Pitani ku nkhani yake # link, for screen reader ##

Pitani ku mitu ya nkhani

NKHANI YA PACHIKUTO | KODI MUNGATANI MUNTHU YEMWE MUNKAMUKONDA AKAMWALIRA?

Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo

Anthu Amene Anamwalira Adzakhalanso Ndi Moyo

Mwina mukukumbukira kuti a Gail omwe tawatchula m’nkhani yachiwiri ija, ankakayikira zoti adzaiwala imfa ya amuna awo a Robert. Komabe panopa akuyembekezera kudzaonananso ndi amuna awo m’dziko latsopano limene Mulungu walonjeza. A Gail anati: “Lemba limene limandisangalatsa kwambiri ndi la Chivumbulutso 21:3, 4.” Lembali limati: “Mulunguyo adzakhala nawo. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwawo, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulira, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”

A Gail ananenanso kuti: “Lembali limandikhazika mtima pansi. Komabe ndimamvera chisoni kwambiri anthu amene sadziwa kuti n’zotheka kudzaonananso ndi achibale awo omwe anamwalira.” Panopa a Gail amakonda kugwira ntchito yolalikira ndipo amauza anthu zimene Mulungu walonjeza zoti kutsogoloku “imfa sidzakhalaponso.”

Yobu ankadziwa kuti Mulungu adzamuukitsa

Mwina munganene kuti zimenezi n’zosatheka. Koma taonani zimene Yobu ananena atadwala mwakayakaya. (Yobu 2:7) Pa nthawiyi Yobu ankalakalaka atafa, komabe ankakhulupirira kuti Mulungu akhoza kudzamuukitsa. Iye anati: “Zikanakhala bwino mukanandibisa m’Manda . . . Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha. Mudzalakalaka ntchito ya manja anu.” (Yobu 14:13, 15) Yobu ankadziwa kuti ngati atamwalira, Mulungu angalakelake kumuonanso, zomwe zingapangitse kuti amuukitse.

Posachedwapa dzikoli likadzakhala paradaiso, Mulungu adzaukitsa Yobu komanso anthu ena ambiri. (Luka 23:42, 43) Imeneyi si nkhambakamwa chifukwa lemba la Machitidwe 24:15 limatitsimikizira kuti “kudzakhala kuuka.” Yesu naye ananenanso kuti: “Musadabwe nazo zimenezi, chifukwa idzafika nthawi pamene onse ali m’manda achikumbutso adzamva mawu ake ndipo adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29) Yobu adzaona mmene Mulungu adzakwaniritsire lonjezo limeneli. Ndipo iye adzakhalanso ndi “mphamvu” komanso thupi lake lidzakhala losalala ‘kuposa mmene analili ali mnyamata.’ (Yobu 33:24, 25) Zimenezi zidzachitikiranso anthu onse amene amatumikira Mulungu mokhulupirika.

Mwina mfundo zimene takambirana m’nkhaniyi sizingathetseretu chisoni chanu ngati munthu amene munkamukonda anamwalira. Komabe kuganizira zimene Mulungu walonjeza m’Baibulo kungakuthandizeni kudziwa kuti mudzaonananso ndi anthu amene anamwalira komanso kuti musamangokhala ndi chisoni.—1 Atesalonika 4:13.

Kodi mukufuna kudziwa mfundo zinanso zomwe zingakuthandizeni mukakhala ndi chisoni? Kapena mukufunanso mutadziwa kuti “N’chifukwa chiyani Mulungu walola kuti zoipa zizichitika komanso kuti anthu azivutika?” Ngati ndi choncho, pitani pawebusaiti yathu ya jw.org/ny kuti mupeze mfundo zomwe zingakuthandizeni komanso mayankho a mafunso amene muli nawo.