Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

Kodi Mukuyesetsa Kukhala Ngati Khristu?

Kodi Mukuyesetsa Kukhala Ngati Khristu?

‘Tifike pa msinkhu wauchikulire umene Khristu anafikapo.’—AEF. 4:13.

NYIMBO: 69, 70

1, 2. Kodi Mkhristu aliyense ayenera kuyesetsa kuchita chiyani, nanga tingaziyerekezere ndi chiyani?

MUNTHU akamagula zipatso mumsika, sikuti amangoyang’ana zikuluzikulu kapena zotchipa. Koma amasankha zipatso zimene zapsa bwinobwino. Amafuna zimene zili zokoma, zonunkhira bwino komanso zothandiza m’thupi.

2 Nayenso munthu amene wadzipereka kwa Mulungu ndiponso kubatizidwa tingamuyerekezere ndi chipatso. Iye amafunika kupitiriza kukula mpaka kukhala Mkhristu wolimba kapena kuti wolimba. Choncho ayenera kupitiriza kulimbitsa ubwenzi wake ndi Mulungu. Mtumwi Paulo analembera kalata Akhristu a ku Efeso kuti awalimbikitse kuchita zimenezi. Iye anawauza kuti ‘afike pa umodzi m’chikhulupiriro komanso pa kumudziwa molondola Mwana wa Mulungu, inde, kufikira adzakhale achikulire, ofika pa msinkhu umene Khristu anafikapo.’—Aef. 4:13.

3. Kodi Akhristu masiku ano amafanana bwanji ndi anthu a mumpingo wa ku Efeso?

3 Pamene Paulo ankalemba kalatayi, mpingo wa ku Efeso unali utakhazikitsidwa zaka zingapo zapitazo. Anthu ambiri mumpingowu anali atafika pokhala Akhristu olimba. Koma ena ankafunikabe kulimbitsa ubwenzi wawo ndi Mulungu. Ndi mmene zililinso ndi Mboni za Yehova masiku ano. Abale ndi alongo ambiri akhala akutumikira Mulungu kwa nthawi yaitali ndipo ndi Akhristu olimba. Koma pali ena amene sanafikebe pamenepo. Mwachitsanzo, chaka chilichonse anthu ambirimbiri amabatizidwa ndipo amafunika kupitiriza kukula mpaka kufika pokhala Akhristu olimba. Kodi inuyo muli m’gulu la anthu oterewa?—Akol. 2:6, 7.

KODI AKHRISTU ANGAKULE BWANJI?

4, 5. Kodi Akhristu olimba akhoza kukhala osiyana pa zinthu ziti, nanga amafanana pa zinthu ziti? (Onani chithunzi patsamba 3.)

4 Zipatso zingakhale zosiyanasiyana koma pali zinthu zina zofanana zimene zimaonetsa kuti zipatsozo ndi zakupsa. Nawonso Akhristu olimba akhoza kukhala osiyana mitundu, mayiko, msinkhu kapena zimene achita pa moyo wawo. Akhozanso kusiyana chikhalidwe kapena zimene amakonda. Koma pali makhalidwe ena amene onsewa amakhala nawo omwe amasonyeza kuti ndi Akhristu olimba. Kodi ena mwa makhalidwe amenewo ndi ati?

5 Mkhristu wolimba amayesetsa ‘kutsatira mapazi a Yesu mosamala kwambiri.’ (1 Pet. 2:21) Yesu ananena kuti tiyenera kukonda Yehova ndi mtima wathu wonse, moyo wathu wonse ndi maganizo athu onse. Ananenanso kuti tiyenera kukonda anzathu mmene timadzikondera tokha. (Mat. 22:37-39) Mkhristu wolimba amayesetsa kutsatira malangizo amenewa. Iye amasonyeza kuti kukhala pa ubwenzi wolimba ndi Yehova ndiponso kukonda kwambiri anzake ndi kofunika kwambiri.

Akhristu achikulire amasonyeza kuti ndi odzichepetsa akamachita zinthu mogwirizana ndi achinyamata amene akutsogolera masiku ano (Onani ndime 6)

6, 7. (a) Kodi Mkhristu wolimba amakhala ndi makhalidwe ati? (b) Kodi tiyenera kudzifunsa funso liti?

6 Koma pali makhalidwe enanso amene Mkhristu wolimba amasonyeza. (Agal. 5:22, 23) Amakhala wofatsa, wodziletsa ndiponso woleza mtima. Makhalidwe amenewa amamuthandiza kuti akakumana ndi mavuto asamakwiye kapena kutaya mtima. Mkhristu wolimba akamaphunzira Baibulo payekha, amafufuza mfundo zimene zingamuthandize kusiyanitsa zoyenera ndi zolakwika. Ndiyeno amatsatira zimene waphunzirazo n’kumasankha zinthu zimene sizingasokoneze ubwenzi wake ndi Yehova. Amakhala wodzichepetsa n’kumakumbukira kuti nthawi zonse malangizo ndiponso mfundo za Yehova n’zothandiza kuposa maganizo ake. * Amalalikiranso mwakhama komanso amathandiza kuti mpingo ukhale wogwirizana.

7 Kaya tatumikira Yehova kwa nthawi yaitali bwanji, tiyenera kudzifunsa kuti, ‘Kodi pali zinthu zina zimene ndiyenera kusintha kuti ndikhale Mkhristu wolimba n’kumafanana ndi Yesu?’

“CHAKUDYA CHOTAFUNA NDI CHA ANTHU OKHWIMA MWAUZIMU”

8. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti ankamvetsa bwino Malemba?

8 Yesu Khristu ankadziwa bwino kwambiri Mawu a Mulungu. Ngakhale pamene anali ndi zaka 12 zokha, ankatha kukambirana Malemba ndi aphunzitsi a kukachisi. Baibulo limanena kuti: “Onse amene anali kumumvetsera anadabwa kwambiri ndi mayankho ake komanso poona kuti anali womvetsa zinthu kwambiri.” (Luka 2:46, 47) Yesu atayamba utumiki wake, ankathanso kuyankha adani ake pogwiritsa ntchito Mawu a Mulungu moti iwo ankasowa chonena.—Mat. 22:41-46.

9. (a) Kodi Mkhristu ayenera kuchita chiyani kuti akhale wolimba? (b) Kodi tiyenera kukhala ndi cholinga chiti tikamaphunzira Baibulo?

9 Mkhristu amene akufuna kufanana ndi Yesu amayesetsanso kudziwa bwino Baibulo. Iye amaliphunzira mozama podziwa kuti “chakudya chotafuna ndi cha anthu okhwima mwauzimu.” (Aheb. 5:14) Mkhristu wolimba amafunitsitsa kuti ‘adziwe molondola Mwana wa Mulungu.’ (Aef. 4:13) Kodi inuyo mumawerenga Baibulo tsiku lililonse? Kodi mumaphunzira Baibulo panokha ndiponso kuchita Kulambira kwa Pabanja mlungu uliwonse? Mukamaphunzira Baibulo, muzifufuza mfundo zimene zingakuthandizeni kumvetsa bwino mmene Yehova amaonera zinthu. Kenako muziyesetsa kugwiritsa ntchito mfundozo posankha zochita n’cholinga choti mulimbitse ubwenzi wanu ndi Yehova.

10. Kodi chimachitika n’chiyani ngati Mkhristu wolimba amaphunzira Mawu a Mulungu mwakhama?

10 Koma Mkhristu wolimba amazindikira kuti kungodziwa bwino Baibulo si kokwanira. Iye ayeneranso kukonda kwambiri mfundo zimene amaphunzira zokhudza Mulungu. Ndiyeno amaona kuti kuchita zimene Yehova amafuna n’kofunika kwambiri kuposa zofuna zake. Iye amayesetsa kusintha maganizo ake ndiponso zochita zake kuti zigwirizane ndi mfundo za Yehova. Amayesetsanso “kuvala umunthu watsopano umene unalengedwa mogwirizana ndi chifuniro cha Mulungu” ndipo amatsatira “zofunika pa chilungamo chenicheni ndi pa kukhulupirika.” (Werengani Aefeso 4:22-24.) Anthu amene analemba Baibulo ankatsogoleredwa ndi mzimu woyera wa Mulungu. Choncho munthu akamaphunzira Baibulo mwakhama n’kumakonda mfundo zake amatsogoleredwanso ndi mzimu woyera. Izi zimamuthandiza kuti akhale Mkhristu wolimba.

TIZIYESETSA KUGWIRIZANA MUMPINGO

11. Kodi anthu amene Yesu ankakhala nawo anali ndi mavuto ati?

11 Pamene Yesu anali padzikoli, ankakhala ndi anthu ochimwa. Nawonso makolo ake ndi achibale ake sanali angwiro. Ngakhale ophunzira ake enieniwo ankakangananso chifukwa chotengera maganizo odzikuza amene anthu ambiri anali nawo. Mwachitsanzo, usiku woti Yesu aphedwa mawa lake, “panabuka mkangano woopsa pakati pawo za amene anali kuoneka wamkulu kwambiri.” (Luka 22:24) Koma Yesu sankakayikira zoti ophunzirawo adzakhala Akhristu olimba n’kupanga mpingo wogwirizana. Usiku womwewo, Yesu anapempherera atumwi akewo ponena kuti: “Onsewa akhale amodzi, mmene inu Atate ndi ine tilili ogwirizana, kuti iwonso akhale ogwirizana ndi ife, . . . kuti iwo akhale amodzi mmene ifenso tilili amodzi.”—Yoh. 17:21, 22.

12, 13. (a) Kodi lemba la Aefeso 4:15, 16 limatilimbikitsa kuchita chiyani mumpingo? (b) N’chiyani chinathandiza m’bale wina kuti ayambe kugwirizana ndi anthu mumpingo?

12 Mkhristu wolimba amathandiza kuti mpingo ukhale wogwirizana. (Werengani Aefeso 4:1-6, 15, 16.) Tonsefe timafuna kuti tizichita zinthu mogwirizana mumpingo. Koma kuti zimenezi zitheke, Mawu a Yehova amasonyeza kuti tiyenera kukhala odzichepetsa. Mkhristu wolimba amadzichepetsa n’kumayesetsa kukhala mwamtendere ndi Akhristu anzake ngakhale pamene iwo alakwitsa zinazake. Kodi inuyo mumatani ngati munthu wina mumpingo wakukhumudwitsani kapena walakwitsa zinthu zina? Kodi mumayamba kumupewa ndiponso kusiya kumulankhula? Kapena kodi mumayesetsa kukonza ubwenzi wanu ndi munthuyo? Mkhristu wolimba amayesetsa kuthetsa vutolo osati kulikulitsa.

13 Chitsanzo chabwino pa nkhaniyi ndi m’bale wina dzina lake Uwe. Kale ankakhumudwa kwambiri chifukwa cha zinthu zimene abale ndi alongo ankalakwitsa. Koma kenako anayamba kuphunzira za Davide m’Baibulo ndiponso m’mabuku athu ena. N’chifukwa chiyani anasankha kuphunzira za Davide? Uwe anati: “Atumiki a Yehova ena ankachitira Davide zinthu zoipa. Mwachitsanzo, Mfumu Sauli ankafuna kumupha ndipo anthu ena anafuna kumuponya miyala. Ngakhale mkazi wake anamulankhula mwachipongwe. (1 Sam. 19:9-11; 30:1-6; 2 Sam. 6:14-22) Koma Davide sankalola kuti zochita za anthu ena zimulepheretse kupitiriza kukonda Yehova.” Uwe ananenanso kuti: “Khalidwe lina limene Davide anali nalo linali chifundo ndipo ndinazindikira kuti inenso ndiyenera kukhala ndi khalidwe limeneli. Zimene ndinaphunzirazo zinandithandiza kusintha mmene ndimaonera zolakwa za Akhristu anzanga. Panopa ndinasiya kuganizira zimene ena amalakwitsa ndipo ndimayesetsa kuthandiza kuti mpingo ukhale wogwirizana.” Kodi inunso mumayesetsa kuchita zimenezi?

PEZANI ANZANU M’GULU LA YEHOVA

14. Kodi Yesu ankasankha anthu otani kuti akhale anzake apamtima?

14 Yesu Khristu ankacheza ndi wina aliyense. Zimenezi zinachititsa kuti anthu azimasuka naye, kaya akhale amuna, akazi, achinyamata, achikulire ngakhalenso ana. Komatu Yesu ankasamala kwambiri posankha anzake apamtima. Iye anauza atumwi ake okhulupirika kuti: “Mupitiriza kukhala mabwenzi anga mukamachita zimene ndikukulamulani.” (Yoh. 15:14) Yesu anasankha anthu amene ankatumikira Yehova ndi mtima wonse kuti akhale anzake apamtima. Kodi inunso mumasankha anthu amene amatumikira Yehova mokhulupirika kuti akhale anzanu apamtima? Tiyeni tsopano tikambirane ubwino wochita zimenezi.

15. Kodi chingachitike n’chiyani ngati achinyamata asankha kucheza ndi Akhristu amene akhala akutumikira Yehova mokhulupirika?

15 Zipatso zambiri zimapsa bwino kukakhala kadzuwa. Ndiyeno chikondi cha abale ndi alongo chimakhala ngati kadzuwa kothandiza kuti nafenso tifike pokhala Akhristu olimba. Tiyerekeze kuti ndinu wachinyamata ndipo mukuganizira zimene mungachite pa moyo wanu. Kucheza ndi anthu amene akhala akutumikira Yehova mokhulupirika ndiponso mogwirizana ndi mpingo kungakuthandizeni kwambiri. Anthu oterewa ayenera kuti akumanapo ndi mavuto pa moyo wawo komanso potumikira Mulungu. Choncho akhoza kukuthandizani kusankha bwino zimene mungachite pa moyo wanu. Kucheza nawo kungakuthandizeni kuti muzisankha zinthu mwanzeru komanso kuti mukule mpaka kufika pokhala Akhristu olimba.—Werengani Aheberi 5:14.

16. Kodi Akhristu olimba anathandiza bwanji mlongo wina?

16 Mlongo wina dzina lake Helga ananena kuti atatsala pang’ono kumaliza sukulu, anzake kusekondale ankakambirana zolinga zawo. Ambiri ankafuna kupita kuyunivesite n’cholinga choti adzapeze ntchito yabwino. Koma Helga anakambirana nkhaniyi ndi anzake a mumpingo. Iye anati: “Ambiri mwa anzangawa ndi aakulu kuposa ineyo ndipo anandithandiza kwambiri. Anandilimbikitsa kuyamba utumiki wa nthawi zonse. Nditamaliza sukulu ndinachita upainiya kwa zaka 5. Panopa padutsa zaka zambiri kuchokera nthawi imeneyo ndipo ndikusangalala kuti ndinachita zambiri potumikira Yehova ndili wachinyamata. Sindinong’oneza bondo ngakhale pang’ono.”

17, 18. Kodi tingatani kuti tizitumikira bwino Yehova?

17 Zinthu zikhoza kutiyendera bwino tikamayesetsa kutsanzira Yesu. Ubwenzi wathu ndi Yehova udzalimba kwambiri komanso tidzakhala ndi mtima wofuna kuchita zambiri pomutumikira. Munthu amatumikira bwino Yehova akafika pokhala Mkhristu wolimba. Yesu anauza otsatira ake kuti: “Onetsani kuwala kwanu pamaso pa anthu, kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kuti alemekeze Atate wanu wakumwamba.”—Mat. 5:16.

18 Monga tanena kale, Akhristu olimba amathandiza kwambiri mumpingo. Akafuna kusankha zochita, chikumbumtima chawo chimawalimbikitsa kutsatira Mawu a Mulungu. Koma kodi tingatani kuti chikumbumtima chizitithandiza kusankha bwino zochita? Nanga tingalemekeze bwanji zimene anzathu asankha mogwirizana ndi chikumbumtima chawo? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso amenewa.

^ ndime 6 Mwachitsanzo, abale achikulire angapatsidwe malangizo oti asiye kuyang’anira zinthu zina m’gulu la Yehova n’kulola kuti achinyamata apitirize. Ndiyeno achikulirewo angachite bwino kuchita zinthu mogwirizana ndi achinyamatawo.