Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Samalani Ndi Anthu Ogwilizana Nao Masiku Ano Otsiliza

Samalani Ndi Anthu Ogwilizana Nao Masiku Ano Otsiliza

“Kugwilizana ndi anthu oipa kumaononga makhalidwe abwino.”—1 AKOR. 15:33.

NYIMBO: 73, 119

1. Kodi tikukhala m’nthawi yotani?

TIKUKHALA ‘m’nthawi yapadela komanso yovuta.’ Kuyambila mu 1914 pamene “masiku otsiliza” anayamba, zinthu padziko lapansi zafika poipa kwambili kuposa kale. (2 Tim. 3:1-5) Ndipo dzikoli lidzapitilizabe kuipilaipila cifukwa ulosi wa m’Baibulo unakambilatu kuti: “Anthu oipa ndi onyenga adzaipilaipilabe.”—2 Tim. 3:13.

2. Kodi anthu ambili amakonda kusangalala ndi zinthu zotani? (Onani cithunzi pamwamba.)

2 Anthu ambili amapenyelela kapena kucita zinthu zimene Baibulo limaletsa monga zaciwawa, zaciwelewele, zamizimu, ndi zinthu zina zoipa kuti asangalale. Mwacitsanzo, pa Intaneti, pa TV, m’mafilimu, m’mabuku ndi m’magazini amaonetsa kuti ciwawa ndi ciwelewele n’zabwino. Ndipo makhalidwe ena amene kale anali kuonedwa kuti ndi oipa avomelezedwa mwalamulo m’madela ena. Koma zimenezo sizitanthauza kuti Mulungu amavomeleza makhalidwe oipa amenewo.—Ŵelengani Aroma 1:28-32.

3. Kodi anthu amene amatsatila mfundo za m’Baibulo amaonedwa bwanji?

3 Otsatila a Yesu a m’nthawi ya atumwi anapewelatu zosangalatsa zoipa. Iwo anali kunyozedwa ndi kuzunzidwa cifukwa ca makhalidwe ao abwino. Mtumwi Petulo analemba kuti: “Cifukwa cakuti simukupitiliza kuthamanga nao limodzi m’cithaphwi ca makhalidwe oipa, anthu a m’dzikoli sakumvetsa, conco amakunyozani.” (1 Pet. 4:4) Masiku anonso, anthu amene amatsatila mfundo za Mulungu amaonedwa kuti ndi okhalila. Kuonjezela apo, “onse ofuna kukhala ndi moyo wodzipeleka kwa Mulungu mwa Kristu Yesu, naonso adzazunzidwa.”—2 Tim. 3:12.

“KUGWILIZANA NDI ANTHU OIPA KUMAONONGA MAKHALIDWE ABWINO”

4. Kodi Malemba amatilangiza kucita ciani ponena za dzikoli?

4 Malemba amalangiza anthu amene afuna kucita cifunilo ca Mulungu kuti asamakonde dziko ndi zinthu za m’dziko. (Ŵelengani 1 Yohane 2:15, 16.) Acipembedzo, andale, otsatsa malonda, ndiponso zinthu zimene amagwilitsila nchito kufalitsa uthenga wao zonse zimacilikizidwa ndi “mulungu wa nthawi ino,” Satana Mdyelekezi. (2 Akor. 4:4; 1 Yoh. 5:19) Conco, pokhala Akristu tiyenela kusamala ndi anthu amene timagwilizana nao. Baibulo limaticenjeza mosapita mbali kuti: “Musasoceletsedwe. Kugwilizana ndi anthu oipa kumaononga makhalidwe abwino.”—1 Akor. 15:33.

5, 6. Ndi anthu otani amene tiyenela kupewa kugwilizana nao? Nanga n’cifukwa ciani?

5 Kuti tisaononge makhalidwe athu abwino, tiyenela kupewa kugwilizana ndi anthu ocita zoipa. Mfundo imeneyi imagwilanso nchito kwa aja amene amakamba kuti amalambila Mulungu koma mwadala amaphwanya malamulo ake. Ngati Akristu amenewo acita chimo lalikulu ndipo sanalape, tifunika kuleka kugwilizana nao.—Aroma 16:17, 18.

6 Ngati tigwilizana ndi anthu amene samvela malamulo a Mulungu, tingayambe kucita zimene io amacita n’colinga cakuti atikonde. Mwacitsanzo, ngati timagwilizana ndi anthu amene amakonda ciwelewele, tingayambe kulakalaka kucita ciwelewele. Izi zacitikilapo Akristu ena odzipeleka, cakuti acotsedwa mumpingo cifukwa cakuti sanalape. (1 Akor. 5:11-13) Ndipo ngati sanalape, amakhala oipa kwambili monga mmene Petulo anafotokozela.—Ŵelengani 2 Petulo 2:20-22.

7. Kodi mabwenzi athu apamtima ayenela kukhala anthu otani?

7 Ngakhale kuti tifunika kukhala okoma mtima kwa anthu amene satsatila malamulo a Mulungu, tiyenela kusamala kuti anthuwo asakhale mabwenzi athu apamtima. N’kulakwa Mkristu wa Mboni za Yehova amene sali pabanja kukhala pacibwenzi ndi munthu amene si Mboni, ndiponso amene salemekeza miyezo yapamwamba ya Mulungu. Kukhala Mkristu wokhulupilika n’kwabwino kwambili kuposa kukondedwa ndi anthu amene satsatila malamulo a Yehova. Mabwenzi athu apamtima ayenela kukhala anthu ocita cifunilo ca Mulungu. Yesu anati: “Aliyense wocita cifunilo ca Mulungu, ameneyo ndiye m’bale wanga, mlongo wanga ndi mai anga.”—Maliko 3:35.

8. Kodi Aisiraeli anakumana ndi mavuto otani cifukwa cogwilizana ndi anthu oipa?

8 Aisiraeli anakumana ndi mavuto aakulu cifukwa cogwilizana ndi anthu oipa. Yehova atawapulumutsa ku ukapolo ku Iguputo ndi kuwatsogolela m’Dziko Lolonjezedwa, iye anawalangiza mmene anayenela kucitila zinthu ndi anthu a m’dzikolo. Iye anati: “Usawelamile milungu yao kapena kuitumikila, ndipo usapange ciliconse cofanana ndi zifanizilo zao, koma uzigwetse ndithu ndi kuphwanya zipilala zao zopatulika. Muzitumikila Yehova Mulungu wanu.” (Eks. 23:24, 25) N’zomvetsa cisoni kuti Aisiraeli ambili sanamvele malangizo a Mulungu. (Sal. 106:35-39) Conco, popeza kuti io sanakhulupilike kwa Mulungu, Yesu anawauza kuti: “Tsopano tamvelani! Mulungu wacoka n’kukusiyilani nyumba yanuyi.” (Mat. 23:38) Yehova anakana Aisiraeli, ndipo m’malo mwake, anasankha mpingo wacikristu kukhala anthu ake.—Mac. 2:1-4.

SAMALANI NDI ZIMENE MUMAŴELENGA NDI KUONELELA

9. N’cifukwa ciani tiyenela kusamala ndi zinthu zimene dzikoli limafalitsa ndi kuulutsa?

9 Zinthu zambili zimene dzikoli limafalitsa ndi kuulutsa zingaononge Akristu mwakuuzimu. Zinthu zimenezi sizingathandize Akristu kukhulupilila Yehova ndi malonjezo ake. M’malo mwake, zimalimbikitsa anthu kudalila dziko loipali la Satana. Motelo, tifunika kukhala osamala kwambili ndi zinthu zimene timaŵelenga, kuonelela, ndi kumva, zimene zingatipangitse kukhala ndi “zilakolako za dziko.”—Tito 2:12.

10. N’ciani cidzacitikila zinthu zoŵelenga ndiponso zoonelela zoipa?

10 Kuŵelenga ndi kuonelela zinthu zoipa kudzatha posacedwapa. Zonse zidzaonongedwela pamodzi ndi dziko la Satanali. Mau a Mulungu amati: “Dziko likupita limodzi ndi cilakolako cake, koma wocita cifunilo ca Mulungu adzakhala kosatha.” (1 Yoh. 2:17) Nayenso wamasalimo anaimba kuti: “Pakuti ocita zoipa adzaphedwa. Koma oyembekezela Yehova ndi amene adzalandile dziko lapansi. Koma anthu ofatsa adzalandila dziko lapansi, ndipo adzasangalala ndi mtendele woculuka.” Kodi adzasangalala mpaka liti? Baibulo limati: “Olungama adzalandila dziko lapansi, ndipo adzakhala mmenemo kwamuyaya.”—Sal. 37:9, 11, 29.

11. Kodi Mulungu amatipatsa cakudya ca kuuzimu m’njila yotani?

11 Mosiyana ndi dzikoli, gulu la Yehova limafalitsa ndi kuulutsa zinthu zimene zimatithandiza kukhala ndi makhalidwe abwino. Makhalidwe amenewa adzaticititsa kukapeza moyo wosatha. Popemphela kwa Yehova, Yesu anati: “Pakuti moyo wosatha adzaupeza akamaphunzila ndi kudziŵa za inu, Mulungu yekhayo amene ali woona, ndi za Yesu Khristu, amene inu munamutuma.” (Yoh. 17:3) Pogwilitsila nchito gulu lake, Atate wathu wakumwamba amatipatsa cakudya ca kuuzimu coculuka ndi colimbikitsa. Ndife odalitsidwa kwambili kukhala ndi magazini, mabulosha, mabuku, mavidiyo, ndi Webusaiti yathu, zimene zimacilikiza kulambila koona. Ndiponso, gulu la Yehova limakonza misonkhano imene imacitika m’mipingo yoposa 110,000 padziko lonse. Pa misonkhano ya mpingo imeneyo komanso yadela ndi yacigawo, timaphunzila mfundo za m’Baibulo zimene zimalimbitsa cikhulupililo cathu mwa Mulungu ndi malonjezo ake.—Aheb. 10:24, 25.

KWATILANI NDI KUKWATIWA KOKHA “MWA AMBUYE”

12. Fotokozani malangizo a m’Baibulo okhudza kukwatila kapena kukwatiwa kokha “mwa Ambuye.”

12 Akristu amene afuna kukwatila kapena kukwatiwa afunika kusamala ndi anthu amene amagwilizana nao. Mau a Mulungu amanena mosapita m’mbali kuti: “Musamangidwe m’goli ndi osakhulupilila, cifukwa ndinu osiyana. Pali ubale wotani pakati pa cilungamo ndi kusamvela malamulo? Kapena pali kugwilizana kotani pakati pa kuwala ndi mdima?” (2 Akor. 6:14) Baibulo limalangiza atumiki a Mulungu kuti ayenela kukwatila kapena kukwatiwa kokha “mwa Ambuye,” kutanthauza kuti ayenela kupeza Mboni yodzipeleka ndi yobatizidwa imene imatsatila ziphunzitso za m’Malemba. (1 Akor. 7:39) Akristu amene amakwatila kapena kukwatiwa kwa Mkristu mnzake, amapeza bwenzi lodzipeleka kwa Yehova ndipo limawathandiza kukhalabe okhulupilika kwa Mulungu.

13. Ndi malangizo otani okhudza cikwati amene Mulungu anapatsa Aisiraeli?

13 Yehova amawafunila zabwino atumiki ake, ndipo iye sanasinthe maganizo pankhani yokhudza cikwati. Ganizilani zimene Yehova anauza Aisiraeli ponena za anthu amene sanali kum’tumikila. Kupitila mwa Mose, iye anawalamula kuti: “Usadzacite nao mgwilizano wa ukwati. Usadzapeleke ana ako aakazi kwa ana ao aamuna ndipo usadzatenge ana ao aakazi ndi kuwapeleka kwa ana ako aamuna. Pakuti adzapatutsa ana ako aamuna kuti asanditsatile ndipo adzatumikila ndithu milungu ina. Pamenepo mkwiyo wa Yehova udzakuyakilani ndipo adzakuonongani ndithu mofulumila.”—Deut. 7:3, 4.

14, 15. N’ciani cinacitikila Solomo cifukwa conyalanyaza malangizo a Yehova?

14 Solomo mwana wa Davide atayamba kulamulila, anapempha nzelu kwa Mulungu ndipo anapatsidwa nzelu zoculuka. Mfumu Solomo anachuka kwambili cifukwa ca nzelu zake monga wolamulila. Mfumukazi ya ku Sheba itapita kukamuona Solomo, inati: “Sindinakhulupilile mauwo mpaka pamene ndabwela n’kuona ndi maso anga, ndipo ndaona kuti ndinangouzidwa hafu cabe. Nzelu zanu ndi ulemelelo wanu zaposa zinthu zimene ndinamva.” (1 Maf. 10:7) Koma citsanzo ca Solomo cikutiphunzitsanso zomwe zingacitikile munthu amene wanyalanyaza lamulo la Mulungu ndi kukwatila kapena kukwatiwa kwa munthu amene satumikila Yehova.—Mlal. 4:13.

15 Ngakhale kuti Mulungu anamucitila zinthu zabwino, Solomo ananyalanyaza lamulo la Mulungu lakuti asakwatile akazi a mitundu yowazungulila amene sanali kulambila Yehova. Solomo anakonda “akazi ambili acilendo” cakuti anadzakhala ndi akazi 700 ndiponso 300 apambali. Kodi zotsatilapo zake zinali zotani? Pamene iye anali kukalamba, akazi ake anali “atapotoza mtima wake moti iye anali kutsatila milungu ina . . . Cotelo Solomo anayamba kucita zinthu zimene zinali zoipa m’maso mwa Yehova.” (1 Maf. 11:1-6) Anthu oipa amene Solomo anagwilizana nao anamucititsa kucita zinthu mopanda nzelu moti anasiya kulambila Mulungu. Limeneli ndi cenjezo lamphamvu kwa Akristu amene afuna kukwatila kapena kukwatiwa ndi munthu amene sakonda Yehova.

16. Kodi Baibulo limapeleka malangizo otani kwa atumiki a Yehova amene ali pa banja ndi wosakhulupilila?

16 Nanga bwanji ngati munthu wakhala mlambili wa Yehova ali kale pa banja ndi munthu wosakhulupilila? Baibulo limati: “Inu akazi, muzigonjela amuna anu kuti ngati ali osamvela mau akopeke, osati ndi mau, koma ndi khalidwe lanu.” (1 Pet. 3:1) Mau amenewa amanena za akazi acikristu, koma amagwilanso nchito kwa amuna amene anakhala Mboni ali kale okwatila. Baibulo limatilangiza momveka bwino kuti: Khalani mwamuna kapena mkazi wabwino ndipo muzitsatila miyezo yapamwamba ya Mulungu yokhudza ukwati. Anthu ambili osakhulupilila anaphunzila coonadi pambuyo poona khalidwe labwino la mnzao wa m’cikwati amene anasintha ndi kutsatila zimene Mulungu amafuna.

MUZIGWILIZANA NDI ANTHU AMENE AMAKONDA YEHOVA

17, 18. N’cifukwa ciani Nowa ndi Akristu oyambilila anapulumuka cionongeko ca m’nthawi yao?

17 Kugwilizana ndi anthu oipa kungakucititseni kusamvela Yehova, koma kugwilizana ndi anthu abwino kungakuthandizeni kukhala okhulupilika kwa iye. Ganizilani za Nowa, iye anali kukhala m’dziko loipa koma sanakhale paubwenzi ndi anthu a m’dzikolo. Panthawiyo, “Yehova anaona kuti kuipa kwa anthu kwaculuka padziko lapansi, ndipo malingalilo onse a m’mitima ya anthu anali oipa okhaokha nthawi zonse.” (Gen. 6:5) Conco Yehova anaganiza zobweletsa cigumula kuti aononge dziko loipalo. Koma, “Nowa anali munthu wolungama. Iye anali wopanda colakwa pakati pa anthu a m’nthawi yake. Nowa anayenda ndi Mulungu woona.”—Gen. 6:7-9.

18 Nowa sanafune kugwilizana ndi anthu amene sanali kulambila Mulungu. Iye ndi banja lake anatangwanika ndi kucita cifunilo ca Mulungu kuphatikizapo kumanga cingalawa. Panthawi imodzimodziyo Nowa anali “mlaliki wa cilungamo.” (2 Pet. 2:5) Kulalikila, kumanga cingalawa, ndiponso kugwilizana ndi anthu a m’banja lake kunacititsa Nowa kuika maganizo ake pa kucita zinthu zabwino zimene zinakondweletsa Mulungu. Cifukwa ca ici, Nowa ndi banja lake anapulumuka pa Cigumula. Timayamikila kwambili Nowa ndi mkazi wake, kuphatikizapo ana ake aamuna ndi akazi ao cifukwa tili ndi moyo kaamba ka kukhulupilika kwao ndi kucita zinthu zokondweletsa Yehova. Akristu enanso oyambilila amene anali omvela ndi okhulupilika anali kupewa kugwilizana ndi anthu osamvela Mulungu ndipo anapulumuka ciwonongeko ca Yelusalemu mu 70 C.E.—Luka 21:20-22.

Kugwilizana ndi okhulupilila anzathu kungatithandize kuganizila za dziko latsopano (Onani ndime 19)

19. N’ciani cingatithandize kukhalabe okhulupilika kwa Yehova?

19 Ife alambili a Yehova tiyenela kutsatila citsanzo ca Nowa ndi banja lake, ndiponso Akristu oyambilila amene anali omvela. Tifunika kukhala osiyana ndi dongosolo loipali limene tikukhalamo. Pali abale ndi alongo okhulupilika mamiliyoni ambili amene tingasankhe kuti akhale anzathu. Iwo adzatithandiza ‘kukhala olimba m’cikhulupililo’ pamene tikukhala m’nthawi yovutayi. (1 Akor. 16:13; Miy. 13:20) Zidzakhaladi zosangalatsa kupulumuka mapeto a dongosolo loipali ndi kukhala m’dziko latsopano la Yehova. Conco, n’kofunika kuti tizisamala ndi anthu amene timagwilizana nao masiku ano otsiliza.