo sanali kuwasonyeza ukali wake wonse.” Kuganizila vesi limeneli kudzatithandiza kuyamikila kwambili Yehova cifukwa ca cikondi ndi cisamalilo cimene amationetsa. Tisamakaikile kuti Yehova amatikonda kwambili.—Ŵelengani 1 Petulo 5:6, 7.

7. N’cifukwa ciani tiyenela kulikonda kwambili Baibulo?

7 Tifunika kukonda kwambili Baibulo cifukwa ndiye njila yaikulu imene Mulungu amalankhulila nafe. Makolo amafunika kulankhulana momasuka ndi ana ao kuti azikondana ndi kukhulupililana. Kodi Yehova amalankhula nafe bwanji? Ngakhale kuti sitinamuonepo kapena kumva mau ake, iye “amalankhula” nafe kupitila m’Mau ake ouzilidwa, ndipo ife timafunika kumumvela. (Yes. 30:20, 21) Popeza kuti tinadzipeleka kwa Yehova, iye amafuna kuti azititsogolela ndi kutiteteza kuti tisavulale mwakuuzimu. Amafunanso kuti timudziŵe ndi kum’khulupilila.—Ŵelengani Salimo 19:7-11; Miyambo 1:33.

Ngakhale kuti Yehova kupitila mwa Yehu anapatsa uphungu Yehosafati, sanalephele kuona “zinthu zabwino” mwa mfumuyo (Onani ndime 8 ndi 9)

8, 9. Kodi Yehova afuna kuti tidziŵe ciani? Pelekani citsanzo ca m’Baibulo.

8 Yehova afuna kuti tidziŵe kuti amatikonda, ndi kuti sayang’anitsitsa pa zolakwa zathu. Koma amayesetsa kuona zabwino mwa ife. (2 Mbiri 16:9) Mwacitsanzo, iye anaona zabwino zimene Mfumu Yehosafati ya Yuda inacita. Panthawi ina, Yehosafati anacita zinthu mopanda nzelu mwa kugwilizana ndi Mfumu Ahabu ya Isiraeli pankhondo yofuna kulandanso mzinda wa Ramoti-giliyadi m’manja mwa Asiriya. Ngakhale kuti aneneli onyenga 400 anatsimikizila Ahabu kuti adzapambana nkhondoyo, mneneli woona wa Yehova, Mikaya, anakambilatu kuti Ahabu adzagonjetsedwa. Ahabu anafa pankhondoyo, koma Yehosafati anapulumuka ngakhale kuti anatsala pang’ono kuphedwa. Yehosafati atabwelela ku Yerusalemu, Yehu mwana wa Haneni, wamasomphenya anamudzudzula cifukwa cogwilizana ndi Ahabu pankhondoyo. Ngakhale zinali conco, Yehu anauzanso Yehosafati kuti: “Pali zinthu zabwino zimene zapezeka mwa inu.”—2 Mbiri 18:4, 5, 18-22, 33, 34; 19:1-3.

9 Kuciyambi kwa ulamulilo wake, Yehosafati analamula akalonga, Alevi, ndi ansembe kuti apite m’mizinda yonse ya Yuda kukaphunzitsa anthu Cilamulo ca Yehova. Zimenezi zinathandiza kwambili cakuti anthu a m’madela onse ozungulila Yuda anayamba kuopa Yehova. (2 Mbiri 17:3-10) Ngakhale kuti Yehosafati anacita zinthu mopanda nzelu, Yehova sanaiŵale zabwino zimene anacita poyamba. Nkhani ya m’Baibulo imeneyi imatikumbutsa kuti ngakhale kuti ndife opanda ungwilo, Yehova adzapitilizabe kutionetsa cikondi cake cosatha ngati timayesetsa kucita zinthu zom’kondweletsa.

MUZIYAMIKILA MWAI WA PEMPHELO

10, 11. (a) N’cifukwa ciani tingakambe kuti pemphelo ndi mwai wamtengo wapatali wocokela kwa Yehova? (b) Kodi Mulungu amayankha bwanji mapemphelo athu?

10 Tate wacikondi amamvetsela pamene ana ake akukamba naye. Amafuna kudziŵa zimene zimawadetsa nkhawa cifukwa amawakonda. Nayenso Atate wathu wakumwamba, Yehova, amatimvela tikamakamba naye kupitila m’pemphelo, umene ndi mwai wamtengo wapatali.

11 Tingapemphele kwa Yehova nthawi iliyonse. Iye sanaike malile a nthawi imene tiyenela kukamba naye. Iye ndi Bwenzi lathu limene ndi lokonzeka nthawi zonse kumvetsela zokamba zathu. Taylene, amene tamuchula poyamba paja, anati: “Munthu angauze Mulungu ciliconse cimene akufuna.” Ngati tiuza Mulungu zakukhosi kwathu kupyolela mpemphelo, iye amayankha mapemphelo athu kupitila m’Baibulo, m’magazini athu, kapena pogwilitsila nchito Akristu anzathu. Yehova amamva mapemphelo athu ndipo amatimvetsetsa kuposa munthu wina aliyense. Umenewu ndi umboni wakuti ali ndi cikondi cosatha kwa ife.

12. N’cifukwa ciani tiyenela kuŵelenga mapemphelo olembedwa m’Baibulo? Pelekani citsanzo.

12 Tingaphunzile zambili tikamaŵelenga mapemphelo olembedwa m’Baibulo. Nthawi zina, tingacite bwino kukambilana mapemphelo amenewa pa nthawi ya kulambila kwa pabanja. Kuganizila mmene atumiki a Yehova akale anali kufotokozela maganizo ao kwa Mulungu kungatithandize kupeleka mapemphelo atanthauzo. Mwacitsanzo, mungaŵelenge pemphelo losonyeza kulapa limene Yona anapeleka pamene anali m’mimba mwa cinsomba. (Yona 1:17–2:10) Mungaŵelengenso pemphelo locokela pansi pa mtima limene Solomo anapeleka kwa Yehova popeleka kacisi. (1 Maf. 8:22-53) Komanso, mungasinkhesinkhe za pemphelo lacitsanzo limene Yesu anapeleka. (Mat. 6:9-13) Koposa zonse, “zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu.” Mukatelo, “mtendele wa Mulungu umene umaposa kuganiza mozama kulikonse, udzateteza mitima yanu ndi maganizo anu.” Zimenezi zidzatithandiza kuti tiziyamikila kwambili cikondi cosatha cimene Yehova amatisonyeza.—Afil. 4:6, 7.

MUZIYAMIKILA DIPO

13. Ndi mwai wotani umene anthu ali nao cifukwa ca mphatso ya dipo?

13 Dipo la Yesu ndi mphatso yathu yamtengo wapatali. Mphatso imeneyi inapelekedwa n’colinga cakuti ‘tidzapeze moyo.’ (1 Yoh. 4:9) Ponena za mphatso imeneyi, mtumwi Paulo analemba kuti: “Kristu anafela anthu osapembedza Mulungu pa nthawi yoikidwilatu. Pakuti n’capatali kuti munthu wina afele munthu wolungama. Zoonadi, mwina wina angalimbe mtima kufela munthu wabwino. Koma Mulungu akuonetsa cikondi cake kwa ife, moti pamene tinali ocimwa, Kristu anatifela.” (Aroma 5:6-8) Dipo ndi umboni waukulu koposa wakuti Mulungu amatikonda kwambili. Ndipo mphatso imeneyi inatsegula mwai wakuti anthu azitha kukhala pa ubwenzi ndi Yehova.

14, 15. Kodi dipo limapindulitsa bwanji (a) Akristu odzozedwa? (b) a nkhosa zina?

14 Pali anthu ena ocepa amene Yehova anawasonyeza cikondi cake cosatha m’njila yapadela kwambili. (Yoh. 1:12, 13; 3:5-7) Cifukwa codzozedwa ndi mzimu woyela, anthu amenewa amachedwa “ana a Mulungu.” (Aroma 8:15, 16) Paulo anakamba kuti Akristu odzozedwa ‘anawakweza ndi kuwakhazika pamodzi m’malo akumwamba mogwilizana ndi Kristu Yesu.’ (Aef. 2:6) Iwo anapatsidwa mwai umenewu cifukwa cakuti ‘anaikidwa cidindo ca mzimu woyela wolonjezedwawo, umene ndi cikole ca coloŵa cao cam’tsogolo,’ kutanthauza ‘ciyembekezo codzalandila zimene awasungila kumwamba.’—Aef. 1:13, 14; Akol. 1:5.

15 Koma anthu ambili amene amakhulupilila dipo, ali ndi mwai wokhala mabwenzi a Yehova. Mtsogolo io adzakhala ana a Mulungu, ndiponso adzakhala ndi moyo wosatha m’Paladaiso pano padziko lapansi. Conco, kupitila m’nsembe ya dipo, Yehova anaonetsa kuti amakonda anthu. (Yoh. 3:16) Ngati tili ndi ciyembekezo codzakhala ndi moyo wosatha padziko lapansi tiyenela kupitilizabe kutumikila Yehova mokhulupilika. Tikatelo, sitiyenela kukaikila kuti iye adzatidalitsa kwambili m’dziko latsopano. Conco, m’pomveka kunena kuti dipo ndi umboni waukulu wakuti Mulungu amatikonda kwambili.

MUZIYAMIKILA CIKONDI CA YEHOVA

16. Kodi kuganizila zinthu zimene Yehova amaticitila kungatithandize bwanji?

16 Sitingakwanitse kuchula zinthu zonse zimene Yehova amaticitila cifukwa ca cikondi cake cosatha. Wamasalimo Davide anaimba kuti: “Kwa ine maganizo anu ndi ofunika kwambili, inu Mulungu, ndipo ndi oculuka zedi. Nditati ndiyese kuwaŵelenga, angakhale oculuka kwambili kuposa mcenga.” (Sal. 139:17, 18) Tiyenela kuganizila zinthu zabwino zimene Yehova amaticitila cifukwa ca cikondi cake. Kucita zimenezi kudzatithandiza kuti tiyambe kumukonda kwambili. Motelo, tifunika kucita zonse zimene tingathe pom’tumikila.

17, 18. Tingaonetse motani kuti timakonda Mulungu?

17 Pali zinthu zambili zimene tingacite zoonetsa kuti timakonda Yehova. Mwacitsanzo, timaonetsa kuti timakonda Mulungu ndi anzathu mwa kugwila mwakhama nchito yolalikila uthenga wa Ufumu. (Mat. 24:14; 28:19, 20) Timaonetsanso kuti timakonda kwambili Yehova mwa kukhalabe okhulupilika tikakumana ndi mayeselo. (Ŵelengani Salimo 84:11; Yakobo 1:2-5.) Tikakumana ndi mayeselo aakulu, sitiyenela kukaikila kuti Mulungu amaona mavuto athu, ndi kuti adzatithandiza cifukwa ndife amtengo wapatali kwa iye.—Sal. 56:8.

18 Kukonda Yehova kumatilimbikitsa kusinkhasinkha za cilengedwe cake ndi nchito zake zodabwitsa. Timasonyeza kuti timakonda Mulungu ndi Mau ake mwa kuphunzila Baibulo mwakhama. Kukonda Yehova kudzatithandiza kuti tizipemphela kwa iye nthawi zonse. Ndiponso, cikondi cathu pa Mulungu cimakula tikamasinkhasinkha za nsembe ya dipo imene iye anapeleka kaamba ka macimo athu. (1 Yoh. 2:1, 2) Izi ndi zina mwa zinthu zambili zimene tingacite zoonetsa kuti timakonda Yehova cifukwa ca cikondi cake cosatha.