Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI MUNTHU YEMWE MUNKAMUKONDA AKAMWALIRA?

Kodi Tingalimbikitse Bwanji Amene Ali Ndi Chisoni?

Kodi Tingalimbikitse Bwanji Amene Ali Ndi Chisoni?

Kodi munayamba mwasowapo chonena pamene munkafuna kutonthoza munthu yemwe ankalira maliro a wachibale wake? Nthawi zina timangokhala chete chifukwa chosowa zonena kapena zimene tingachite. Komatu pa nthawiyi tingathe kuchita zinazake zomwe zingathandize munthuyo.

Chinthu chofunika kwambiri ndi kupita kumaliroko, n’kuuza woferedwayo mawu enaake achidule monga akuti, “Pepani kwambiri.” Anthu a zikhalidwe zina amatha kukumbatira kapena kusisita woferedwayo padzanja ndipo zimenezi zimasonyeza kuti akumuganizira. Ngati woferedwayo akunena zinazake, muzimumvetsera mosonyeza kuti mukumumvetsa. Mungachitenso bwino kwambiri kugwira ntchito zina monga kuphika, kusamalira ana kapenanso kumuthandiza zinthu zina zokhudza dongosolo la maliro ngati m’pofunika kutero. Ndipotu kuchita zimenezi kungamuthandize kwambiri kuposa kungomuuza mawu olimbikitsa.

Pakapita nthawi mukhoza kumafotokoza zinthu zina zokhudza munthu yemwe anamwalirayo monga makhalidwe abwino kapena zinthu zina zosangalatsa zomwe munkachitira naye limodzi. Woferedwayo angasangalale kwambiri mutakambirana naye nkhani ngati zimenezi. Mwachitsanzo, mayi wina dzina lake Pam, yemwe mwamuna wake anamwalira zaka 6 zapitazo anati: “Nthawi zina anthu amandiuza zinthu zabwino zimene mwamuna wanga Ian ankachita ndipo zimenezi zimandisangalatsa kwambiri.”

Kafukufuku wina anasonyeza kuti anthu amakonda kuthandiza munthu pa nthawi imene wangoferedwa. Koma pakangodutsa nthawi amasiyiratu kumuthandiza. Ndiyetu mungachite bwino kwambiri kumapitabe kumakamuona woferedwayo nthawi zonse. * Anthu ambiri amene aferedwa amasangalala mukamawachezera pafupipafupi chifukwa zimawathandiza kuti asamangokhalira kumva chisoni.

Taganizirani zimene zinachitikira mtsikana wina wa ku Japan dzina lake Kaori. Mayi ake atamwalira, panangodutsa chaka ndi miyezi itatu mchemwali wakenso n’kumwalira. Koma chosangalatsa n’choti anzake sanasiye kumulimbikitsa. Pa anzakewa panali mayi ena dzina lawo a Ritsuko, omwe ankayesetsa kumulimbikitsa ndi kumukonda kwambiri. Kaori ananena kuti: “Kunena zoona sizinkandisangalatsa kuti a Ritsuko azichita zimenezi, chifukwa sindinkafuna kuti aliyense azichita zinthu zofuna kuti ndizimuona ngati mayi anga. Ndinkaonanso kuti palibe amene angakwanitse kuchita zimene mayi anga ankachita. Komabe a Ritsuko ankandikonda kwambiri ndipo nanenso ndinayamba kuwakonda ngati mayi anga. Mlungu uliwonse tinkapitira limodzi kolalikira ndiponso kumisonkhano yampingo. Nthawi zambiri ankandiitanira kunyumba kwawo, kundibweretsera zakudya komanso ankandilembera makalata. Zonse zimene a Ritsuko ankandichitira zinandithandiza kwambiri.”

Patha zaka 12 kuchokera pamene mayi a Kaori anamwalira. Panopo Kaori anakwatiwa ndipo amalalikira nthawi zonse limodzi ndi mwamuna wake. Kaori ananenanso kuti: “A Ritsuko sanasiyebe kundilimbikitsa. Nthawi zonse ndikapita kwa bambo anga, ndimayesetsa kupita kunyumba kwawo kukawaona ndipo ndikamacheza nawo amandilimbikitsa kwambiri.”

Chitsanzo china ndi cha a Poli, omwe amakhala ku Cyprus ndipo ndi a Mboni za Yehova. Amuna awo dzina lawo a Sozos anali ndi chotupa muubongo ndipo anamwalira ali ndi zaka 53. A Sozos ankakondana kwambiri ndi akazi awo ndipo ankakondanso kuitanira ana ndi akazi amasiye kunyumba kwawo kuti akacheze ndi kudyera nawo limodzi chakudya. (Yakobo 1:27) A Poli ananena kuti: “Ndimadandaula kuti imfa inanditengera mwamuna wanga wokhulupirika yemwe ndinakhala naye pabanja kwa zaka 33.” Komabe iwo amasangalala chifukwa anzawo amawalimbikitsa nthawi zonse.

Mungachite zinthu zosiyanasiyana pothandiza amene ali ndi chisoni

Kenako a Poli anasamukira ku Canada ndi mwana wawo wazaka 15 dzina lake Daniel. Atafika kumeneko sanachedwe kuyamba kusonkhana ndi mpingo wa Mboni za Yehova wa m’dera limene ankakhala. A Poli ananena kuti: “Anthu a mumpingo watsopanowu sankadziwa zimene zinatichitikira komanso mavuto amene tikukumana nawo. Komabe iwo ankatimasukira ndi kutilimbikitsa potichitira zinthu zabwino ndiponso kutiuza mawu olimbikitsa. Zimenezi zinali zothandiza kwambiri chifukwa mwana wanga ankawasowa kwambiri bambo ake. Akulu a mumpingo umene tinkasonkhanawo ankamukondanso kwambiri Daniel. Ndipo mkulu wina ankayesetsa kumutenga akamapita kocheza kapenanso kosewera mpira.” Panopa Daniel ndi mayi ake akusangalala kwambiri.

Zimene zafotokozedwa m’nkhaniyi zikusonyeza kuti pali zambiri zimene tingachite kuti tilimbikitse anthu amene ali ndi chisoni. Baibulo limanenanso zinthu zosangalatsa zomwe tikuyembekezera mtsogolomu ndipo zimenezi zimatitonthoza.

^ ndime 6 Anthu ena amalemba tsiku limene winawake anamwalira n’cholinga choti azikumbukira kulimbikitsa woferedwayo tsikulo lisanafike kapena likafika.