Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO | MUNTHU AMENE MUMAKONDA AKAMWALILA

Akufa Adzakhalanso ndi Moyo

Akufa Adzakhalanso ndi Moyo

Kumbukilani kuti Gail amene tamuchula m’nkhani zapita zija, anakaikila ngati adzakwanitsa kupilila imfa ya mwamuna wake Rob. Komabe, iye ali ndi ciyembekezo cakuti adzaonananso naye m’dziko latsopano la Mulungu. Iye anati: “Ndimakonda lemba la Chivumbulutso 21:3, 4. Lembali limati: “Iye adzakhala pamodzi nao, ndipo io adzakhala anthu ake. Zoonadi, Mulunguyo adzakhala nao. Iye adzapukuta misozi yonse m’maso mwao, ndipo imfa sidzakhalaponso. Sipadzakhalanso kulila, kapena kubuula, ngakhale kupweteka. Zakalezo zapita.”

Gail anati: “Lonjezo limeneli ndi lolimbikitsa kwambili. Ndimacitila cifundo anthu amene okondedwa ao anamwalila, amenenso sadziŵa za ciyembekezo cakuti akufa adzaukitsidwa.” Gail amacita zinthu mogwilizana ndi zimene amakhulupilila mwa kugwila nchito yodzipeleka monga mlaliki wa nthawi zonse. Iye amauzako anzake za lonjezo la Mulungu limene lidzakwanilitsidwa mtsogolo lakuti “imfa sidzakhalaponso.”

Yobu anali ndi cidalilo cakuti adzakhalanso ndi moyo

Mwina mungakambe kuti zimenezo ‘n’zosatheka.’ Koma kumbukilani citsanzo ca munthu wina dzina lake Yobu. Iye anadwala kwambili. (Yobu 2:7) Ngakhale kuti Yobu analakalaka kufa, anali ndi cikhulupililo cakuti Mulungu adzamuukitsa n’kukhalanso ndi moyo. Yobu anati: “Zikanakhala bwino mukanandibisa m’Manda, . . . Inu mudzaitana ndipo ine ndidzayankha. Mudzalakalaka nchito ya manja anu.” (Yobu 14:13, 15) Yobu anali ndi cidalilo cakuti Mulungu adzamukumbukila ndi kumuukitsa.

Posacedwapa, Mulungu adzaukitsa Yobu limodzi ndi ena ambili, dzikoli likadzakhala paladaiso. (Luka 23:42, 43) Lemba la Machitidwe 24:15 limatitsimikizila kuti: “Kudzakhala kuuka.” Yesu nayenso akutitsimikizila kuti: “Musadabwe nazo zimenezi, cifukwa idzafika nthawi pamene onse ali m’manda acikumbutso adzamva mau ake ndipo adzatuluka.” (Yohane 5:28, 29) Yobu adzaona lonjelo limeneli likukwanilitsidwa. Iye adzakhalanso ndi ‘mphamvu monga mmene analili pa unyamata wake,’ ndipo ‘mnofu wake udzasalala kuposa wa mwana.’ (Yobu 33:24, 25) Izi n’zimene zidzacitikila anthu amene amayamikila makonzedwe acikondi a Mulungu, akuti akufa adzakhalanso ndi moyo padziko lapansi.

Ngati munthu amene mumakonda anamwalila, mwina mukuona kuti mfundo zimene takambilanazi sizingathetseletu cisoni canu. Koma kuganizila mozama malonjezo a Mulungu opezeka m’Baibulo, kudzakuthandizani kukhala ndi ciyembekezo komanso mphamvu zakuti mupilile cisoni.—1 Atesalonika 4:13.

Kodi mufuna kudziŵa zambili zokhudza zimene mungacite kuti mupilile cisoni canu? Kapena kodi mufuna kupeza mayankho a mafunso monga lakuti “N’cifukwa ciani Mulungu amalolela kuti anthu azivutika?” Pitani pa webusaiti yathu ya jw.org kuti mupeze mayankho otonthoza ndi othandiza a m’Baibulo.