Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Tizikonzekera Moyo wa M’dziko Latsopano

Tizikonzekera Moyo wa M’dziko Latsopano

“Uwalamule kuti azichita zabwino . . . kuti agwire mwamphamvu moyo weniweniwo.”—1 TIM. 6:18, 19.

NYIMBO: 125, 40

1, 2. Kodi ndi zinthu ziti zimene inuyo mukuyembekezera m’dziko latsopano (a) zokhudza anthu? (Onani chithunzi pamwambapa.) (b) zokhudza Yehova?

AMBIRIFE tikamva mawu akuti “moyo weniweniwo” timaganizira za moyo wosatha m’dziko latsopano. Paja mtumwi Paulo anagwiritsa ntchito mawu akuti “moyo weniweniwo “ ponena za “moyo wosatha.” (Werengani 1 Timoteyo 6:12, 19.) Tikuyembekezera kudzakhala ndi moyo mpaka muyaya ndipo tidzasangalala. Tsiku lililonse tizidzadzuka thupi lathu lili bwinobwino, tili osangalala ndiponso tikuganiza bwino. (Yes. 35:5, 6) Zidzakhala zosangalatsa kucheza ndi achibale, anzathu ngakhalenso anthu amene aukitsidwa. (Yoh. 5:28, 29; Mac. 24:15) Tidzakhalanso ndi mwayi wophunzira zinthu monga zasayansi, nyimbo ndi zomangamanga.

2 Koma tiyenera kukumbukira kuti zinthu zofunika kwambiri zimene zidzachitike m’dziko latsopano ndi zokhudza Yehova. Tidzasangalala podziwa kuti dzina lake layeretsedwa ndiponso wasonyeza kuti ndi woyeneradi kulamulira. (Mat. 6:9, 10) Tidzakhalanso ndi mwayi woona cholinga chake chokhudza anthu padzikoli chikukwaniritsidwa. Pa nthawiyi zidzakhala zosavuta kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova chifukwa uchimo udzayamba kuchepa mpaka kutheratu.—Sal. 73:28; Yak. 4:8.

3. Kodi tiyenera kuyamba kukonzekera chiyani panopa?

3 N’zotheka kudzapeza madalitso amenewa. Paja Yesu ananena kuti ‘zinthu zonse n’zotheka ndi Mulungu.’ (Mat. 19:25, 26) Koma kuti tidzakhaledi m’dzikolo n’kudzalandira moyo wosatha, tiyenera kuyamba panopa kukonzekera. Tikatero tidzakhala ngati ‘tikugwira mwamphamvu moyo weniweniwo.’ Koma kodi tingachite bwanji zimenezi popeza tidakali m’dziko loipali?

KODI TINGAKONZEKERE BWANJI?

4. Perekani chitsanzo chosonyeza zimene tingachite pokonzekera moyo wa m’dziko latsopano.

4 Kodi tingakonzekere bwanji moyo wa m’dziko latsopano? Kuti tiyankhe, tiyeni tiyerekezere kuti tikufuna kusamukira m’dziko lina. Mwina pokonzekera tingayambe kuphunzira chilankhulo ndi chikhalidwe cha m’dzikolo. Mwina tingayesenso kudya chakudya cha kumeneko. Pokonzekera, tingayesetse kuchita zinthu ngati kuti tasamukira kale m’dzikolo. N’chimodzimodzi ndi moyo wa m’dziko latsopano. Tiyenera kuyamba panopa kuchita zinthu ngati tili kale m’dzikolo. Kodi ndi zinthu ziti zimene tingachite?

5, 6. Kodi kugonjera malangizo a gulu kungatithandize bwanji kukonzekera moyo wa m’dziko latsopano?

5 M’dziko la Satanali anthu ambiri safuna kuuzidwa zochita ndipo zotsatira zake zimakhala zoipa kwambiri. Kusamvera Mulungu kwayambitsa mavuto osaneneka. (Yer. 10:23) Koma m’dziko latsopano aliyense azidzagonjera ulamuliro wa Mulungu ndipo zidzakhala zosiyana kwambiri ndi dziko la Satanali. Timalakalaka kwambiri nthawi imene anthu onse azidzamvera Mulungu wathu wachikondi.

6 Zidzakhala zosangalatsa pamene Yehova azidzatitsogolera kuti tikongoletse dzikoli, tiphunzitse anthu oukitsidwa komanso tithandize pokwaniritsa cholinga chake. Koma kodi pa nthawiyo tidzalolera kugwira ntchito imene sitisangalatsa? Kodi tidzagonjera n’kumaigwira mosangalala? Mwina tayankha kale kuti inde. Koma funso ndi lakuti, kodi tayamba kale kugonjera malangizo amene gulu la Yehova limapereka? Ngati timatero, ndiye kuti tikukonzekera moyo wa m’dziko latsopano.

7, 8. (a) N’chifukwa chiyani tiyenera kukhala omvera? (b) Kodi zinthu zasintha bwanji pa moyo wa Akhristu ena? (c) Kodi sitiyenera kukayikira chiyani tikamaganizira za moyo wa m’dziko latsopano?

7 Tingakonzekerenso moyo wa m’dziko latsopano poyesetsa kukhala ndi mtima womvera ndiponso wokhutira ndi zimene tili nazo. Ngati masiku ano timamvera amene akutitsogolera n’kumagwira mosangalala ntchito zatsopano zimene tingapatsidwe, ndiye kuti tidzateronso m’dziko latsopano. (Werengani Aheberi 13:17.) Aisiraeli atalowa m’dziko lolonjezedwa sankasankha okha malo oti azikhala koma ankachita kupatsidwa. (Num. 26:52-56; Yos. 14:1, 2) Panopa sitikudziwa kuti tidzauzidwa kukakhala kuti m’dziko latsopano. Koma mtima womvera udzatithandiza kuti tisadzadandaule kukatumikira Yehova kulikonse kumene tingadzauzidwe.

8 Kukhala m’dziko latsopano n’kumalamulidwa ndi Ufumu wa Mulungu kudzakhala kosangalatsa kwambiri. N’zoona kuti zinthu zikhoza kusintha pa moyo wathu koma tiyenera kuchita zonse zimene tingathe pomvera gulu la Yehova ndiponso kugwira ntchito yake. Mwachitsanzo, abale ndi alongo ena ku Beteli ya ku United States anapemphedwa kuti apite kukachita utumiki wina. Oyang’anira oyendayenda ena anapemphedwanso kuti akachite upainiya wapadera mwina chifukwa cha uchikulire kapena mavuto ena. Onsewa akusangalala ndipo Yehova akuwadalitsa. Ifenso tiyenera kukhala okhutira, kupempha Yehova kuti atithandize komanso kuchita zonse zimene tingathe pomutumikira. Tikatero tidzakhala osangalala ndipo Yehova adzatidalitsa. (Werengani Miyambo 10:22.) Mwina tikaganizira za m’dziko latsopano timalakalaka kukakhala kwinakwake. Koma n’kutheka kuti tidzapemphedwa kukakhala kumene sitinkaganizirako. Koma kaya pa nthawiyo adzatiuza kuti tikakhale kuti kapena tigwire ntchito iti, sitikukayikira kuti tidzakhala oyamikira ndiponso osangalala.—Neh. 8:10.

9, 10. (a) Kodi tidzafunika kukhala oleza mtima pa nkhani ziti m’dziko latsopano? (b) Kodi tingasonyeze bwanji kuti ndife oleza mtima panopa?

9 Mwina pa nthawi zina m’dziko latsopano tidzafunika kukhala oleza mtima. Mwachitsanzo, tikhoza kudzamva kuti anthu ena aukitsidwa ndipo achibale awo komanso anzawo akusangalala. Koma mwina ife tidzafunika kudikirabe kuti achibale athu aukitsidwe. Ngati izi zitachitikadi, kodi tidzasangalala ndi anzathuwo n’kumadikira moleza mtima? (Aroma 12:15) Ngati panopa timayembekezera malonjezo a Yehova moleza mtima sitidzavutika kuleza mtima pa nthawiyo.Mlal. 7:8.

10 Nthawi zina gulu la Yehova limasintha mmene limafotokozera mfundo zina za m’Baibulo. Kodi timaphunzira mfundozo mwakhama n’kumakhala oleza mtima ngakhale pamene sitikuzimvetsa bwino? Ngati timatero ndiye kuti sitidzavutika kukhala oleza mtima m’dziko latsopano pamene Yehova azidzatipatsa malangizo ake.—Miy. 4:18; Yoh. 16:12.

11. Kodi Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kukhala ndi mtima wotani, ndipo mtima umenewo udzatithandiza bwanji m’dziko latsopano?

11 Chinthu china chofunika kwambiri pokonzekera moyo wa m’dziko latsopano ndi mtima wokhululuka. Paja mu Ulamuliro wa Zaka 1,000 wa Khristu mudzakhala olungama ndi osalungama, choncho padzatenga nthawi kuti anthu onse akhale angwiro. (Mac. 24:15) Kodi tidzayesetsa kuchita zinthu mwachikondi? Tiyenera kuyesetsa panopa kukhala ndi mtima wokhululuka kuti tisadzavutike pa nthawiyo.—Werengani Akolose 3:12-14.

12. Kodi zimene timachita panopa zidzatithandiza bwanji m’dziko latsopano?

12 N’kutheka kuti mwina m’dziko latsopano sitizidzapeza chilichonse pa nthawi imene tikufuna. Komabe tidzafunika kukhalabe ndi mtima woyamikira ndiponso wokhutira ndi zilizonse zimene tapatsidwa. Choncho makhalidwe amene Yehova akutiuza kuti tikhale nawo panopa adzafunikanso m’dziko latsopano. Tikamayesetsa kukhala ndi makhalidwe abwinowa ndiye kuti tikukonzekera zimene tizidzachita kwamuyaya. Tikamatero timasonyeza kuti tikuyembekezera ndiponso kukonzekera ‘dziko latsopano limene likubweralo.’ (Aheb. 2:5; 11:1) Timasonyezanso kuti tikufunitsitsa kudzakhala m’dziko lachilungamo limene aliyense azidzamvera Yehova.

TIZIKONDA KWAMBIRI KUTUMIKIRA YEHOVA PANOPA

Tizilalikira mwakhama

13. N’chiyani chidzakhala chofunika kwambiri m’dziko latsopano?

13 N’zoona kuti tidzakhala ndi chakudya chamwanaalirenji ndiponso zinthu zina zofunika zambirimbiri m’dziko latsopano. Koma tidzasangalala kwambiri chifukwa chophunzira za Yehova ndiponso kumutumikira. (Mat. 5:3) Tizidzaona kuti kulambira Yehova n’kofunika kwambiri ndipo tidzasangalaladi pomutumikira. (Sal. 37:4) Choncho pamene tikukonzekera moyo weniweniwo tiyeneranso kuona kuti kutumikira Yehova n’kofunika kwambiri.—Werengani Mateyu 6:19-21.

14. Kodi ndi zolinga ziti zimene zingathandize achinyamata kukonzekera moyo wa m’dziko latsopano?

14 Kodi tingatani kuti tizikonda kwambiri kutumikira Yehova? Chinthu chimodzi chimene tingachite ndi kukhala ndi zolinga. Ngati ndinu wachinyamata, mungachite bwino kuwerenganso nkhani zina zimene zalembedwa m’mabuku athu zokhudza utumiki wa nthawi zonse. Mukawerenga mukhoza kukhala ndi cholinga chochita utumiki winawake. * Mukhozanso kulankhula ndi anthu ena amene achita utumiki wa nthawi zonse kwa zaka zambiri. Kuchita utumiki wa nthawi zonse panopa kungakuthandizeni kukonzekera kuti mukapitirize kutumikira Mulungu m’dziko latsopano. Zimene mungaphunzire pa utumikiwo panopa zidzakuthandizani kwambiri panthawiyo.

Tizigwira nawo ntchito zosiyanasiyana m’gulu la Yehova

15. Kodi tonsefe tingakhale ndi zolinga ziti?

15 Pali zolinga zambiri zimene tonsefe tingakhale nazo. Mwachitsanzo, tingayesetse kukhala ndi luso linalake mu utumiki. Kapena tingayesetse kumvetsa bwino mfundo za m’Baibulo ndiponso mmene tingazigwiritsire ntchito. Tikhozanso kuchita khama kuti tiziwerenga bwino ndiponso kuyankha pa misonkhano. Apa mfundo ndi yakuti munthu ayenera kukhala ndi zolinga kuti azitumikira Yehova mosangalala komanso azikonzekera moyo wa m’dziko latsopano.

TAYAMBA KALE KUDALITSIDWA

Tiziwerenga mwakhama mabuku athu

16. N’chifukwa chiyani tinganene kuti kutumikira Yehova n’kosangalatsa kwambiri?

16 Kodi kukonzekera moyo wa m’dziko latsopano kukutanthauza kuti tizikhala moyo wosasangalala panopa? Ayi ndithu. Pajatu kutumikira Yehova n’kosangalatsa kwambiri kuposa china chilichonse. Sikuti timatumikira Yehova mokakamizika n’cholinga choti tingopulumuka basi. Tikutero chifukwa chakuti tinalengedwa kuti tizikonda kutumikira Mulungu. Choncho kutsogoleredwa ndi Yehova ndiponso kukhala naye pa ubwenzi n’kumene kumathandiza munthu kukhala wosangalala. (Werengani Salimo 63:1-3.) Tikamatumikira Yehova ndi mtima wonse tingapeze madalitso ambiri ngakhale panopa. Kunena zoona, enafe takhala tikulandira madalitso osiyanasiyana kwa nthawi yaitali ndipo taonadi kuti kutumikira Mulungu n’kwabwino kwambiri.—Sal. 1:1-3; Yes. 58:13, 14.

Tizifunsa nzeru kwa Akhristu anzathu

17. Kodi m’dziko latsopano tidzakhalanso ndi mwayi wotani?

17 M’dziko latsopano tidzakhalanso ndi mwayi wochita zinthu zimene zimatisangalatsa. Tikutero chifukwa chakuti Yehova anatilenga ndi mtima wofuna kuchita zimenezo. (Mlal. 2:24) Iye adzaonetsetsa kuti ‘akupereka zofuna za chamoyo chilichonse.’ (Sal. 145:16) N’zoona kuti kuchita zosangalatsa n’kothandiza, koma timasangalala nazo kwambiri ngati tayamba kaye kuchita zinthu zolimbitsa ubwenzi wathu ndi Yehova. Umu ndi mmene zidzakhalirenso m’dziko latsopano. Choncho si kulakwa kuchita zinthu zimene zimatisangalatsa koma tiyenera kuona kuti kutumikira Yehova ndiponso madalitso amene amatipatsa n’zofunika kwambiri pa moyo.—Mat. 6:33.

18. Kodi tingasonyeze bwanji kuti tikuyembekezera dziko latsopano?

18 M’dziko latsopano tidzasangalala kwambiri kuposa mmene tingaganizire. Choncho tiyeni tiyambe panopa kukonzekera moyo weniweniwo. Tiziyesetsa kusonyeza makhalidwe abwino ndiponso kulalikira mwakhama. Tizikonda kwambiri kutumikira Mulungu. Tizikhulupiriranso malonjezo a Yehova ndiponso tizisonyeza kuti tikuyembekezera dziko latsopano.