Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI A MBONI ZA YEHOVA NDI ANTHU OTANI?

Kodi Timapeza Bwanji Ndalama Zoyendetsera Ntchito Yathu?

Kodi Timapeza Bwanji Ndalama Zoyendetsera Ntchito Yathu?

Chaka chilichonse timasindikiza komanso kugawira Mabaibulo ndi mabuku kapena zinthu zina zofotokoza nkhani za m’Baibulo zokwana mamiliyoni ambiri. Timamanganso maofesi, kumene timagwirira ntchito zathu komanso nyumba zosindikizira mabuku m’mayiko osiyanasiyana. Tilinso ndi nyumba zabwino zomwe timakalambiramo Mulungu. Nyumba zimenezi timazitchula kuti Nyumba za Ufumu. Koma kodi ndalama zopangira zinthu zonsezi timazipeza bwanji?

Ndalamazi ndi zomwe anthu amapereka mwa kufuna kwawo. (2 Akorinto 9:7) M’chaka cha 1879, magazini yachiwiri ya Zion’s Watch Tower [dzina lakale la magazini ya Nsanja ya Olonda], inati: “Sitikayikira zoti YEHOVA ndi amene akutsogolera ntchito yofalitsa magazini ino ya ‘Zion’s Watch Tower,’ motero sitidzapemphetsa kwa anthu kapena kuwachonderera kuti athandize pa ntchito imeneyi.” Kuchokera nthawi imeneyo, sitinapemphetsepo ndalama ndiponso sitidzapemphetsa ndalama zoyendetsera ntchito yathu.

Anthu amatumiza okha ndalama zoyendetsera ntchitoyi ku maofesi athu, pomwe ena amaponya m’mabokosi omwe amapezeka m’Nyumba za Ufumu. Sitimapereka chakhumi, kuyendetsa mbale kapena kulipiritsa anthu omwe timaphunzira nawo Baibulo kapenanso omwe timawapatsa magazini athu. Sitipatsidwa malipiro ena alionse tikamalalikira, kuphunzitsa mumpingo kapena tikamamanga nyumba zolambiriramo. Zimenezi n’zogwirizana ndi zimene Yesu ananena zoti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere.” (Mateyu 10:8) Choncho, onse amene amagwira ntchito pa maofesi komanso kumalikulu athu, kuphatikizapo amene ali m’Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, amangodzipereka ndipo salandira malipiro alionse.

M’chaka cha 2011, Khoti Loona za Ufulu wa Anthu ku Ulaya, linati: “Ntchito zonse za Mboni za Yehova zimayendetsedwa ndi ndalama zomwe anthu amapereka mwa kufuna kwawo. Aliyense amakhala ndi ufulu wopereka ndalama zomwe angakwanitse.”

Ndalama zimene anthu amapereka zimagwiritsidwanso ntchito pothandiza anthu amene akhudzidwa ndi ngozi zachilengedwe. Zimenezi n’zimenenso Akhristu oyambirira ankachita. Akhristuwa ankathandizanso anzawo omwe akumana ndi mavuto. (Aroma 15:26) Ifenso timathandiza anthu omwe akumana ndi vuto linalake. Timawamangira nyumba komanso malo olambirira ngati awonongeka. Timawathandizanso ndi chakudya, zovala komanso mankhwala.